Cisanu, October 16
Musalole kuti mtima wanu upatukile kunjila zake. Musasocele nʼkuyamba kuyenda mʼnjila zake.—Miy. 7:25
Nkhani ya mnyamatayu itionetsa zimene zingacitikile mlambili aliyense wa Yehova. Aliyense angagwele m’chimo lalikulu, pambuyo pake n’kuganiza kuti chimolo linacitika “mwadzidzidzi.” Kapena anganene kuti, Zinangocitika. Koma akaganizila mofatsa zimene zinacitikazo, angazindikile kuti pali zina zimene sanasamale nazo zimene zinam’tsogolela ku chimo lalikulu. Zimenezo zingaphatikizepo kukhala na mabwenzi oipa, zosangalatsa zosayenela, komanso kupezeka pa malo olakwika nthawi zambili, kapena pa intaneti. Mwinanso iye analeka kupemphela, kuŵelenga Baibo, kusonkhana, komanso kutengako mbali mu nchito yolalikila. Monga zinacitikila kwa mnyamata wochulidwa m’buku la Miyambo, chimo la munthuyu sikuti linacitika mwadzidzidzi ayi, panali zinthu zina zimene zinam’tsogolela ku chimolo. Tiphunzilapo ciyani pa nkhaniyi? Tisapewe cabe kucita chimo, koma tipewenso zimene zingatitsogolele ku chimolo. Solomo anamveketsa bwino mfundo imeneyi.—Mat. 5:29, 30. w24.07 16 ¶10-11
Ciwelu, October 17
Tili ndi cuma cimeneci mʼziwiya zadothi.—2 Akor. 4:7.
Kodi cuma cimeneci n’ciani? Ndi nchito yolalikila uthenga wa Ufumu, imene imapulumutsa miyoyo. (2 Akor. 4:1) Nanga ziwiya zadothi n’ciani? Ndi atumiki a Mulungu, amene amagawilako ena uthenga wabwino. M’nthawi ya Paulo, a zamalonda anali kusewenzetsa ziwiya zadothi ponyamula zinthu zamtengo wapatali monga cakudya, vinyo, ndi ndalama. Mofananamo, Yehova watipatsa uthenga wabwino wamtengo wapatali. Ndi thandizo lake, timakhala ndi mphamvu zofunikila kuti tilalikile uthenga wabwino mokhulupilika. Nthawi zina, tingamaope anthu kapena kuopa kutsutsidwa. Nanga tingagonjetse bwanji mantha amenewa? Ganizilani pemphelo limene atumwi anapeleka atalamulidwa kuti aleke kulalikila. M’malo mocita mantha, io anapempha Yehova kuti ‘apitilize kulankhula molimba mtima.’ Yehova anayankha pemphelo lao nthawi yomweyo. (Mac. 4:18, 29, 31) Ngati nthawi zina mumacita mantha, muzimupempha Yehova kuti atithandize kukulitsa cikondi cathu pa anthu kuti tileke kuopa kuwauzako uthenga wabwino. w24.04 16 ¶8-9
Sondo, October 18
Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.—Mat. 6:9.
Cikondi cathu pa Yehova cimatilimbikitsa kuyeletsa dzina lake. Timafuna kutengapo gawo pa nchito yoyeletsa dzina la Mulungu ku citonzo cimene Satana wabweletsa pa dzinalo cifukwa ca mabodza ake oipa. (Gen. 3:1-5; Yobu 2:4; Yoh. 8:44) Tikakhala mu ulaliki, timakhala ofunitsitsa kumukhalila kumbuyo Mulungu wathu, na kuuzako amene afuna kumvetsela coonadi cokhudza iye. Tifuna kuti munthu aliyense adziŵe kuti khalidwe lake lalikulu ni cikondi, komanso kuti amalamulila mwacilungamo. Tifunanso kuti adziŵe kuti posacedwa, Ufumu wake udzathetsa mavuto onse na kubweletsa mtendele, komanso cimwemwe kwa anthu onse. (Sal. 37:10, 11, 29; 1 Yoh. 4:8) Tikawadziŵitsa zimenezi, timayeletsa dzina lake. Timakhalanso okhutila tikadziŵa kuti timacita zinthu mogwilizana na dzina lathu. w24.05 18 ¶12