April
Lachitatu, April 1
Zimene Atate wanga akufuna ndi zoti aliyense wovomereza Mwana komanso kumukhulupirira akhale ndi moyo wosatha.—Yoh. 6:40.
Kuti tipindule ndi thupi komanso magazi a Yesu, tiyenera kukhulupirira dipo. (Aef. 1:7) Anthu omwe Yesu anawatchula kuti “nkhosa zina” sayenera kudya kapena kumwa vinyo pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (Yoh. 10:16) Ngakhale zili choncho iwo amapindula ndi thupi komanso magazi a Yesu Khristu. Iwo amadya chakudya chimenechi akamakhulupirira kuti nsembe ya Yesu ingawapulumutse. (Yoh. 6:53) Koma anthu omwe amadya mkate komanso kumwa vinyo amasonyeza kuti ali m’pangano latsopano ndipo adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Choncho kaya ndife odzozedwa kapena a nkhosa zina tiyenera kusonyeza chikhulupiriro kuti tikapeze moyo wosatha. w24.12 13 ¶14, 16
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 12 kutacha) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6
TSIKU LA CHIKUMBUTSO
Dzuwa Litalowa
Lachinayi, April 2
Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.—Luka 12:32.
Pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, Yesu anapereka mkate wopanda chofufumitsa kwa atumwi ake ndipo anawauza kuti ukuimira thupi lake. Kenako anawapatsa vinyo n’kuwauza kuti akuimira ‘magazi ake apangano.’ (Maliko 14:22-25; Luka 22:20; 1 Akor. 11:24) Zimene ananenazitu n’zofunika kwambiri. Pangano latsopanoli silikukhudza anthu onse koma ndi lapakati pa Yehova ndi “nyumba [yauzimu] ya Isiraeli,” yomwe ndi anthu amene adzalamulire ndi Yesu “mu Ufumu wa Mulungu.” (Aheb. 8:6, 10; 9:15) Pa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, Yesu ankalankhula za “kagulu ka nkhosa.” Kagulu kameneka kanayamba ndi atumwi ake okhulupirika omwe analipo m’chipindamo. Amenewa ndi amene adzalamulire naye kumwamba. w24.12 11 ¶9-10
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 13 kutacha) Mateyu 26:17-19; Maliko 14:12-16; Luka 22:7-13 (Zochitika pa Nisani 14 dzuwa litalowa) Yohane 13:1-5; 14:1-3
Lachisanu, April 3
Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.—Yoh. 3:16.
Yesu anaperekedwa ndi mmodzi wa anzake apamtima, anamangidwa, ananyozedwa, ananeneredwa zabodza, anaweruzidwa kuti aphedwe komanso anazunzidwa. Pamapeto pake asilikali anamutengera kumalo amene anakamuphera pomupachika pamtengo. Yesu anapirira mokhulupirika ululu komanso mavuto onse omwe anakumana nawo. Koma Yehova Mulungu ndi amene anamva ululu kwambiri poona Mwana wake akuvutika. Ngakhale kuti iye ali ndi mphamvu zopanda malire, sanalowererepo n’kuthetsa mavuto omwe Mwana wake anakumana nawo. N’chifukwa chiyani analolera kuti Mwana wake avutike komanso aphedwe? Mwachidule tingati ndi chikondi. Nsembe ya Yesu ndi umboni waukulu wakuti Yehova amakukondani kwambiri inuyo. Iye anachita zazikulu polola kuti amve ululu woopsa n’cholinga choti akupulumutseni ku uchimo ndi imfa. (1 Yoh. 4:9, 10) Choncho iye amafuna kuthandiza wina aliyense wa ife kuti apambane pankhondo yolimba ndi uchimo. w24.08 6 ¶13-14
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 14 kutacha) Yohane 19:1-42
Loweruka, April 4
Khristu anavutika chifukwa cha inu.—1 Pet. 2:21.
Tingamvetse bwino kuti Yehova amatikonda, tikaganizira mmene zinamupwetekera kuti apereke dipo. Satana amanena kuti palibe mtumiki wa Yehova yemwe angakhalebe wokhulupirika ngati atakumana ndi mavuto aakulu. Pofuna kutsutsa bodza limeneli, Yehova analola kuti Yesu avutike asanafe. (Yobu 2:1-5) Yehova ankaona pamene Yesu ankanyozedwa ndi adani ake, kukwapulidwa ndi asilikali komanso kukhomereredwa pamtengo. Kenako Yehova anaona Mwana wake wokondedwayo akuvutika ndi ululu mpaka kufa. (Mat. 27:28-31, 39) Yehova anali ndi mphamvu yoletsa zonsezi kuti zisachitike. (Mat. 27:42, 43) Koma ngati Mulungu akanachita zimenezi, dipo silikanaperekedwa ndipo tikanakhalabe opanda chiyembekezo. Choncho Yehova analola kuti Mwana wake avutike mpaka kufa. w25.01 22 ¶7
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 15 kutacha) Mateyu 27:62-66 (Zochitika pa Nisani 16 dzuwa litalowa) Yohane 20:1
Lamlungu, April 5
Iwo anamuona masiku onse 40.—Mac. 1:3.
Pa Nisani 16 mu 33 C.E., ophunzira a Yesu anali ndi chisoni komanso mantha. Ophunzira awiri anachoka ku Yerusalemu kupita ku Emau. Munthu wina anayamba kuyenda nawo limodzi mumsewu. Iwo anamufotokozera zinthu zokhumudwitsa zimene zinachitikira Yesu. Munthuyo anayamba kukambirana nawo zinthu zimene sakanadzaiwala. Iye anawafotokozera chifukwa chake Yesu ankayenera kuvutika komanso kufa pogwiritsa ntchito “zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneri analemba.” Atafika ku Emau, munthuyo anadziulula kuti anali Yesu ndipo anali ataukitsidwa. (Luka 24:13-35) Pa masiku 40 omaliza a moyo wake padzikoli, Yesu anaonekera maulendo angapo kwa ophunzira ake. Pa nthawiyi, ophunzira a Yesu omwe anali achisoni komanso amantha, anasintha n’kuyamba kusangalala komanso kukhala olimba mtima ndipo ankalalikira komanso kuphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu. w24.10 12 ¶1-3
Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 16 kutacha) Yohane 20:2-18
Lolemba, April 6
Muzilimbitsa chikhulupiriro chanu choyera kwambiri.—Yuda 20.
Pakapita nthawi, mwana amakula n’kukhala munthu wamkulu koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. Chitsanzo ndi zomwe zinachitikira abale a ku Korinto. Iwo analandira uthenga wabwino, anabatizidwa, analandira mzimu woyera ndipo anaphunzira zambiri kuchokera pa malangizo a mtumwi Paulo. (Mac. 18:8-11) Komabe ngakhale kuti panali patapita zaka zambiri kuchokera pamene anabatizidwa, ambiri anali adakali osalimba mwauzimu. (1 Akor. 3:2) Kuti tifike pokhala aakulu mwauzimu, choyamba tiyenera kukhala ndi mtima wofuna kukhala olimba mwauzimu. Anthu amene amasankha kukhala “osadziwa zinthu” n’kumangokhalabe makanda mwauzimu, sapita patsogolo. (Miy. 1:22) Sitikufuna kukhala ngati anthu akuluakulu amene amadalirabe makolo awo kuti aziwasankhira zochita. M’malomwake timaonetsetsa kuti tikupitirizabe kukula mwauzimu. Ngati mukuchita khama kuti mukule mwauzimu, muzipempha Yehova kuti akupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.”—Afil. 2:13. w24.04 4 ¶9-10
Lachiwiri, April 7
Yehova . . . sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe.—2 Pet. 3:9.
Yehova amatiuza mmene amamvera pa nkhani yoweruza anthu. (Ezek. 33:11) Yehova safulumira kuwonongeratu anthu. Iye ndi wachifundo chachikulu ndipo amasonyeza chifundocho ngati pakufunika kutero. Kodi ndi zinthu ziti zimene tikudziwa za anthu amene sadzaukitsidwa? Baibulo limangotchula zitsanzo zochepa. Yesu ananena kuti Yudasi Isikarioti sadzaukitsidwa. (Maliko 14:21; Yoh. 17:12) Yudasi, modziwa komanso mwadala, anachita zinthu motsutsana ndi Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake. (Maliko 3:29) Yesu ananenanso kuti atsogoleri a chipembedzo ena amene ankamutsutsa alibenso chiyembekezo chakuti adzauka. (Mat. 23:33; Yoh. 19:11) Mtumwi Petulo anachenjezanso kuti anthu ampatuko osalapa, sadzaukitsidwa.—Aheb. 6:4-8; 10:29. w24.05 4 ¶10-11
Lachitatu, April 8
Yehova amateteza okhulupirika.—Sal. 31:23.
Tikapitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, Satana sangachite chilichonse chomwe chingativulaze mpaka kalekale. (1 Yoh. 3:8) Yehova adzapitiriza kuteteza anzake okhulupirika ku zinthu zomwe zingawavulaze mwauzimu ngakhalenso imfa. (Chiv. 21:4) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kukhala mlendo mutenti ya Yehova ndipo timasangalala kukhala naye pa ubwenzi mpaka kalekale. (Ezek. 37:27) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipitirize kukhala alendo ake? Ngati mutaitanidwa kunyumba kwa mnzanu, mungafune kudziwa zimene iye angakonde kuti muchite. Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingafune kudziwa zimene Yehova angakonde kuti anthu omwe akufuna kupitiriza kukhala alendo mutenti yake azichita. Kukonda Yehova kumatilimbikitsa kuti tizichita zonse zomwe tingathe kuti ‘tizimusangalatsa pa chilichonse.’ (Akol. 1:10) Tisamaiwale zimenezi ndipo nthawi zonse tizimupatsa ulemu waukulu. Zimenezi zingatithandize kuti tizipewa kuchita zinthu zomwe zingamukhumudwitse. Choncho timafunitsitsa kuti ‘tiziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wathu.’—Mika 6:8. w24.06 4 ¶8-9
Lachinayi, April 9
Analowererapo kuti athandize anthu ochimwa.—Yes. 53:12.
Yehova anamupempha Abulahamu kuti apereke mwana wake Isaki monga nsembe. Zimenezitu ziyenera kuti zinali zovuta kwambiri kwa Abulahamu. Koma ngakhale zinali choncho, iye anali wokonzeka kumvera. Koma atangotsala pang’ono kupha mwana wakeyo, Mulungu anamuletsa. Chitsanzo chimenechi chimaphunzitsa anthu onse okhulupirira Mulungu mfundo ya choonadi yofunika kwambiri. Mfundo yake ndi yakuti Yehova anali wofunitsitsa kupereka Mwana wake wokondedwa monga nsembe. Izi zikusonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu. (Gen. 22:1-18) Patapita zaka zambiri, Mulungu anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli chomwe chinkasonyeza kuti anthu a Mulungu ankafunika kupereka nsembe mobwerezabwereza kuti machimo awo azikhululukidwa. (Lev. 4:27-29; 17:11) Nsembe zimenezi zinkaimira nsembe yaikulu imene ikanadzapulumutsiratu anthu ku uchimo. Aneneri a Mulungu anauziridwa kuti alembe zokhudza mbadwa yolonjezedwa, yomwe ndi Mwana wapadera wa Mulungu. Iwo anafotokoza kuti Mwanayo adzazunzidwa komanso kuphedwa n’cholinga chofuna kupulumutsa anthu kuphatikizapo inuyo ku uchimo ndi imfa.—Yes. 53:1-12. w24.08 4 ¶7-8
Lachisanu, April 10
Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimaganizira mozama chilamulocho tsiku lonse.—Sal. 119:97.
Mukamawerenga Baibulo muzionetsetsa kuti mukupeza njira yogwiritsa ntchito zomwe mwawerenga. Mukawerenga kachigawo kenakake ka Mawu a Mulungu, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji zimenezi panopa kapena m’tsogolo?’ Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mukuwerenga Baibulo pa 1 Atesalonika 5:17, 18. Pambuyo powerenga mavesi awiriwa, mukhoza kuima n’kuganizira ngati mumapemphera pafupipafupi komanso kuchokera pansi pa mtima. Mukhoza kuganiziranso zinthu zimene inuyo mumayamikira. Mwina mukuganizira zinthu zitatu zimene Yehova wakuchitirani ndipo mukufuna mumuthokoze. Ngati mutamachita zimenezi ngakhale kwa nthawi yochepa, mukhoza kukhala munthu amene amamva Mawu a Mulungu n’kumawachita. Mukhoza kupindula kwambiri mukamachita zimenezi tsiku lililonse pa mavesi a m’Baibulo amene mumawerenga. Mukatero mudzakhala munthu amene amachita zimene Mawu a Mulungu amanena. w24.09 4-5 ¶9-10
Loweruka, April 11
Samalani kuti musataye zinthu zimene tinakuthandizani kuti muzipeze nʼcholinga choti mudzalandire madalitso onse amene Mulungu wakukonzerani.—2 Yoh. 8.
Yehova anatilenga m’njira yapadera. Ngakhale kuti timasangalala tikalandira, timasangalala kwambiri tikapatsa anthu ena zinthu. Timamva bwino tikathandiza Akhristu anzathu ndipo timasangalala akayamikira. Koma kaya munthu atiyamikira kapena ayi, ifeyo timasangalala chifukwa tachita zinthu zoyenera. Musamaiwale kuti mukapereka zinthu “Yehova akhoza kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.” (2 Mbiri 25:9) Sitingapereke zinthu kuposa zimene Yehova angatipatse. Ndipo palibe chinthu chosangalatsa ngati kubwezeredwa ndi Yehova. Choncho tiyeni tipitirize kutsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wopatsa. w24.09 31 ¶20-21
Lamlungu, April 12
Ndimakutamandani ndi mtima wanga wonse, inu Yehova Mulungu wanga, ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale.—Sal. 86:12.
Yehova ndi wachifundo. (Sal. 103:13; Yes. 49:15) Amaganizira ena ndipo tikamamva ululu nayenso zimamupweteka. (Zek. 2:8) Iye amaonetsetsa kuti tikhale anzake. (Sal. 25:14; Mac. 17:27) Yehova ndi wodzichepetsa ndipo “amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.” (Sal. 113:6, 7) Tonsefe timafuna kupereka ulemerero kwa Mulungu wathu wamkulu. Timapereka ulemerero kwa Yehova chifukwa timafuna kuti ena amudziwe. Anthu ambiri samudziwa bwinobwino Yehova. Zili choncho chifukwa chakuti Satana wawachititsa khungu pofalitsa mabodza okhudza Mulungu. (2 Akor. 4:4) Iye wachititsa anthu kukhulupirira kuti Yehova ndi wankhanza, sasamala za anthu komanso ndi amene amachititsa mavuto ambiri m’dzikoli. Koma ife timadziwa zoona zokhudza Mulungu wathu. Tili ndi mwayi wothandiza ena kudziwa zokhudza iye komanso kumupatsa ulemerero.—Yes. 43:10. w25.01 3 ¶6-7
Lolemba, April 13
Satana . . . akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.—Chiv. 12:9.
Mu nthawi ya Yesu, anthu otsutsa ankanena zinthu zabodza zokhudza Mwana wa Mulungu wangwiro amene ankachita zodabwitsa. Mwachitsanzo, atsogoleri achipembedzo ankauza anthu kuti mphamvu zimene Yesu ankagwiritsa ntchito potulutsa ziwanda anapatsidwa ndi “wolamulira ziwanda.” (Maliko 3:22) Pa nthawi imene ankaimbidwa mlandu, atsogoleri achipembedzo ankanena kuti Yesu ndi wonyoza Mulungu ndipo analimbikitsa anthu kuti iye aphedwe. (Mat. 27:20) Pambuyo pake, pamene otsatira a Khristu ankalalikira uthenga wabwino, anthu otsutsa “anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo” kuti azizunza Akhristu. (Mac. 14:2, 19) Pofotokoza lemba la Machitidwe 14:2, Nsanja ya Olonda ya December 1, 1998, inanena kuti: “M’malo mongokana uthengawu, Ayuda otsutsawa anayamba kukopa anthu a mitundu ina kuti azidana ndi Akhristu.” Satana sanasiye kunena zabodza. Masiku ano, iye “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” w24.04 11 ¶15-16
Lachiwiri, April 14
Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?—Gen. 18:25.
Kuukitsidwa kwa munthu sikukudalira kuti wafa pa nthawi iti. Yehova ndi Woweruza wolungama ndipo nthawi zonse amaweruza mwachilungamo. (Sal. 33:4, 5) Choncho tingakhale otsimikiza kuti “Woweruza wa dziko lonse lapansi” adzachita zoyenera. N’zomvekanso kunena kuti kuukitsidwa kwa munthu kuti akhale ndi moyo wosatha sikukudalira kumene ankakhala. N’zosamveka kuti Yehova adzaweruza anthu ambirimbiri kuti ndi “mbuzi” chifukwa chakuti ankakhala m’mayiko amene analibe mwayi woti amve uthenga wa Ufumu. (Mat. 25:46) Woweruza wolungama wa dziko lonse amaganizira kwambiri anthu amenewa kuposa ifeyo. Sitikudziwa mmene Yehova adzachitire zinthu pa nthawi ya chisautso chachikulu. N’kutheka kuti ena mwa anthu amenewa adzakhala ndi mwayi wophunzira zokhudza Yehova, kumukhulupirira komanso kuyamba kumutumikira pamene azidzayeretsa dzina lake.—Ezek. 38:16. w24.05 12 ¶14-15
Lachitatu, April 15
Muzikondana.—Yoh. 15:12.
Nthawi zonse anthu a Yehova amathandizana. (2 Akor. 8:4) Komabe iwo nthawi zina amafunika kulimba mtima kuti achite zimenezi. Mwachitsanzo kukakhala nkhondo, akulu amazindikira kuti abale ndi alongo awo amafunika kulimbikitsidwa, kupatsidwa zinthu zofunika pa moyo komanso chakudya chauzimu. Chifukwa chokonda nkhosa, iwo amalolera kuika moyo wawo pangozi kuti apereke thandizo lofunika kwa abale awo. Pa nthawi ngati imeneyi, timafunika kuchita zinthu mogwirizana. Tiyenera kutsatira malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumaonanso zimene anakonza pa nkhani yokonzekera ngozi komanso kutsatira malangizo a gulu pa nthawi ya ngoziyo. (1 Akor. 14:33, 40) Muzikhala olimba mtima koma muzichita zinthu mosamala. (Miy. 22:3) Muziganiza kaye musanachite zinazake. Muziyesetsa kuti mukhale otetezeka. Muzidalira Yehova. Iye angakuthandizeni kuti mupereke thandizo kwa abale anu muli otetezeka. w24.07 4 ¶8; 5 ¶11
Lachinayi, April 16
Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova, . . . ndipo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.—Sal. 18:6.
Mfumu Davide ankadziwa Yehova ndipo ankamudalira. Pamene Mfumu Sauli komanso adani ake ankafuna kumupha, Davide anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize. Mulungu atayankha pemphero lake n’kumupulumutsa, Davide ananena kuti: “Yehova ndi wamoyo.” (Sal. 18:46) Polankhula mawu amenewa, Davide sankatanthauza kuti ankangodziwa kuti Mulungu aliko. Buku lina linanena kuti Davide ankakhulupirira kuti Yehova “ndi Mulungu wamoyo yemwe nthawi zonse amathandiza anthu ake.” Zimene zinachitika pa moyo wa Davide zinamutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo ndipo zinamulimbikitsa kuti apitirize kumutumikira komanso kumutamanda. (Sal. 18:28, 29, 49) Kukhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu wamoyo kungatithandize kuti tizimutumikira ndi mtima wonse. Tidzapeza mphamvu kuti tizipirira mayesero komanso tizichita zambiri pomutumikira. Tidzakhalanso ofunitsitsa kupitiriza kukhala naye pa ubwenzi. w24.06 20-21 ¶3-4
Lachisanu, April 17
Musalole kuti aliyense akusocheretseni.—2 Ates. 2:3.
Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a mtumwi Paulo opita kwa Atesalonika? Tikamva zinazake zomwe sizikugwirizana ndi zomwe timaphunzira m’Baibulo kapenanso mphekesera, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru. M’dziko lomwe poyamba linkatchedwa Soviet Union, adani athu anafalitsa kalata yooneka ngati ikuchokera kulikulu lathu. Kalatayo inalimbikitsa abale ena kuti apange kagulu kena kapadera koima pakokha. Kalatayo inkaoneka ngati yachokeradi kulikulu lathu. Koma abale okhulupirika sanapusitsidwe. Iwo anazindikira kuti uthenga wa m’kalatayo sunkagwirizana ndi zomwe akhala akuphunzitsidwa. Masiku anonso adani athu amagwiritsa ntchito njira zamakono pofuna kutisokoneza kapena kutichititsa kuti tisamagwirizane. M’malo molola kuti wina aliyense “asinthe maganizo [athu]” omwe ndi olondola, tingadziteteze poganizira mosamala ngati zimene tamva kapena kuwerenga zikugwirizana ndi mfundo za choonadi zomwe tikuzidziwa kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1. w24.07 12 ¶14-15
Loweruka, April 18
Wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza.—1 Yoh. 2:1.
Nkhani yofunika kwambiri imene aliyense afunika kusankha ndi yokhudza kudzipereka kwa Yehova n’kukhala m’banja la anthu amene amamulambira. Yehova amafuna kuti munthu aliyense achite zimenezi. Chifukwa chiyani? Iye amafuna kuti akhale nawo pa ubwenzi komanso apeze moyo wosatha. (Deut. 30:19, 20; Agal. 6:7, 8) Koma Yehova sakakamiza anthu kuti azimutumikira. Amafuna kuti aliyense azisankha yekha zimene akufuna kuchita. Kodi chimachitika n’chiyani ngati Mkhristu wobatizidwa waphwanya lamulo la Mulungu n’kuchita tchimo lalikulu? Ngati sangalape, ayenera kuchotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:13) Komabe ngakhale zili choncho, Yehova amayembekezera kuti munthu amene wachita zoipayo adzabwerera kwa iye. Ndipotu n’chifukwa chake anapereka dipo kuti anthu ochimwa amene alapa azikhululukidwa. Mulungu wathu wachikondi amapempha anthu amene achita tchimo kuti alape.—Zek. 1:3; Aroma 2:4; Yak. 4:8. w24.08 14 ¶1-2
Lamlungu, April 19
Mtima wako ukakhala wanzeru, ndithu mtima wanga udzasangalala.—Miy. 23:15.
Pamene mtumwi Yohane ankalemba kalata yake yachitatu, anthu ena anali atayamba kufalitsa zinthu zabodza zimene zinachititsa kuti mumpingo anthu asamagwirizane. Koma ena anapitiriza ‘kuyendabe mʼchoonadi.’ Iwo ankamvera Yehova ndipo anapitiriza “kuyenda motsatira malamulo.” (2 Yoh. 4, 6) Akhristu okhulupirikawa anasangalatsa Yohane komanso Yehova. (Miy. 27:11) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kukhala okhulupirika kumachititsa kuti tizisangalala. (1 Yoh. 5:3) Mwachitsanzo, timakhala osangalala tikadziwa kuti tikusangalatsa Yehova. Iye amasangalala akaona tikukana mayesero n’kumatsatira mfundo za choonadi. Angelo nawonso amasangalala kumwamba. (Luka 15:10) Ifenso timasangalala tikamaona Akhristu anzathu akukhalabe okhulupirika (2 Ates. 1:4) Dzikoli likadzawonongedwa tidzasangalala podziwa kuti tinakhalabe okhulupirika kwa Yehova m’dziko lolamuliridwa ndi Satana. w24.11 12 ¶17-18
Lolemba, April 20
Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.—1 Akor. 10:24.
Kodi nthawi yomudziwa munthuyo iyenera kukhala yaitali bwanji musanamufunsire? Mukafulumira kufotokozera munthu maganizo anu, mudzaoneka ngati wopupuluma. (Miy. 29:20) Koma mukachedwanso mudzaoneka ngati munthu wozengereza makamaka ngati munthu winayo akudziwa kuti mukumufuna. (Mlal. 11:4) Kumbukirani kuti musanapite kukamufotokozera munthu maganizo anu, musamaganize kuti mulimonsemo akulolani basi. Muzingokhala wotsimikiza kuti mwakonzeka kulowa m’banja ndipo mukuona kuti munthu winayo akhoza kukhala wokuyenerani. Kodi mungatani ngati mwazindikira kuti munthu winawake akukufunani? Ngati munthuyo simukumufuna musamachite zinthu ngati mukumufuna. Si bwino kupangitsa munthu wina kuganiza kuti mukhoza kukhala naye pa chibwenzi pomwe sizili choncho.—Aef. 4:25. w24.05 22-23 ¶9-10
Lachiwiri, April 21
Ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu.—Yoh. 14:3.
Odzozedwa okhulupirika okha ndi amene ‘adzatengedwe’ kapena kuti kulandiridwa ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Wodzozedwa aliyense amene sadzapitiriza kukhalabe maso sadzatengedwa limodzi ndi “osankhidwa ake.” (Mat. 24:31) Komabe anthu a Mulungu onse, kaya ali ndi chiyembekezo chotani, ayenera kuona mawu a Yesu monga chenjezo lowathandiza kupitiriza kukhala maso komanso okhulupirika. Timamudziwa bwino Mulungu wathu, choncho sitikayikira zimene amasankha. Sitimakhumudwa ngati Yehova wasankha kudzoza anthu ena okhulupirika m’masiku athu ano. Timakumbukira fanizo la Yesu lonena za anthu omwe anabwera kudzagwira ntchito m’munda wampesa cha m’ma 5 koloko madzulo. (Mat. 20:1-16) Anthu omwe anaitanidwa kudzagwira ntchito m’munda wampesawo mochedwa, analandira ndalama zofanana ndi anthu omwe anayamba kugwira ntchitoyo m’mawa. Mofanana ndi zimenezi, kaya odzozedwa asankhidwa pa nthawi iti, iwo adzalandira mphoto yawo yakumwamba ngati atakhalabe okhulupirika. w24.09 24 ¶15-17
Lachitatu, April 22
Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.—1 Pet. 2:21.
Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino cha zomwe tingachite tikachitiridwa zopanda chilungamo. Taganizirani zimene iye anachitiridwa ndi achibale ake komanso anthu ena. Achibale ake ankanena kuti iye wachita misala. Atsogoleri achipembedzo ankati iye amachita zinthu mogwirizana ndi ziwanda. Nawonso asilikali a Chiroma anamunyoza ndi kumuchitira nkhanza mpaka anafika pomupha. (Maliko 3:21, 22; 14:55; 15:16-20, 35-37) Koma Yesu anapirira zonsezi ndipo sanabwezere. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chakechi? (1 Pet. 2:21-23) Yesu anatisiyira chitsanzo chosonyeza zimene tiyenera kuchita ena akatichitira zopanda chilungamo. Iye ankadziwa nthawi yoyenera kukhala chete komanso yoyenera kulankhula. (Mat. 26:62-64) Iye sankayankhapo pa bodza lililonse limene anthu ankamunenera. (Mat. 11:19) Akamalankhula, sankanyoza kapena kuopseza anthu amene ankamuimba mlandu. w24.11 4-5 ¶9-10
Lachinayi, April 23
Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa.—1 Tim. 1:15.
Tiyerekeze kuti mwapatsa munthu wina amene mumamukonda mphatso yokongola komanso yothandiza. Kodi mungamve bwanji ngati atangoiponya penapake osaiganiziranso? Kunena zoona, mukhoza kusangalala ngati atamaigwiritsa ntchito komanso kusonyeza kuyamikira. Mofanana ndi zimenezi, Yehova amasangalala tikamasonyeza kuti timayamikira mphatso ya dipo komanso chikondi chimene anatisonyeza potipatsa mphatso yamtengo wapataliyi. (Yoh. 3:16; Aroma 5:7, 8) Koma nthawi ikamapita, tikhoza kuyamba kuona mopepuka mphatso imeneyi. Zingakhale ngati tatenga mphatso ya Mulungu n’kungoiponya penapake. Zili ngati timasangalala nayo koma sitifuna kuti izikhala poonekera. Kuti zimenezi zisatichitikire tiyenera kumaganizira nthawi zonse zimene Mulungu ndi Khristu anatichitira. w25.01 26 ¶1-2
Lachisanu, April 24
Uziganizira mozama zinthu zimenezi ndipo uzizichita modzipereka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.—1 Tim. 4:15.
Kuti m’bale akhale mkulu, sayenera kukhala woti wangobatizidwa kumene. Ngakhale kuti sizidalira kuti munthu akhale woti anabatizidwa zaka zambiri m’mbuyomo, pamafunika nthawi ndithu kuti akule mwauzimu. Mofanana ndi Yesu, muyenera kukhala wodzichepetsa komanso kukhala wokonzeka kugwira ntchito iliyonse imene Yehova angakupatseni. (Mat. 20:23; Afil. 2:5-8) Mungasonyeze kuti ndinu “wokhulupirika” potsatira mfundo zolungama za Yehova komanso malangizo amene gulu limatipatsa. Malemba amanena momveka bwino kuti woyang’anira ayenera kukhala wodziwa kuphunzitsa. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti muyenera kukhala waluso kwambiri pokamba nkhani? Ayi. Akulu ambiri oyenerera, si aluso kwambiri pophunzitsa. Komabe amaphunzitsa mogwira mtima mu utumiki ndi pa maulendo aubusa. w24.11 23-24 ¶14-15
Loweruka, April 25
Ndimakonda malamulo anu kuposa golide, ngakhale golide wabwino kwambiri.—Sal. 119:127.
Mukapeza nkhani yomwe simukuimvetsa m’Baibulo, muzifufuza. Ndipo tsiku lonse muziganizira zimene mwaphunzira zokhudza Yehova, Mwana wake komanso mmene amakukonderani. (Sal. 119:97) Musamagwe ulesi ngati nthawi zina simukupeza mfundo zatsopano kapena zochititsa chidwi pamene mukuwerenga kapena kufufuza. Pa nthawiyi mumakhala ngati munthu amene akufufuza golide. Anthu omwe akufufuza golide amakhala maola mwinanso masiku asanapeze ngakhale kachidutswa ka golide. Iwo amalezabe mtima chifukwa amadziwa kuti kachidutswa kalikonse ka golide ndi kamtengo wapatali. Mofanana ndi zimenezi, mfundo iliyonse ya m’Baibulo imene mungapeze ndi yamtengo wapatali. (Miy. 8:10) Choncho muzileza mtima ndipo muzipitiriza kuwerenga Baibulo nthawi zonse.—Sal. 1:2. w25.01 25 ¶14-15
Lamlungu, April 26
Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.—Akol. 3:13.
Yehova amafuna kuti tizikhululukira anthu amene atilakwira. (Sal. 86:5; Luka 17:4; Aef. 4:32) Tingakhumudwe kwambiri chifukwa cha zimene wina walankhula kapena kuchita makamaka ngati munthuyo ndi mnzathu wapamtima kapena wachibale wathu. (Sal. 55:12-14) Nthawi zina ululu umene timamva umayerekezeredwa ndi kubayidwa ndi mpeni. (Miy. 12:18) Tingayesetse kunyalanyaza mmene tikumvera koma kuchita zimenezi kungafanane ndi kusiya mpeni pabala pomwepo. Mofanana ndi zimenezi, sitingayembekezere kuti tiyamba kumva bwino pongonyalanyaza mmene tikumvera. Chinthu choyamba chimene nthawi zambiri timachita munthu akatikhumudwitsa ndi kukwiya. Baibulo limavomereza kuti tingathe kukwiya. Koma limatichenjeza kuti tisamalole kuti mkwiyo uzitilamulira. (Sal. 4:4; Aef. 4:26) Chifukwa chiyani? Chifukwa kukwiya sikukhala ndi zotsatirapo zabwino. (Yak. 1:20) Kumbukirani kuti kukwiya kumangochitika kokha, koma timachita kusankha kuti tikhalebe okwiya. w25.02 15 ¶4-6
Lolemba, April 27
Nzeru zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeruzo.—Mlal. 7:12.
Yesu anasonyeza kuti si nzeru kukhala ndi ndalama popanda kukhala “wolemera kwa Mulungu.” (Luka 12:16-21) Pajatu amati zamawa sizidziwika. (Miy. 23:4, 5; Yak. 4:13-15) Akhristufe timakumananso ndi vuto lina. Yesu ananena kuti tiyenera kukhala okonzeka kusiya chuma chathu kuti tikhale ophunzira ake. (Luka 14:33) Akhristu a ku Yudeya analolera kusiya zinthu zawo ndipo sankadandaula. (Aheb. 10:34) Masiku anonso abale ndi alongo ambiri alolera kusiya zinthu zawo kapena ntchito n’cholinga choti asalowerere ndale. (Chiv. 13:16, 17) Kodi n’chiyani chinawathandiza kuchita zimenezo? Iwo amakhulupirira kwambiri lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Timayesetsa kukonzekera zam’tsogolo, koma tikakumana ndi mavuto amwadzidzidzi timakhulupirira kuti Yehova adzatithandiza. w25.03 29 ¶13-14
Lachiwiri, April 28
Popeza tamaliza kuphunzira mfundo zoyambirira zokhudza Khristu, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu. Tisayambe kuyalanso maziko.—Aheb. 6:1.
Yehova sayembekezera kuti tizikula tokha mwauzimu. Choncho watipatsa abusa ndi aphunzitsi mumpingo, omwe anaphunzitsidwa bwino kuti azithandiza munthu aliyense n’cholinga choti akhale ‘wachikulire’ mwauzimu n’kufika “pa msinkhu wa munthu wamkulu ngati mmene Khristu analili.” (Aef. 4:11-13) Yehova amatipatsanso mzimu woyera kuti uzitithandiza kukhala ndi “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:14-16) Komanso Mulungu anauzira anthu kuti alembe mabuku 4 a Uthenga Wabwino kuti atisonyeze mmene Yesu ankachitira zinthu ali padziko lapansi, mmene ankaganizira komanso mmene ankalankhulira. Tikamatsanzira kaganizidwe ka Yesu komanso mmene ankachitira zinthu, tingakhale Akhristu olimba mwauzimu. Koma kuti tikule mwauzimu tiyenera kuphunzira zambiri osati chabe “mfundo zoyambirira zokhudza Khristu.” Zimenezi ndi zina mwa mfundo zoyambirira zimene Akhristu amazikhulupirira. w24.04 4-5 ¶11-12
Lachitatu, April 29
Kuganiza bwino kudzakuyangʼanira, ndipo kuzindikira kudzakuteteza.—Miy.2:11.
Tsiku lililonse timafunika kusankha zochita. Zina zimakhala zosavuta monga kusankha zomwe tingadye m’mawa kapena nthawi imene tikufuna kukagona. Koma pali zina zomwe zimakhala zovuta chifukwa zimakhudza thanzi lathu, anthu amene timawakonda, kulambira kwathu komanso ngati tingakhale osangalala kapena ayi. Timafuna tizisankha zinthu zimene zingatithandize ifeyo komanso banja lathu. Koma chofunika kwambiri n’chakuti timafuna kuti zimene timasankha zizisangalatsa Yehova. (Aroma 12:1, 2) Chofunika kuti munthu asankhe bwino zochita ndi kudziwa mfundo zonse. N’chifukwa chiyani zimenezi ndi zofunika? Tiyerekeze kuti munthu ali ndi vuto lalikulu ndipo wapita kukakumana ndi dokotala. Kodi dokotalayo angapereke thandizo asanayeze kapena kufunsa mafunso wodwalayo? Ayi ndithu. Inunso musanasankhe zochita muzidziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo. w25.01 14 ¶1-3
Lachinayi, April 30
Yehova wakukhululukira tchimo lako ndipo suufa.—2 Sam. 12:13.
Kodi ndi zinthu ziti zomwe tikudziwa zokhudza chifundo cha Yehova? Nanga wasonyeza bwanji kuti “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe”? (2 Pet. 3:9) Taganizirani mmene anasonyezera chifundo kwa anthu ena amene anachita machimo akuluakulu. Mfumu Davide anachita machimo akuluakulu monga chigololo komanso kupha munthu. Koma Davide analapa ndipo Yehova anamuchitira chifundo n’kumukhululukira. (2 Sam. 12:1-12) Mfumu Manase anachita zinthu zoipa kwambiri kwa nthawi yaitali pa moyo wake. Ngakhale zinali choncho, Yehova anamuchitira chifundo n’kumukhululukira chifukwa chakuti analapa. (2 Mbiri 33:9-16) Zitsanzo zimenezi zikutikumbutsa kuti Yehova amasonyeza chifundo ngati pali zifukwa zosonyezera chifundocho. Iye adzaukitsa anthu ngati amenewa chifukwa chozindikira kuti anachita machimo akuluakulu ndipo analapa. w24.05 4 ¶12