Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 March tsamba 20-25
  • Muzikhala Ozindikira Kuti ‘Zinthu Zizikuyenderani Bwino’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikhala Ozindikira Kuti ‘Zinthu Zizikuyenderani Bwino’
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MUZICHITA ZINTHU MODZICHEPETSA OSATI MODZIKUZA
  • MUZICHITA ZINTHU MODEKHA OSATI MUTAKWIYA
  • MUZICHITA ZINTHU MOLIMBÀ MTIMA OSATI MWAMANTHA
  • ZIMENE TINGACHITE KUTI TIPITIRIZEBE KUKHALA OZINDIKIRA
  • Kamtsikana Kanalankhula Molimba Mtima Kudziko la Eni
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Kamtsikana Kanathandiza Mkulu wa Asilikali
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Ankafuna Kuthandiza Ena
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Poyamba Anakana Kumvera Koma Kenako Anamvera
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 March tsamba 20-25

MAY 25-31, 2026

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga Khala Wanzeru”

Muzikhala Ozindikira Kuti ‘Zinthu Zizikuyenderani Bwino’

“Munthu wosonyeza kuzindikira pochita zinthu, zidzamuyendera bwino.”—MIY. 16:20.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene kuzindikira kungatithandizire tikafunika kusankha zochita pa zinthu zovuta.

1-2. Kodi kuzindikira kumatanthauza chiyani, nanga kungatithandize bwanji?

KODI winawake anayamba wakuchitiranipo zinthu mopanda ulemu? Kodi munaweruzidwapo molakwika kapena kukhumudwitsidwa? Kapena kodi munakumanapo ndi zinthu zimene zinakuchititsani mantha? Ngati ndi choncho, ndiye kuti mukudziwa kuti zimakhala zovuta kuchita zinthu moganiza bwino pa nthawi ngati zimenezi. Koma n’zosangalatsa kuti Baibulo limatchula za khalidwe linalake limene lingatithandize pa zochitika zimenezi ndi zinanso, lomwe ndi kuzindikira.

2 Kuzindikira ndi luso lotha kuona zinthu zomwe ndi zovuta kuzidziwa. Khalidweli limatithandiza kumvetsa chifukwa chake zinazake zachitika komanso chifukwa chake munthu wina wachita zinthu m’njira inayake. Choncho kuzindikira kungatithandize kuchita zinthu mwanzeru komanso moganiza bwino. Mwachitsanzo, kuzindikira kumatithandiza kuti ‘tizilamulira milomo yathu’ komanso tizidziwa nthawi yoyenera ‘kukhala chete.’ (Miy. 10:19; Sal. 4:4) Kungatithandizenso kuti tizilamulira mkwiyo wathu ndiponso tizinyalanyaza zimene ena atilakwira. Kuzindikira kungatithandize kuti tizimvetsera ena akamatipatsa malangizo komanso kutithandiza kuti tikonze zimene talakwitsa. (Miy. 19:20) Tikakhala ozindikira, zolankhula ndi zochita zathu zimasangalatsa Yehova komanso zimathandiza ifeyo ndi anthu ena kukhala osangalala. Ndipo tikakhumudwitsidwa sitingakwiye kwambiri mpaka kuchita zinthu zolakwika. Tiyeni tikambirane zitsanzo zitatu za m’Baibulo zosonyeza mmene kuzindikira kungatithandizire kukhala odzichepetsa, odekha komanso kuti tizidalira kwambiri Yehova.

MUZICHITA ZINTHU MODZICHEPETSA OSATI MODZIKUZA

3. Kodi Namani anali ndani?

3 Kuti zinthu zizitiyendera bwino, timafunika kupewa mtima wodzikuza. (1 Pet. 5:5) Ndiye kodi kuzindikira kungatithandize bwanji kuti tithe kuchita zimenezi? Taganizirani chitsanzo cha Namani. Iye ankakhala ku Siriya, dziko lomwe linali kumpoto kwa Isiraeli. Namani anali mkulu wa asilikali a Siriya wodziwika bwino. Komabe, iye ankadwala matenda oopsa kwambiri apakhungu a khate.—2 Maf. 5:1.

4. Kodi Namani anasonyeza bwanji kuti anali wozindikira?

4 Mkazi wa Namani anali ndi kamtsikana ka Chiisiraeli kamene kankamugwirira ntchito ndipo kanamuuza kuti ku Isiraeli kuli mneneri yemwe akanachiritsa mwamuna wake. (2 Maf. 5:​2, 3) Mwina Namani akanaganiza kuti, ‘Kamtsikana kantchitoka komanso kochokera kwa adani athu kangandiuze chiyani?’ Koma Namani anasonyeza kuti anali wozindikira. M’malo monyalanyaza zimene kamtsikanako kananena, modzichepetsa anamvera. Iye anatenga chilolezo kwa mfumu ya Siriya choti apite ku Isiraeli kuti akachiritsidwe.—2 Maf. 5:​4, 5.

5. Kodi chinachitika n’chiyani Namani atafika ku Isiraeli?

5 Namani anafika kwa Mfumu Yehoramu ali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwa. Komabe, Yehoramu ankaganiza kuti mfumu ya Siriya ikungofuna kulimbana naye basi. Mneneri Elisa atamva zimenezi, anapempha Yehoramu kuti amutumize Namani kwa iye. (2 Maf. 5:​6-9) Koma zinthu sizinachitike mmene Namani ankaganizira. Elisa sanatuluke n’komwe m’nyumba mwake kudzalandira Namani kapena kulankhula naye. M’malomwake anangotumiza munthu kuti akamuuze zoyenera kuchita kuti achire.—2 Maf. 5:10.

6. (a) Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinachititsa Namani kulephera kutsatira malangizo amene anapatsidwa? (b) Kodi atumiki a Namani anasonyeza bwanji kuti anali ozindikira, nanga zotsatira zake zinali zotani? (2 Mafumu 5:​13, 14)

6 Poyamba, Namani sanasangalale ndi zimene munthu uja anamuuza. Iye “anapsa mtima” “nʼkumapita atakwiya kwambiri.” (2 Maf. 5:​11, 12) N’kutheka kuti anachita zimenezi poona kuti sanapatsidwe ulemu monga mkulu wa asilikali. Ayeneranso kuti ankaganiza kuti malangizo amene anamupatsa ankasonyeza kuti Elisa sankalemekeza dziko la Siriya. Choncho Namani anaganiza zobwerera kwawo ngakhale kuti anali asanachiritsidwe. Komabe atumiki ake anasonyeza kuti anali ozindikira ndipo anamupempha kuti aiganizirenso bwino nkhaniyi. Pamapeto pake, iye anadzichepetsa n’kutsatira malangizo amene Elisa anamupatsa ndipo anachiritsidwa.—Werengani 2 Mafumu 5:​13, 14.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Namani? (Miyambo 22:4) (Onaninso zithunzi.)

7 Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani? Timasonyeza kuti ndife ozindikira tikamaganiza kaye tisanachite chilichonse. Timasonyezanso kuzindikira tikamapewa kusankha zochita pongotengera mmene tikumvera. Kuzindikira kungatithandize kukhala odzichepetsa. Munthu wodzichepetsa amazindikira kuti sadziwa zonse. Nthawi zina timafunikira ena kuti atithandize kumvetsa zinthu ndipo Yehova ndi amene angatithandize kwambiri pa nkhaniyi. Ngakhale kuti Namani anali asanayambe kulambira Yehova, iye anasonyeza kuzindikira podzichepetsa n’kumvera anthu ena monga mtsikana wa Chiisiraeli, atumiki ake ndipo chofunika kwambiri n’chakuti anamvera Elisa, mneneri wa Yehova. Namani anasiya kukhala wonyada. Pamapeto pake, iye anasankha zinthu mwanzeru ndipo zinamuyendera bwino. Ifenso tikalandira malangizo ochokera m’Malemba omwe sitikugwirizana nawo kapena ochokera ku gulu amene sitikuwamvetsa, tisanachite chilichonse tingachite bwino kuima kaye n’kuganizira ngati zimene tikufuna kulankhula kapena kuchita zisonyeze ngati ndife odzikuza kapena odzichepetsa.—Werengani Miyambo 22:4.

Zithunzi: M’bale akusonyeza kuzindikira pomwe akumvetsera modzichepetsa. 1. Akumvetsera pomwe m’bale wachinyamata akumupatsa malangizo a m’kabuku ka “Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso.” 2. Akumvetsera pamene mlongo wachikulire akumufotokozera zokhudza ulaliki wapashelefu. 3. Akumvetsera pamene akuonera pulogalamu ya JW Broadcasting pa tabuleti yake.

Mofanana ndi Namani, ifenso tizidzichepetsa n’kumamvetsera anthu ena akamatipatsa malangizo, akamatiuza za vuto linalake kapena tikalandira malangizo ochokera ku gulu la Yehova (Onani ndime 7)


MUZICHITA ZINTHU MODEKHA OSATI MUTAKWIYA

8. Kodi ndi pa zochitika ziti pamene zingakhale zovuta kuchita zinthu modekha?

8 Kuzindikira kungatithandize kuti tikhalebe odekha ngati patachitika zinazake zimene zatikhumudwitsa m’malo mochita zinthu titakwiya. Kunena zoona, zimenezi si zophweka chifukwa nthawi zina timakhala ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukwiya ndi zolankhula kapena zochita za ena. (Aef. 4:26) Tiyeni tikambirane mmene Davide komanso Abigayeli anasonyezera kuzindikira pa nthawi imene zinthu zinali zovuta.

9. Kodi Nabala anamuchitira zotani Davide?

9 Taganizirani zimene zinachitika pamene Davide ndi atumiki ake ankathawa Sauli m’chipululu cha Parana. (1 Sam. 25:1) Ali m’chipululumo, iwo ankateteza abusa ndi nkhosa za munthu winawake wolemera dzina lake Nabala. (1 Sam. 25:​15, 16) Nthawi yometa ubweya wa nkhosa itafika, Davide anatumiza anthu ake kwa Nabala kuti akamufunire zabwino komanso akamupemphe kuti awagawireko chilichonse chimene akanakonda kuwapatsa. (1 Sam. 25:​6-8) Koma Nabala sanayamikire zinthu zonse zabwino zimene Davide ndi atumiki ake anamuchitira. Iye anayankha mwamwano ndipo ananyoza Davide ndi atumiki akewo.—1 Sam. 25:​10, 11.

10. Kodi Davide ndi Abigayeli anasonyeza bwanji kuti anali ozindikira? (1 Samueli 25:​32, 33) (Onaninso chithunzi.)

10 Kodi inuyo mukanakhala Davide mukanatani? Tikhoza kumvetsa chifukwa chake Davide anakwiya kwambiri. Iye anali munthu wosachedwa kukhudzika ndi zinthu ndipo pa nthawiyi anakwiya kwambiri moti ankafuna kupha Nabala. (1 Sam. 25:​13, 21, 22) Ndipotu anali atauyamba kale ulendo wokapha Nabala pamene anakumana ndi Abigayeli, yemwe anali mkazi wanzeru wa Nabalayo. Ndiye kodi Abigayeli anasonyeza bwanji kuti anali wozindikira? Iye anazindikira kuti Davide anali munthu wabwino ngakhale kuti pa nthawiyi anali atakwiya. Ndiye anachita zonse zimene akanatha pomuthandiza kuti achite zinthu modekha komanso mwanzeru. Abigayeli anamupatsa Davide mphatso ndipo modzichepetsa anam’patsanso malangizo anzeru. (1 Sam. 25:​18, 23-31) Davide anasonyeza kuzindikira pomvetsera zimene Abigayeli ananena ndipo anadziwa kuti mawu akewo anasonyeza mmene Yehova ankaonera nkhaniyo. Zotsatira zake, mtima wa Davide unakhala m’malo ndipo sanalakwitse kwambiri zinthu.—Werengani 1 Samueli 25:​32, 33.

Davide akumvetsera mwatcheru pamene Abigayeli wagwada n’kumamuchonderera. Amuna amene ali ndi Davide ali chapafupi ndipo akuona zimene zikuchitika. Atumiki a Abigayeli anyamula mphatso zambiri ndipo ali kumbuyo kwa Abigayeliyo.

Davide ndi Abigayeli anapewa mavuto chifukwa chochita zinthu mozindikira (Onani ndime 10)


11. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji wina akatikhumudwitsa? (Miyambo 19:11)

11 Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani? Kuzindikira kungatithandize kuti tichite zinthu mwamtendere pakachitika zinazake, ngakhale patakhala zifukwa zomveka zoti tikwiyire. Kungatithandizenso kuti tiganizire zotsatira za zimene tingalankhule kapena kuchita. (Werengani Miyambo 19:11.) Abigayeli atamukumbutsa Davide mmene zochita zake zingakhudzire Yehova, zinamuthandiza kuti achite zinthu modekha. Mukakwiya kapena kukhumudwa ndi zinazake, muzipewa kuchita zinthu mosaganiza bwino. (Yak. 1:19) Muzipemphera kwa Yehova komanso kudzipatsa nthawi yokwanira kuti mudziwe mmene iye akuionera nkhaniyo ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti muchite zinthu modekha.

12. Kodi anthu ena angatithandize bwanji kukhala ozindikira komanso odekha?

12 Yehova anagwiritsa ntchito Abigayeli pothandiza Davide kuti achite zinthu mozindikira. Mofanana ndi zimenezi, angagwiritsenso ntchito anthu ena kuti atithandize kuchita zinthu mwanzeru komanso modekha. Ndiye ngati mwakhumudwa ndi zinazake, mungachite bwino kufunsa maganizo kwa Mkhristu wolimba mwauzimu yemwe angakuthandizeni kuona nkhaniyo mmene Yehova akuionera. (Miy. 12:15; 20:18) Komabe, ngati muli ndi mwayi wothandiza mnzanu amene wakhumudwa, mungatani kuti muzitsanzira Abigayeli? Muzimuthandiza mnzanuyo kuona nkhaniyo mmene Yehova akuionera. Yehova adzadalitsa khama lanu mukamathandiza ena kuti akhale ozindikira komanso odekha.

MUZICHITA ZINTHU MOLIMBÀ MTIMA OSATI MWAMANTHA

13. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji kuti tisamachite mantha?

13 Nthawi zina tingakumane ndi zinthu zochititsa mantha. Koma kuzindikira kungatithandize kuona kuti chilichonse chimene chikutichititsa mantha m’dzikoli si champhamvu tikachiyerekezera ndi mphamvu zodabwitsa za Yehova. (Sal. 27:1) Yehova angatithandize pa vuto lililonse ngakhale pamene zikuoneka kuti tasoweratu mtengo wogwira. Zimenezi ndi zomwe zinachitikira mneneri Yona. Iye anali munthu wolimba mwauzimu koma ankafunika kukhala wozindikira kuti akwanitse utumiki wovuta umene anapatsidwa.

14. Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinachititsa Yona kuopa kuchita zimene Yehova anamuuza?

14 Yehova anapatsa Yona utumiki wovuta kwambiri. Iye ankafunika kupita ku Nineve kukalengeza uthenga wachiweruzo. (Yona 1:​1, 2) Kodi inuyo mukanamva bwanji mukanapatsidwa utumiki ngati umenewu? Kuti Yona ayende wapansi kuchoka ku Isiraeli kukafika mumzinda wa Nineve wa Asuri, zinamutengera pafupifupi mwezi wathunthu. Asuri anali ankhanza kwambiri komanso achiwawa. Ndipotu mzinda wa Nineve unkadziwika kuti “mzinda wokhetsa magazi.” (Nah. 3:​1, 7) M’malo movomera utumiki umene anapatsidwa, Yona anaganiza zothawa.—Yona 1:3.

15. Kodi n’chiyani chinamuthandiza Yona kuti azikhulupirira kwambiri Yehova? (Yona 2:​6-9)

15 Pamene Yona ankathawa, Yehova anamukumbutsa kuti ali ndi mphamvu pomupulumutsa modabwitsa. (Yona 1:​15, 17) Apa Yona anaphunzirapo kanthu. Iye anasiya kuona kuti utumiki umene anapatsidwa ndi wochititsa mantha ndipo anayamba kuganizira kwambiri zoti Yehova akhoza kumuteteza ku zoopsa zilizonse. (Werengani Yona 2:​6-9.) Yehova atamupatsanso mwayi wina wa utumiki, iye sanakane. Yona anapita ku Nineve ndipo kumeneko utumiki wake unayenda bwino kwambiri.—Yona 3:5.

16. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji tikakumana ndi zinthu zochititsa mantha? (Miyambo 29:25) (Onaninso zithunzi.)

16 Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani? Tisamalole chilichonse, makamaka kuopa anthu, kutilepheretsa kulambira Yehova. (Werengani Miyambo 29:25.) Kuzindikira kunathandiza Yona kuti asamangoganizira za mavuto amene akanakumana nawo pa utumiki wake koma aziganizira kwambiri mmene Yehova akanamuthandizira. Mofanana ndi Yona, tisamaganizire zinthu zochititsa mantha, koma tiziganizira kwambiri mmene Yehova wakhala akutithandizira komanso kutiteteza. Tiziganiziranso zitsanzo za abale ndi alongo amene anakwanitsa kulimbana ndi zinthu zochititsa mantha kapena kuchita mautumiki ovuta kwambiri chifukwa chodalira Yehova. (Aheb. 13:6) Choncho tiyeni tizikhala ozindikira podalira kwambiri Yehova komanso kuthandiza ena kuti azichitanso zomwezo.

Zithunzi: 1. Mneneri Yona akukalowa pageti la mzinda wa Nineve. 2. M’bale wachinyamata akuyenda mukolido kusukulu momwe mukuchitika zinthu zimene Yehova sasangalala nazo. Mbendera zooneka ngati utawaleza zapachikidwa mukolidoyo. Mnyamata wina akuvutitsa mnzake.

Chitsanzo cha Yona chikutiphunzitsa kuti kuzindikira kungatithandize kuti tizitsatira malangizo a Mulungu komanso zinthu zizitiyendera bwino tikakumana ndi mavuto (Onani ndime 16)


ZIMENE TINGACHITE KUTI TIPITIRIZEBE KUKHALA OZINDIKIRA

17. Kodi tingatani kuti tipitirize kukhala ozindikira?

17 Monga mmene taonera, kuzindikira kungatithandize kuti tizichita zinthu mwanzeru tikakumana ndi zinthu zovuta. Kodi tingatani kuti tipitirize kukhala ozindikira? Yehova ndi amene angatithandize kwambiri kuti tikhale ozindikira ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito Mawu ake ndiponso mzimu woyera. (Neh. 9:20; Sal. 32:8) Iye amatipatsa malangizo otithandiza kuchita zinthu mwanzeru komanso kuti tisamangochita zinthu potengera mmene tikumvera. (Sal. 119:​97-101) Timakhala ozindikira tikamaganizira kwambiri zimene Baibulo limanena komanso kupempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera. Zimenezi zimatithandiza kuona zinthu mmene Yehova amazionera komanso kuti zolankhula ndi zochita zathu zizisonyeza mmene iye amaganizira.—Miy. 21:​11, mawu a m’munsi.

18. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?

18 Tiyeni tipitirize kupempha Yehova kuti atithandize kukhala ozindikira komanso tiziona kuti khalidweli ndi lofunika kwambiri. (Sal. 14:2) Tikamachita zimenezi, sitidzasiya “kuchita zinthu mozindikira.” (Miy. 21:16) Koma tidzakhala otsimikiza mtima kuti tizichita zinthu mozindikira nthawi zonse komanso pa chilichonse. Tikatero, ‘zinthu zidzatiyendera bwino.’

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI NDIFE OZINDIKIRA NGATI MMENE ANACHITIRA . . .

  • Namani?

  • Davide ndi Abigayeli?

  • Yona?

NYIMBO NA. 42 Pemphero la Mtumiki wa Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena