PHUNZIRANI KUCHOKERA KWA YESU
Muzipeza Nthawi Yophunzira za Mulungu
Zinthu zingamakuyendereni bwino ngati mutamapeza nthawi yophunzira za Mulungu. Zimenezi zimakuthandizani kuti mukhale naye pa ubwenzi. Taganizirani zimene Yesu anaphunzitsa pa nkhani imeneyi.
Zimene Yesu ananena
“Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.
Tonse timafuna titapeza mayankho amafunso akuti: Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani anthu akuvutika chonchi? N’chiyani chimachitika munthu akamwalira? Tingakhale osangalala ngati titadziwa mayankho a mafunso amenewa.
“Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.”a—Mateyu 4:4.
Mofanana ndi mmene zimakhalira kuti timafunika kudya chakudya, timafunikanso kudya chakudya cha uzimu. Yesu anafotokoza momveka bwino kuti, timafunika kudalira Yehova nthawi zonse kuti tikwaniritse zosowa zathu zauzimu.
“Mawu anu ndi choonadi.”—Yohane 17:17.
Yesu anatchula njira yaikulu imene Mulungu amakwaniritsira zosowa zathu za uzimu yomwe ndi kudzera “m’Mawu Ake, Baibulo.
Tikukulimbikitsani kuti muzipeza nthawi yophunzira mawu a Mulungu komanso muzikwaniritsa zosowa zanu za uzimu ”n’cholinga choti muzikhaladi osangalala. Zotsatirazi ndi zina zimene zingakuthandizeni:
Mukhoza kuwerenga Baibulo kwaulere.
Mungapemphe kuti muziphunzira Baibulo kwaulere mochita kukambirana ndi wa Mboni za Yehova.
a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”