Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 138
  • “Mudzamva phokoso la nkhondo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mudzamva phokoso la nkhondo”
  • Nkhani Zina
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Yesu anaphunzitsa
  • Zimene Yesu adzachite
  • Kodi Anthu Adzasiya Liti Kumenya Nkhondo?—Zimene Baibulo Limanena
    Nkhani Zina
  • Dziko Lopanda Nkhondo Posachedwa
    Galamukani!—1996
  • Zimene Zikutidziŵitsa Kuti Armagedo Ili Pafupi
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Mulungu Amagwirizana Ndi Zoti Anthu Azimenya Nkhondo Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nkhani Zina
mrt nkhani 138
Zithunzi: Yesu akulankhula ndi otsatira ake zokhudza nthawi imene tikukhala ino. Zithunzi zing’onozing’ono zikusonyeza nkhondo zimene zikuchitika masiku ano: msewu umene wawonongedwa, utsi wa bomba limene laphulika ukukwera m’mwamba, asilikali okhala ndi zida akuyendayenda m’misewu ndipo alinso ndi akasinja.

PHUNZIRANI KUCHOKERA KWA YESU

“Mudzamva Phokoso la Nkhondo”

“Kuchokera pamene ndinayamba ntchito ya utolankhani m’zaka za m’ma 1960, ndalemba nkhani zokhudza nkhondo zokwana 40 zimene zachitika padziko lonse lapansi. Ndinaona chidani chachikulu cha pakati pa dziko la America ndi la Soviet Union chitafika pachimake kenako n’kutha mosayembekezereka. Koma sindinaonepo chaka chodetsa nkhawa kwambiri ngati mmene chaka cha 2025 chakhalira. Chakachi chakhala chodetsa nkhawa, choyamba chifukwa chakuti mwachitika nkhondo zikuluzikulu, ndipo chachiwiri ndi chakuti zikuonekeratu kuti imodzi mwa nkhondozi ikhudza kwambiri dziko lonse lapansi m’njira yoti sizinachitikeponso m’mbuyo monsemu.”—John Simpson, amene ankayang’anira ntchito yokonza nkhani za padziko lonse ku BBC.

Anthu ali ndi nkhawa chifukwa cha nkhondo zimene zikuchitika padziko lonse lapansi. Ambiri sakudziwa ngati nkhondo zimenezi zidzathe. Koma kodi Yesu anaphunzitsa zotani?

Zimene Yesu anaphunzitsa

Yesu ananeneratu za nkhondo zimene zikuchitika panozi. Iye anachenjeza otsatira ake kuti: “Mudzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo.”—Mateyu 24:6.

Ngakhale kuti nkhondo ndi zinthu zachiwawa zimene zikuchitika masiku ano ndi zodetsa nkhawa kwambiri, tili ndi chifukwa chabwino chokhalira ndi chiyembekezo. Chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa chakuti Yesu ananena kuti nkhondo zikuluzikulu limodzi ndi zochitika zina zambiri, zidzakhala “chizindikiro” chosonyeza kuti tili ‘kumapeto a nthawi ino.’ (Mateyu 24:3; Luka 21:7) Zimenezi zikutanthauza kuti posachedwapa Yesu athetsa nkhondo zonse. Kodi azithetsa bwanji?

Zimene Yesu adzachite

Posachedwapa, Yesu amene ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, ‘athetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.

Kuti mumve zambiri zokhudza mtendere umene tikuyembekezerawu, mmene udzabwerere komanso mmene zimenezi zidzakukhudzireni, werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo Komanso Zachiwawa Zidzathetsedwa Bwanji.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena