LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es26 masa. 37-46
  • April

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • April
  • Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
  • Tumitu
  • Citatu, April 1
  • TSIKU LA CIKUMBUTSO
    Dzuwa Likalowa
    Cinai, April 2
  • Cisanu, April 3
  • Ciwelu, April 4
  • Sondo, April 5
  • Mande, April 6
  • Ciwili, April 7
  • Citatu, April 8
  • Cinai, April 9
  • Cisanu, April 10
  • Ciwelu, April 11
  • Sondo, April 12
  • Mande, April 13
  • Ciwili, April 14
  • Citatu, April 15
  • Cinai, April 16
  • Cisanu, April 17
  • Ciwelu, April 18
  • Sondo, April 19
  • Mande, April 20
  • Ciwili, April 21
  • Citatu, April 22
  • Cinai, April 23
  • Cisanu, April 24
  • Ciwelu, April 25
  • Sondo, April 26
  • Mande, April 27
  • Ciwili, April 28
  • Citatu, April 29
  • Cinai, April 30
Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
es26 masa. 37-46

April

Citatu, April 1

Zimene Atate wanga akufuna ndi zoti aliyense wovomeleza Mwana komanso kumukhulupilila akhale ndi moyo wosatha.​—Yoh. 6:40.

Kuti tikapindule cifukwa ca mnofu wa Yesu komanso magazi ake, tiyenela kuonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo. (Aef. 1:7) A “nkhosa zina” sayenela kudya mkate kapena kumwa vinyo pocita mwambo wa Mgonelo wa Ambuye. (Yoh. 10:16) Ngakhale n’telo, iwo amapindula na mnofu wa Yesu Khristu komanso magazi ake. Amacita zimenezi poonetsa cikhulupililo mu nsembe ya dipo ya Yesu komanso mu madalitso amene nsembeyo imatheketsa. (Yoh. 6:53) Mosiyanako na zimenezi, aja amene ayenela kudya kudya mkate komanso kumwa vinyo amaonetsa kuti analowa m’pangano latsopano ndipo ali na ciyembekezo cokalamulila monga mafumu kumwamba. Conco, kaya ndife a nkhosa zina kapena odzozedwa, tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba mu nsembe ya dipo kuti tikakhale na moyo wosatha. w24.12 13 ¶14, 16

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 12) Mateyo 26:​1-5, 14-16; Luka 22:​1-6

TSIKU LA CIKUMBUTSO
Dzuwa Likalowa
Cinai, April 2

Musaope, kagulu ka nkhosa inu, cifukwa Atate wanu wavomeleza kukupatsani Ufumu.​—Luka 12:32.

Pamene Yesu anali kuyambitsa Mgonelo wa Ambuye, anapatsa ophunzila ake mkate wopanda cofufumitsa ndipo anawauza kuti unali kuimila thupi lake. Kenako atawapatsa kapu ya vinyo, anawauza kuti vinyowo unali kuimila “magazi a pangano.” (Maliko 14:​22-25; Luka 22:20; 1 Akor. 11:24) Pangano latsopano limeneli limapangidwa na a ‘m’nyumba [yauzimu] ya Isiraeli,’ amene adzalamulila pamodzi na Yesu “mu Ufumu wa Mulungu,” (Aheb. 8:​6, 10; 9:15) Zimene Yesu anakamba pa Mgonelo wa Ambuye zinali kupita kwa kagulu kocepa kochedwa “kagulu ka nkhosa.” Atumwi ake okhulupilika amene analipo pomwe anali kuyambitsa mwambowo, ndiwo anayambilila kukhala m’kagulu kocepa kameneka. Anthu amenewa ndiwo adzapita kumwamba kukakhala na Yesu. w24.12 11 ¶9-10

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 13) Mateyo 26:​17-19; Maliko 14:​12-16; Luka 22:​7-13 (Zocitika dzuwa likalowa: Nisani 14) Yohane 13:​1-5; 14:​1-3

Cisanu, April 3

Mulungu anakonda kwambili dziko moti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupilila asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.​—Yoh. 3:16.

Yesu anapelekedwa m’manja mwa anthu, anamangidwa, ananyozedwa, anatonzedwa, anamenyedwa, ndipo pamapeto pake anagamulidwa kuti aphedwe. Asilikali anamutengela kumalo kumene anali kudzamupacikila, ndipo anamukhomelela pamtengo. Yesu anapilila zoŵaŵa komanso mavuto amenewa mokhulupilika. Komabe, Yehova anavutika koposelapo pomuona Mwana wakeyo akuvutika. Yehova ali na mphamvu zopanda malile. Conco akanafuna, akanaloŵelelapo kuti Mwana wake asafe imfa yowawa imeneyo. Koma sanatelo. Cifukwa ciyani? Cikondi n’cimene cinamupangitsa kuti acite zimenezi komanso kukula kwa cikondi cimene Yehova ali naco pa imwe. Iye anapeleka Mwana wake na kupilila zambili kuti akupulumutseni ku ucimo na imfa. (1 Yoh. 4:​9, 10) Iye amafuna kuthandiza aliyense wa ife kupambana polimbana na ucimo! w24.08 6 ¶13-14

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 14) Yohane 19:​1-42

Ciwelu, April 4

Khristu anavutika cifukwa ca inu.​—1 Pet. 2:21.

Kuti timvetse mmene Yehova amatikondela, tiyenela kuganizila mmene zinamupwetekela kuona Mwana wake akuvutika. Satana amakamba kuti palibe angakhalebe wokhulupilika kwa Mulungu panthawi zovuta. Pofuna kuonetsa kuti zimenezo n’zabodza, Yehova analola Yesu kuvutika asanamwalile. (Yobu 2:​1-5) Yehova anali kuona pamene anthu anali kunyoza Yesu, pamene asilikali anali kumumenya, komanso pamene anali kumukhomelela pamtengo. Kenako Yehova anaona pamene Mwana wake wokondeka anali kufa imfa yowawa. (Mat. 27:​28-31, 39) Yehova anali nazo mphamvu zothetsa kuvutika kwa Mwana wake. (Mat. 27:​42, 43) Komabe, Mulungu akanacita zimenezo, dipo silikanapelekedwa, ndipo anthufe tikanakhala opanda ciyembekezo. Conco, Yehova analola Mwana wake kuvutika mpaka pamene anatsilizika. w25.01 22 ¶7

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 15) Mateyo 27:​62-66 (Zocitika dzuwa likalowa: Nisani 16) Yohane 20:1

Sondo, April 5

Iwo anamuona masiku onse 40.​—Mac. 1:3.

Tsiku lake ni pa Nisani 16, mu 33 C.E. Ophunzila a Yesu ali m’nkhongono zii pokhudzika na cisoni, komanso pokhwethemuka na mantha. Aŵili a iwo akutuluka mu Yerusalemu kuloŵela kumudzi wa Emau. Mwadzidzidzi, akuona munthu wacilendo akubwela n’kuyamba kuyenda nawo. Ophunzilawo akusimbila munthuyo za kukhumudwa kwawo na zimene zacitika kwa Yesu. Kenako, mlendoyo akuyamba nawo nkhani yomwe isinthiletu zinthu pa moyo wawo. “Kuyambila ndi Zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneli analemba,” iye anakufotokozela ophunzilawo cifukwa cake Mesiya anafunika kuvutika komanso kufa. Pofika ku Emau kuja, mlendoyo akudziulula kwa iwo, kuti ni Yesu amene waukitsidwa! (Luka 24:​13-35) Yesu ataukitsidwa, anakhala masiku 40 pa dziko lapansi asanabwelele kumwamba. M’masiku 40 amenewo, iye anaonekela kwa ophunzila ake maulendo ambili. Pa nthawi imeneyo, Yesu analimbikitsa ophunzila ake amene anali acisoni komanso amantha. Iwo anakhalanso acimwemwe komanso olimba mtima kuti apite kukalalikila na kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu. w24.10 12 ¶1-3

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 16) Yohane 20:​2-18

Mande, April 6

Muzilimbitsa cikhulupililo canu coyela kwambili.​—Yuda 20.

Kukula mwakuthupi kumacitika mwacibadwa. Koma si mmene zimakhalila kuti munthu akhwime mwauzimu. Mwacitsanzo, abale na alongo ku Korinto analandila uthenga wabwino, anabatizika, analandila mzimu woyela, ndiponso anapindula na malangizo a Paulo. (Mac. 18:​8-11) Komabe, pambuyo pa zaka zambili cibatizikileni, ambili anakhalabe osakhwima. (1 Akor. 3:2) Kuti tikhale okhwima, coyamba tiyenela kukulitsa cikhumbo cofuna kukhala Mkhristu wokhwima. Amene amafuna “kukhalabe osadziŵa zinthu” amasankha kukhalabe makanda, ndipo sapita patsogolo mwauzimu. (Miy. 1:22) Sitifuna kukhala ngati anthu aakulu mwakuthupi amene amapitiliza kudalila makolo awo kuwapangila zisankho. M’malomwake, timasenza tokha udindo wodzidyetsa kuti tikule mwauzimu. Ngati mukuyesetsa kuti mukhale wokhwima, pemphelani kwa Yehova kuti akupatseni cikhumbo na mphamvu kuti mukwanitse kucita zimenezo.​—Afil. 2:13. w24.04 4 ¶9-10

Ciwili, April 7

Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.​—2 Pet. 3:9.

Mokoma mtima, Yehova amatiuza mmene amamvela poweluza anthu. (Ezek. 33:11) Yehova safulumila kuwonongeletu anthu kwamuyaya. Iye ni wacifundo cacikulu, ndipo amacionetsa pakakhala pofunikila. Tidziŵa zotani ponena za anthu amene sadzaukitsidwa? Baibo imachula zitsanzo za anthu ocepa cabe amene sadzaukitsidwa. Yesu anaonetsa kuti Yudasi Isikariyoti sadzaukitsidwa. (Maliko 14:21; Onani Yoh. 17:12.) Yudasi anali kudziŵa kuti zimene anali kucita zinali zosemphana na Yehova komanso Mwana Wake. Koma mwadala anasankha kuzicita. Mofananamo, Yesu ananena kuti atsogoleli azipembedzo amene anali kumutsutsa adzafa opanda ciyembekezo. (Mat. 23:33; onani Yoh. 19:11.) Nayenso mtumwi Paulo anacenjeza ampatuko osalapa kuti sadzaukitsidwa.​—Aheb. 6:​4-8; 10:29. w24.05 4 ¶10-11

Citatu, April 8

Yehova amateteza okhulupilika.​—Sal. 61:4.

Tikakhalabe oyandikana na Yehova, Satana sangacite ciliconse cimene cingativulaze mpaka kale-kale. (1 Yoh.3:8) M’dziko latsopano, Yehova adzapitiliza kuteteza mabwenzi ake okhulupilika ku imfa, komanso ku zinthu zimene zingawavulaze kuuzimu. (Chiv. 21:4) Ni mwayi wapadela zedi kukhala mlendo m’tenti ya Yehova, kutanthauza kusangalala na ubale wabwino na iye umene udzakhalapo mpaka kale-kale. (Ezek. 37:27) Tiyenela kucita ciyani kuti tipitilize kukhala alendo ake? Mukaitanidwa ku nyumba ya munthu winawake, mungafune kudziŵa zimene iye afuna kuti mucite. Mofananamo, nafenso tiyenela kudziŵa zimene Yehova amafuna kuti tizicita kuti tikhalabe alendo. Cikondi pa Yehova cimatisonkhezela kucita zonse zotheka kuti ‘tizimusangalatsa pa ciliconse.’ (Akol. 1:10) Nthawi zonse tiyenela kum’patsa ulemu waukulu. Ulemu umenewu udzatithandiza kupewa makhalidwe amene angamukhumudwitse. Ndife ofunitsitsa kuyenda “modzicepetsa” na Mulungu wathu.​—Mika 6:8. w24.06 4 ¶8-9

Cinai, April 9

Analowelelapo kuti athandize anthu.​—Yes. 53:12.

Yehova anapempha Abulahamu kuti apeleke mwana wake Isaki nsembe. Izi ziyenela kuti zinamuvutitsa maganizo kwambili Abulahamu. Ngakhale n’telo, iye anali wofunitsitsa kumvela Yehova. Pamene Abulahamu anatsala pang’ono kupha mwana wake, Mulungu anamuletsa. Komabe citsanzoci cimaphunzitsa anthu onse okhulupilika zimene Yehova anali kudzacita m’tsogolo. Iye anali kudzalolela kupeleka nsembe Mwana wake wokondeka. Yehova anali kudzacita zimenezi cifukwa amakonda kwambili anthu. (Gen. 22:​1-18) Patapita zaka zambili, Yehova anapatsa Aisiraeli Cilamulo. Mu Cilamulo cimeneco, Yehova anawauza kuti azipeleka nsembe zanyama kuti macimo awo azikhululukidwa. (Lev. 4:​27-29; 17:11) Nsembe zimenezi zinali kuimila makonzedwe a nsembe yaikulu imene Mulungu analinganiza, yomwe inali kudzapulumutsa anthu ku ucimo kothelatu. Mulungu anauzila aneneli kulemba za mbewu yolonjezedwa. Mbewu imeneyi ni Mwana wa Mulungu wapadela, ndipo anali kudzavutika komanso kuphedwa kuti apulumutse anthu, kuphatikizapo inu, ku ucimo na imfa!​—Yes. 53:​1-12. w24.08 4 ¶7-8

Cisanu, April 10

Ndimakonda kwambili cilamulo canu! Ndimaganizila mozama cilamuloco tsiku lonse.​—Sal. 119:97.

Poŵelenga Baibo, muziona mmene mungagwilitsile nchito zimene mwaŵelenga. Pamene mukuŵelenga Mawu a Mulungu, muzidzifunsa kuti, ‘Ningaseŵenzetse bwanji zimene naŵelengazi pali pano kapena m’tsogolo?’ Tiyelekeze kuti mwaŵelenga 1 Atesalonika 5:​17, 18. Mutaŵelenga mavesi aŵili amenewa, mungadzifunse ngati mumapemphela pafupi-pafupi, komanso ngati mumapeleka mapemphelo ocokela pansi pa mtima. Kuwonjezela apo, mungaganizile zinthu zimene mumayamikila. Mwina mungaganizile kuti muyamikile Yehova pa zinthu zitatu. Ngakhale mutacita zimenezi kwa mphindi zocepa, kudzakuthandizani kuti mukhale munthu womva Mawu a Mulungu na kuwacita. Ganizilani mmene mungapindulile mukamacita zimenezi tsiku lililonse pamene muŵelenga Baibo! Kucita izi kudzakuthandizani kuti muzicita zimene Mawu a Mulungu amanena. w24.09 4-5 ¶9-10

Ciwelu, April 11

Samalani kuti musataye zinthu zimene tinakuthandizani kuti muzipeze nʼcolinga coti mudzalandile madalitso onse amene Mulungu wakukonzelani.​—2 Yoh. 8.

Yehova anatilenga m’njila yapadela. Ngakhale kuti timasangalala tikalandila mphatso, timakhala na cimwemwe coculuka tikamapatsa ena. Timakhala acimwemwe tikakwanitsa kuthandiza okhulupilila anzathu. Ndipo timakondwela akatiyamikila pa zimene tacitazo. Komabe, kaya atiyamikile kapena ayi, timakhalabe acimwemwe podziŵa kuti tacita cinthu coyenela. Musaiŵale kuti zilizonse zimene mungapatse ena, “Yehova akhoza kukupatsani zambili kuposa zimenezo.” (2 Mbiri 25:9) Anthufe sitingathe kupatsa ena zambili kuposa zimene Yehova amatipatsa. Ndipo kulibe zosangalatsa kuposa zimene Yehova amatibwezela tikacitila ena zabwino. Conco tiyeni tisaleke kutengela citsanzo ca Atate wathu wa kumwamba ca kuwolowa manja. w24.09 31 ¶20-21

Sondo, April 12

Ndimakutamandani ndi mtima wanga wonse, inu Yehova Mulungu wanga, ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.​—Sal. 86:12.

Yehova ndi wacifundo. (Sal. 103:13; Yes. 49:15) Tikamavutika, iyenso zimam’khudza. (Zek. 2:8) Amacititsa kuti zikhale zosavuta kuti timufikile. (Sal. 25:14; Mac. 17:27) Kuwonjezela apo, Yehova ndi wodzicepetsa, moti “amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumucotsa m’fumbi.” (Sal. 113:​6, 7) Kunena zoona, kodi izi si zifukwa zamphamvu zotisonkhezela kum’patsa ulemelelo Mulungu wathu wamkulu? Timapatsa Yehova ulemelelo cifukwa timafuna kuti ena amudziwe. Ambili sadziwa zoona zake zokhudza Yehova. N’cifukwa ciyani? Cifukwa n’cakuti Satana waaphimba maganizo pofalitsa mabodza amkunkhuniza onena za iye. (2 Akor. 4:4) Satana wapangitsa anthu kukhulupilila kuti Yehova ndi wamkali, sasamala za anthu, komanso kuti ndiye wacititsa ambili mwa mavuto amene timakumana nawo m’dzikoli. Koma ife timadziwa zenizeni ponena za Mulungu wathu. Ndipo tili ndi mwayi wouza anthu coonadi ponena za Mulungu wathu, ndi kuwathandiza kuti nawonso ayambe kumupatsa ulemelelo.​—Yes. 43:10. w25.01 3 ¶6-7

Mande, April 13

Satana . . . akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.​—Chiv. 12:9.

Ngakhale kuti Yesu Mwana wa Mulungu anali wangwilo, ndipo anali kucita zozizwitsa, adani a Mulungu anali kufalitsa mabodza ambili okhudza iye. Mwacitsanzo, atsogoleli a zipembedzo anali kuuza anthu kuti mphamvu zotulutsa ziŵanda zimene Yesu anali nazo anapatsidwa na “wolamulila ziŵanda.” (Maliko 3:22) Pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu, atsogoleli a cipembedzo anamunamizila kuti ananyoza Mulungu. Iwo analimbikitsa khamu la anthu kugamula kuti Yesu aphedwe. (Mat. 27:20) Patapita nthawi, pamene otsatila a Khristu anali kulalikila uthenga wabwino, anthu otsutsa “anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo” kuti azunze Akhristuwo. (Mac. 14:​2, 19) Ponena za Machitidwe 14:​2, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1998, inafotokoza kuti: “Kuonjezela pa kukana uthengawo, Ayuda otsutsa anayamba kufalitsa mphekesela zoipa akumayesa kupangitsa anthu akunja kuti akhale ndi maganizo oipa ponena za Akhristu.” Masiku ano, Satana akupitilizabe “kusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. w24.04 11 ¶15-16

Ciwili, April 14

Ndinu Woweluza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simucita cilungamo?​—Gen. 18:25.

Kuti munthu akakhale na moyo wosatha sizidalila kuti anamwalila liti. Yehova ni woweluza wangwilo ndipo amaweluza mwacilungamo. (Sal. 33:​4, 5) Ndife otsimikiza kuti “Woweluza wa dziko lonse lapansi” adzacita zoyenela. Komanso, kuti munthu akakhale na moyo wosatha sizidalila kumene akukhala. Yehova sangaweluze anthu ofika m’mamiliyoni kuti ni “mbuzi” cabe cifukwa akukhala kumene analibe mwayi wolandila uthenga wa Ufumu kuti asinthe umoyo wawo. (Mat. 25:46) Woweluza wa dziko lonse wolungama amawadela nkhawa anthu amenewo kuposa mmene ife tingacitile. Sitidziŵa mmene Yehova adzayendetsele zinthu pa cisautso cacikulu. Mwina ena mwa anthu amenewo adzakhala na mwayi wophunzila za Yehova, kumukhulupilila, na kuwolokela ku mbali yake pamene iye adzapangitsa anthu onse padziko kuti am’dziŵe.​—Ezek. 38:16. w24.05 12 ¶14-15

Citatu, April 15

Muzikondana.​—Yoh. 15:12.

Anthu a Mulungu amakonda kuthandizana. (2 Akor. 8:4) Komabe nthawi zina zimafunikila kulimba mtima kuti ticite zimenezi. Mwa citsanzo, nkhondo ikabuka, akulu amazindikila kuti abale na alongo awo amafunikila cilimbikitso, thandizo la kuthupi komanso lauzimu. Cifukwa ca cikondi cawo pa nkhosa, akulu amaika miyoyo yawo pa ciopsezo kuti apeleke zofunikila kwa nkhosazo. Pa nthawi zovuta ngati zimenezo, tifunikila tizikhalabe ogwilizana. Tsatilani malangizo ocokela ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Akulu nthawi zonse ayenela kumabwelelamo m’malangizo kuti azikhala okonzeka komanso odziŵa mocitila tsoka likagwa. (1 Akor. 14:​33, 40) Khalani olimba mtima komabe osamala. (Miy. 22:3) Ganizilani mofatsa musanacitepo kanthu. Musaike moyo wanu pa ciopsezo mwadala. Dalilani Yehova. Iye angakuthandizeni kuti mupeleke thandizo kwa abale anu muli otetezeka. w24.07 4 ¶8; 5 ¶11

Cinai, April 16

Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova, . . . ndipo makutu ake anamva kulila kwanga kopempha thandizo.​—Sal. 18:6

Davide anali kum’dziŵa bwino Yehova, ndipo anali kum’dalila. Pomwe Mfumu Sauli na anthu ena anali kufuna kupha Davide, iye anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize. Mulungu atayankha pemphelo lake na kumupulumutsa, iye ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Ponena mawu amenewa, Davide sanali kungovomeleza kuti Mulungu aliko ayi. Pothilila ndemanga pa mawu amenewa, buku lina linanena kuti Davide anali kuonetsa cidalilo cake mwa Yehova “monga Mulungu wamoyo amene nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Inde, Davide anadzionela yekha pa zocitika za pa umoyo wake kuti Mulungu wake ni wamoyo, ndipo zimenezi zinam’sonkhezela kupitiliza kum’tumikila na kum’tamanda. (Sal. 18:​28, 29, 49) Kukhala otsimikiza kuti Yehova ni Mulungu wamoyo kumatithandiza kumutumikila na mtima wonse. Kumatithandizanso kupilila mavuto amene tingakumane nawo na kupitiliza kugwila nchito molimbika pom’tumikila. Cina, kumatithandiza kukhalabe naye pa ubwenzi. w24.06 20-21 ¶3-4

Cisanu, April 17

Musalole kuti aliyense akusoceletseni mwa njila iliyonse.​—2 Ates. 2:3.

Tiphunzilapo ciyani pa mawu amene mtumwi Paulo analembela Atesalonika? Tikamva nkhani inayake imene sigwilizana na zimene tinaphunzila m’Baibo, kapena tikamva nkhani inayake yocititsa cidwi koma yodabwitsa, tiyenela kukhala osamala. Mu ulamulilo wakale wa Soviet Union, adani athu anapatsa abale kalata yooneka ngati yacokela ku likulu lathu. Kalata imeneyo inalimbikitsa abale na alongo kuti adzipatule ku gulu la Yehova na kupanga gulu lawo lodziimila palokha. Kalata imeneyo inali kuoneka ngati yacokeladi kulikulu lathu. Koma abale na alongo okhulupilika sanapusitsidwe. Iwo anazindikila kuti zimene kalatayo inakamba zinali zosiyana na zimene anaphunzila. Masiku anonso, adani a coonadi amaseŵenzetsa njila zamakono na colinga cakuti atisokoneze na kubweletsa magaŵano pakati pathu. M’malo molola “kuti wina aliyense asinthe maganizo” athu mosavuta, tiyeni tidziteteze mwa kuganizilapo mozama ngati zimene tamva kapena kuŵelengazo zigwilizana na coonadi cimene tinaphunzila kale.​—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1. w24.07 12 ¶14-15

Ciwelu, April 18

Wina akacita chimo, tili ndi wotithandiza.​—1 Yoh. 2:1.

Cisankho cofunika kopambana cimene munthu aliyense angapange ni cisankho codzipatulila kwa Yehova na kukhala m’banja la alambili ake. Yehova amafuna kuti munthu aliyense apange cisankho cimeneci. N’cifukwa ciyani? Iye amafuna kuti anthu akhale paubwenzi wabwino na iye, komanso kuti akhale na moyo kwamuyaya. (Deut. 30:​19, 20; Agal. 6:​7, 8) Komabe, Yehova sakakamiza munthu aliyense kuti am’tumikile. Iye amalola munthu aliyense kupanga cisankho com’tumikila kapena ayi. N’ciyani cimacitika ngati Mkhristu wobatizika waphwanya malamulo a Mulungu na kucita chimo lalikulu? Ngati munthuyo si wolapa, ayenela kucotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:13) Ngakhale n’telo, Yehova amakhala wofunitsitsa kuti munthuyo alape na kubwelela kwa iye. Ni iko komwe, ici ndiye cifukwa cacikulu cimene Yehova anapelekela dipo. Colingaco cinali cakuti zizikhala zotheka munthu wocimwa akalapa kukhululukidwa macimo ake. Mulungu wathu wacikondi amapempha ocimwa kuti alape.​—Zek. 1:3; Aroma 2:4; Yak. 4:8. w24.08 14 ¶1-2

Sondo, April 19

Mtima wako ukakhala wanzelu, ndithu mtima wanga udzasangalala.​—Miy. 23:15.

Panthawi imene mtumwi Yohane analemba za cimwemwe cimene cimabwela munthu akakhala womvela kwa Mulungu. Panthawiyo, anthu ena anali kufalitsa ziphunzitso zabodza na kubweletsa magaŵano mumpingo. Ngakhale n’telo, ena anali ‘kuyendabe m’coonadi.’ Iwo anali kumvela Yehova ndipo anali “kuyenda motsatila malamulo ake.” (2 Yoh. 4, 6) Zimene Akhristu okhulupilikawo anacita, zinasangalatsa Yohane komanso Yehova. (Miy. 27:11) Kodi tiphunzilapo ciyani? Kukhala wokhulupilika kumabweletsa cimwemwe. (1 Yoh. 5:3) Mwacitsanzo, timakhala acimwemwe podziŵa kuti timakondweletsa Yehova. Yehova amakondwela tikakaniza mayeselo a dzikoli na kutsatila malamulo ake. Nawonso angelo kumwamba amasangalala. (Luka 15:10) Nafenso timakhala acimwemwe tikaona Mkhristu mnzathu akukhalabe wokhulupilika. (2 Ates. 1:4) Ndipo dongosolo loipali likadzapita, tidzakhala acimwemwe podziŵa kuti tinakhala okhulupilika kwa Yehova m’dziko lolamulidwa na Satana. w24.11 12 ¶17-18

Mande, April 20

Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.​—1 Akor. 10:24.

Kodi muyenela kumuyang’anila kwa utali wanji munthu musanamufikile? Mukamufikila mofulumila angakuoneni kuti ndinu wopupuluma. (Miy. 29:20) Koma ngati mungatenge nthawi yaitali kwambili, angakuoneni kukhala munthu wokayika-kayika, wosadziŵa bwino cimene afuna, maka-maka akazindikila kuti mumamufuna. (Mlal. 11:4) Komanso kumbukilani kuti, musanamufikile munthuyo musakhale wotsimikiza na mtima wonse kuti mudzakwatilana naye basi. M’malomwake, khalani wotsimikiza kuti inuyo ndinu wokonzeka kuloŵa m’banja, komanso kuti n’kutheka munthu winayo angakhale mnzanu wokuyenelelani. Koma bwanji ngati mwaona kuti munthu wina akukufunani? Ngati inuyo simukumufuna, onetsani zimenezo mwa kacitidwe kanu. Kungakhale kupanda cikondi kucita zinthu moonetsa ngati inunso mukufuna kukhala naye pacibwenzi, pamene sizili conco. Aef. 4:25. w24.05 22-23 ¶9-10

Ciwili, April 21

Ndidzabwelanso kudzakutengelani kwathu.​—Yoh. 14:3.

Anthu okhawo amene anadzozedwadi na Yehova na kukhalabe okhulupilika ndiwo adzakhala mu Ufumu wakumwamba limodzi na Yesu Odzozedwa amene sadzakhalabe maso mwauzimu, sadzasonkhanitsidwa pamodzi na “osankhidwa ake.” (Mat. 24:31) Ndipo anthu onse a Mulungu amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo padziko lapansi, nawonso ayenela kumvela cenjezo la Yesu na kukhalabe maso komanso okhulupilika. Popeza tafika pomudziŵa bwino Yehova, sitikayikila kuti iye amacita zinthu mwacilungamo. Conco sitikhumudwa Yehova akasankha kudzoza anthu ena okhulupilika m’masiku athu ano. Timakumbukila zimene Yesu anakamba m’fanizo la munda wa mpesa, zokhudza anthu amene anayamba kugwila nchito ca m’ma 5 koloko madzulo. (Mat. 20:​1-16) Anthu amene anayamba kugwila nchito m’munda wa mpesa ca m’madzulo analandila malipilo ofanana ndendende na aja amene anayamba kugwila nchito m’maŵa. Mofananamo, zilibe kanthu kuti munthu anadzozedwa liti, iye adzalandila mphoto ya kumwamba akakhalabe wokhulupilika. w24.09 24 ¶15-17

Citatu, April 22

Khristu anavutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiyilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.​—1 Pet. 2:21.

Yesu anatipatsa citsanzo cabwino ca zimene tingacite kuti tipilile zopanda cilungamo. Yesu anacitilidwapo zopanda cilungamo kucokela kwa acibale ake, komanso kwa anthu amene sanali acibale ake. Acibale ake amene sanamukhulupilile anakamba kuti wacita misala. Nawonso atsogoleli acipembedzo anakamba kuti iye anatenga mphamvu zake kwa ziŵanda. Kuwonjezela apo, asilikali Aciroma anamunyoza ndipo anamupha. (Maliko 3:​21, 22; 14:55; 15:​16-20, 35-37) Ngakhale n’telo, Yesu anapilila zopanda cilungamo zonse zimene anamucitila, ndipo sanabwezele. Tiphunzilapo ciyani ku citsanzo cake? (1 Pet. 2:​21-23) Yesu anatisiyila citsanzo cabwino kwambili cimene tingatsatile tikamakumana na zopanda cilungamo. Anali kudziŵa nthawi yolankhula komanso yokhala cete. (Mat. 26:​62-64) Nthawi zina, anthu ena akamunenela mabodza iye anali kukhala cete. (Mat. 11:19) Ndipo Yesu akalankhula, sanali kuwanyoza anthu omuvutitsa kapena kuwaopseza. w24.11 4-5 ¶9-10

Cinai, April 23

Khristu Yesu anabwela mʼdziko kudzapulumutsa ocimwa.​—1 Tim. 1:15.

Yelekezani kuti mwapatsa munthu amene mumakonda mphatso yokongola komanso yothandiza kwambili. N’zosacita kufunsa kuti mungakhumudwe kwambili ngati munthuyo angaike mphatsoyo m’bokosi lake losungilamo zinthu popanda kuiganizilapo! Kumbali ina, mungamve bwino ngati munthuyo akuigwilitsa nchito mphatsoyo ndipo amaiyamikila. Mfundo yake ndi yotani pamenepa? Nayenso Yehova anatipatsa Mwana wake monga mphatso. Mosakaikila, amasangalala kwambili tikamaonetsa kuti timaiyamikila mphatso imeneyi komanso cikondi cake, cimene cinamusonkhezela kupeleka dipo! (Yoh. 3:16; Aroma 5:​7, 8) Komabe, nthawi ikamapita tingaleke kuona dipo monga mphatso yamtengo wapatali. Kucita zimenezi kungakhale ngati kuika mphatso ya Mulungu m’bokosi losungilamo zinthu, popanda kuionanso kapena kuiganizila. Kuti izi zisacitike, nthawi zambili tiyenela kumaganizila zimene Mulungu ndi Khristu aticitila. w25.01 26 ¶1-2

Cisanu, April 24

Uziganizila mozama zinthu zimenezi ndipo uzizicita modzipeleka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.​—1 Tim. 4: 15.

M’bale amene angayenelele kukhala mkulu sayenela kukhala “woti wangobatizidwa kumene.” Ngakhale kuti mukabatizika sipayenela kupita zaka zambili kuti mukayenelele kukhala mkulu, mufunikilabe nthawi kuti mukhale Mkhristu wokhwima. Musanaikidwe kukhala mkulu, muyenela kuonetsa kuti ndinu wodzicepetsa, komanso kuti ndinu wokonzeka kuyembekezela modekha mpaka pamene Yehova angakupatseni mautumiki owonjezela, monga mmene Yesu anacitila. (Mat. 20:23; Afil. 2:​5-8) Mungaonetse kuti ndinu “wokhulupilika” mwa kukhalabe kumbali ya Yehova na kutsatila mfundo zake zolungama. Mungaonetsenso khalidweli mwa kutsatila malangizo omwe iye amapeleka kudzela m’gulu lake. Malemba amanena momveka bwino kuti woyang’anila ayenela kukhala “wodziŵa kuphunzitsa.” Kodi izi zitanthauza kuti muyenela kukhala mlankhuli waluso kwambili? Ayi. Pali akulu ambili ofikapo amene si alankhuli aluso kwenikweni, koma amaphunzitsa bwino mu ulaliki komanso pocita maulendo aubusa. w24.11 23-24 ¶14-15

Ciwelu, April 25

Ndimakonda malamulo anu kuposa golide, ngakhale golide wabwino Kwambili.​—Sal. 119:127.

Mukapeza mfundo ina imene simunamvetse m’Baibo, muzifufuza. Ndipo kwa tsiku lonse, sinkhasinkhani mfundo zimene mwapeza ndi kuona zimene muphunzilapo ponena za Yehova, Mwana wake, ndi cikondi cawo pa inu. (Sal. 119:​97, ftn.) Musalefuke ngati simunapeze mfundo yatsopano kapena yocititsa cidwi powelenga kapena pofufuza. Ganizilani za munthu amene amafunafuna golide. Moleza mtima, munthuyo amathela maola ambili ngakhalenso masiku kuti apeze ngakhale kacidutswa kakang’ono kwambili ka golide. Ngakhale n’telo, amalimbikila cifukwa kacidutswa kalikonse ka golide n’kamtengo wapatali kwa iye. Ndiye kuli bwanji kupeza mfundo zatsopano za coonadi! (Miy. 8:10) Conco khalani oleza mtima, ndipo pitilizani kutsatila ndandanda yanu ya kuwelenga Baibulo.​—Sal. 1:2. w25.01 25 ¶14-15

Sondo, April 26

Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso muzicita cimodzimodzi.​—Akol. 3:13.

Yehova amafuna kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kukhululukila amene atilakwila. (Sal. 86:5; Luka 17: 4; Aef. 4:32) Zimakhala zopweteka munthu wina akatikambila mawu oipa kapena akaticita zoipa. Ndipo cimatiwawa kwambili makamaka ngati munthuyo ndi mnzathu kapena wacibale wathu. (Sal. 55:​12-14) Nthawi zina, zingatipweteke kwambili moti tingamve monga munthu watilasa ndi lupanga. (Miy. 12:18) Mwina tingafune kungopondeleza mkwiyo wathu. Kucita zimenezi kungakhale ngati talasidwa ndi mpeni koma n’kuusiya pacilondapo osaucotsa. Mofananamo, sitingayembekezele kuti tidzamvako bwino ngati tangopondeleza mkwiyo wathu munthu wina akatilakwila. Munthu akatilakwila, n’cibadwa kukwiya. Ndipo ngakhale Baibulo limavomeleza mfundoyi. Koma limaticenjeza kuti tisalole mkwiyo kutilamulila. (Sal. 4:4; Aef. 4:26) Cifukwa ciyani? Cifukwa munthu akakwiya sapanga zisankho zanzelu. (Yak. 1:20) Kumbukilani, mkwiyo wanu ena amacita kuuputa. Koma kukhalabe cikwiyile n’cisankho canu. w25.02 15 ¶4-6

Mande, April 27

Nzelu zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeluzo.​—Mla. 7:12.

Pogwilitsa nchito fanizo, Yesu anaonetsa kuti n’kupanda nzelu kuunjika cuma padziko lapansi popanda kukhala “wolemela kwa Mulungu.” (Luka 12:​16-21) Zamawa sizidziwika. (Miy. 23:​4, 5; Yak. 4:​13-15) Cifukwa cokhala otsatila a Yesu, timakumana ndi mavuto amene anthu ena sakumana nawo. Pa nkhaniyi, Yesu anati tiyenela kukhala okonzeka “kusiya” zinthu zathu zonse zakuthupi kuti tikhale otsatila ake. (Luka 14:33) Akhristu a ku Yudeya analolela kusiya zinthu zawo zakuthupi ali acimwemwe. (Aheb. 10:34) Masiku anonso, abale ambili alolela kutayikilidwa katundu wawo wakuthupi cifukwa cokana kukhalila mbali m’zandale. (Chiv. 13:​16, 17) Cawathandiza n’ciyani kucita zimenezi? Iwo amakhulupilila ndi mtima wonse lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb 13:5.) Timacita zonse zotheka pokonzekela tsogolo lathu. Koma ngati zinthu za mwadzidzidzi zatigwela, timadalila kuti Yehova adzatithandiza. w25.03 29 ¶13-14

Ciwili, April 28

Popeza tamaliza kuphunzila mfundo zoyambilila zokhudza Khristu, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu. Tisayambe kuyalanso maziko.​—Aheb. 6:1.

Yehova satiyembekezela kufika pa ucikulile wauzimu pa ife tokha. Amene amatumikila monga abusa komanso aphunzitsi mu mpingo wa Cikhristu, ni okonzeka kutithandiza. Iwo amatithandiza kufika “pa msinkhu wa munthu wamkulu” mwauzimu, “ngati mmene Khristu analili.” (Aef. 4:​11-13) Yehova amapelekanso mzimu wake woyela potithandiza kuti tikhale na “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:​14-16) Kuwonjezela apo, Mulungu anauzila anthu kulemba Mauthenga Abwino anayi, potionetsa mmene Yesu anali kuganizila komanso kucitila zinthu pamene anali kucita utumiki wake pa dziko lapansi. Mwa kutengela maganizo a Yesu na kacitidwe kake ka zinthu, tingakwanilitse colinga cathu cokhala Mkhristu wokhwima. Koma kuti tifike pa ucikulile wauzimu tiyenela kucita zambili kuposa pa kuphunzila “mfundo zoyambilila zokhudza Khristu,” zomwe ni ziphunzitso zoyambilila za Cikhristu. w24.04 4-5 ¶11-12

Citatu, April 29

Kuganiza bwino kudzakuyangʼanila, ndipo kuzindikila kudzakuteteza.​—Miy. 2:11.

Tsiku lililonse timafunikila kupanga zisankho. Zisankho zina monga kusankha cakudya cam’mawa kapena nthawi yopita kukagona ndi zosavuta kupanga. Koma zina zimakhala zovuta. Zisankhozo zingakhudze thanzi lathu, cimwemwe cathu, okondedwa athu kapena ubwenzi wathu ndi Yehova. Timafuna kuti zisankho zimene tapanga zitipindulile ife eni komanso a m’banja mwathu. Koma koposa zonse, timafuna kuti zisankho zathu zizikondweletsa Yehova. (Aroma 12:​1, 2) Sitepe imene munthu ayenela kutsatila kuti apange cisankho canzelu ndi kudziwa zoona zake zokhudza nkhaniyo. Zimenezi n’zofunika cifukwa ciyani? Tiyelekeze kuti munthu wapita kwa dokotala kukafunsa za matenda aakulu amene ali nawo. Kodi dokotala angapeleke mankhwala kwa munthuyo asanamupime kapena kumufunsako mafunso? Kutalitali! Mofanana ndi dokotala wabwino, inunso mungapange zisankho zanzelu ngati coyamba mumaganizila mfundo zonse zimene mwapeza zokhudzana ndi cisankho cimene mufuna kupanga. w25.01 14 ¶1-3

Cinai, April 30

Yehova wakukhululukila chimo lako ndipo suufa.​—2 Sam. 12:13.

Tidziŵa ciyani ponena za cifundo ca Yehova? Kodi iye waonetsa bwanji kuti “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe”? (2 Pet. 3:9) Ganizilani mmene anaonetsela cifundo cake kwa anthu amene anacitapo macimo akulu-akulu. Mfumu Davide anacitapo macimo akulu-akulu, kuphatikizapo cigololo komanso kupha munthu. Komabe Davide analapa, ndipo Yehova anam’khululukila. (2 Sam. 12:​1-12) Mfumu Manase nayenso anacita zinthu zoipa kwambili kwa nthawi yaikulu ya moyo wake. Ngakhale kuti Manase anacita zoipa zambili, iye analapa ndipo Yehova anamucitila cifundo na kum’khululukila. (2 Mbiri 33:​9-16) Zitsanzo zimenezi zitikumbutsa kuti Yehova amacita cifundo pakakhala cifukwa cocitila zimenezi. Iye adzaukitsa anthu ngati amenewa cifukwa iwo anazindikila kuti anacita macimo aakulu ndipo analapa. w24.05 4 ¶12

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani