LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es26 masa. 17-26
  • February

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • February
  • Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
  • Tumitu
  • Sondo, February 1
  • Mande, February 2
  • Ciwili, February 3
  • Citatu, February 4
  • Cinai, February 5
  • Cisanu, February 6
  • Ciwelu, February 7
  • Sondo, February 8
  • Mande, February 9
  • Ciwili, February 10
  • Citatu, February 11
  • Cinai, February 12
  • Cisanu, February 13
  • Ciwelu, February 14
  • Sondo, February 15
  • Mande, February 16
  • Ciwili, February 17
  • Citatu, February 18
  • Cinai, February 19
  • Cisanu, February 20
  • Ciwelu, February 21
  • Sondo, February 22
  • Mande, February 23
  • Ciwili, February 24
  • Citatu, February 25
  • Cinai, February 26
  • Cisanu, February 27
  • Ciwelu, February 28
Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
es26 masa. 17-26

February

Sondo, February 1

Munthu amalemekezeka akapewa mkangano, koma aliyense wopusa amafulumila kuyambitsa mkangano.​—Miy. 20:3.

Abale amene ali na makhalidwe abwino a Cikhristu ni ofunika kwambili mumpingo. Munthu “wololela” amalimbikitsa mtendele. Ngati mufuna kuti ena azikuonani kuti ndinu wololela, muziwamvetsela akamafotokoza maganizo awo, komanso muzimvetsa mmene akumvela. Yelekezani kuti ndinu mkulu, ndipo muli pamiting’i ya bungwe la akulu. Ngati akulu anzanu angagwilizane pa cigamulo cimene sicisemphana na mfundo za m’Baibo, kodi mungagwilizanebe na cigamuloco ngakhale kuti n’cosiyana na zimene inuyo mukufuna? Simuyenela kuumiliza ena kucita zinthu mmene inu mukufunila. Koma mumadziŵa kuti kumvetsela maganizo a anthu ena n’kothandiza. (Gen. 13:​8, 9; Miy. 15:22) M’malo mosuliza zokamba za ena, kapena kukangana nawo, muzicita nawo zinthu mokoma mtima komanso mosamala. Pokhala munthu wokonda mtendele, muzicita khama kubwezeletsa mtendele ngakhale pamene zinthu zili zovuta. (Yak. 3:​17, 18) Mukamakambilana mokoma mtima na anthu ena, kuphatikizapo aja amene amatitsutsa, mungawakhazike mtima pansi.​—Ower. 8:​1-3; Miy. 25:15; Mat. 5:​23, 24. w24.11 23 ¶13

Mande, February 2

Iye adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela kumphepo 4, kucokela kumalekezelo a dziko lapansi kukafika kumalekezelo amumlengalenga.​—Maliko 13:27.

Ngakhale kuti Khristu anatifela “kamodzi kokha basi,” akali kucitabe zinthu zotithandiza. (Aroma 6:10) Motani? Akali kupitiliza kutithandiza kupindula ndi dipo. Ganizilani zimene akucita palipano. Akutumikila monga Mfumu, Mkulu wa Ansembe, komanso mutu wa mpingo. (1 Akor. 15:25; Aef. 5:23; Aheb. 2:17) Cina, ndi amenenso akuyang’anila nchito yosonkhanitsa odzozedwa ndi a khamu lalikulu. Nchito imeneyi idzatha cisautso cacikulu cisanathe. (Mat. 25:32) Kuwonjezela apo, kudzela mwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, Yesu amapatsa cakudya cauzimu atumiki ake okhulupilika m’masiku ano otsiliza. (Mat. 24:45) Ndipo mu ulamulilo wake wa zaka 1,000, adzapitiliza kuticitila zinthu zabwino. Pamene Yehova anapeleka Mwana wake, sanangomupeleka kuti atifele ayi, koma kuti aticitilenso zinthu zina zambili zabwino! w25.01 24 ¶12

Ciwili, February 3

Kuonedwa olungama cifukwa ca kukoma mtima kwake kwakukulu kumene wakusonyeza powamasula ndi dipo lolipilidwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulele.​—Aroma 3:24.

Yehova akakhululuka, amatelo ndi mtima wonse ndipo sakumbukilanso macimo athu. Izi zimatipatsa mwayi wokhalanso paubale wolimba ndi Atate wathu wakumwamba. Timadziwanso kuti kukhululukidwa macimo ndi mphatso imene Yehova amatipatsa. Amatelo cifukwa amatikonda komanso ndi wowolowa manja, ndipo amacita zimenezi mwa cisomo cake. Aliyense wa ife ayenela kuyamikila kwambili podziwa kuti Yehova ndi Mulungu amene ‘amakhululuka ndi mtima wonse’! (Sal. 130:4; Aroma 4:8) Komabe, kuti tikhululukidwe, ifenso tiyenela kucita cinacake cofunikila. Yesu anakamba kuti: “Ngati simukhululukila anthu macimo awo, Atate wanu sadzakukhululukilaninso macimo anu.” (Mat. 6:​14, 15) Conco, m’pofunika kuti nafenso tizitengela citsanzo ca Yehova ca kukhululukila ena. w25.02 13 ¶18-19

Citatu, February 4

Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe.​—Mac. 24:15.

Ganizilani za anthu a ku Sodomu na Gomora. Munthu wokhulupilika dzina lake Loti anali kukhala pakati pawo. Koma kodi tinganene motsimikiza kuti Loti anawalalikila onsewo? Ayi. N’zoona kuti iwo anali oipa, koma kodi anali kutha kusiyanitsa cabwino na coipa? Kumbukilani kuti cigulu ca amuna a mumzindawo cinafuna kugwilila alendo omwe anabwela kwa Loti. Baibo imanena kuti “pacigulupo panali anyamata komanso acikulile.” (Gen. 19:4; 2 Pet. 2:7) Kodi tinganenedi mwatsimitsimi kuti Mulungu wacifundo, Yehova, anawaweluza onsewo popanda ciyembekezo cakuti angadzaukitsidwe? Yehova anatsimikizila Abulahamu kuti anthu olungama mu mzindawo sanali kufika ngakhale 10. (Gen. 18:32) Iwo anali osalungama, m’pake kuti Yehova anawaweluza kuti awonongedwe cifukwa ca zocita zawo. Koma kodi tinganene motsimikiza kuti palibe aliyense wa iwo amene adzaukitsidwa pamene “Mulungu adzaukitsa . . . osalungama”? Ayi, sitingatelo mwatsimitsimi! w24.05 2 ¶3; 3 ¶8

Cinai, February 5

Pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba na cilungamo cake, ndipo zinthu zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.​—Mat. 6:33.

Cifukwa ca kusintha kwa zacuma, ena akopeka kulowa nchito yowapangitsa kukhala kutali ndi banja lawo. Koma ambili amadzazindikila atadzigwilitsa kale fuwa lamoto kuti cimeneco sicinali cisankho canzelu. Musanalowe nchito yatsopano, osangoganizila pa ndalama zimene mudzapata koma muziganizilanso ngati nchitoyi idzatsamwitsa uzimu wanu. (Luka 14:28) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ukwati wanga udzakhudzidwa motani ndikakhala kutali ndi mnzanga wamuukwati? Kodi ndidzikwanitsa kupezeka pa misonkhano, kulalikila, komanso kuyanjana ndi Akhristu anzanga?’ Ngati ndinu kholo muyenelanso kudzifunsa funso lofunika kwambili lakuti: ‘Ngati sindikhala ndi ana anga, kodi ndidzakwanitsa bwanji “kuwalela powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwilizana ndi zimene Yehova amanena?” (Aef. 6:4) Popanga zisankho, muzipewa kutsatila a m’banja mwanu kapena anzanu amene satsatila mfundo za m’Baibulo. M’malomwake, muzitsatila kaganizidwe ka Mulungu. w25.03 29 ¶12

Cisanu, February 6

Tisakhalenso ana.​—Aef. 4:14.

Mkhristu amene amakhalabe khanda mwauzimu angatengeke mosavuta na “zinthu zacinyengo” komanso mabodza amene ampatuko amaphunzitsa mocenjela. Iye angamacitile ena nsanje, kubweletsa mikangano, kukhumudwa msanga, kapena kugonja akayesedwa. (1 Akor. 3:3) Malemba amayelekezela kukula kwauzimu na zimene zimacitika kuti munthu akule mwakuthupi. (Aef. 4:15) Mwana sadziŵa zambili ndipo amafunika kumuyang’anila. Mayi angagwile dzanja mwana wake podutsa msewu. Pomwe mwanayo akusinkhuka, amayi ake angamamulole kudutsa yekha msewu. Koma angapitilize kumukumbutsa kuti aziyang’ana mbali zonse ziŵili asanadutse poopela ngozi. Mwanayo akakula angamapewe yekha ngozi za pa msewu zimenezi. Mofananamo, Akhristu okhwima akafuna kupanga zisankho, amaseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kuti adziŵe maganizo a Yehova na kuwatsatila. w24.04 3 ¶5-6

Ciwelu, February 7

Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?​—Sal. 15:1.

Kwa zaka zambili-mbili, mabwenzi a Mulungu anali cabe zolengedwa zauzimu zimene zinali kukhala naye kumwamba. Pambuyo pake, Yehova analenga anthu, ndipo nawonso anapatsidwa mwayi wokhala alendo ake. M’kupita kwa nthawi, ena mwa alendowo anadzaphatikizapo Inoki, Nowa, Abulahamu, na Yobu. Alambili oona amenewo anafotokozedwa kuti anali mabwenzi a Mulungu, kapena amene “anayenda ndi Mulungu woona.”(Gen. 5:24; 6:9; Yobu 29:4; Yes. 41:8) Kwa zaka mahandiledi ambili, Yehova wakhala akuitana mabwenzi ake kuti akhale alendo m’tenti yake. (Ezek. 37:​26, 27) Mwacitsanzo, ulosi wa Ezekieli umatiphunzitsa kuti Mulungu amafunitsitsa kuti alambili ake okhulupilika akhale naye pa ubwenzi wolimba. Analonjeza kuti adzacita “nawo pangano la mtendele.” Ulosi umenewu unali kunena za nthawi pamene alambili a Yehova amene ali na ciyembekezo cokakhala kumwamba, na amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, adzakhala “gulu limodzi” m’tenti yake yophiphilitsa. (Yoh. 10:16) Ulosi umenewu ukukwanilitsika masiku ano. w24.06 2 ¶2, 4; 3 ¶5

Sondo, February 8

Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu.​—1 Ates. 2:2.

Monga anthu a Mulungu, timakhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu na mtima wonse. Koma kucita izi nthawi zambili kumalila kulimba mtima. (Mat. 6:33) Mwa citsanzo, timafunika kukhala olimba mtima kuti titsatile malamulo a Yehova na kulalikila uthenga wabwino m’dziko loipali. Ndipo nthawi zambili timafunika kulimba mtima kuti tisakhalile mbali m’zandale m’dongosolo logaŵikana lino. (Yoh. 18:36) Atumiki ambili a Yehova amakumana na mavuto azacuma, kumenyedwa, kapena kuponyedwa m’ndende cifukwa cokana kutengako mbali m’ndale kapena kuloŵa usilikali. Timapeza mphamvu na kukhala olimba mtima tikaganizila zitsanzo za anthu omwe anakhala kumbali ya ufumu wa Mulungu molimba mtima. Mfumu yathu, Khristu Yesu, anakanilatu kumunyengelela kuti atengeko mbali m’zandale za m’dziko la Satanali. (Mat. 4:​8-11; Yoh. 6:​14, 15) Nthawi zonse anadalila Yehova kuti amupatse mphamvu. w24.07 3 ¶4; 4 ¶7

Mande, February 9

Anathyola cipatso ca mtengowo nʼkudya. Kenako anatenga zina nʼkukapatsa mwamuna wake pa nthawi imene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.​—Gen. 3:6.

Yehova anaika nkhani yomvetsa cisoni imeneyi m’Baibo kuti itithandize. Imatithandiza kumvetsa cifukwa cake iye amadana kwambili na ucimo. Ucimo umatilekanitsa na Atate wathu ndipo umabweletsa imfa. (Yes. 59:2) Ndiye cifukwa cake Satana, mngelo wopanduka uja amene anayambitsa mavuto onsewa, amakonda ucimo. Ndipo iye amalimbikitsa anthu kuti azicimwa masiku ano. N’kutheka kuti pamene Satana anacimwitsa Adamu na Hava m’munda wa Edeni, anaganiza kuti wakwanitsa kulepheletsa cifunilo ca Yehova. Koma iye sanadziŵe kuti Yehova ni Mulungu wacikondi cacikulu. Mulungu sanasinthe colinga cake cimene anali naco pa mbadwa za Adamu na Hava. Iye amakonda anthu. Conco Adamu na Hava atacimwa, nthawi yomweyo Mulungu anapeleka ciyembekezo kwa anthu onse. (Aroma 8:​20, 21) Yehova anadziŵa kuti padzakhala anthu ena amene adzasankha kumukonda komanso amene adzafuna thandizo lake polimbana na ucimo. Pokhala Atate wawo komanso Mlengi wawo, iye anali kudzawamasula ku ucimo na kuwathandiza kuti amuyandikile. w24.08 3 ¶3-4

Ciwili, February 10

Muzitha kusankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambili.​—Afil. 1:10.

Ambili mwa anthu a Yehova ni otangwanika kwambili. Timagwila nchito yakuthupi kuti tipeze zofunika paumoyo, komanso kuti tisamalile mabanja athu. (1 Tim. 5:8) Akhristu ambili amasamalila acibale awo, odwala, kapena okalamba. Ndipo aliyense wa ife ayenela kusamalila thanzi lake. Zimenezi zimafuna nthawi. Kuwonjezela pa maudindo amenewa, tilinso na zocita zina zofunika mumpingo. Ndipo udindo wina wofunika umene tili nawo, ni kutengako mbali mokangalika pa nchito yolalikila. Kwa ife Akhristu, kuŵelenga Baibo ni cimodzi mwa zinthu “zofunika kwambili.” Conco tifunika kuyesetsa kupeza nthawi yoŵelenga Baibo. Ponena za munthu wacimwemwe, salimo yoyambilila imati: “Amakonda kwambili cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga ndi kuganizila mozama cilamuloco masana ndi usiku.” (Sal. 1:​1, 2) Izi zionetsa kuti tiyenela kumapatula nthawi yoŵelenga Baibo. Kodi nthawi yabwino yoŵelenga Baibo ni iti? Aliyense angasankhe nthawi imene ingamukomele. Koma cofunika kwambili ni kusankha nthawi imene ingakuloleni kuti muziŵelenga Baibo tsiku lililonse. w24.09 3 ¶5-6

Citatu, February 11

Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.​—Agal. 6:5.

Kodi Mkhristu wokhwima angafunikile thandizo la anthu ena? Inde. Nthawi zina Akhristu okhwima nawonso angafunikile thandizo la anthu ena. Munthu wosakhwima amayembekezela ena kumuuza zocita, kapena kumupangila zisankho zimene iye mwini ayenela kupanga. Kumbali ina, Mkhristu wofikapo mwauzimu angapemphe nzelu kwa ena na kuona zokumana nazo za anthu ena, na kudzipangila yekha cisankho podziŵa kuti Yehova amayembekezela aliyense “kunyamula katundu wake.” Anthu okhwima mwakuthupi amasiyana m’maonekedwe. Mofananamo, nawonso Akhristu okhwima amasiyana m’makhalidwe awo. Angasiyane pa nzelu, kulimba mtima, kuwolowa manja, komanso mmene amaonetsela cifundo. Kuwonjezela apo, Akhristu okhwima angapange zisankho zosiyana pa nkhani imodzi, koma zovomelezeka mwa Malemba. Zimenezi zimacitika pa nkhani zimene zimafuna cikumbumtima. Kuzindikila zimenezi kumawathandiza kupewa kuweluzana pa nkhani zimene asiyana zisankho. M’malo mwake, iwo amaika maganizo awo pa zimene zingawathandize kuti akhalebe ogwilizana.​—Aroma 14:10; 1 Akor. 1:10. w24.04 4 ¶7-8

Cinai, February 12

Nkhawa zitandiculukila, munanditonthoza komanso kundisangalatsa.​—Sal. 94:19.

Kodi mungacite ciyani ngati mumadzionabe kukhala wosafunika? Ŵelengani na kusinkhasinkha mavesi a m’Baibo amene angakutsimikizileni kuti Yehova amakuonani kuti ndinu wofunika. Musamadziyelekezele na anthu ena, koma muziganizila zimene mungakwanitse kucita. Yehova sakuyembekezelani kucita zimene simungakwanitse. (Sal. 103:​13, 14) Ngati munthu wina anakucitam’poni nkhanza, kukunyozani, kapena kukucitani nkhanza za kugonana, musamadziimbe mlandu, cifukwa sikunali kufuna kwanu. Kumbukilani kuti Yehova adzaweluza anthu amene amacitila ena zopanda cilungamo. Koma amathandiza amene amacitidwa zopanda cilungamo. (1 Pet. 3:12) Musakaikile kuti Yehova angakuseŵenzetseni pothandiza ena. Iye wakupatsani mwayi wokhala wanchito mnzake pogwila nchito yolalikila. (1 Akor. 3:9) Cifukwa ca zovuta zimene munakumana nazo pa umoyo wanu, mwina cakhala cosavuta kwa inu kuonetsa cifundo kwa anthu amene nawonso amadziona kukhala osafunika. Ndipo mungacite zambili pothandiza anthu otelo. w24.10 7-8 ¶6-7

Cisanu, February 13

Kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa osankhidwa ake, amene amafuulila kwa iye masana ndi usiku, pamene akuwalezela mtima? Ndithu ndikukuuzani, iye adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa iwo mwamsanga.​—Luka 18:​7, 8.

Yehova amasamala kwambili za mmene anthu amacitila nafe zinthu. “Yehova amakonda cilungamo.” (Sal. 37:28) Yesu anatitsimikizila kuti Yehova ‘adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika . . . mwamsanga’ panthawi yake yoyenela. Posacedwa, iye adzacotsapo mavuto onse komanso kupanda cilungamo kwa mtundu uliwonse. (Sal. 72:​1, 2) Tikuyembekezela nthawi pamene Yehova adzacotsapo mavuto onse amene amabwela cifukwa ca zopanda cilungamo. Koma pali pano, iye amatithandiza kupilila tikacitidwa zopanda cilungamo. (2 Pet. 3:13) Mwacitsanzo, iye amatiphunzitsa mmene tingacitile zinthu mwanzelu kuti tisaonjezele mavuto, anthu ena akaticitila zopanda cilungamo. Amacita izi mwa kutionetsa mmene Mwana wake anacitila zinthu pamene anacitidwa zopanda cilungamo. Amatipatsanso malangizo othandiza amene tingaseŵenzetse tikacitidwa zopanda cilungamo. w24.11 2-3 ¶3-4

Ciwelu, February 14

Muwapatse cakudya.​—Mat. 14:16.

Yesu atauza ophunzila ake kuti apatse gululo cakudya, zinali kuoneka zosatheka cifukwa panali amuna pafupifupi 5,000. Ndipo kuŵelengela akazi na ana, n’kutheka kuti anthuwo anali kufika 15,000. (Mat. 14:21) Kenako Andireya, mmodzi wa atumwiwo anakamba kuti: “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda 5 ya mkate wa balele ndi tinsomba tiŵili. Koma nanga zimenezi zingakwanile cigulu ca anthu conseci?” (Yoh. 6:9) Mkate wa balele unali cakudya cimene cinali kudyedwa kwambili na anthu osauka komanso anthu ena. Ndipo nsomba ziŵilizo ziyenela kuti zinali zothilidwa mcele komanso zouma. Komabe, cakudya cimene mnyamatayo anali naco cinali cocepa kwambili pociyelekezela na anthu amene analipo. Yesu anafuna kuwaceleza anthuwo. Conco anawauza kuti akhale pansi m’magulu pa udzu wobiliŵila. (Maliko 6:​39, 40; Yoh. 6:​11-13.) Kenako Yesu anayamikila Atate wake kaamba ka mkate na nsombazo. Panali poyenela kucita zimenezo cifukwa m’ceniceni, Mulungu ndiye anali Mpatsi wa cakudyaco. Citsanzo ca Yesu cimeneci citiphunzitsa phunzilo lofunika kwambili lakuti nthawi zonse tiyenela kupemphela tisanadye cakudya. Kenako Yesu anauza atumwi ake kuti agaŵile cakudyaco, ndipo anthuwo anadya na kukhuta. w24.12 2-3 ¶3-4

Sondo, February 15

Tamandani Yehova Mulungu wanu.​—1 Mbiri 29:20.

Yesu ali padziko lapansi, anapatsa Atate wake ulemelelo mwa kunena kuti iwo ndi amene anamupatsa mphamvu yocitila zozizwitsa. (Maliko 5:​18-20) Njila ina imene Yesu anali kupatsila Yehova ulemelelo ndi zimene anali kukamba ponena za Atate wake, komanso mmene anali kucitila ndi ena. Mwacitsanzo, panthawi ina Yesu anali kuphunzitsa m’sunagoge. Pakati pa anthu omwe anali kumumvetsela, panali mayi wina amene anali wogwidwa ndi ciwanda kwa zaka 18. Ciwandaco cinamupangitsa kukhala wopindika msana moti sanali kutha kuwelamuka. Zinali zosautsadi! Yesu atagwidwa ndi cifundo, anapita kwa mayiyo, ndipo mokoma mtima anamuuza kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” Kenako Yesu anaika manja ake pa iye, ndipo nthawi yomweyo mayiyo anawelamuka “n’kuyamba kutamanda Mulungu.” Mayiyo anayamika Yehova kwambili cifukwa thanzi lake linabwelela m’malo. (Luka 13:​10-13) Mayiyu anali ndi cifukwa cabwino copatsila Yehova ulemelelo. Ifenso tili ndi zifukwa zabwino zom’patsila ulemelelo. w25.01 2-3 ¶3-4

Mande, February 16

Mutikhululukile macimo athu.​—Luka 11:4.

Pa ife tokha, n’zosatheka kupezanso zabwino zonse zimene Adamu ndi Hava anataya. (Sal. 49:​7-9) Popanda thandizo, tikanakhala tilibe ciyembekezo codzakhala ndi moyo m’tsogolo kapena codzaukitsidwa. Tikanakhala opanda ciyembekezo monga mmene zimakhalila nyama ikafa. (Mlal. 3:19; 2 Pet. 2:12) Atate wathu wacikondi Yehova, watipatsa mphatso imene imabweza nkhongole zonse za ucimo zimene tinalandila monga colowa kwa Adamu. Pokamba za mphatso imeneyi, Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambili dziko moti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupilila asaonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Kuonjezela apo, mphatso imeneyi imatipatsa mwayi wokhala paubwenzi wabwino ndi Yehova. Timapindula cifukwa ca mphatso yamtengo wapatali imeneyi ndipo macimo athu, kapena kuti “nkhongole,” amakhululukidwa. w25.02 3 ¶3-6

Ciwili, February 17

[Saulo] anapita kukabatizidwa.​—Mac. 9:18.

N’ciyani cinathandiza Saulo kubatizika? Yesu waulemeleloyo ataonekela kwa Saulo, Saulo anacita khungu. (Mac. 9:​3-9) Kwa masiku atatu, iye anasala kudya, ndipo mosakaikila anali kusinkhasinkha zimene zinali zitangomucitikila. Saulo anatsimikiza kuti Yesu ndiye anali Mesiya, komanso kuti otsatila ake ndiwo anali m’cipembedzo coona. Pali zimene tingaphunzileko kwa Saulo. Akanafuna, akanalola kunyada kapena mantha oopa anthu kumulepheletsa kubatizika. Koma sanatelo. Saulo anali wokonzeka kukhala Mkhristu ngakhale kuti anali kudziwa kuti adzazunzidwa. (Mac. 9:​15, 16; 20:​22, 23) Pambuyo pobatizika, iye anapitiliza kudalila Yehova kuti amuthandize kupilila mayeso osiyanasiyana. (2 Akor. 4:​7-10) Mukabatizika ndi kukhala wa Mboni za Yehova, mungakumane ndi mavuto kapena zinthu zina zoyesa cikhulupililo canu. Koma dziwani kuti thandizo lilipo. Mulungu ndi Khristu adzakupatsani thandizo lofunikila kuti mukhale wokhulupilika.​—Afil. 4:13. w25.03 4 ¶8-9

Citatu, February 18

Sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikupita.​—1 Akor. 9:26.

Kuŵelenga Baibo ni ciyambi cabe. Koma pali zina zimene tiyenela kucita kuti tipindule mokwanila tikamaŵelenga Mawu a Mulungu. Kuti timvetsetse mfundoyi, tiyelekeze motele: Madzi ni ofunika kuti zomela zikule. Koma mvula ikagwa yambili m’kanthawi kocepa, madzi oculuka amangopitilila ndipo saloŵa m’nthaka. Zimakhala bwino mvula ikamagwa pang’ono-pang’ono, cifukwa madzi amaloŵa bwino m’nthaka ndipo zomela zimakula bwino. Mofananamo, tiyenela kupewa kuŵelenga Baibo mothamanga, moti n’kulephela kusinkhasinkha zimene taŵelenga, kuzikumbukila, komanso kuzigwilitsa nchito. (Yak. 1:24) Kodi nthawi zina mumaona kuti mumaŵelenga Baibo mothamanga? Kodi muyenela kucita ciyani mukazindikila zimenezi? Ŵelengani modekha kuti muzikhala na nthawi yosinkhasinkha zimene mukuŵelengazo, komanso kuti muzitha kukumbukila zimene munali kuŵelenga. Mungawonjezeleko nthawi imene mumathela poŵelenga kuti mukhale na mpata woganizilapo, kapena kuti kusinkhasinkha. w24.09 4 ¶7-9

Cinai, February 19

Muzimvela amene akukutsogolelani.​—Aheb. 13:17.

Akulu akalandila malangizo, ayenela kuwaŵelenga mosamala na kuwaseŵenzetsa mmene angathele. Iwo amalandila malangizo a mmene angatsogozele mbali zina za misonkhano, mmene angapelekele mapemphelo pa mpingo, komanso mmene angasamalile nkhosa za Khristu. Akulu amene amatsatila malangizo a gulu amathandiza anthu amene akuwasamalila kumva kuti ni otetezeka, komanso okondedwa. Tikalandila malangizo kucokela kwa akulu, tiyenela kuwatsatila na mtima wonse. Tikatelo, cidzakhala cosavuta kwa iwo kugwila nchito yawo. Baibo imatilimbikitsa kukhala omvela, komanso ogonjela kwa amene akutitsogolela. (Aheb. 13:​7, 17) Koma kucita zimenezi si kopepuka nthawi zina. Cifukwa ciyani? Cifukwa iwo ni opanda ungwilo. Komabe, tikamaika maganizo athu pa zophophonya zawo m’malo mwa zimene amacita bwino, tingamathandize adani athu. Motani? Tingayambe kukaikila zakuti Mulungu akutsogolela gulu lathu. w24.04 10 ¶11-12

Cisanu, February 20

Iye adzalekanitsa anthu.​—Mat. 25:32.

Kodi onse amene adzafa pa cisautso cacikulu adzakhala alibe ciyembekezo codzaukitsidwa? Malemba amakamba momveka bwino kuti anthu amene amatsutsa Yehova adzawonongedwa na magulu ake a nkhondo pa Aramagedo, ndipo sadzaukitsidwa. (2 Ates. 1:​6-10) Nanga n’ciyani cidzacitikile anthu amene adzafa panthawiyo cifukwa ca ukalamba, matenda, ngozi, kapena kuphedwa na anthu ena? (Mlal. 9:11; Zek. 14:13) Kodi n’kutheka kuti angadzakhale pakati pa anthu “osalungama” amene adzaukitsidwa m’dziko latsopano? (Mac. 24:15) Sitidziŵa. Koma tidziwako zinthu zingapo zimene zidzacitika m’tsogolo. Mwacitsanzo, tidziŵa kuti pa Aramagedo anthu adzaweluzidwa mogwilizana na zimene anacitila abale ake a Khristu. (Mat. 25:40) Ndipo amene adzaweluzidwe kukhala nkhosa, ni amene anali kucilikiza odzozedwa komanso Khristu. Chiv. 12:17. w24.05 10-11 ¶9-11

Ciwelu, February 21

Yehova ndi wamoyo! Litamandike Thanthwe langa. Mulungu amene amandipulumutsa alemekezeke.​—Sal. 18:46.

Baibo imafotokoza kuti ino ni “nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Kuwonjezela pa mavuto amene anthu onse amakumana nawo m’dongosolo lino la zinthu, anthu a Yehova amakumananso na citsutso komanso mazunzo. N’ciyani cimatithandiza kupitiliza kulambila Yehova ngakhale kuti timakumana na mavuto amenewa? Cinthu cacikulu cimene cimatithandiza n’cakuti timakhulupilila na mtima wathu wonse kuti Yehova ni “Mulungu wamoyo.” (Yer. 10:10; 2 Tim. 1:12) Yehova alikodi ndipo amatisamalila tikakumana na mavuto. Iye amafuna-funa mipata yotithandizila. (2 Mbiri 16:9; Sal. 23:4) Kumuona kuti ni Mulungu wamoyo kudzatithandiza kupilila mavuto alionse amene tingakumane nawo. w24.06 20 ¶1-2

Sondo, February 22

Njila ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa mʼmawa kumene kumawonjezeleka mpaka kunja kutawala kwambili.​—Miy. 4:18.

Tiyenela kudalilabe gulu la Yehova. Zikacita kuonekelatu kuti m’pofunika kusintha kamvedwe ka mfundo inayake ya m’Baibo, kapena kusintha mmene gulu limacitila zinthu, abale amene amatitsogolela sazengeleza kupanga masinthidwe. Cimene iwo amacitila zimenezi si cina ayi, koma kufuna kukondweletsa Yehova. Amaonetsetsanso kuti zigamulo zawo zimazikika m’Mawu a Mulungu, amene ndiwo muyeso umene mtumiki wa Mulungu aliyense ayenela kuutsatila. Mtumwi Paulo anatilangiza kuti: “Gwilitsitsabe citsanzo ca mawu olondola.” (2 Tim. 1:13) “Mawu olondola” aimila ziphunzitso za Cikhristu zopezeka m’Baibo. (Yoh. 17:17) Ziphunzitso zimenezo ndizo maziko a zonse zimene timakhulupilila. Gulu la Yehova latiphunzitsa kukangamila ku mawu olondola amenewo. Tikacita zimenezi tidzadalitsidwa. w24.07 11-12 ¶12-13

Mande, February 23

Yehova . . . akukulezelani mtima cifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.​—2 Pet. 3:9.

Mtumwi Petulo anamvetsa mmene zimamvekela kulapa na kukhululukidwa. Conco iye anayamba kuphunzitsa ena za nkhani ya kulapa na kukhululuka. Patapita kanthawi pambuyo pa Cikondwelelo ca Pentekosite, Petulo anakamba nkhani kwa khamu la Ayuda osakhulupilila, ndipo anawafotokozela kuti Ayudawo anapha Mesiya. Ngakhale n’telo, iye anawalimbikitsa mwacikondi kuti: “Lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwele kucokela kwa Yehova.” (Mac. 3:​14, 15, 17, 19) Motelo, Petulo anaonetsa kuti kulapa kumasonkhezela munthu wocimwa kutembenuka, kutanthauza kusintha kaganizidwe kake na kacitidwe kake ka zinthu. Ndipo munthuyo amayamba kutsatila njila yatsopano yomwe ingakondweletse Mulungu. Mtumwiyu anawaonetsanso kuti Yehova akanafafaniza macimo awo kapena kuti kuwacotselatu. N’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amatikhululukila na mtima wonse tikalapa macimo athu ngakhale kuti tinacita macimo aakulu! w24.08 12 ¶14

Ciwili, February 24

Musamakonde ndalama.​—Aheb. 13:5.

Kukhala na cikhulupililo colimba cakuti mapeto a dzikoli afika posacedwa, kudzatithandiza kupewa kukondetsetsa cuma. Pa nthawiyo anthu adzatayila, “siliva wawo . . . m’misewu.” Adzatelo cifukwa adzazindikila kuti “siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.” (Ezek. 7:19) M’malo mothela nthawi yathu kufunafuna ndalama zambili, tiyenela kupanga zisankho zimene zidzatithandiza kukhala umoyo wosalila zambili, kwinaku tikutumikila Yehova. Izi zitanthauza kuti tiyenela kupewa nkhongole zosafunikila. Tizipewanso kuseŵenzetsa nthawi yathu yoculuka kusamalila katundu amene tili naye kale. Kuwonjezela apo, tizisamala kuti tisamaone cuma kukhala cinthu cofunika kwambili pa umoyo wathu. (Mat. 6:​19, 24) Pamene tikuyandikila mapeto a dongosolo lino la zinthu, cikhulupililo cathu cidzayesedwa pa nkhani yokondetsetsa zinthu zakuthupi komanso pa nkhani zina. w24.09 11 ¶13-14

Citatu, February 25

Amene akuganiza kuti waima bwinobwino asamale kuti asagwe.​—1 Akor. 10:12.

N’zotheka kugonjetsa zina mwa zofooka zathu. Koma zilipo zina zimene tingalimbane nazo kwa nthawi yaitali. Ganizilani zinacitika kwa mtumwi Petulo. Pa nthawi inayake iye anakana Yesu katatu cifukwa coopa anthu. (Mat. 26:​69-75) Koma anaoneka ngati anali atawathetsa mantha amenewo pamene analalikila molimba mtima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. (Mac. 5:​27-29) Komabe pambuyo pa zaka, iye kwakanthawi analeka kudya pamodzi na Akhristu a mitundu ina, ‘cifukwa ankaopa anthu odulidwa.’ (Agal. 2:​11, 12) Mantha a Petulo anali atabwelelanso. N’kutheka kuti anali asanawathetseletu mantha amenewo. Zaconco zingaticitikile nafenso. Komabe, tigangonjetse cofooka cosathelapo mwa kutsatila ulangizi wa Yesu pa nkhani ya mayeselo wakuti: “Khalanibe maso.” (Mat. 26:41) Ngakhale pa nthawi imene mukumva kuti ndinu wolimba, pewanibe malo kapena zinthu zimene zingakubweletseleni mayeselo. Limbikilanibe kucita zinthu zimene zinakuthandizani kugonjetsa cofooka cimeneco kumbuyoku. ​—2 Pet. 3:14. w24.07 18-19 ¶17-19

Cinai, February 26

Anapeleka mphatso za amuna.​—Aef. 4:8.

Palibe munthu anakhalapo wowolowa manja kuposa Yesu. Ali pa dziko lapansi, anathandiza ena poseŵenzetsa mphamvu zake zocitila zozizwitsa. (Luka 9:​12-17) Iye anatipatsa mphatso yopambana zonse mwa kupeleka moyo wake potifela. (Yoh. 15:13) Yesu anapitiliza kukhala wowolowa manja ngakhale ataukitsidwa. Iye analonjeza kuti adzapempha Yehova kuti atipatse mzimu woyela kuti utiphunzitse na kutilimbikitsa. Ndipo anacitadi zimenezi. (Yoh. 14:​16, 17, mawu a m’munsi; 16:13) Kuwonjezela apo, pa misonkhano ya mpingo, Yesu amatiphunzitsa mmene tingagwilile nchito yopanga ophunzila pa dziko lonse lapansi. (Mat. 28:​18-20) Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu atakwela kumwamba, “anapeleka mphatso za amuna.” (Aef. 4:​7, 8) Paulo anafotokoza kuti Yesu anapeleka amuna amenewa, kuti athandizile mpingo m’njila zosiyana-siyana. (Aef. 1:​22, 23; 4:​11-13) Koma amuna amenewa ni opanda ungwilo. Conco amalakwitsa nthawi zina. (Yak. 3:2) Ngakhale n’telo, Ambuye wathu, Yesu Khristu, amawaseŵenzetsa kuti atithandize. Iwo alidi mphatso kwa ife! w24.10 18 ¶1-2

Cisanu, February 27

Kuzindikila kudzakuteteza.​—Miy. 2:11.

Davide anauza mwana wake Solomo kuti zinthu zikanapitiliza kumuyendela bwino malinga ngati anakhalabe womvela kwa Yehova Mulungu. N’zacisoni kuti m’kupita kwa nthawi, Solomo anayamba kulambila milungu ina. Yehova sanasangalale naye, conco analeka kumupatsa nzelu komanso kumuthandiza kuti apitilize kulamulila mwacilungamo. (1 Maf. 11:​9, 10; 12:4) Kodi tiphunzilapo ciyani? Tikakhala omvela zinthu zidzatiyendela bwino paumoyo. (Sal. 1:​1-3) N’zoona kuti Yehova sanatilonjeze kutipatsa cuma komanso ulemelelo monga wa Solomo. Koma tikamamvela Mulungu wathu, iye adzatipatsa nzelu zimene zidzatithandiza kupanga zisankho zabwino. (Miy. 2:​6, 7; Yak. 1:5) Mfundo zake zingatithandize pamene tikupanga zisankho pa nkhani zokhudza nchito, maphunzilo, zosangalatsa, komanso ndalama. Kutsatila mfundo zake kudzateteza ubwenzi wathu na iye, ndipo tidzakhala na moyo wosatha. (Miy. 2:​10, 11) Kudzatithandizanso kukhala na mabwenzi abwino, komanso kukhala na banja lacimwemwe. w24.11 10-11 ¶11-12

Ciwelu, February 28

Muzifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizila zimene zili zabwino ndipo gwilani mwamphamvu zabwinozo.​—1 Ates. 5:21.

Makolo, muli na mipata yosiyanasiyana yokambilana na ana anu zinthu zokhudza Baibo kapena zokhudza kukhulupilila Mulungu. Mipata imeneyi ingapezeke mukapita kumalo osungilako zinthu zakale. Mungaonetse mwana wanu mmene zocitika za m’mbili yakale kapena zinthu zina zikugwilizanila na Baibo. Kucita izi kungam’thandize kuona kuti zimene Baibo imakamba n’zoona. Mwina mungaphunzitse mwana wanu za mwala wolembedwa na Amowabu. Mwalawo wakhalapo kwa zaka 3,000, ndipo pali dzina la Mulungu lakuti Yehova. Kope la mwala umenewu limapezekanso mu miziyamu yakuti “Baibo na Dzina la Mulungu” ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova ku Warwick, m’dziko la America. Mwala wolembedwa na Amowabu umenewu umaonetsa kuti Mfumu Mesa wa ku Mowabu anapandukila Aisiraeli. Zimenezi n’zogwilizana na zimene Baibo imakamba. (2 Maf. 3:​4, 5) Mwana wanu akadzionela yekha umboni wakuti Baibo imakamba zoona komanso wakuti ni yodalilika, cikhulupililo cake cidzalimbilako. w24.12 14 ¶4; 15 ¶6

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani