Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 March tsamba 32
  • Muzikhala Olimba Mtima Komanso Okhulupirika Ngati Benaya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikhala Olimba Mtima Komanso Okhulupirika Ngati Benaya
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Nkhani Yofanana
  • Tizitsanzira Atumiki a Yehova Amene Anali Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • “Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Muzikhala Olimba Mtima Ngati Zadoki
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • “Mudzakhala Wokhulupirika”
    Nsanja ya Olonda—2010
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 March tsamba 32

MUNTHU WOTCHULIDWA M’BAIBULO

Muzikhala Olimba Mtima Komanso Okhulupirika Ngati Benaya

Benaya anali msilikali wolimba mtima yemwe anatumikira Mfumu Davide komanso Solomo. Ngakhale kuti anali mwana wa wansembe ndipo sankafunika kumenya nkhondo, iye ankamenya nawo nkhondo za Yehova ndipo anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Mwachitsanzo, Benaya anapha mkango m’chitsime chopanda madzi komanso munthu yemwe anali wamkulu modabwitsa. Davide ankakhulupirira kwambiri Benaya moti anamuika kukhala mkulu wa asilikali omulondera.—2 Sam. 23:​20-23.

Benaya anakhalabe wokhulupirika kwa Davide pamene Abisalomu komanso Adoniya anaukira ulamuliro wake. (2 Sam. 8:18; 15:18; 1 Maf. 1:8) Davide atakalamba, Benaya anathandiza Solomo kukhala mfumu. (1 Maf. 1:​32-40) Benaya anali wokhulupirika kwa Yehova komanso kwa mafumu amene Yehovayo anawasankha, ngakhale pamene anthu ena sanali okhulupirika.

Ifenso timafunika kukhala olimba mtima kuti tithe kulimbana ndi mdani wathu wamkulu Satana ndiponso amene ali kumbali yake. Ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuti tipitiriza kutsatira mfundo za Yehova. (Aef. 6:11; 1 Pet. 5:​8, 9) Ngakhale pamene ena asankha kusiya Yehova, timakhalabe okhulupirika kwa iye ndipo sitikayikira kuti adzatidalitsa.—2 Sam. 22:26.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena