LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es26 masa. 26-36
  • March

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • March
  • Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
  • Tumitu
  • Sondo, March 1
  • Mande, March 2
  • Ciwili, March 3
  • Citatu, March 4
  • Cinai, March 5
  • Cisanu, March 6
  • Ciwelu, March 7
  • Sondo, March 8
  • Mande, March 9
  • Ciwili, March 10
  • Citatu, March 11
  • Cinai, March 12
  • Cisanu, March 13
  • Ciwelu, March 14
  • Sondo, March 15
  • Mande, March 16
  • Ciwili, March 17
  • Citatu, March 18
  • Cinai, March 19
  • Cisanu, March 20
  • Ciwelu, March 21
  • Sondo, March 22
  • Mande, March 23
  • Ciwili, March 24
  • Citatu, March 25
  • Cinai, March 26
  • Cisanu, March 27
  • Ciwelu, March 28
  • Sondo, March 29
  • Mande, March 30
  • Ciwili, March 31
Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
es26 masa. 26-36

March

Sondo, March 1

Munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu wa macimo ake.​—Aroma 6:7.

Timaŵelenga m’Baibo za anthu amene anali olungama, amene kenako anadzakhala osalungama. Citsanzo ni Mfumu Solomo. Iye anaphunzitsidwa bwino njila za Mulungu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambili. Koma pambuyo pake anayamba kulambila milungu yonyenga. Macimo ake anamukhumudwitsa ngako Yehova, ndipo anabweletsa mavuto ambili pa mtundu wa Isiraeli kwa zaka mahandiledi. N’zoona kuti Malemba amanena kuti Solomo atamwalila “anagona pamodzi ndi makolo ake,” kuphatikizapo amuna okhulupilika monga Mfumu Davide. (1 Maf. 11:​5-9, 43; 2 Maf. 23:13) Koma kodi popeza iye anaikidwa m’manda limodzi ndi makolo ake, zitanthauza kuti basi iye adzaukisidwanso? Baibo siinena kalikonse. Koma ciukitso ni mphatso yocokela kwa Mlengi wacikondi. Ndipo amangoipeleka kwa anthu omwe iye akufuna kuti am’tumikile kwamuyaya. (Yobu 14:​13, 14; Yoh. 6:44) Kodi Solomo adzalandilako mphatso imeneyi? Yehova ndiye adziŵa, ife sitidziŵa. Cimene tidziŵa n’cakuti, Yehova adzacita cilungamo. w24.05 4 ¶9

Mande, March 2

Ndidzakhala mlendo mutenti yanu mpaka kalekale.​—Sal. 61:4

Tikadzipatulila kuti tikhale paubale na Yehova, timakhala alendo m’tenti yake yophiphilitsa. Timakhala na cakudya cauzimu coculuka, ndipo timasangalalanso kukhala pa ubwenzi wabwino na anthu ena, amenenso ni alendo a Yehova. Tenti Yake yophiphilitsa siipezeka kumalo amodzi okha. Tenti imeneyi imapezeka kulikonse kumene kuli alambili ake okhulupilika. (Chiv. 21:3) Nanga bwanji za anthu okhulupilika amene anamwalila? Kodi m’pomveka kunena kuti akali alendo m’tenti ya Yehova? Inde! Tikutelo cifukwa ciyani? Cifukwa Yehova amawakumbukila bwino ngako. Zili ngati ali moyo kwa iye. Yesu anafotokoza kuti: “Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza mu nkhani ya citsamba ca minga, pamene ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, cifukwa kwa iye onsewa ndi amoyo.”​—Luka 20:​37, 38. w24.06 3 ¶6-7

Ciwili, March 3

Yehova ndi mphamvu yanga komanso cishango canga.​—Sal. 28:7.

Zadoki anapita ku Heburoni atanyamula zida zake, ndipo anali wokonzeka kumenya nkhondo. (1 Mbiri 12:38) Iye anali wokonzeka kupita na Davide ku nkhondo kuti akateteze Isiraeli kwa adani ake. Ngakhale kuti Zadoki sanali ciyambakale pa zankhondo, anali munthu wolimba mtima kwambili. Kodi wansembe Zadoki anaphunzila kwa ndani kukhala wolimba mtima? Iye anali kupezeka pakati pa amuna amphamvu komanso olimba mtima. Mosakaikila iye anaphunzila kwa iwo poona citsanzo cawo. Mwacitsanzo, cifukwa Davide anali ‘kutsogolela Aisiraeli ku nkhondo’ molimba mtima, Aisiraeli onse anafuna kumulonga ufumu. (1 Mbiri 11:​1, 2) Davide nthawi zonse anali kudalila thandizo la Yehova kuti agonjetse adani ake. (Sal. 138:3) Zadoki anaphunzilanso ku zitsanzo za amuna ena olimba mtima monga Yehoyada na mwana wake Benaya amene anali msilikali. Anaphunzilanso zambili kwa atsogoleli 22 a m’nyumba ya bambo ake amene anali kumbali ya Davide.​—1 Mbiri 11:​22-25; 12:​26-28. w24.07 3 ¶5-6

Citatu, March 4

Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwakukulu . . . nʼcolinga coti ulape.​—Aroma 2:4.

Saulo wa ku Tarisi anali kuzunza mwankhanza otsatila okondeka a Khristu. Koma Yesu woukitsidwayo anali kudziŵa kuti Paulo angathe kusintha na kulapa. Iye na Atate wake anaona makhalidwe abwino mwa Saulo. Yesu anakamba kuti: “Munthu ameneyu ndi ciwiya canga cosankhidwa.” (Mac. 9:15) Yesu anagwilitsa nchito cozizwitsa kuti athandize Saulo kulapa. (Mac. 7:58–8:3; 9:​1-9, 17-20) Pambuyo pokhala Mkhristu, Saulo amene pambuyo pake anadzachedwa Paulo, nthawi zambili anali kukamba za ciyamikilo cimene anali naco kwa Yehova na Yesu pomukomela mtima komanso pomucitila cifundo. (1 Tim. 1:​12-15) Paulo atamva za khalidwe locititsa manyazi la ciwelewele mumpingo wa Cikhristu wa ku Korinto, kodi anacita ciyani? Mmene iye anacitila na nkhani imeneyi, kumatiphunzitsa mmene Yehova amaonetsela cikondi mwa kupeleka cilango kwa atumiki ake, komanso kuwaonetsa cifundo akalapa. w24.08 13 ¶15-16

Cinai, March 5

Nʼcifukwa cake Mwana wa Mulungu anaonekela kuti awononge nchito za Mdyelekezi.​—1 Yoh. 3:8.

M’kupita kwa zaka, Yehova mwapang’ono-pang’ono anamveketsa bwino zimene anthu ocimwa angacite kuti amuyandikile. Munthu woyamba yemwe anaika cikhulupililo cake mwa Yehova pambuyo pa cipanduko ca mu Edeni anali Abele, mwana waciŵili wa Adamu na Hava. Popeza Abele anali kukonda Yehova, ndipo anali kufunitsitsa kumukondweletsa na kumuyandikila, anapeleka nsembe kwa iye. Abele anali m’busa, conco anatenga ena mwa ana a nkhosa zake na kuwapeleka nsembe kwa Yehova. Kodi Yehova anamva bwanji na nsembeyo? Iye “anasangalala ndi Abele komanso nsembe yake.” (Gen. 4:4) Yehova anakondwelanso na nsembe zimene anthu ena amene anali kumukonda komanso kumukhulupilila anapeleka. Mmodzi wa anthuwa anali Nowa. (Gen. 8:​20, 21) Mwa kulandila nsembe zawo, Yehova anaonetsa kuti anthu ocimwa angathe kumukondweletsa komanso kumuyandikila. w24.08 3 ¶5-6

Cisanu, March 6

Mapazi anga anangotsala pangʼono kusocela, mapazi anga anangotsala pangʼono kuteleleka.​—Sal. 73:2.

Anthu ena akaticita zopanda cilungamo, tingakhumudwe kwambili kapena kuvutika maganizo. (Mlal. 7:7) Atumiki okhulupilika, monga Yobu na Habakuku, nawonso anamvapo mwa njila imeneyi. (Yobu 6:​2, 3; Hab. 1:​1-3) M’pomveka kumva conco. Ngakhale n’telo, tiyenela kukhala osamala kuti tisacite zolakwika ndi kuwonjezela mavuto. Tikaona kuti anthu amene amacita zopanda cilungamo sakulandila cilango, tingayambe kuganiza kuti kucita zoyenela kulibe phindu. Wamasalimo wina anaona kuti anthu oipa zinthu zinali kuwayendela bwino ndipo anali kupondeleza anthu olungama. Iye anati: “Izi nʼzimene oipa amacita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.” (Sal. 73:12) Wamasalimoyu anakhumudwa kwambili cifukwa ca zopanda cilungamo zimene anaona, moti anayamba kuganiza kuti kutumikila Yehova kulibe phindu. Anafika pokamba kuti: “Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi, zinali zopweteka kwa ine.”​—Sal. 73:​14, 16. w24.11 3 ¶5-7

Ciwelu, March 7

Mʼpatseni Yehova zimene akuyenela kulandila, inu mabanja a mitundu ya anthu, mʼpatseni Yehova zimene akuyenela kulandila cifukwa ca ulemelelo ndi mphamvu zake.​—Sal. 96:7.

Timamupatsa ulemelelo Yehova cifukwa timamulemekeza kwambili. Tili ndi zifukwa zambili zomulemekezela. Mwacitsanzo, Yehova ndi wamphamvuzonse, mphamvu zake zilibe malile. (Sal. 96:​4-7) Cina, ali ndi nzelu zakuya zimene zimaonekela bwino m’zinthu zimene anapanga. Kuwonjezela apo, iye ndiye kasupe wa moyo, ndipo watipatsa zonse zofunikila kuti tipitilize kukhala ndi moyo. (Chiv. 4:11) Cinanso n’cakuti ndi wokhulupilika. (Chiv. 15:4) Kuwonjezela pa izi, zonse zimene amacita zimayenda bwino, ndipo amasunga malonjezo ake nthawi zonse. (Yos. 23:14) Ndiye cifukwa cake ponena za Yehova, mneneli Yeremiya anati: “Pakati pa anzelu onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiletu aliyense wofanana ndi inu.” (Yer. 10:​6, 7) Kunena zoona, tili ndi zifukwa zabwino zolemekezela Atate wathu wakumwamba. Koma sikuti Yehova amangocita zinthu zimene zimapangitsa kuti tizimulemekeza. Iye alinso ndi makhalidwe abwino amene amatipangitsa kuti tizimukonda kwambili. Koposa zonse, timamupatsa ulemelelo Yehova cifukwa timamukonda mocokela pansi pa mtima. w25.01 3 ¶5-6

Sondo, March 8

Mʼcotseni munthu woipayo pakati panu.​—1 Akor. 5:13.

Adani a Mulungu amafuna kuti tiziona zinthu zimene gulu lathu limacita bwino kuti ni zolakwika. Mwacitsanzo, timaphunzila m’Malemba kuti Yehova amayembekezela alambili ake kukhala oyela kuthupi, m’makhalidwe, komanso kuuzimu. Iye amafuna kuti munthu aliyense wocita zoipa koma wosalapa acotsedwe mu mpingo. (1 Akor. 5:​11, 12; 6:​9, 10) Timatsatila lamulo la m’Malemba limeneli. Koma cifukwa ca zimenezi, adani athu amanena kuti ndife anthu okhwimitsa zinthu, oweluza mopanda cilungamo, komanso opanda cikondi. Tiyenela kuzindikila gwelo la mabodza amenewa. Satana Mdyelekezi ndiye amasonkhezela anthu kunena mabodza amenewa. Iye ni “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44; Gen. 3:​1-5) Conco n’zosadabwitsa kuti Satana amaseŵenzetsa anthu ake kufalitsa mabodza ponena za gulu la Yehova. w24.04 10-11 ¶13-14

Mande, March 9

Adzakwanilitsidwa.​—Ezek. 33:33.

Ngakhale cisautso cacikulu citayamba kale, n’kutheka kuti anthu amene adzaona kugwa kwa “Babulo Wamkulu” adzakumbukila kuti Mboni za Yehova zinali kunena za cocitika cimeneci kwa zaka zambili. Kodi amene adzaone zocitika zimenezi angadzasinthe maganizo awo? (Chiv. 17:5) Ngati anthuwo angadzasinthe maganizo awo, zingakhale monga zinacitikila ku Iguputo m’nthawi ya Mose. Kumbukilani kuti “gulu la anthu a mitundu yosiyana-siyana” linatsagana nawo Aisiraeli potuluka mu Iguputo. Ena mwa anthuwo cikhulupililo cawo cinayamba kukula ataona kuti Milili 10 imene Mose anacenjeza inacitikadi. (Eks. 12:38) Ngati zotelozi zingadzacitike pambuyo pakuti Babulo Wamkulu wawonongedwa, kodi tingadzakhumudwe poona kuti anthu ena awolokela kumbali yathu mapeto atatsala pang’ono kufika? Kutalitali! Tifuna kutengela umunthu wa Atate wathu wa kumwamba yemwe ni, “Mulungu wacifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wacikondi cokhulupilika coculuka komanso coonadi.”​—Eks. 34:6. w24.05 11 ¶12-13

Ciwili, March 10

Gwilitsitsabe citsanzo ca mawu olondola.​—2 Tim. 1:13.

N’ciyani cingacitike tikapatuka pa “mawu olondola”? Ganizilani citsanzo ici. M’zaka za zana loyamba, Akhristu ena anali kufalitsa nkhani yakuti tsiku la Yehova linali litafika kale. Zioneka kuti anthu anakhala na maganizo amenewo cifukwa ca kalata inayake, imene iwo anaganiza kuti mtumwi Paulo ndiye anailemba. M’malo mofufuza kuti adziŵe zoona za nkhaniyo, Akhristu ena ku Tesalonika anaikhulupilila nkhaniyo, na kuyamba kuifalitsanso kwa Akhristu anzawo. Iwo sakanapusitsidwa akanakumbukila zimene mtumwi Paulo anawaphunzitsa pamene anali pakati pawo. (2 Ates. 2:​1-5) Mtumwi Paulo anacenjeza abale ake kuti asamakhulupilile nkhani iliyonse imene amva. Pofuna kuwathandiza kuti asadzapusitsidwenso m’tsogolo, mtumwi Paulo anamaliza kalata yake yaciŵili kwa Atesolonika na mawu akuti: “Landilani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa. Nthawi zonse ndimalemba conci mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembela.”​—2 Ates. 3:17. w24.07 12 ¶13-14

Citatu, March 11

Mukufunika kukhala opilila.​—Aheb. 10:36.

Akhristu a Ciheberi anafunika kupilila zinthu zoyesa cikhulupililo cawo pomwe zinthu zinali kuipilaipila mu Yudeya. Ngakhale kuti ena mwa Akhristuwo anakumanapo na cizunzo, ambili a iwo anakhala Akhristu pa nthawi yomwe kunali mtendele. Mtumwi Paulo ananena kuti, ngakhale kuti Akhristuwo anapilila zinthu zambili zoyesa cikhulupililo cawo, iwo sanakumane na mavuto monga amene Yesu anakumana nawo, moti mpaka kuphedwa. (Aheb. 12:4) Koma pamene Cikhristu cinayamba kufalikila, Ayuda otsutsa anayamba kuwacitila nkhanza kwambili Akhristu. Zaka zingapo, Ayuda oposa 40 “anakonza ciwembu nʼkulumbila pocita kudzitembelela kuti saadya kapena kumwa ciliconse mpaka atapha Paulo.” (Mac. 22:22; 23:​12-14) Ngakhale kuti Akhristuwo anali kudzakumana na cidani komanso kuzunzidwa, iwo sanali kufunika kusiya kusonkhana pamodzi kuti alambile. Anafunikanso kupitiliza kulalikila uthenga wabwino, komanso kusungabe cikhulupililo cawo cili colimba. w24.09 12 ¶15

Cinai, March 12

[Yesu] anauza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambila lelo, uyu akhala mwana wanu.”​—Yoh. 19:26.

Yohane anali mtumwi amene Yesu Khristu anali kumukonda kwambili. (Mat. 10:2) Iye anagwila nchito yolalikila pamodzi na Yesu, ndipo anamuona akucita zozizwitsa. Yohane anakhalabe na Yesu m’nthawi zovuta. Anali kuona pamene Yesu anali kuphedwa, ndipo anamuonanso pamene anaukitsidwa. Anaonanso pamene Cikhristu cinali kufalikila m’zaka za zana loyamba, kucoka pa kagulu kocepa ka anthu okhulupilila mpaka pamene uthenga wabwino “unalalikidwa padziko lonse.” (Akol. 1:23) Yohane anakhala moyo wautali, ndipo cakumapeto kwa moyo wake anauzilidwa kulembako ena mwa mabuku a m’Baibo. Iye analemba zinthu zocititsa cidwi zokhudza “chivumbulutso cimene Yesu Khristu anapeleka.” (Chiv. 1:1) Yohane analemba buku la Uthenga Wabwino lodziŵika na dzina lake. Ndipo analembanso makalata atatu ouzilidwa. Kalata yake yacitatu anali kulembela Mkhristu wina wake wokhulupilika dzina lake Gayo, amene anali kumuona ngati mwana wake wakuuzimu wokondeka. (3 Yoh. 1) Zimene mtumiki wokhulupilikayo analemba atakalamba, zakhala zikulimbikitsa otsatila onse a Yesu kufikila masiku ano. w24.11 12 ¶15-16

Cisanu, March 13

Inunso amuna, . . . muziwapatsa ulemu.​—1 Pet. 3:7.

Mwamuna yemwe amakonda mkazi wake, amamuona kukhala wamtengo wapatali ndipo amamucengeta. Amamuona ngati mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Yehova. (Miy. 18:22; 31:10) Mwa kutelo, iye amacita naye mokoma mtima, komanso mwaulemu ngakhale pa nkhani yakucipinda. Conco, mwamunayo sangakakamize mkazi wake kucita naye zinthu zimene zingapangitse mkaziyo kukhala wosamasuka, kumva kuti akucitidwa nkhanza, komanso kuvutitsa cikumbumtima cake. Mwamuna nayenso adzapewa kucita ciliconse cimene cingavutitse cikumbumtima cake pa nkhani imeneyi. (Mac. 24:16) Inu amuna okwatila, dziwani kuti Yehova amaona ndi kuyamikila kuyesetsa kwanu poonetsa kuti mumalemekeza mkazi wanu m’mbali zonse za umoyo wanu. Khalani otsimikiza mtima kuonetsa kuti mumamulemekeza mkazi wanu mwa kupewa khalidwe lililonse limene lingamucotsele ulemu. M’malomwake, citani naye mokoma mtima, mwaulemu, komanso mwacikondi. Mwa kucita zimenezo, mudzamuonetsa kuti mumamukonda komanso kuti mumamuona kuti ndi wamtengo wapatali. Mukamalemekeza mkazi wanu, mudzateteza cinthu camtengo wapatali kwambili kwa inu, comwe ndi ubwenzi wanu ndi Yehova.​—Sal. 25:14. w25.01 13 ¶17-18

Ciwelu, March 14

Anadzipeleka mʼmalo mwa ife kuti atilanditse. . . ndiponso kuti atiyeletse, kuti tikhale anthu ake apadela, odzipeleka pa nchito zabwino.​—Tito 2:14.

Cimodzi cimasiyanitsa atumiki a Yehova ndi anthu amene amati naonso ndi Akhristu, ndi kukangalika kwawo pogwila nchito yolalikila. Ndiye n’ciyani cingatithandize kukhalabe okangalika komanso kuwonjezela cangu cathu pa nchito yolalikila? Kukambilana citsanzo ca Yesu kungatithandize kukhalabe okangalika pogwila nchito yolalikila. Yesu sanaleke kukhalabe wokangalika pocita utumiki wake. Ndipo pamene nthawi inali kupita, iye anawonjezela cangu cakeco. Yesu m’fanizo lake, anayelekezela nchito yake ndi munthu wosamalila munda wampesa yemwe anagwila nchito molimbika kwa zaka zitatu kusamalila mtengo wa mkuyu umene sunabeleke zipatso. Nayenso Yesu anatha zaka zitatu akulalikila kwa Ayuda, koma ambili a iwo sanalabadile uthenga wake. Wosamalila munda wampesa sanataye ciyembekezo cakuti tsiku lina mtengo wa mkuyuwo udzabeleka zipatso. Nayenso Yesu sanataye ciyembekezo pa anthu amene anali kuwalalikila cakuti angasinthe, ndipo sanacepetse cangu cake pa nchitoyo. (Luka 13:​6-9) Tikamatsatila zimene anaphunzitsa ndi kutengela zimene anacita, ifenso tingakhale okangalika. w25.03 14-15 ¶1-4

Sondo, March 15

Munthu wocenjela amadziwa zimene akucita.​—Miy. 13:16.

Bwanji ngati mwaona munthu amene muganiza kuti angakhale wokuyenelelani? Kodi muyenela kumufikila nthawi yomweyo? Baibo imakamba kuti munthu wocenjela amafufuza asanacitepo kanthu. Conco, n’kwanzelu kuyamba mwamuyang’anila capatali musanamuuze maganizo anu. Kodi kuyang’anila munthu capatali kuyenela kucitika motani? Pa misonkhano ya mpingo kapena pa maceza a gulu, mungadziŵeko zinthu zina zokhudza munthuyo monga uzimu wake, umunthu wake, komanso makhalidwe ake. Kodi ali na mabwenzi otani, ndipo amakonda kukamba zinthu zotani? (Luka 6:45) Kodi zolinga zake n’zofanana ni zanu? Mungafunseko akulu a mu mpingo mwawo, kapena Akhristu okhwima amene amam’dziŵa bwino. (Miy. 20:18) Mungawafunse za mbili yake, komanso makhalidwe ake. (Rute 2:11) Pamene mukuyang’anila munthuyo capatali, samalani kuti musamukhumudwitse na kacitidwe kanu. Musungileni ulemu wake, pewani kumulondalonda, kapena kuloŵelela m’nkhani za munthu mwini. w24.05 22 ¶7-8

Mande, March 16

Pamapeto pake ndinaulula chimo langa kwa inu.​—Sal. 32:5.

Potengela citsanzo ca Yesu, akulu sakhala ofulumila kugamula kuti munthu wocita colakwayo sangalape. Ena angalape pa kukumana kwawo koyamba na komiti ya akulu. Koma ena angafunikile nthawi. Conco, akulu angalinganize kuti akumane na munthuyo maulendo angapo. N’kutheka kuti pambuyo pokumana naye koyamba, Mkhristu wolakwayo angayambe kuganizilapo mozama pa zimene anauzidwa. Angaonetse kudzicepetsa mwa kupempha Yehova kuti amukhululukile chimo lake. (Sal. 32:5; 38:18) Conco, pa kukumana kwawo kotsatila na munthuyo, n’kutheka kuti munthuyo angaonetse khalidwe losiyana na limene anaonetsa pa kukumana kwawo koyamba. Kuti athandize munthuyo kulapa, akulu amamucitila cifundo komanso kumukomela mtima. Iwo amapemphela kwa Yehova kuti adalitse zoyesayesa zawo pothandiza Mkhristu wolakwayo kuzindikila kulakwa kwake na kum’thandiza kuti alape.​—2 Tim. 2:​25, 26. w24.08 22-23 ¶12-13

Ciwili, March 17

Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense,’ akutelo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Conco siyani kucita zoipa kuti mupitilize kukhala ndi moyo.​—Ezek. 18:32.

Yehova safuna kuti munthu aliyense akawonongeke! Iye amafuna kuti ocimwa agwilizanenso naye. (2 Akor. 5:20) Ndiye cifukwa cake Yehova wakhala akulimbikitsa atumiki ake amene anamusiya kuti alape na kubwelela kwa iye. Akulu mumpingo amagwila nchito pamodzi na Yehova pamene akuyesetsa kuthandiza anthu amene anacita macimo aakulu kuti alape. (Aroma 2:4; 1 Akor. 3:9) Kumwamba kumakhala cimwemwe cacikulu munthu wocimwa akalapa! Atate wathu wa kumwamba, Yehova, amasangalala kwambili nthawi zonse nkhosa yosocela ikabwelela mumpingo. Cikondi cathu pa Yehova cimakulilako tikamaganizila cifundo cake komanso kukoma mtima kwake kwakukulu.​—Luka 1:78. w24.08 31 ¶16-17

Citatu, March 18

Yesu atadziwa kuti anthu akufuna kubwera kudzamugwira kuti amuveke ufumu, anachoka nʼkupitanso kuphiri yekhayekha.​—Yoh. 6:15.

Yesu akanalola kuti anthuwo amuveke ufumu, akanakhala kuti akutengako mbali m’ndale za Ayuda, amene anali kulamulidwa na Aroma. Yesu ‘anacoka n’kupita ku phili.’ Conco, ngakhale kuti ena anamukakamiza kutengamo mbali m’zandale, iye sanatelo. Pali phunzilo lofunika kwambili kwa ife pamenepa! N’zoona kuti ena sangatipemphe kuculukitsa cakudya, kucilitsa odwala mozizwitsa, kapena kutiika kuti tikhale wolamulila wawo. Koma iwo angatilimbikitse kutengako mbali m’zandale mwa kuvota, kapena kukamba mawu okhalila kumbuyo munthu winawake amene iwo aona kuti angasinthe zinthu. Komabe, citsanzo ca Yesu citionetsa bwino zimene tiyenela kucita. Iye anakana kutengamo mbali m’ndale za dzikoli moti pambuyo pake anafika pokamba kuti: “Ufumu wanga si wam’dzikoli.” (Yoh. 17:14; 18:36) Akhristu masiku ano ayenela kutengela kaganizidwe ka Yesu komanso kacitidwe kake ka zinthu. Monga mmene Yesu anacitila, nafenso timacilikiza Ufumu wa Mulungu, kuuzako ena za Ufumuwo, komanso kuupemphelela kuti ubwele.​—Mat. 6:10. w24.12 4 ¶5-6

Cinai, March 19

Aliyense amene ali ndi malamulo anga ndipo amawatsatila, ndi amene amandikonda. Komanso amene amandikonda, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsela bwinobwino kwa iye.​—Yoh. 14:21.

Mukamawelenga, ganizilani mmene mungagwilitsile nchito zimene mukuwelengazo. Mwacitsanzo, tengelani cilungamo ca Yehova mwa kucita zinthu mopanda tsankho ndi ena. Tengelani cikondi cimene Yesu ali naco pa Yehova komanso pa anthu mwa kukhala okonzeka kuvutika kaamba ka dzina lake, komanso kudzipeleka pothandiza Akhristu anzanu. Cina, tengelani citsanzo ca Yesu mwa kupitiliza kulalikila ena, kuti nawonso akhale ndi mwayi woonetsa cikhulupililo mu nsembe yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa. Tikapitiliza kuphunzila za dipo, tidzawonjezela cikondi cathu pa Yehova ndi Mwana wake. Zotulukapo zake n’zakuti iwonso adzatikonda mowilikiza. (Yak. 4:8) Conco, tiyeni tigwilitse nchito zinthu zimene Yehova watipatsa kuti tiphunzile za dipo. w25.01 25 ¶16-17

Cisanu, March 20

Macimo anga onse mwawaponyela kumbuyo kwanu.​—Yes. 38:17.

Mawu a pa Lemba la lelo anganenedwenso kuti, “Mwacotsa macimo anga onse kuti musawaonenso.” Mawu ofanizila amenewa amaonetsa kuti Yehova amatenga macimo a munthu wolapa ndi kuwataila kutali kwambili kuti asawaonenso. Mawu a Hezekiya amenewa tingawanenenso motele: “Mwacititsa macimo anga kukhala ngati sanacitikepo.” Baibo imagogomeza mfundo imeneyi pogwilitsa nchito mawu ena ofanizila olembedwa pa Mika 7:​18, 19. Pa lembali, Yehova akufotokozedwa kuti akutaila macimo athu pa nyanja yakuya. M’nthawi zakale, zinali zosatheka kutenganso cinthu cimene caponyedwa pamalo ozama am’nyanja. Pogwilitsa nchito mawu ofanizila amene takambilana, taona kuti Yehova akatikhululukila, amacotsa macimo athu kuti tisadzadziimbenso mlandu pa macimowo. Zoonadi, monga Davide anakambila, “osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zocita zawo zosamvela malamulo ndipo macimo awo akhululukidwa..” (Aroma 4:7) Uku ndiko kukhululuka kwenikweni! w25.02 9 ¶7-8

Ciwelu, March 21

“Kondwelani ndipo muzisangalala mpaka kalekale ndi zimene ndikulenga.”​—Yes. 65:18.

Pali paradaiso winawake padziko lapansi masiku ano wodzala na anthu amene amacita zabwino. Anthu amene ali m’paradaiso ameneyu amafika m’mamiliyoni, ndipo amasangalala na mtendele weniweni. Iwo ndi otsimikiza mtima kusacokamo, ndipo amafunanso kuti anthu ambili abwele kudzagwilizana nawo m’paradaiso wauzimu ameneyu! N’zocititsa cidwi kuti Yehova wapanga malo ophiphilitsa abata m’dziko limene Satana walisandutsa kukhala lacidani, loipa, komanso loopsa. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Mulungu wathu wacikondi amadziwa mmene dongosolo lino la zinthu limatikhudzila, ndipo amapeleka citetezo cimene timafunikila kuti tipitilize kukula mwauzimu. Mawu ake amafotokoza paradaiso wauzimu kuti ndi “malo othawilapo,” komanso “dimba lothililidwa bwino.” (Yes. 4:6; 58:11) Cifukwa ca dalitso la Yehova, nzika za paradaiso ameneyu zimakhala ndi cimwemwe, ndipo n’zotetezeka m’masiku otsiliza ovuta ano.​—Yes. 54:14; 2 Tim. 3:1. w24.04 20 ¶1-2

Sondo, March 22

Nthawi zonse muzipemphela kwa Mulungu.​—Afil. 4:6.

Ngati mufuna kudzaloŵa m’banja, n’zosacita kufunsa kuti mumaipemphelela nkhaniyi kuti mukapeze munthu wokuyenelelani. Zoona zake n’zakuti, Yehova salonjeza kuti adzasankhila aliyense munthu wodzakwatilana naye. Ngakhale n’telo, iye amasamala zofuna zanu komanso mmene mukumvela, ndipo adzakuthandizani pamene mufuna-funa munthu wokuyenelelani. Conco, pitilizani kumuuza zofuna zanu komanso mmene mukumvela. (Sal. 62:8) Pemphelani kuti akupatseni nzelu, komanso kuti mukhale woleza mtima. (Yak. 1:5) Ngakhale kuti simunapeze munthu wokuyenelelani nthawi yomweyo, Yehova analonjeza kuti adzakusamalilani kuthupi, na kukuonetsani cikondi cimene mufunikila. (Sal. 55:22) Koma pali cenjezo: Nkhani yofuna munthu womanga naye banja isamacite kutengelatu maganizo anu onse. (Afil. 1:10) Cimwemwe ceniceni sicidalila kukhala mbeta kapena kukhala pabanja, cimadalila ubale wanu na Yehova. (Mat. 5:3) Ndipo pamene mukali mbeta, muli na mipata yoculuka yowonjezela utumiki wanu (1 Akor. 7:​32, 33) Seŵenzetsani nthawi yanu ya umbeta mwanzelu. w24.05 21 ¶4; 22 ¶6

Mande, March 23

Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.​—Afil. 2:4.

Kodi muyenela kukhala pacibwenzi kwa nthawi yaitali bwanji? Kupanga zisankho mopupuluma, nthawi zambili kumatsogolela kumavuto. (Miy. 21:5) Conco, muyenela kukhala pacibwenzi kwa nthawi yokwanila kuti mumudziŵe bwino mnzanuyo. Koma simuyenela kukhala pacibwenzi kwa nthawi yaitali popanda zifukwa zomveka. Baibo imati, “Cinthu cimene umayembekezela cikalepheleka, mtima umadwala.” (Miy. 13:12) ‘Kodi anthu ena angacite ciyani kuti athandize amene ali pacibwenzi’? Tingawaitanile kucakudya, pa kulambila kwathu kwa pabanja, kapena kuti adzacite nafe zosangalatsa. (Aroma 12:13) Ngati n’kotheka, mungawathandize akafuna thandizo la mayendedwe, munthu owapelekeza, kapena akafuna malo abwino ocezela. (Agal. 6:10)” Ngati akupemphani kuti muwapelekeze, bwanji osauona ngati mwayi wowathandiza? Koma khalani osamala kuti musawasiye ali okha-okha, ndipo pa nthawi imodzimodziyo khalani ozindikila kuti muwapatse mpata akafuna kukambilana zakukhosi. w24.05 30 ¶13-14

Ciwili, March 24

Ndamupatsa nthawi kuti alape.​—Chiv. 2:21.

Akulu amayesetsa kudziŵa zinthu zimene zinatsogolela munthuyo kuti acimwe. Mwacitsanzo, kodi n’ciyani cinafooketsa ubwenzi wake na Yehova? Kodi iye anasiya kuŵelenga Baibo mokhazikika kapenanso kupita mu utumiki? Kodi amapemphelabe kwa Yehova kaŵili-kaŵili? Kapena kodi mapemphelo ake anangokhala amwambo cabe? Kodi wakhala akulola maganizo olakwika kuzika mizu mwa iye? Kodi amakonda kuceza na ndani? Kodi amasankha mwanzelu zosangalatsa zimene amaonelela kapena kumvetsela? Kodi zisankho zimene anapanga pa nkhani zimenezi zinakhudza bwanji kaganizidwe kake komanso zikhumbo zake? Kodi iye akuzindikila mmene zisankho zake zaposacedwa na zocita zake zakhudzila Atate wake Yehova? Mwa kufunsa mafunso othandiza amenewa kwa munthuyo, akulu angathandize munthuyo kuzindikila zimene zinacititsa kuti ubwenzi wake na Yehova ufooke. Ndipo mwina zimenezo n’zimene zinam’tsogolela kuti acite colakwa cimeneco. Akulu amacita zimenezi mokoma mtima, ndipo amapewa kumufunsa mafunso oloŵelela kwambili m’nkhani za munthu mwini. (Miy. 20:5) Kuwonjezela apo, iwo angaseŵenzetse mafanizo pothandiza munthuyo kuona na kuzindikila kulakwa kwake. N’kutheka pa kukumana kwawo koyamba na munthuyo, iye angayambe kumva cisoni cifukwa ca zinthu zoipa zimene anacita, ndipo n’kutheka iye angalape. w24.08 22 ¶9-11

Citatu, March 25

Ndikuyenela kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, cifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzacita.​—Luka 4:43.

Yesu analalikila mokangalika “uthenga wabwino wa Ufumu” podziwa kuti ndiyo nchito imene Mulungu anafuna kuti acite. Kwa Yesu, nchitoyi inali yofunika kwambili kuposa cina ciliconse. Anali ‘kuyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi’ kukaphunzitsa ngakhale kumapeto kwenikweni kwa moyo wake. (Luka 13:22) Anaphunzitsanso anthu ena kuti azigwila nawo nchito yolalikila. (Luka 10:1). Masiku anonso, Yehova ndi Yesu amafuna kuti tiziona nchito yolalikila kukhala yofunika kwambili mu umoyo wathu. (Mat. 24:14; 28:​19, 20) Tikamaona anthu mmene Yehova amawaonela, tidzawonjezela cangu cathu pa ulaliki. Iye akufuna kuti anthu ambili amvetsele uthenga wabwino ndi kucitapo kanthu. (1 Tim. 2:​3, 4) Kuti zimenezi zitheke, iye amatiphunzitsa mokhalila alaliki ogwila mtima pofalitsa uthenga wopulumutsa moyo umenewu. Ngakhale anthu atati asalabadile uthenga wathu palipano, angadzakhale ndi mwayi womvetsela cisautso cacikulu cisanathe. w25.03 15-16 ¶5-7

Cinai, March 26

Aliyense amene wamupatsa moni amakhala ngati akucita nawo nchito zake zoipazo.​—2 Yoh. 11.

Mkhristu aliyense ayenela kuseŵenzetsa cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo posankha mmene acitile zinthu ndi munthu wocotsedwa.” Ena angasankhe kum’patsa moni munthuyo kapena kumulandila pa msonkhano. Komabe sitiyenela kuceza naye munthuyo kapena kucita naye zinthu zina. Ena angafunse kuti, ‘Kodi Baibo siifotokoza kuti munthu amene wapatsa moni munthu wotelo akucita naye nchito zake zoipazo?’ (2 Yoh. 9-11) Nkhani yonse ya pa lembali ionetsa kuti malangizowa amakamba za ampatuko, komanso amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. (Chiv. 2:20) Conco ngati munthu amalimbikitsa ziphunzitso za mpatuko kapena makhalidwe oipa, akulu sadzakonza zakuti akamuyendele. Komabe pali ciyembekezo cakuti anthu otelowa angasinthe. Mpaka pamene munthuyo adzasinthe, sitiyenela kum’patsa moni kapena kumuitanila ku msonkhano wa mpingo. w24.08 30-31 ¶14-15

Cisanu, March 27

Iwo ankavutikabe kuti amvetse zinthu zonse.​—Maliko 6:52.

Pambuyo podyetsa khamu la anthu, Yesu na atumwi ake anacoka pa malowo na kubwelela ku Kaperenao pabwato. Kenako iye anapita ku phili. Anatelo pofuna kupewa kuti khamu la anthulo lisamulonge ufumu. (Yoh. 6:​16-20) Pamene atumwi anali kupalasa bwato, anayang’anizana na cimphepo camphamvu ca mkuntho cimene cinapangitsa mafunde pa nyanjapo. Kenako Yesu anabwela kwa iwo akuyenda pamadzi. Ndipo anauza mtumwi Petulo kuti nayenso ayende pamadzipo. (Mat. 14:​22-31) Yesu atangokwela m’bwatolo, cimphepo camkuntho cija cinaleka. Zimenezi zinacititsa ophunzilawo kukamba kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” (Mat. 14:33) Ngakhale n’telo, iwo anali asanaone kugwilizana pakati pa cozizwitsa cimeneci na zimene zinacitika pamene anali na khamu la anthu lija. Maliko anakamba kuti: “Ophunzilawo anadabwa kwambili cifukwa sanamvetsetse tanthauzo la cozizwitsa ca mitanda ya mkate ija.” (Maliko 6:​50-52) Iwo anali asanamvetse kuculuka kwa mphamvu zocitila zozizwitsa zimene Yehova anali atapatsa Yesu. w24.12 5 ¶7

Ciwelu, March 28

Amene amafuna kuti anthu osiyanasiyana apulumuke nʼkukhala odziwa choonadi molondola.​—1 Tim. 2:4.

Palinso njila ina imene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova. Njilayo ndi kuyesetsa kucita zonse zimene tingathe pa nyengo ino ya Cikumbutso poonetsa Yehova kuti timayamikila dipo. Kuwonjezela pa kukhala ndi colinga cokapezekapo pa Cikumbutso ca caka cino, tingaitanilekonso ena kuti akapezekepo. Afotokozeleni mmene Cikumbutso cimacitikila. Zingakhalenso zothandiza kuwaonetsa vidiyo ya pa jw.org yakuti N’cifukwa Ciani Yesu Anafa? komanso yakuti Kukumbukila Imfa ya Yesu. Akulu afunika kucita khama kuitanila ozilala kuti akapezekeko. Ganizilani cimwemwe cosaneneka cimene cimakhalako kumwamba komanso padziko lapansi, ngati zina mwa nkhosa zosocela za Yehova zathandizidwa kubwelela kwa iye! (Luka 15:​4-7) Pa Cikumbutso, sitiyenela kungopatsa moni abale ndi alongo amene tikuwadziwa kale ayi. Koma tiyenelanso kupatsa moni acatsopano, komanso amene akhala sakupezeka pa misonkhano kwa nthawi yaitali. Tiyenela kuwapangitsa kumva kuti ndi olandilidwa!​—Aroma 12:13. w25.01 29 ¶15

Sondo, March 29

Mulungu anatumiza Mwana wake monga nsembe yophimba macimo athu.​—1 Yoh. 4:10.

Dipo limatithandiza kuona kuti Yehova ndi wacilungamo. Koma koposa pamenepo, limatithandizanso kumvetsa kuzama kwa cikondi cake pa ife. (Yoh. 3:16; Yoh. 4:​9, 10) Nkhani ya dipo imatiphunzitsa kuti Yehova amafuna kuti tikakhale ndi moyo kwamuyaya. Kuwonjezela apo, imatiphunzitsanso kuti amafuna tikhale m’banja mwake. Ganizilani izi: Adamu atacimwa, Yehova anamuthamangitsa m’banja la alambili ake. Pa cifukwa cimeneci, tonse tinabadwila kunja kwa banja la Mulungu. Pa maziko a dipo, Yehova amatikhululukila macimo athu, ndipo m’tsogolo anthu onse omvela komanso acikhulupililo, adzawalowetsa m’banja mwake. Komabe ngakhale palipano, tingakhale paubale wolimba ndi Yehova komanso ndi alambili anzathu. Kunena zoona, Yehova amatikonda kwambili!​—Aroma 5:​10, 11. w25.01 21 ¶6

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 9) Yohane 12:​12-19; Maliko 11:​1-11

Mande, March 30

Zimene anacita potisonyeza cikondi cake ndi izi.​—1 Yoh. 4:9.

N’zosacita kufunsa kuti inunso mumaona kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali. (2 Akor. 9:15) Imfa ya Yesu inatheketsa kuti inu mukhale paubwenzi wathithithi ndi Yehova Mulungu. Mulinso ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. Tili ndi zifukwa zambili zomuyamikilila Yehova amene anatipatsa dipo cifukwa cakuti amatikonda kwambili. Pofuna kutithandiza kukhalabe oyamikila, komanso kuti tisaiwale zimene Yehova ndi Yesu anaticitila, Yesu anatilamula kuti tizikumbukila imfa yake caka ciliconse. (Luka 22:​19, 20) Caka cino, Cikumbutso cidzakhalako pa Cinayi, April 2, 2026. N’zosakaikitsa kuti tonse tikukonzekela kukapezekapo. Tidzapindula kwambili ngati pa nyengo ya Cikumbutso tasinkhasinkha zimene Yehova ndi Mwana wake aticitila. w25.01 20 ¶1-2

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 10) Yohane 12:​20-50

Ciwili, March 31

Landilani malangizo anga osati siliva, komanso kudziwa zinthu mʼmalo mwa golide woyenga bwino kwambili.​—Miy. 8:10.

Mukapitiliza kusinkhasinkha zimene Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu akucitilani, mudzaphunzila zinthu zatsopano zokhudza cikondi cawo. Pa nyengo ya Cikumbutso ca caka cino, mungawelenge mwacifatse buku limodzi kapena kuposelapo la Uthenga Wabwino. Musamawelenge macaputala ambilimbili pa nthawi imodzi. M’malomwake, muziwelenga modekha ndi kuyesetsa kupeza zifukwa zowonjezela zokondela Yehova ndi Yesu. Ngati mwakhala m’coonadi kwa zaka zambili, mungaganize kuti n’zosatheka kuphunzila mfundo zatsopano pankhani zodziwika bwino monga cilungamo ca Mulungu, cikondi cake, komanso dipo. Koma zoona zake n’zakuti, tidzapitilizabe kuphunzila zinthu zatsopano zokhudza nkhani zimenezi komanso zina. Conco muziwelenga zofalitsa zathu zozikika pa Baibo. w25.01 24-25 ¶13-15

Kuwelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika masana: Nisani 11) Luka 21:​1-36

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani