Kuthandiza Anthu Amene Ali ndi Vuto Losaona
Padziko lonse, anthu pafupifupi 43 miliyoni ali ndi vuto losaona ndipo anthu 295 miliyoni amaona movutikira.a N’zomvetsa chisoni kuti ambiri mwa anthu amenewa amachitiridwa zinthu mopanda chifundo kapenanso mopanda chilungamo.
Kodi Mulungu amaona bwanji anthu amene ali ndi vuto losaona? Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza anthu amenewa? Nanga a Mboni za Yehova akuwathandiza bwanji masiku ano?
Mmene Mulungu amaonera anthu amene ali ndi vuto losaona
Baibulo limasonyeza kuti Yehovab amaganizira kwambiri anthu amene ali ndi vuto losaona. Mulungu amafuna kuti anthu aziwachitira zinthu mwachilungamo komanso kuti azipindula ndi maphunziro amene iye amapereka. Amawapatsanso chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo.
Lemba: “Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa munthu amene ali ndi vuto losaona.”—Deuteronomo 27:18.
Tanthauzo: Kalekale, Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa anthu ake chinkateteza anthu amene anali ndi vuto losaona kuti asamachitiridwe nkhanza.
Lemba: “Mulungu alibe tsankho.”—Machitidwe 10:34.
Tanthauzo: Mulungu amaona kuti anthu amene ali ndi vuto losaona ndi ofunika mofanana ndi anthu amene alibe vutoli.
Lemba: Yesu “anathandizanso anthu ambiri amene anali ndi vuto losaona kuti ayambe kuona.”—Luka 7:21.
Tanthauzo: Pamene anali padzikoli, Yesu anathandiza anthu amene anali ndi vuto losaona kuti ayambenso kuona. Zimenezi zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite m’tsogolo.
Lemba: “Maso a anthu amene ali ndi vuto losaona adzatsegulidwa.”—Yesaya 35:5.
Tanthauzo: Yehova akulonjeza kuti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu ukayamba kulamulira dziko lapansili, anthu amene ali ndi vuto losaona adzayamba kuona.
Mmene a Mboni za Yehova akuwathandizira
Padziko lonse, a Mboni za Yehovafe timalalikira uthenga wabwino umene umapereka chiyembekezo kwa anthu amene ali ndi vuto losaona. Timachita bwanji zimenezi?
Timafalitsa Mabaibulo, mabuku othandiza pophunzira Baibulo ndiponso mavidiyo zimene anthu amene ali ndi vuto losaona komanso amene amaona movutikira angakwanitse kugwiritsa ntchito. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo mabuku a zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona, mabuku azilembo zikuluzikulu komanso zinthu zongomvetsera.
Timakhala ndi misonkhano imene aliyense angapindule nayo, kuphatikizapo amene ali ndi vuto losaona.
Timaphunzira Baibulo ndi anthu mwa njira yokambirana ndi munthu aliyense payekha.c
Zinthu zonsezi ndi zaulere. Zili choncho chifukwa Yesu analamula kuti: “Munalandira kwaulere, muzipereka kwaulere.”—Mateyu 10:8.
A Mboni za Yehova amaganizira kwambiri anthu amene ali ndi vuto losaona. Amene akufuna kulambira nafe Mulungu amapeza mabwenzi abwino omwe ndi ofunitsitsa kuwathandiza. Tamvani zimene a Mboni za Yehova ena omwe ali ndi vuto losaona ananena.
Talita Alnashi wa ku Sweden, anabadwa ndi vuto loti amaona movutikira. Onani mmene makolo ake anamuphunzitsira Baibulo ndiponso mmene anzawo akhala akuthandizira iyeyo ndi anthu a m’banja lake komanso kuwasonyeza chikondi.
James Ryan wa ku United States, anabadwa ndi vuto losamva ndipo kenako anasiya kuona. Onani zimene zimamuthandiza kuti azisangalala.
Cynthia Pablo wa ku Philippines, ali ndi vuto losamva komanso losaona. Kodi Akhristu anzake anamuthandiza bwanji pa nthawi yovuta ya mliri wa COVID-19? Onani nkhani ya Chingelezi yakuti “Congregation Supports Deaf and Blind Sister During Pandemic.”
Kodi timapereka zinthu ziti zothandiza pophunzira Baibulo?
Mabuku a zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona. Timafalitsa Baibulo lathunthu kapena kambali chabe ka Baibulo la zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona, m’zilankhulo zingapo. (Kuti muone zilankhulo zake, onani bokosi lakuti “Baibulo la Dziko Latsopano la zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona.”) Timafalitsanso zinthu zambiri zothandiza pophunzira Baibulo za zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona. Pofuna kuthandiza anthu amene akufuna kuphunzira kuwerenga zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona, tinatulutsa kabuku ka Chingelezi kakuti Learn to Read Braille. Kabukuka kanakonzedwa m’njira yakuti munthu amene amaona azitha kuphunzitsa munthu amene ali ndi vuto losaona kuwerenga.
Mungapeze mabuku a zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona kwa wa Mboni za Yehova aliyense kapena mungapemphe kuti wa Mboni adzacheze nanu.
Pangani dawunilodi mafaelo amene mungawagwiritse ntchito pa chipangizo chotchedwa notetakerd pa jw.org.
Mabuku a zilembo zazikulu opulinta komanso a pazipangizo zamakono. Tili ndi mabuku ambiri a zilembo zazikulu amene amathandiza anthu omwe amaona movutikira. Webusaiti yathu ya jw.org inapangidwa m’njira yakuti izionetsa zinthu bwinobwino ngakhale mutazikulitsa kwambiri. Pulogalamu ya JW Library imalolanso kusintha kakulidwe ka zilembo.
Mungapeze mabuku a zilembo zazikulu kwa wa Mboni za Yehova aliyense kapena mungapemphe kuti wa Mboni adzacheze nanu.
Pangani dawunilodi mabuku a pa zipangizo zamakono omwe ndi ofanana ndi mabuku ochita kupulinta, pa jw.org.
Zinthu zongomvetsera. Tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano longomvetsera, m’zilankhulo zoposa 200. Kuwonjezera pamenepo, tili ndi mabuku ambiri ofotokozera Baibulo ongomvetsera. Nthawi zambiri zinthu zimenezi zimafotokozeranso zithunzi.
Onerani kapena pangani dawunilodi zinthu zongomvetsera pa webusaiti ya jw.org komanso pa pulogalamu ya JW Library.
Pangani dowunilodi mafaelo a Chingelezi amene amawerengedwa ndi screen reader kapena mapulogalamu ena a pazipangizo zamakono pawebusaiti ya jw.org.e
Mavidiyo okhala ndi mawu ofotokozera.f A Mboni za Yehova amatulutsa mavidiyo a nkhani za m’Baibulo okhala ndi mawu ofotokozera n’zilankhulo zoposa 100. Mavidiyo amenewa amathandiza anthu kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo.
Mvetserani mawu ofotokozera m’mavidiyo otsatirawa:
Misonkhano komanso zochitika zina. Padziko lonse pali mipingo imene timasonkhana mlungu uliwonse kuti tiphunzire komanso kulambira. Chaka chilichonse, timakhalanso ndi misonkhano ikuluikulu kumene timakaphunzira Baibulo. Pazochitika zathu zimene pamakhala mavidiyo, timayesetsa kuti tikhalenso ndi mavidiyo a mawu ofotokozera. Ngati mwayi ulipo, pa misonkhano yathu komanso zochitika zina pakakhala anthu amene saona komanso ali ndi vuto losamva, pamakhala woti azimasulira polankhula ndi manja kwinaku atagwira mikono yawo. Timalandira munthu aliyense mopanda tsankho.
José Luis Ayala yemwe amakhala ku Mexico. Anabadwa ndi vuto losamva kenako anasiya kuona ali ndi zaka 29. Onani mmene misonkhano yathu inam’thandizira komanso mmene anathandizidwira kuti aziphunzitsa bwino mawu a Mulungu.
a “Kuona movutikira” kumatanthauza vuto la maso limene munthu amakhala nalo lomwe silingathe ndipo limakhudza zochitika za moyo wake wa tsiku ndi tsiku. Munkhaniyi mawu a kuti, “vuto losaona” likuphatikizapo kusaona ngakhale pang’ono komanso kuona movutikira.
b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”
c Mukhoza kupempha kuti muone mmene phunziro la Baibulo laulere limachitikira.
d Notetaker ndi kachipangizo kakang’ono kamakono kamene kamagwiritsidwa ntchito powerenga zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona kapena kumvetsera pamene kakuwerenga. Akafuna kuwerenga zilembozi amatsitsa kapena kukweza timapini n’cholinga choti pabwere zilembo za anthu amene ali ndi vuto losaona. Munthu akakhala ndi notetaker samafunikira kukhala ndi mabuku ambiri ochita kupulinta.
e Ma screen reader komanso mapulogalamu ena a pakompyuta amawerenga mokweza, mawu amene ali pa sikirini kapena mawu amene anajambulidwa kale. Zimenezi zimathandiza munthu kuti apite mwachindunji pa nkhani kapena ndime imene akufuna kuwerenga.
f Mawu ofotokozera, ndi mawu ojambulidwa amene amaikidwa muvidiyo pofuna kufotokoza zinthu zina zimene zikuchitika muvidiyoyo.