Lachisanu, October 16
Musalole kuti mtima wanu upatukire kunjira zake. Musasochere nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zake.—Miy. 7:25.
Nkhani imene Solomo analemba imasonyeza zimene zingachitikire mtumiki wa Yehova aliyense. Iye angathe kuchita tchimo lalikulu n’kumaona kuti zachitika “mwadzidzidzi.” Kapenanso angathe kunena kuti zangochitika. Koma ataganizira bwinobwino zimene zinachitika, akhoza kupeza kuti pali zina zomwe anachita mosaganiza bwino zomwe zachititsa kuti achite tchimolo. Zinthu zimenezi zingaphatikizepo zosangalatsa zosayenera, kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa kapena kupezeka m’malo okayikitsa, kaya malo enieni kapena pa intaneti. N’kuthekanso kuti mwina anasiya kupemphera, kuwerenga Baibulo, kupezeka pamisonkhano kapenanso kugwira ntchito yolalikira. Choncho mofanana ndi wachinyamata wa m’buku la Miyambo, tchimo lake silingakhale kuti langochitika mwadzidzidzi. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sitiyenera kungopewa tchimo, koma tiyeneranso kupewa zinthu zimene zingachititse kuti tichite tchimolo. Solomo anamveketsa bwino mfundo imeneyi.—Mat. 5:29, 30. w24.07 16 ¶10-11
Loweruka, October 17
Tili ndi chuma chimenechi mʼziwiya zadothi.—2 Akor. 4:7.
Kodi chuma chimenechi n’chiyani? Ndi ntchito yolalikira za Ufumu yomwe ndi yopulumutsa miyoyo. (2 Akor. 4:1) Nanga ziwiya zadothi n’chiyani? Zikuimira atumiki a Mulungu omwe amauza ena uthenga wabwino. M’nthawi ya Paulo, amalonda ankagwiritsa ntchito mitsuko yadothi ponyamula zinthu zofunika monga chakudya, vinyo komanso ndalama. Mofanana ndi zimenezi, Yehova watipatsa uthenga wabwino womwe ndi wamtengo wapatali. Mothandizidwa ndi Yehova, tingathe kupeza mphamvu zomwe timafunikira kuti tipitirize kulalikira uthenga wabwino mokhulupirika. Nthawi zina tikhoza kumaopa anthu kapenanso kuopa kuti akana uthenga wathu. Kodi tingalimbane bwanji ndi vutoli? Taganizirani pemphero limene atumwi anapereka atalamulidwa kuti asiye kulalikira. M’malo mochita mantha n’kusiya, iwo anapempha Yehova kuti awathandize kuti apitirize kulankhula molimba mtima. Yehova anayankha pemphero lawo nthawi yomweyo. (Mac. 4:18, 29, 31) Inunso nthawi zina mukayamba kuopa anthu, muzimupempha kuti akuthandizeni kuti muzikonda kwambiri anthu n’cholinga choti musaope kuwauza uthenga wabwino. w24.04 16 ¶8-9
Lamlungu, October 18
Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.—Mat. 6:9.
Kukonda Yehova kumatilimbikitsanso kuti tiziyeretsa dzina lake. Zimenezi zikutanthauza kuti timafunitsitsa kuuza ena kuti zinthu zoipa zomwe Satana amanena zokhudza Yehova si zoona. (Gen. 3:1-5; Yobu 2:4; Yoh. 8:44) Tikamalalikira, timafunitsitsa kuuza anthu onse omwe angamvetsere zoona zenizeni zokhudza Yehova. Timafuna kuti aliyense adziwe kuti khalidwe lake lalikulu ndi chikondi, amalamulira mwachilungamo ndiponso kuti posachedwapa Ufumu wake uthetsa mavuto onse n’kubweretsa mtendere ndi chimwemwe kwa anthu. (Sal. 37:10, 11, 29; 1 Yoh. 4:8) Tikamauza anthu zinthu ngati zimenezi zokhudza Yehova, timakhala tikuyeretsa dzina lake. Timasangalalanso chifukwa timadziwa kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi dzina lathu. w24.05 18 ¶12