JUNE 1-7, 2026
NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
Tikhoza Kumasangalalabe Ngakhale Kuti Anthu Ena Amadana Nafe
“Ndinu osangalala anthu akamadana nanu.”—LUKA 6:22.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tikambirana zimene zimachititsa kuti tizisangalalabe ngakhale kuti anthu ena amadana nafe chifukwa timatumikira Yehova.
1. Kodi Yesu ananena chiyani, nanga n’chifukwa chiyani zinali zodabwitsa?
PA ULALIKI wake wa paphiri, Yesu anati: “Ndinu osangalala anthu akamadana nanu.” (Luka 6:22) Mawuwa ayenera kuti anadabwitsa anthu amene ankamumvetsera. Ndipotu palibe amene amasangalala anthu akamadana naye. Ndiye n’chifukwa chiyani Yesu analankhula zimenezi? Limeneli ndi funso lofunika kuliganizira chifukwa anthu ambiri masiku ano amadana ndi otsatira a Yesu. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake anthu amadana nafe komanso zimene zingatithandize kuti tizisangalalabe.
N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU AMADANA NAFE?
2-3. Kodi chimodzi mwa zifukwa zimene zimachititsa kuti Akhristu azizunzidwa ndi chiyani, nanga kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tiziwaona bwanji amene amatizunza? (Yohane 16:2, 3)
2 Anthu amadana nafe chifukwa choti timalambira Yehova. Ponena za anthu amene azidzazunza ngakhalenso kupha ena mwa ophunzira ake, Yesu anati: “Sakundidziwa komanso sakudziwa Atate.” (Werengani Yohane 16:2, 3.) Kodi ndi ndani amene amachititsa kuti anthu ena azidana ndi anthu a Mulungu? Ndi Satana, “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:3, 4) Iye wachititsa khungu anthu ndipo amawalimbikitsa kuti azitsutsa anthu amene amadziwa ndi kukonda Mulungu. (Yoh. 8:42-44) Kodi kudziwa zimenezi kumachititsa kuti tiziwaona bwanji anthu amene amatitsutsa? Sitidana nawo chifukwa timadziwa kuti apusitsidwa ndi Satana.
3 Taganizirani chitsanzo cha Pavel,a amene amakhala m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa. Iye anamangidwa, kumenyedwa kwambiri komanso anaikidwa muselo yayekha chifukwa chopitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. Pavel ananena kuti: “N’zodziwikiratu kuti Satana ndi ziwanda ndi amene akulimbana nafe kuti tisamalambire Yehova. Zikuoneka kuti anthu ambiri ogwira ntchito kundende samadana nafe. Amakhala kuti akungogwira ntchito yawo.” M’bale wina wa ku Croatia amene ankazunzidwa ndi makolo ake omwe si a Mboni anati: “Ndinazindikira kuti mdani wanga weniweni ndi Satana, osati makolo anga.”—Aef. 6:12.
4. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yesu komanso Sitefano? (Onaninso chithunzi.)
4 Sitimadana ndi anthu omwe amatitsutsa. Ndipotu timathanso kuwapempherera. (Mat. 5:44) Pa nkhaniyi tingaphunzire zambiri kwa Yesu komanso wophunzira wake Sitefano. Asilikali a Chiroma atamukhomerera pamtengo wozunzikirapo, Yesu anapemphera kuti: “Atate, akhululukireni.” (Luka 23:34) Apatu ankapempha Yehova kuti akhululukire asilikali amene analamulidwa kuti amuphe. Ayeneranso kuti ankaganizira gulu la anthu, amene molimbikitsidwa ndi atsogoleri awo achipembedzo, ankakuwa kuti iye aphedwe. Yesu anazindikira kuti anthuwa sankadziwa kwenikweni chimene akuchita. Mofanana ndi Yesu, Sitefano anapempha Mulungu kuti akhululukire anthu amene ankamupha. (Mac. 7:58-60) Kodi Yehova anayankha pemphero la Yesu komanso la Sitefano? Inde. Anthu ambiri amene ankafuna kuti Yesu aphedwe, pambuyo pake analapa n’kuyamba kumukhulupirira ndipo kenako anabatizidwa. (Mac. 2:36-41) Ngakhalenso Saulo, amene anavomereza kuti Sitefano aphedwe, anakhala Mkhristu ndipo ankamva chisoni kwambiri chifukwa cha zimene anachita.—1 Tim. 1:13.
Mofanana ndi Yesu komanso Sitefano amene anapempherera anthu amene ankawazunza, ifenso tingapempherere amene akutizunza (Onani ndime 4)
5. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira César?
5 Masiku anonso Yehova amamvetsera tikamapempherera anthu amene amatitsutsa. Taganizirani chitsanzo cha César amene amakhala ku Venezuela. Bambo ake ankamuchitira nkhanza chifukwa choti anakhala wa Mboni. Iye anati: “Mayi anga anali mkazi komanso mayi wabwino. Ngakhale kuti nthawi zonse ankaika zinthu zokhudza Ufumu pa malo oyamba, ankasamalira bambo anga mwachikondi. Amayi anandiphunzitsa ine ndi abale anga kuti tizilemekeza bambo athu komanso tiziwamvera, kupatula ngati atatiuza zinthu zosemphana ndi zimene Mulungu amafuna.” Patapita zaka zingapo bambo ake anayamba kusintha. Iye anati: “Tsiku lina nditapemphera kuchokera pansi pamtima, ndinapempha bambo anga kuti ndiziphunzira nawo Baibulo. Sindingathe kufotokoza mmene ndinasangalalira atavomera kuti ndiziphunzira nawo.” Patapita nthawi bambo a César anabatizidwa. Si anthu onse amene amatitsutsa omwe angasinthe chonchi. Koma ena amasintha mmene amationera tikamawalankhula mwaulemu komanso akaona khalidwe lathu labwino. Ndipotu akasintha timasangalala. Timafunitsitsa kuona Yehova, yemwe ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi” wachifundo, akukokera anthu ngati amenewa kwa iye.—Gen. 18:25.
6. Mogwirizana ndi Maliko 13:13, kodi anthu amadana nafe pa chifukwa chinanso chiti?
6 Anthu amadana nafe chifukwa choti timalemekeza Yesu. Iye ananena kuti anthu onse adzadana ndi Akhristu oona “chifukwa cha dzina [lake].” (Werengani Maliko 13:13.) Kodi “dzina” la Yesu limaimira chiyani? Limaimira makhalidwe ake komanso udindo wake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Anthu amene amadana nafe sakhulupirira Yesu Khristu, amene Yehova wamusankha kuti akhale wolamulira koma amakhulupirira olamulira am’dzikoli. Yesu wakhala akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kuyambira mu 1914. Posachedwapa iye achotsa maboma onse omwe amalimbana ndi ulamuliro wake.
7-8. Kodi anthu amadana nafe pa chifukwa chinanso chiti? (Yohane 15:18-20) (Onaninso zithunzi.)
7 Anthu amadana nafe chifukwa chakuti sitili mbali ya dziko la Satanali. Yesu ananena kuti anthu adzadana ndi ophunzira ake chifukwa choti ‘sali mbali ya dzikoli.’ (Werengani Yoh. 15:18-20.) Mofanana ndi Akhristu oyambirira, sitimatengera mmene anthu am’dzikoli amaganizira, mmene amachitira zinthu komanso mmene amalankhulira. Chifukwa cha zimenezi, abale ndi alongo ambiri amanyozedwa kuntchito kapena kusukulu. (1 Pet. 4:3, 4) Komabe timasangalala kuti n’kupita kwa nthawi anthu ena amene amatitsutsa amayamba kutilemekeza.
8 Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wa ku Central America dzina lake Ignacio. Iye ankaphunzira pasukulu ina ndipo mphunzitsi wina ankamunyoza chifukwa cha makhalidwe ake abwino. Mphunzitsiyo anamufunsa kuti ankakwanitsa bwanji kutsatira mfundo za Baibulo ngakhale kuti anthu ankamunyoza pasukulupo. Ignacio anafotokoza kuti amaona kuti malamulo a Mulungu amamuteteza. Kenako anaitanira mphunzitsiyo kumisonkhano yampingo. Iye sanakhulupirire ataona kuti mphunzitsiyo wabweradi. Mphunzitsiyo anachita chidwi ndi chikondi cha anthu amumpingowo ndipo anapitiriza kusonkhana. Pambuyo pake atayamba kuphunzira Baibulo, nayenso anayamba kutsutsidwa. Komabe anapitiriza kuphunzira mpaka anabatizidwa.
Posatengera msinkhu wathu, tonse tingathe kulimba mtima n’kufotokozera ena zimene timakhulupirira (Onani ndime 8)b
9-10. (a) Kodi ndi chifukwa china chiti chimene chimachititsa Akhristu kukhala osiyana ndi anthu am’dziko la Satanali? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha mtumwi Paulo?
9 Timakhalanso osiyana ndi anthu am’dziko la Satanali chifukwa sitimalowerera ndale komanso nkhondo. (Yoh. 18:36) Mogwirizana ndi malangizo amene ali pa Aroma 13:1, timayesetsa kumvera malamulo a boma. Komabe monga Akhristu, sitilowerera nkhani zandale. Choncho sitifuna kuti anthu ativotere komanso sitivotera anthu ena chifukwa ndife okhulupirika kwa Yehova ndi Ufumu wake, umene wolamulira wake ndi Khristu. A Mboni ambiri anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Ngakhale kuti ali m’ndende, iwo amapitirizabe kulalikira. Akamachita zimenezi amakhala kuti akutsanzira mtumwi Paulo, yemwe kwa zaka zambiri anakhala pa ukaidi wosachoka panyumba ndiponso m’ndende. (Mac. 24:27; 28:16, 30) Iye anapitiriza kulalikira anthu onse amene akanamumvetsera, kuphatikizapo oyang’anira ndende, nduna, abwanamkubwa, mafumu ndipo mwinanso Nero, amene anali mfumu ya Roma.—Mac. 9:15.
10 Mofanana ndi zimenezi, abale athu omwe ali m’ndende amalalikira kwa aliyense amene angamvetsere kuphatikizapo oweruza, akuluakulu aboma komanso oyang’anira ndende. M’bale wina amene wakhala m’ndende kwa zaka zoposa 6 chifukwa chosalowerera ndale, ananena kuti amaona nthawi imene anakhala m’ndende kuti sinali chilango koma utumiki umene Yehova anamupatsa kuti apeze anthu angati nkhosa. Timasangalala Yehova akatigwiritsa ntchito kuti tilalikire uthenga wabwino kwa anthu ngati amenewa. (Akol. 4:3) Tsopano tiyeni tikambirane zina zimene zimachititsa kuti tizisangalala ngakhale kuti anthu amadana nafe chifukwa chotumikira Yehova.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAKHALABE OSANGALALA ANTHU AKAMADANA NAFE?
11. Kodi kuzunzidwa kungatithandize bwanji kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba? Perekani chitsanzo.
11 Timadziwa kuti anthu akamadana nafe, amakhala akukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo. Mu ulosi woyambirira wa m’Baibulo, Yehova ananena kuti Satana ndi onse amene amamutsatira adzadana ndi aliyense amene amakonda Yehova komanso kumutumikira. (Gen. 3:15) Nthawi zambiri zimene Yesu ankanena, zomwe timazipeza m’mabuku 4 a Uthenga Wabwino, zimatsimikizira ulosiwu. (Mat. 10:22; Maliko 13:9-12; Luka 6:22, 23; Yoh. 15:20) Akhristu ena omwe analemba Baibulo nawonso analemba zomwezi. (2 Tim. 3:12; Yak. 1:2; 1 Pet. 4:12-14; Yuda 3, 17-19) Choncho anthu ena akayamba kutitsutsa sitimadabwa koma timasangalala podziwa kuti ulosi wa m’Baibulo ukukwaniritsidwa. Zimenezi zimatitsimikizira kuti tikutumikira Mulungu woona. Mlongo wina yemwe amakhala m’dziko limene ntchito yathu ndi yoletsedwa anati: “Nditadzipereka kwa Yehova ndinkadziwa kuti nthawi iliyonse ndikhoza kuzunzidwa. Choncho sindichita mantha kapena kudabwa ndikakumana ndi mayesero.” Mwamuna wa mlongoyu anali mmodzi mwa anthu amene ankamutsutsa. Iye ankamuzunza ndipo anamuwotchera Baibulo ndi mabuku ena. Koma m’malo mochita mantha, mlongoyu anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Aheb. 10:39) Iye anati: “Baibulo linaneneratu kuti tidzazunzidwa, choncho zimenezi ziyenera kuchitika. Kuzunzidwa kunanditsimikizira kuti ndapeza chipembedzo choona.”
12. Kodi m’bale wina anakwanitsa bwanji kupirira pamene ankazunzidwa?
12 Timayembekezera kuti tidzazunzidwa komabe zimakhala zovuta kuti tipirire tikayamba kuzunzidwa. Pofotokoza zimene zinkamuchitikira ali m’ndende, m’bale wina ananena kuti: “Nthawi zina ndinkavutika maganizo komanso kuda nkhawa ndipo ndinkangolira.” Ndiye n’chiyani chinathandiza m’baleyu kupirira? Iye anati, “Nthawi zonse ndinkapemphera. M’mawa uliwonse ndikangodzuka ndinkapemphera ndipo tsiku likamadutsa, ndinkapempheranso zinthu zikavuta. Ndipo pakachitika zinthu zopanda chilungamo zomwe zandikwiyitsa ndinkadzitsekera m’bafa n’kuyamba kupemphera.” M’bale wathuyu ankaganiziranso zitsanzo za anthu okhulupirika akale komanso a masiku ano. Zimenezi zinamuthandiza kuti apirire pamene ankazunzidwa komanso apeze mtendere umene Yesu analonjeza otsatira ake.—Yoh. 14:27; 16:33.
13. N’chiyani chingatithandize kupirira anthu ena akamadana nafe?
13 Tili ndi chikondi chomwe ndi champhamvu kuposa chidani. Yesu ankakonda Atate wake ndi mtima wonse mpaka nthawi imene anaphedwa. Iye ankakondanso anzake. (Yoh. 13:1; 15:13) Ifenso tikamakonda Yehova komanso abale ndi alongo athu, tidzakwanitsa kupirira anthu ena akamadana nafe. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambirane chitsanzo cha mtumwi Paulo.
14. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kukhala wokhulupirika pamene ankayembekezera kuphedwa?
14 Atatsala pang’ono kuphedwa, Paulo analembera mnzake wapamtima Timoteyo kuti: “Mulungu sanatipatse mzimu wamantha, koma wamphamvu [ndi] wachikondi.” (2 Tim. 1:7) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani? Ankatanthauza kuti kukonda kwambiri Yehova kungathandize Mkhristu kukhala wokonzeka kukumana ndi mayesero ovuta kwambiri. (2 Tim. 1:8) Ndipotu zimenezi ndi zimene zinamuthandiza kukhala wolimba mtima pamene ankayembekezera kuphedwa ndipo sanasiye kulambira koona.—Mac. 20:22-24.
15. Kodi masiku ano abale ndi alongo amasonyeza bwanji chikondi chololera kuvutikira ena? (Onaninso chithunzi.)
15 Timakonda kwambiri Akhristu anzathu omwe amakhalabe okhulupirika akamazunzidwa. Ena amalolera kuika moyo wawo pangozi pofuna kuthandiza abale ndi alongo awo ngati mmene anachitira Akula ndi Purisila, amene analolera kuika moyo wawo pangozi kuti athandize Paulo. (Aroma 16:3, 4) Mwachitsanzo, ku Russia abale ambiri amapita kumakhoti kukalimbikitsa anzawo amene amangidwa. Mmodzi mwa alongo amene anamangidwa ataona gulu la abale ndi alongo atabwera kukhotiko, anakhudzidwa kwambiri moti anasowa chonena kwa kanthawi. Chikondi chololera kuvutikira ena chimene abale ndi alongowo anasonyeza chinamulimbikitsa pa nthawi imene ankafunika kulimbikitsidwa kwambiri. Timasangalala chifukwa chikondi chathu n’champhamvu kwambiri kuposa chidani.
Ngakhale m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa, abale ndi alongo amasonyezana chikondi chololera kuvutikira ena (Onani ndime 15)c
16. N’chifukwa chiyani mtumwi Petulo ananena kuti anthu amene amazunzidwa chifukwa chotumikira Mulungu ali ndi chifukwa chokhalira osangalala? (1 Petulo 4:14)
16 Timadziwa kuti Mulungu amasangalala tikamapirira anthu akamadana nafe. (Werengani 1 Petulo 4:14.) Mtumwi Petulo ananena kuti anthu amene amapirira akamazunzidwa chifukwa chotumikira Mulungu amakhala ndi chifukwa chowapangitsa kusangalala. Kuzunzidwako ndi umboni wakuti mzimu wa Mulungu ‘uli pa iwo.’ Petulo ankadziwa mmene munthu amamvera akadziwa kuti Mulungu akusangalala naye komanso akamapirira pamene akuzunzidwa. Patapita nthawi yochepa kuchokera pa Pentekosite mu 33 C.E., asilikali a Chiyuda apakachisi anatumizidwa kuti akamange Petulo ndi atumwi ena chifukwa choti ankalalikira. Koma Petulo analankhula molimba mtima za chikhulupiriro chake. (Mac. 5:24-29) Ngakhale pamene anakwapulidwa, iye ndi atumwi anzake sanasiye kulalikira. M’malomwake iwo anasangalala “chifukwa Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” Ifenso tikhoza kumasangalala tikamapirira mayesero.—Mac. 5:40-42.
17. Kodi Yesu anawauza chiyani ophunzira ake usiku woti aphedwa mawa lake?
17 Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Amene amandikonda, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda.” (Yoh. 14:21) Tikuyembekezera nthawi imene anthu onse azidzatikonda, osati kudana nafe, chifukwa chotumikira Yehova. (2 Ates. 1:6-8) Koma panopa timalimbikitsidwa komanso kupeza mphamvu tikamakumbukira zifukwa zimene zimatipangitsa kukhala osangalala anthu akamadana nafe.
NYIMBO NA. 149 Tiimbire Yehova Chifukwa Wapambana
a Mayina ena asinthidwa.
b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI : Chithunzi choyerekezera chosonyeza Ignacio akulalikira aphunzitsi ake.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Chithunzi choyerekezera chosonyeza abale ndi alongo akulimbikitsa Mkhristu mnzawo yemwe akukaikidwa m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupirira.