LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es26 masa. 47-57
  • May

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May
  • Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
  • Tumitu
  • Cisanu, May 1
  • Ciwelu, May 2
  • Sondo, May 3
  • Mande, May 4
  • Ciwili, May 5
  • Citatu, May 6
  • Cinai, May 7
  • Cisanu, May 8
  • Ciwelu, May 9
  • Sondo, May 10
  • Mande, May 11
  • Ciwili, May 12
  • Citatu, May 13
  • Cinai, May 14
  • Cisanu, May 15
  • Ciwelu, May 16
  • Sondo, May 17
  • Mande, May 18
  • Ciwili, May 19
  • Citatu, May 20
  • Cinai, May 21
  • Cisanu, May 22
  • Ciwelu, May 23
  • Sondo, May 24
  • Mande, May 25
  • Ciwili, May 26
  • Citatu, May 27
  • Cinai, May 28
  • Cisanu, May 29
  • Ciwelu, May 30
  • Sondo, May 31
Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
es26 masa. 47-57

May

Cisanu, May 1

Mulungu alibe tsankho.​—Aroma 2:11.

Yehova atapulumutsa anthu ake mu ukapolo ku Iguputo, anasankha ansembe kuti azitumikila pa cihema. Anasankhanso Alevi kuti azigwila nchito zina zopatulika za pa cihema. Koma kodi amene anali kutumikila pa cihema, kapena amene anali kukhala pafupi naco, anali kusamalidwa mwapadela? Ayi! Yehova alibe tsankho. Mwisiraeli aliyense anali na mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino na Yehova. Mwacitsanzo, Yehova anaonetsetsa kuti mtundu wonse wa Isiraeli unali kutha kuona cipilala ca mtambo, komanso cipilala ca moto zomwe zinali kukhala pamwamba pa cihema. (Eks. 40:38) Mtambo ukayamba kuyenda, ngakhale amene anali kukhala kutali na cihema anali kutha kuuona, ndipo anali kusonkhanitsa katundu wawo, kupasula matenti awo, na kuyendela pamodzi na mtundu wonse wa Isiraeli. (Num. 9:​15-23) N’cimodzi-modzinso masiku ano, mosasamala kanthu za kumene timakhala, Yehova akhoza kutisamalila na kutiteteza. w24.06 4 ¶10-12

Ciwelu, May 2

Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithawe, cifukwa palibe amene angapulumuke mʼmanja mwa Abisalomu.​—2 Sam. 15:14.

Moyo wa Davide unali paciopsezo. Mwana wake Abisalomu anali atatsimikiza mtima kuti amulanda ufumu basi. (2 Sam. 15:​12, 13) Davide anafunika kuthaŵa kucoka mu Yerusalemu nthawi yomweyo! Pamene atumiki ake anali kucoka, Davide anazindikila kuti afunika kusiya m’mbuyo mmodzi wa atumiki ake kuti azimuuza mapulani a Abisalomu. Conco iye anatuma Zadoki na ansembe ena kuti abwelele mu mzinda kukakhala ngati akazitape. (2 Sam. 15:​27-29) Iwo anafunika kugwila nchito imeneyi mosamala kwambili. Davide anauza Zadoki komanso mnzake wokhulupilika Husai kuti amuthandize na pulani imene anapanga. (2 Sam. 15:​32-37) Potsatila pulaniyo Husai anakwanitsa kukhala phungu wodalilika wa Abisalomu, ndipo anamupatsa pulani ya mmene angam’thilile nkhondo Davide. Koma pulaniyo kwenikweni inali kupeleka mpata kwa Davide wokonzekela kuukilako. Kenako Husai anauza Zadoki komanso Abiyatara za pulani imene anauza Abisalomu. (2 Sam. 17:​8-16) Ndipo amuna aŵili amenewa anatumiza uthengawo kwa Davide. Uthengawo unacita mbali yaikulu poteteza moyo wa Davide.​—2 Sam. 17:​21, 22. w24.07 4-5 ¶9-10

Sondo, May 3

Yehova wanena kuti: “Bwelani tsopano, tiyeni tikambilane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.”​—Yes. 1:18.

Atumiki ena a Yehova amadziimbabe mlandu mopitilila malile cifukwa ca zoipa zimene anacita asanabatizike kapena atabatizika kale. Koma tisaiŵale kuti Yehova amatikonda kwambili, mwakuti anapeleka dipo kuti macimo athu akhululukidwe. Conco, iye amafuna kuti tiilandile mphatso ya dipo imeneyi. Yehova amatitsimikizila kuti akatithandiza kuti ‘tikhalenso pa ubwenzi wabwino’ na iye samakumbukilanso macimo athu. Ndife oyamikila kwambili kuti Atate wathu wacikondi, Yehova, samakumbukila macimo athu akale, ndipo saiŵala zabwino zimene timacita. (Sal. 103:​9, 12; Aheb. 6:10) Ngati mumadziimba mlandu cifukwa ca zimene munacita kumbuyoku, mungacite bwino kuganizila zimene mukucita pali pano na zimene mudzacita m’tsogolo. Simungasinthe zomwe zinacitika kale. Koma mungatamande Yehova na kumukondweletsa pali pano. Mungamaganizilenso za tsogolo labwino limene wakulonjezani. w24.10 8 ¶8-9

Mande, May 4

Muvale umunthu watsopano.​—Akol. 3:10.

Nthawi zina mungacite ulesi kuŵelenga Baibo mukaona kuti pali zambili zimene mufunika kuwongolela. Ganizilani citsanzo ici. Tinene kuti pa tsiku loyamba la kuŵelenga Baibo kwanu, mwapeza uphungu wakuti sitiyenela kucita zinthu mokondela. (Yak. 2:​1-8) Ndipo mwaona kuti mufunika kusintha mmene mumacitila zinthu na ena, moti mwatsimikiza mtima kucita zimenezo. Pa tsiku laciŵili, mukuŵelenga mavesi amene aonetsa kufunika kolamulila lilime lathu. (Yak. 3:​1-12) Zimenezi zakupangitsani kuzindikila kuti nthawi zina mumakamba zinthu zosalimbikitsa. Conco mwatsimikiza mtima kuti muzikamba zinthu zolimbikitsa. Pamene mukuŵelenga Baibo pa tsiku lacitatu, mukupeza cenjezo lakuti sitiyenela kukhala bwenzi la dziko. (Yak. 4:​4-12) Conco mukuzindikila kuti muyenela kukhala wosamala na zimene mumaŵelenga, kuonelela, komanso kumvetsela. Podzafika tsiku lacinayi, mungayambe kuona kuti pali zambili zimene mufunika kuwongolela, moti mukucita ulesi. Musalefuke. Koma kumbukilani kuti tifunika kupitiliza kuvala “umunthu watsopano. w24.09 5-6 ¶11-12

Ciwili, May 5

Muvomeleze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyela. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za ciyembekezo canu, koma muziwayankha mofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.​—1 Pet. 3:15.

Yesu anadziŵa kuti Yehova anali kuona zopanda cilungamo zimene zinali kumucitikila. Iye anali na cikhulupilillo cakuti Yehova adzacotsapo kupanda cilungamo konse panthawi yake. Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kukhala osamala na zimene timakamba munthu wina akaticitila zopanda cilungamo. Zopanda cilungamo zina zimakhala zazing’ono ndipo tingangozinyalanyaza. Kapena tingangokhala cete kuti tipewe kukamba zinthu zimene zingawonjezele mavuto. (Mlal. 3:7; Yak. 1:​19, 20) Koma nthawi zina tingafunike kulankhula tikaona kuti wina akucitidwa zopanda cilungamo kapena tikafunika kukhalila kumbuyo coonadi. (Mac. 6:​1, 2) Koma tikasankha kulankhula, tifunika kuyesetsa kucita zimenezo mofatsa komanso mwaulemu. Tingatengelenso citsanzo ca Yesu mwa kusiya zonse m’manja mwa “Woweluza amene amaweluza mwacilungamo.”​—1 Pet. 3:15. w24.11 5-6 ¶10-12

Citatu, May 6

Angelo a Mulungu amasangalala kwambili cifukwa ca munthu mmodzi wocimwa amene walapa.​—Luka 15:10.

Munthu wocimwa akalapa, zimakhala zokondweletsa zedi! (Luka 15:7) Ngakhale kuti akulu amacita zonse zotheka kuti munthuyo alape, kodi ndani maka-maka amene amathandiza munthuyo kusintha? Kumbukilani zimene mtumwi Paulo analemba ponena za anthu ocimwa. Iye anati: “Mwina Mulungu angawalole kulapa.” (2 Tim. 2:25) Conco Yehova, osati munthu wina aliyense, ndiye amathandiza Mkhristu wolakwayo kusintha kaganizidwe kake na kacitidwe kake ka zinthu. Paulo anafotokoza zinthu zabwino zimene zimacitika munthu akalapa. Iye anafotokoza kuti munthuyo amadziŵa coonadi molondola, nzelu zimamubwelela, ndipo amapulumuka mu msampha wa Mdyelekezi. (2 Tim. 2:26) Munthu amene anacita chimo akalapa, a’m’komiti amapanga makonzedwe ocita maulendo aubusa kwa munthuyo. Amacita zimenezo pofuna kuti munthuyo apitilize kulandila thandizo lofunikila limene lingamuthandize kupewa misampha ya Satana, komanso kuti apitilize kucita zoyenela.​—Aheb. 12:​12, 13. w24.08 23 ¶14-15

Cinai, May 7

Sikuti mukundifunafuna cifukwa coti munaona zizindikilo ayi, koma cifukwa coti munadya mikate nʼkukhuta.​—Yoh. 6:26.

Khamu la anthu limene Yesu anadyetsa, linaika kwambili maganizo awo pa kukhutilitsa zofuna zawo komanso zikhumbo zawo zakuthupi. Motani? Tsiku lotsatila, iwo anapeza kuti Yesu na atumwi ake anali atacoka kudela lawo. Conco, khamu la anthulo linakwela mabwato ocoka ku Tiberiyo na kulowela ku Kaperenao kukafunafuna Yesu. (Yoh. 6:​22-24) Kodi iwo anacita zimenezo cifukwa cakuti anali kufuna kumvetsela zambili za Ufumu? Ayi. Iwo anacita zimenezo cifukwa cakuti anali kufuna kuti Yesu awapatse mkate wina. Tidziŵa bwanji zimenezi? Onani zinacitika khamu la anthu lija litapeza Yesu pafupi na mzinda wa Kaperenao. Yesu mosapita m’mbali anauza anthuwo kuti anabwela kudzam’funafuna cifukwa anali kufuna kukhutilitsa njala yawo yakuthupi. Ngakhale kuti anthuwo ‘anadya mikate n’kukhuta,’ Yesu anawauza kuti cakudya cimeneco “cimawonongeka.” Conco, iye anawalimbikitsa kuti ayenela kuyesetsa kukhala na cakudya “cimene cimabweletsa moyo wosatha.” (Yoh. 6:​26, 27) Yesu anawauza kuti Atate wake angawapatse cakudya cimeneco. w24.12 5 ¶8-9

Cisanu, May 8

Munthu wanzelu amasankha mawu mwanzelu akamalankhula, ndipo mawu ake amakopa anthu ena.​—Miy. 16:23.

Kuti muziphunzitsa mogwila mtima, inu abale, muziseŵenzetsa Mawu a Mulungu pophunzitsa komanso popeleka uphungu. Kuti mucite zimenezi, muyenela kumaŵelenga Baibo komanso zofalitsa zathu mwakhama. (Miy. 15:28) Poŵelenga, muziyesetsa kuona mmene mungagwilitsile nchito Malemba m’njila yoyenela. Ndipo pamene mukuphunzitsa, muziyesetsa kuwafika pamtima omvela anu. Cinanso cingakuthandizeni kukulitsa luso lanu la kuphunzitsa, ni kupempha thandizo kwa akulu ena aluso, na kuyesetsa kucita zimene akuuzani. (1 Tim. 5:17) Akulu ayenela kukhala oti ‘angathe kulimbikitsa’ abale na alongo awo. Nthawi zina akulu ayenela kupeleka uphungu kwa abale na alongo, ngakhale ‘kuwadzudzula’ kumene. Komabe, nthawi zonse akulu ayenela kucita zimenezi mokoma mtima. Ngati ndinu wokoma mtima komanso wacikondi, ndipo mumaseŵenzetsa Mawu a Mulungu pophunzitsa, mudzakhala mphunzitsi waluso cifukwa mudzakhala mukutengela Mphunzitsi Wamkulu, Yesu.​—Mat. 11:​28-30; 2 Tim. 2:24. w24.11 24 ¶16

Ciwelu, May 9

Lengezani ulemelelo wake pakati pa anthu a mitundu ina.​—Sal. 96:3.

Tingapatse Yehova ulemelelo mwa zimene timakamba ponena za iye. Anthu a Yehova ayenela,’ ‘kutamanda dzina lake,’ ‘kulengeza uthenga wabwino wa cipulumutso cake,’ komanso ‘kulengeza ulemelelo wake pakati pa anthu a mitundu ina.’ (Sal. 96:​1-3) Zonsezi ndi njila zimene tingapatsile ulemelelo Atate wathu wakumwamba. (Mac. 4:29) Tingamupatsenso ulemelelo Yehova mwa kum’patsa zinthu zathu za mtengo wapatali. Olambila oona akhala akulemekeza Yehova mwa njila imeneyi. (Miy. 3:9) Mwacitsanzo, Aisiraeli anapeleka ndalama, komanso zinthu zawo za mtengo wapatali pothandizila nchito yomanga kacisi komanso kuisamalila. (2 Maf. 12:​4, 5; 1 Mbiri 29:​3-9) Ena mwa ophunzila a Khristu anali kutumikila Yesu ndi atumwi ake “pogwilitsa nchito cuma cawo.” (Luka 8:​1-3) Nawonso Akhristu a m’nthawi ya atumwi anatumiza ndalama kwa abale ndi alongo awo akuuzimu a kudela kumene kunagwa njala. (Mac. 11:​27-29) Masiku ano, ifenso tingapatse ulemelelo Yehova mwa kucita zopeleka zaufulu. w25.01 4 ¶8; 5 ¶11

Sondo, May 10

Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe mʼmadzi?​—Mac. 10:47.

N’ciyani cinathandiza Koneliyo kubatizika? Baibo limatiuza kuti iye “ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse.” Ndipo Koneliyo anali kupemphela mocondelela kwa Mulungu nthawi zonse. (Mac. 10:2) Koneliyo atalalikidwa uthenga wabwino ndi Petulo, iye ndi a m’banja lake anakhulupilila Khristu ndipo anabatizika nthawi yomweyo. (Mac. 10:​47, 48) Koneliyo anali wokonzeka kupanga masinthidwe alionse ofunikila kuti ayambe kulambila Yehova limodzi ndi banja lake. (Yos. 24:15; Mac. 10:​24, 33) Udindo wa Koneliyo ukanamulepheletsa kukhala Mkhristu. Koma sanalole zimenezo. Kodi mufunikila kusintha zinazake pa umoyo wanu kuti mubatizike? Ngati n’telo, Yehova adzakhala Mthandizi wanu. Mukamayesetsa kumutumikila motsatila mfundo za m’Baibulo, iye adzakudalitsani. w25.03 5 ¶12-13

Mande, May 11

Uzipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu.​—1 Tim. 4:7.

Mukamva nkhani zabodza zokhudza gulu la Mulungu kapena abale amene akutsogolela, muzikumbukila mmene adani a Mulungu anacitila kwa Yesu na ophunzila ake a m’zaka za zana loyamba. Baibo inanenelatu kuti anthu a Mulungu adzazunzidwa na kunamizilidwa. Ndipo n’zimene zikucitika masiku ano. (Mat. 5:​11, 12) Tikazindikila gwelo lenileni la mabodza na kucitapo kanthu mwamsanga, sitingasoceletsedwe. Kodi tiyenela kucitapo ciyani? Kanizani nkhani zabodza. Mtumwi Paulo anapeleka malangizo omveka bwino a zimene tiyenela kucita tikamva nkhani zabodza. Iye anauza Timoteyo kuti: “Uletse anthu ena . . . kuti asamamvele nkhani zonama.” Anamuuzanso kuti: “Uzipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu.” (1 Tim. 1:​3, 4) Timakaniza nkhani zabodza cifukwa tidziŵa gwelo lake. Timagwilitsitsa “mawu olondola” a coonadi.​—2 Tim. 1:13. w24.04 11 ¶16; 13 ¶17

Ciwili, May 12

Amagwilitsa nchito mawu okopa ndiponso acinyengo kuti apusitse anthu oona mtima.​—Aroma 16:18.

Khalanibe ogwilizana nawo anthu okhulupilika kwa Yehova. Mulungu afuna kuti tizimulambila mogwilizana. Tidzakhalabe ogwilizana malinga ngati tikangamilabe ku coonadi. Aliyense amene amafalitsa nkhani zotsutsana na coonadi, amabweletsa magaŵano mu mpingo, ndipo Mulungu amatiuza kuti ‘tiziwapewa.’ Tikapanda kuwapewa, angatikanganule ku coonadi. (Aroma 16:17) Tikazindikila coonadi na kucigwila zolimba tidzakhala athanzi komanso otetezeka kuuzimu. (Aef. 4:​15,16) Tidzakhalanso otetezeka ku ziphunzitso zonama, komanso mauthenga abodza osonkhezeledwa na Satana. Tidzakhalabe otetezeka m’manja mwa Yehova panthawi ya cisautso cacikulu. Motelo, pitilizani kucigwilitsitsa mwamphamvu coonadi, “ndipo Mulungu wamtendele adzakhala nanu.”​—Afil. 4:​8, 9. w24.07 13 ¶16-17

Citatu, May 13

Munthu ameneyu anapeleka nsembe imodzi yamacimo yothandiza mpaka kalekale.​—Aheb. 10:12.

Yesu anaika kwambili maganizo ake pa kuthandiza anthu amene anali kuvutika cifukwa ca ucimo. Ndipo anawapempha anthuwo kuti akhale otsatila ake. Iye anadziŵa kuti anthu anali kukumana na mavuto cifukwa ca ucimo. Yesu anathandiza kwambili anthu amene anali kudziŵika kuti ni ocimwa kwambili. Mwa fanizo, iye anakamba kuti: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufuna.” Anaonjezela kuti: “N’nabwela kudzaitana anthu ocimwa osati olungama.” (Mat. 9:​12, 13) Ndipo n’zimene Yesu anali kucita. Iye anacita zinthu mokoma mtima na mzimayi amene anatsuka mapazi ake na misozi, ndipo anamukhululukila macimo ake. (Luka 7:​37-50) Yesu anaphunzitsa mayi wacisamariya mfundo zofunika za coonadi ngakhale kuti anali kudziŵa kuti mayiyo anali kukhala na mwamuna yemwe sanali wake. (Yoh. 4:​7, 17-19, 25, 26) Mulungu anapatsanso Yesu mphamvu zogonjetsa imfa yomwe imabwela cifukwa ca ucimo. Yesu anaukitsapo amuna, akazi, ana, komanso acikulile amene anamwalila.​—Mat. 11:5. w24.08 4 ¶9-10

Cinai, May 14

Adzaweluza anthu okhala padziko lapansi mwacilungamo ndipo adzaweluza mitundu ya anthu mokhulupilika.​—Sal. 96:13.

Kodi Yehova adzalilemekeza motani dzina lake posacedwa? Adzatelo mwa ziweluzo zake. Posacedwa, adzawononga Babulo Wamkulu cifukwa wabweletsa citonzo pa dzina lake loyela. (Chiv. 17:​5, 16; 19:​1, 2) Ena amene adzaone kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, angadzasankhe kugwilizana nafe pa kulambila koona. Pamapeto pake, Yehova adzawononga dongosolo lonse la Satanali pa Aramagedo, ndi kucotsa onse amene amamutsutsa ndi kunyoza dzina lake. Koma adzapulumutsa onse amene amamukonda ndi kumumvela, amenenso amanyadila kumupatsa ulemelelo. (Maliko 8:38; 2 Ates. 1:​6-10) Pambuyo pa ciyeso comaliza cimene cidzabwela pambuyo pa zaka 1,000 za ulamulilo wa Khristu, Yehova adzakhala atayeletsa dzina lake kothelatu. (Chiv. 20:​7-10) Panthawi imeneyo, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemelelo wa Yehova, ngati mmene madzi amadzazila nyanja.” (Hab. 2:14) Zidzakhala zokondweletsa zedi pa nthawiyo pamene munthu aliyense adzapatse Yehova ulemelelo woyenelela dzina lake! w25.01 7 ¶15-16

Cisanu, May 15

Muyenela kupilila kuti muphunzitsidwe.​—Aheb. 12:7.

N’ciyani cinali kudzathandiza Akhristu a Ciheberiwo kupilila pamene anali kuzunzidwa? Mtumwi Paulo anafuna kuthandiza Akhristuwo kuganizila mapindu amene akanapeza akapilila cizunzo. Conco, anawafotokozela kuti Akhristu akakumana na zinthu zoyesa cikhulupililo cawo, Mulungu angaseŵenzetse nthawi ya mayeselowo kuwaphunzitsa zinazake. Pa nthawiyo, iye angawathandize kukulitsa makhalidwe abwino a Cikhristu. Kuganizila mapindu amene akanapeza akapilila cizunzo, kukanathandiza Akhristuwo kupilila mosavuta. (Aheb. 12:11) Paulo analimbikitsa Akhristu a Ciheberi kukhala olimba mtima komanso kuti asalefuke pokumana na zinthu zoyesa cikhulupililo cawo. Iye anali pamalo abwino owalimbikitsa pa nkhani yopilila. Zinali conco cifukwa asanakhale Mkhristu, iye anali kuzunza Akhristu. Conco anali kumvetsa cizunzo cimene iwo anali kukumana naco. Anali kudziŵanso zimene munthu angacite kuti apilile cizunzo. Anali kudziŵa zimenezi cifukwa anakumana na mazunzo osiyana-siyana atakhala Mkhristu. 2 Akor. 11:​23-25. w24.09 12-13 ¶16-17

Ciwelu, May 16

Pitilizani kukhala maso.​—Mat. 25:13.

Tsiku lililonse likadutsa, tifunika kuwonjezela cangu cathu pa nchito yolalikila. Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi ikutha. Ganizilani zimene Yesu ananenelatu zokhudza nchito yolalikila m’masiku otsiliza, monga mmene lemba la Maliko 13:10 imakambila. Malinga na uthenga wa Mateyu pa nkhani imeneyi, Yesu anakamba kuti uthenga wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse kumene kuli anthu “mapeto” asanafike. (Mat. 24:14) Mawu akuti mapeto amatanthauza kuthelatu kwa dongosolo loipali la Satana. Yehova anaikilatu “tsiku . . . ndi ola” limene zinthu zimenezi zidzacitika. (Mat. 24:36; Mac. 1:7) Tsiku lililonse limene ladutsa limatiyandikizitsa ku tsiku limenelo. (Aroma 13:11) Koma pakali pano tiyenela kupitiliza kulalikila mpaka mapeto adzafike. Pamene tikuganizila ulaliki wathu, tingacite bwino kudzisanthula na funso ili: N’cifukwa ciyani timalalikila uthenga wabwino? Kuyankha mwacidule, cikondi n’cimene cimatilimbikitsa. Zimene timacita pa nchito yolalikila zimaonetsa cikondi cathu pa uthenga wabwino, pa anthu, koma maka-maka pa Yehova na dzina lake. w24.05 14-15 ¶2-3

Sondo, May 17

Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambili.​—Gen. 1:31.

Makolo, limbikitsani mwana wanu kukhala na cidwi comaganizila pa zinthu zacilengedwe. Pamene mukuyenda na mwana wanu ku malo akuminda kapena cakuthengo, muthandizeni kuona mapatani a mpangidwe wa zinthu omwe timaona pa zacilengedwe zocititsa cidwi. Zimenezi n’zofunika cifukwa ciyani? Cifukwa mapatani amenewo amaonetsa luso komanso nzelu zimene Yehova ali nazo zopanga zinthu. Mwacitsanzo, titenge mapatani ooneka ozungulila monga mwa makulungidwe a nkhata. Kwa zaka zambili, asayansi akhala akuwafufuza mapatani amenewo n’kuwaunika kuti awamvetsetse. Wasayansi wina dzina lake Nicola Fameli, anafotokoza kuti mukaŵelenga mizele ya mapatani azungulizunguli amenewo, mumapeza kuti ali mu dongosolo linalake la ziŵelengelo. Mapatani azungulizunguli amenewo timawaona mu zinthu zambili, monga mu mlalang’amba, zigoba za nkhono, m’masamba a zomela zina, komanso kumutu wa mpenyadzuwa. w24.12 16 ¶7

Mande, May 18

Iye angakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo.​—Deut. 30:20.

Papita nthawi yaitali kwambili kucokela pamene Mose, Davide, na Yohane anali na moyo padziko lapansi. Ndipo panthawi imene anali moyo, zinthu zinali zosiyana kwambili na mmene zilili masiku ano. Ngakhale n’telo, pali zambili zimene timafanana nawo. Iwo anali kutumikila Mulungu woona. Nafenso n’zimene timacita. Mofanana na iwo, timapemphela kwa Yehova, timamudalila, ndipo timayang’ana kwa iye kuti atitsogolele. Ndipo monga mmene zinalili na amuna akale amenewa, nafenso timakhulupilila kuti Yehova amadalitsa anthu amene amamumvela. Conco, tiyeni tipitilize kumvela malamulo a Yehova. Tikatelo tidzakhala tikutsatila zimene amuna akale amenewa anakamba m’mawu awo othela. Ndipo tikacita zimenezi, zinthu zidzatiyendela bwino mu zonse zimene tikucita. ‘Tidzakhala na moyo kwa nthawi yaitali,’ inde kwamuyaya! Tidzakhalanso na cimwemwe podziŵa kuti tikukondweletsa Atate wathu wacikondi wakumwamba amene amakwanilitsa malonjezo ake onse m’njila imene sitimaiyembekezela kapena kuiganizila.​—Aef. 3:20. w24.11 13 ¶20-21

Ciwili, May 19

Mulungu wapeleka zocita kwa munthu aliyense mumpingo.​—1 Akor. 12:28.

M’zaka za zana loyamba, abale ena anali kuikidwa kukhala atumiki othandiza. (1 Tim. 3:8) N’kutheka kuti amenewa, ni amene anali kucita “utumiki wothandiza anthu” umene mtumwi Paulo anakambapo. Conco zioneka kuti atumiki othandiza anali kusamalila mbali zina zofunika kuti akulu akhale na nthawi yophunzitsa mu mpingo komanso kuusamalila. Mwacitsanzo, n’kutheka kuti iwo anali kuthandiza kukopolola Malemba kapena kukagula zinthu zoseŵenzetsa pokopolola Malemba. Ganizilani nchito zimene atumiki othandiza amagwila mu mpingo mwanu. (1 Pet. 4:10) Ena angapatsidwe nchito yosamalila maakaunti a mpingo kapena kusamalila magawo. Enanso angapatsidwe nchito yosamalila mabuku kuti ofalitsa azipeza mabuku ofunikila. Atumiki othandiza ena angapatsidwe nchito yosamalila mamaikolofoni, ena ku saundi, ndipo ena angakhale akalinde. Angathandizenso posamalila Nyumba ya Ufumu kuti ikhale yosamalika bwino komanso yaukhondo. Nchito zonsezi zimathandiza kuti mpingo uziyenda bwino. 1 Akor. 14:40. w24.10 19 ¶4-5

Citatu, May 20

Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikila.​—Afil. 4:13.

Tikamakumbukila kuti Yehova ni Mulungu wamoyo komanso kuti ni wokonzeka kutithandiza, tidzatha kupilila mayeso alionse amene tingakumane nawo, kaya akhale aakulu kapena aang’ono. iye ni Wamphamvuzonse, ndipo angatipatse mphamvu kuti tipilile. Izi zimatithandiza kuyang’anizana na mavuto alionse mwacidalilo. Yehova akatithandiza pa mavuto aang’ono amene takumana nawo, timakhala na cidalilo cakuti adzatithandizanso tikadzakumana na mavuto aakulu. Ganizilani zocitika ziŵili izi pa umoyo wa Mfumu Davide. Pamene iye anali m’busa wacinyamata, cimbalangondo cinagwila nkhosa ya atate ake. Pa nthawi inanso mkango unacita cimodzimodzi. Pa zocitika zonsezi, Davide molimba mtima anathamangitsa zilombozo na kupulumutsa nkhosazo. Koma iye sanaone kuti wacita zimenezi mwa mphamvu zake ayi. Anadziŵa kuti Yehova ndiye anam’patsa mphamvu. (1 Sam. 17:​34-37) Kusinkhasinkha zocitikazo kunam’patsa cidalilo Davide cakuti Mulungu wamoyo adzam’patsanso mphamvu m’tsogolo. w24.06 21 ¶5-6

Cinai, May 21

Munthu akayankhila nkhani asanaimvetsetse, kumakhala kupusa ndipo amacita manyazi.​—Miy. 18:13.

Tinene kuti mwaitanidwa ku maceza enaake. Kodi muyenela kupita? Ngati simum’dziwa bwino munthu amene wakonza macezawo komanso zimene walinganiza, mungafunikile kumufunsa mafunso monga akuti: “Kodi macezawo adzacitikila kuti? Nanga adzacitika nthawi yanji? Kodi kudzakhala anthu oculuka motani? Ndani adzayang’anila macezawo? Ndani adzapezekako? Palinganizidwa zocitika zotani? Kodi kudzakhala mowa?” Mayankho a mafunso amenewa angakuthandizeni kupanga cisankho canzelu. Mukamvetsa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo, ganizilam’poni mosamala. Mwacitsanzo, bwanji ngati mwadziwa kuti anthu amene salemekeza mfundo za m’Baibulo adzapezeka ku macezawo, kapena ngati mowa udzagawilidwa mwacisawawa? Kodi n’kutheka macezawo angasinthe n’kukhala phwando la phokoso? (1 Pet. 4:3) Mukamvetsa nkhani yonse, mudzakwanitsa kupanga cisankho canzelu. w25.01 15 ¶4-5

Cisanu, May 22

Ngakhale kuti macimo anu ndi ofiila kwambili, adzayela kwambili.​—Yes. 1:18.

Yehova amagwilitsa nchito mawu ofanizila potithandiza kumvetsa mmene amagwilitsila nchito nsembe ya dipo pofafaniza macimo a anthu olapa. Inki yofiila ikadonthela pa covala coyela, zimakhala zovuta kuyeletsapo. Komabe, pogwilitsa nchito mawu ofanizila amenewa, Yehova akutitsimikizila kuti macimo athu angayeletsedwe kothelatu moti sangaonekenso. Macimo amayelekezedwa ndi “nkhongole.” (Mat. 18:​32-35) Conco nthawi iliyonse tikacimwila Yehova, zimakhala ngati tikuwonjezela nkhongole imene tili nayo kale kwa iye. Moti nkhongoleyo imakhala yaikulu zedi! Koma Yehova akatikhululukila, zimakhala ngati wafafaniza nkhongoleyo. Iye safuna kuti tibweze nkhogole ya macimo amene anawakhululuka kale. Munthu amamva bwino akauzidwa ndi mnzake kuti asabwezenso nkhongole. Nafenso timamva bwino Yehova akatikhululukila macimo athu. w25.02 9-10 ¶9-10

Ciwelu, May 23

Paja si udindo wa ana kusunga cuma kuti cidzathandize makolo awo, koma makolo ndi amene ayenela kusungila cuma ana awo.​—2 Akor. 12:14.

Makolo angafunikile thandizo pamene akukalamba, ndipo ana ambili amakhala okonzeka kuwathandiza. (1 Tim. 5:4) Koma makolo acikhristu amazindikila kuti cimwemwe ceniceni cimabwela cifukwa cothandiza ana awo kukhala atumiki a Yehova, osati cifukwa colela anawo kuti akawathandize kuthupi. (3 Yoh. 4) Mwa citsanzo canu, phunzitsani ana anu kudalila Yehova pamene mukuwakonzekeletsa kuti akathe kudzisamalila okha. Kungoyambila ali ana, athandizeni kuona kufunika kogwila nchito molimbika. (Miy. 29:21; Aef. 4:28.) Pamene akusinkhuka, athandizeni kuti aziikako nzelu kusukulu. Makolo acikhristu angacite bwino kufufuza mfundo za m’Baibulo ndi kuzigwilitsa nchito pothandiza ana awo kuona mmene angagwilitsile nchito maphunzilo awo mwanzelu kuti akathe kudzisamalila okha, komanso kuti azitengamo mbali mokwanila m’nchito yacikhristu. w25.03 30-31 ¶15-16

Sondo, May 24

Muvale umunthu watsopano.​—Aef. 4:24.

Mu Yesaya caputala 65, Yehova anafotokoza mmene zinthu zidzakhalile kwa anthu amene adzakhale m’paradaiso wauzimu. Mawuwo anakwanilitsidwa koyamba mu 537 B.C.E. Panthawiyo, Ayuda olapa anamasulidwa mu ukapolo ku Babulo, ndipo anabwelela ku dziko lawo. Yehova anadalitsa anthu ake, ndipo anawathandiza kukonza mzinda wowonongedwa wa Yerusalemu kuti ukhalenso wokongola. Anawathandizanso kubwezeletsa kacisi wake kuti akhalenso cimake ca kulambila koona. (Yes. 51:11; Zek. 8:3) Kukwanilitsidwa kwaciwili kwa ulosi wa Yesaya kunayamba mu 1919 C.E. pomwe alambili a Yehova amakono anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Ndiyeno paradaiso wauzimu anayamba kukula kuzungulila dziko lonse lapansi. Alaliki a Ufumu okangalika anakhazikitsa mipingo ndipo anabala zipatso zauzimu. Amuna na akazi amene anali aciwawa komanso na makhalidwe aucinyama, anasintha n’kuvala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.” w24.04 20-21 ¶3-4

Mande, May 25

Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.​—Agal. 6:5.

Ku maiko ena, makolo kapena acibale ena acikulile ni amene amasankhila munthu womanga naye banja. Koma kwina, acibale kapena mabwenzi amangokupezela munthu amene ungayambe naye cibwenzi. Iwo amalinganiza zakuti mukakumane kuti muone ngati ndinu oyenelelana. Mukapemphedwa kuti mupezele wina cibwenzi, kapena womanga naye banja, muziganizila zimene aliyense wa iwo akufuna. Mukapeza munthu amene muona kuti angakhale woyenelela, fufuzani zambili zokhudza umunthu wake na makhalidwe ake, koma maka-maka uzimu wake. Kukhala pa ubale wolimba na Yehova kumaposa ndalama, maphunzilo, ngakhale kuchuka. Komabe, kumbukilani kuti aŵiliwo ndiwo ayenela kupanga cisankho, kaya kukwatilana kapena ayi. w24.05 23 ¶11

Ciwili, May 26

Mnzako weniweni amakusonyeza cikondi nthawi zonse.​—Miy. 17:17

Tingathandize amene ali pacibwenzi mwa zokamba zathu. Nthawi zina tingafunike kudziletsa kuti tisalankhule ciliconse. (Miy. 12:18) Mwacitsanzo, tingakhale ofunitsitsa kuuzako anzathu kuti uje na uje ali pacibwenzi, koma anthuwo angafune kukawauza okha za nkhaniyo. Sitiyenela kuwanenela misece amene ali pacibwenzi kapena kuwaimba mlandu pa nkhani zaumwini. (Miy. 20:19; Aroma 14:10; 1 Ates. 4:11) Kuwonjezela apo, sitiyenela kukamba mawu kapena kuwafunsa mafunso oonetsa kuti tikufuna kuti anthuwo akaloŵe m’banja.Nanga bwanji ngati amene ali pacibwenzi asankha kucithetsa? Tiyenela kupewa kuloŵelela m’nkhani zawo kapena kuimba mlandu mmodzi wa iwo. (1 Pet. 4:15) Ngati anthu athetsa cibwenzi sindiye kuti alakwitsa. Nthawi zambili kucita izi kumaonetsa kuti cibwenzico cakwanilitsa colinga cake, comwe ni kuthandiza amene ali pacibwenziwo kupanga cisankho coyenela. Komabe, cibwenzi cikatha, kaŵili-kawili anthuwo amakhala opwetekedwa mtima. Conco, tiyenela kupeza njila zowathandizila. w24.05 31 ¶15-16

Citatu, May 27

Ukafooka pa nthawi imene ukukumana ndi mavuto, mphamvu zako zidzacepa.​—Miy. 24:10.

Ena mwa mayeso ovuta kwambili kuwapilila, ni pamene wa m’banja mwathu kapena mnzathu wapamtima waleka kutumikila Yehova. (Sal. 78:40) Ngati munthuyo tinali naye pa ubale wolimba, zimakhala zovuta kwambili kupilila. Za conco zikakucitikilani, kukumbukila citsanzo ca kukhulupilika ca Zadoki kungakulimbikitseni. Iye anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova pamene mnzake wapamtima Abiyatara anapandukila Yehova. Izi zinacitika Mfumu Davide atatsala pang’ono kumwalila, ndipo mwana wake Adoniya anayesa kudzilonga yekha ufumu umene analonjeza Solomo. (1 Mbiri 22:​9, 10) Abiyatara anasankha kukhala kumbali ya Adoniya. (1 Maf. 1:​5-8) Mwakutelo, Abiyatara anakhala wosakhulupilika kwa Davide ndi Zadoki komanso kwa Yehova! Izi ziyenela kuti zinam’pweteka kwambili Zadoki. Kwa zaka, Zadoki na Abiyatara anali ataseŵenzela pamodzi mogwilizana monga ansembe..​—2 Sam. 8:17; 15:29; 19:​11-14. w24.07 6 ¶14-15

Cinai, May 28

Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zocita zake.​—Miy. 28:14.

Tisakaikile zakuti kukhalabe maso polimbana na mayeselo kumatipindulila. Pocita chimo, ‘tingasangalale kwa nthawi yocepa,’ koma kutsatila miyeso ya Yehova kumatipatsa cimwemwe ceniceni. (Aheb. 11:25; Sal. 19:8) Izi zili conco cifukwa tinapangidwa kuti tizitsatila njila za Yehova. (Gen. 1:27) Tikatelo, tidzakhala na cikumbumtima coyela, komanso na ciyembekezo ca moyo wosatha. (1 Tim. 6:12; 2 Tim. 1:3; Yuda 20, 21) Zoonadi, “thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:41) Koma izi sizitanthauza kuti sitingacitepo kanthu pa zofooka zathu. Yehova amakhala wokonzeka kuti atipatse mphamvu zofunikila. (2 Akor. 4:7) Dziŵani kuti iye amapeleka mphamvu yoposa yacibadwa. Komabe, coyamba tiyenela kuseŵenzetsa mphamvu zathu zacibadwa kuti tidziteteze ku mayeselo a tsiku na tsiku. Yehova adzayankha mapemphelo athu ndi kutipatsa mphamvu yoposa yacibadwa. (1 Akor. 10:13) Inde, na thandizo la Yehova, tingadziteteze kuti tisagwele m’mayeselo. w24.07 19 ¶19-21

Cisanu, May 29

Anthu amene ali ndi cizolowezi cocita chimo.​—1 Tim. 5:20.

Mtumwi Paulo analemba mawu a mlemba lalelo pouza mkulu mnzake Timoteyo. Anacita zimenezo pomuuza mocitila nawo anthu amene ali na “cizolowezi cocita chimo.” Kodi Paulo anatanthauza kuti wocimwayo ayenela kudzudzulidwa pamaso pa mpingo wonse? Pokamba mawu akuti “pamaso pa onse,” iye sanatanthauze mpingo wonse ayi. M’malomwake, anali kunena za anthu ocepa amene angadziŵe za chimo limene munthuyo wacita. Anthuwo angaphatikizepo amene anamuona akucita chimolo, kapena amene munthuyo anawauzako za chimo limene anacita. Zikatelo, akulu ayenela kuuza anthuwo mseli kuti nkhaniyo inasamalidwa, komanso kuti wocimwayo anawongoleledwa. Nthawi zina zimacitika kuti chimolo ladziŵika kwambili mumpingo kapena lidzadziŵika ndithu. Zikakhala conco, kudzudzula munthuyo “pamaso pa onse,” kumaphatikizapo mpingo wonse. Zikatelo, mkulu ayenela kupeleka cilengezo ku mpingo cakuti m’bale kapena mlongoyo anadzudzulidwa. N’cifukwa ciyani ayenela kucita zimenezi? Paulo anati: “Kuti ena onsewo akhale ndi mantha” na kupewa kugwela m’chimo. w24.08 23-24 ¶16-17

Ciwelu, May 30

Amenewa ndi mawu oona a Mulungu.​—Chiv. 19:9

Tiyenela kukhala okangalika potumikila Yehova mpaka mapeto. Odzozedwa ayenela kukhalabe maso kuti ‘akatengedwe’ na Yesu kukalandila mphoto yawo kumwamba. (Mat. 24:40) Odzozedwa amayembekezela mwacidwi “kusonkhanitsidwa” na Yesu kumwamba. Pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, iwo adzakhala mkwatibwi wa Yesu, pa ukwati wa Mwanawankhosa. (2 Ates. 2:1)Ngakhale kuti tsiku la ciweluzo likuyandikila, sitiyenela kucita mantha. Tikakhalabe okhulupilika, Atate wathu wacikondi wa kumwamba adzatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti tidzathe “kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (2 Akor. 4:7; Luka 21:36) Kaya ciyembekezo cathu n’cokakhala kumwamba kapena codzakhala padziko lapansi, tidzakondweletsa Atate wathu ngati timamvela macenjezo opezeka m’mafanizo amene Yesu anakamba. Mwa cisomo ca Yehova, maina athu adzakhala atalembedwa “m’buku” la moyo.​—Dan. 12:1; Chiv. 3:5. w24.09 24-25 ¶19-20

Sondo, May 31

Kwa ine, kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.​—Sal. 73:28.

Monga anacitila wamasalimo, inunso mungathe kuwagonjetsa maganizo olefula. Mungacite bwanji zimenezi? Muziganizila zinthu zabwino zimene muli nazo, komanso mmene Yehova wakudalitsilani. Ndipo muzikumbukila kuti anthu amene satumikila Yehova, salandila thandizo lake. Iwo amangodalila zinthu zakuthupi zimene ali nazo cifukwa alibe ciyembekezo ca za m’tsogolo. Koma ife, Yehova watilonjeza kuti tidzasangalala na zinthu zabwino kwambili m’tsogolo. (Sal. 145:16) Kunena zoona, simunganene motsimikiza mmene umoyo wanu ukanakhalila mukanasankha zinthu mosiyanako na mmene munacitila. Koma cinthu cimodzi cotsimikizika n’cakuti: Mukasankha kucita zina zake cifukwa cokonda Mulungu komanso anthu, simudzasoŵa ciliconse cabwino. w24.10 27 ¶12-13

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani