Courtesy Jamie Christiani/Bulletin of the Atomic Scientists
KHALANI MASO
Asayansi Akokera Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko Kuti Iyandikire 12 Koloko Usiku
Pa 27 January 2026, akatswiri asayansi anasuntha mivi ya Wotchia Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko kuti nthawi iyandikire 12 koloko ya usiku. Pa wotchiyi, nthawi ya 12 Koloko usiku imasonyeza kuwonongedwa kwa dzikoli chifukwa cha zochita za anthu.
“Bungwe la The Bulletin of the Atomic Scientists Science and Security Board, lakokera Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko ndipo kwatsala masekondi 85 kuti 12 koloko ya usiku ikwane. Imeneyi ndi nthawi yaifupi kwambiri, zomwe sizinachitikeponso mbuyomu.”—Bulletin of the Atomic Scientists.
“Asayansi amagwiritsa ntchito Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko pofuna kutithandiza kumvetsa zinazake. Zinthu zikungoipiraipirabe, anthu akulephera kuchita zinthu mogwirizana kuti athetse mavutowa ndipo zinthu zafika poipa kwambiri. Anthu akufunika kusintha ndipo zimenezi ndi zotheka. Iwo akuyenera kuthandiza atsogoleri awo kuti achitepo kanthu mwamsanga.”—Alexandra Bell, president and CEO, Bulletin of the Atomic Scientists.
Kodi dziko lapansili ndi anthu zithadi posachedwapa? Kodi tikuyenera kuopa zimene zidzachitike m’tsogolo? Kodi Baibulo limanena zotani?
Zimene zidzachitike m’tsogolo
Baibulo limanena kuti “dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale” ndipo anthu “adzakhala mmenemo mpaka kalekale.” (Mlaliki 1:4; Salimo 37:29) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu sadzawononga dzikoli kapena kulipangitsa kuti zamoyo zisapezekemo.
Komabe, Baibulo limanena za mapeto. Mwachitsanzo, limanena kuti “dzikoli likupita.”—1 Yohane 2:17.
Kuti mudziwe zimene Baibulo limatanthauza likamanena za mapeto a dzikoli, werengani nkhani yakuti, “Kodi Dzikoli Lidzatha? Kodi Baibulo Limanena Kuti Zinthu Zonse Zidzawonongedwa?”
Kuti muone zimene Baibulo limatanthauza likamanena za mapeto a dzikoli, werengani nkhani yakuti, “Kodi Mapeto a Dzikoli Adzafika liti?”
Khalanibe oganiza bwino
Baibulo lingatithandize kuti tikhalebe oganiza bwino ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Motani?
Baibulo limatipatsa malangizo amene angatithandize. (2 Timoteyo 3:16, 17) Mwachitsanzo, werengani nkhani yakuti “Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri?” kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni kuti musamataye mtima kwambiri mukamakumana ndi mavuto.
Baibulo limatithandiza kuti tiziyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. (Aroma 15:4) Limatiuza zinthu zimene tingayembekezere kuti zichitika panopa komanso m’tsogolo. Ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tisamachite mantha ndi zimene zikuchitika padzikoli.
Kuti muzipindula kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, tikukupemphani kuti muziphunzira Baibulo mwaulere mothandizidwa ndi wa Mboni za Yehova.
a “Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko ndi yongoyerekezera ndipo inapangidwa n’cholinga chofuna kusonyeza nthawi yomwe yatsala kuti dzikoli liwonongeke chifukwa cha zochita za anthu monga za tekinoloje zoopsa kwambiri. Imakumbutsa anthu zamavuto amene tikufunika kuthana nawo kuti tipulumuke m’dzikoli.”—Bulletin of the Atomic Scientists