Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es26 tsamba 26-36
  • March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • March
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
  • Timitu
  • Lamlungu, March 1
  • Lolemba, March 2
  • Lachiwiri, March 3
  • Lachitatu, March 4
  • Lachinayi, March 5
  • Lachisanu, March 6
  • Loweruka, March 7
  • Lamlungu, March 8
  • Lolemba, March 9
  • Lachiwiri, March 10
  • Lachitatu, March 11
  • Lachinayi, March 12
  • Lachisanu, March 13
  • Loweruka, March 14
  • Lamlungu, March 15
  • Lolemba, March 16
  • Lachiwiri, March 17
  • Lachitatu, March 18
  • Lachinayi, March 19
  • Lachisanu, March 20
  • Loweruka, March 21
  • Lamlungu, March 22
  • Lolemba, March 23
  • Lachiwiri, March 24
  • Lachitatu, March 25
  • Lachinayi, March 26
  • Lachisanu, March 27
  • Loweruka, March 28
  • Lamlungu, March 29
  • Lolemba, March 30
  • Lachiwiri, March 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
es26 tsamba 26-36

March

Lamlungu, March 1

Munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu wa machimo ake.—Aroma 6:7.

M’Baibulo timawerenga za anthu olungama amene anadzakhala osalungama. Chitsanzo ndi Mfumu Solomo. Iye anaphunzitsidwa bwino njira za Mulungu ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri, koma kenako anayamba kulambira milungu yabodza. Machimo ake anakwiyitsa kwambiri Yehova ndipo Aisiraeli anavutika ndi zotsatira zake kwa zaka zambiri. N’zoona kuti Malemba amanena kuti Solomo “anaikidwa m’manda” limodzi ndi makolo ake, kuphatikizapo Davide yemwe anali wokhulupirika. (1 Maf. 11:​5-9, 43; 2 Maf. 23:13) Kodi mmene anamuikira m’manda zikutanthauza kuti basi zivute zitani adzaukitsidwa? Baibulo silinena chilichonse. Kuukitsidwa ndi mphatso yomwe Mulungu wachikondi amapereka. Ndipo amaipereka kwa anthu omwe iye akufuna kuwapatsa mwayi womutumikira mpaka kalekale. (Yobu 14:​13, 14; Yoh. 6:44) Ndiye kodi Solomo adzalandira mphatso imeneyi? Yehova yekha ndi amene akudziwa. Koma chomwe ife tikudziwa n’choti Yehova adzachita zinthu mwachilungamo. w24.05 4 ¶9

Lolemba, March 2

Ndidzakhala mlendo mutenti yanu mpaka kalekale.—Sal. 61:4.

Kale, tenti inkakhala malo omwe munthu ankakhalamo kuti apume komanso atetezeke ku zinthu ngati mphepo, dzuwa komanso mvula. Tikadzipereka n’kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, timakhala alendo mutenti yake yophiphiritsa, timapeza chakudya chauzimu chokwanira komanso timakhala pa ubwenzi wabwino ndi ena omwe amakhalanso alendo a Yehova. Tenti ya Yehova sili kudera limodzi lokha. Imapezeka kulikonse komwe kuli atumiki ake okhulupirika. (Chiv. 21:3) Nanga bwanji za anthu okhulupirika omwe anamwalira? Kodi n’zomveka kunena kuti iwo adakali alendo mutenti ya Yehova? Inde. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Yehova amawakumbukirabe ndipo kwa iyeyo ndi amoyo. Yesu anafotokoza kuti: “Zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza munkhani ya chitsamba cha minga, pamene ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye onsewa ndi amoyo.”—Luka 20:​37, 38. w24.06 3 ¶6-7

Lachiwiri, March 3

Yehova ndi mphamvu yanga komanso chishango changa.—Sal. 28:7.

Zadoki anapita ku Heburoni atanyamula zida zake komanso ali wokonzeka kumenya nkhondo. (1 Mbiri 12:38) Iye anali wofunitsitsa kuthandiza Davide pa nkhondo yolimbana ndi adani a Isiraeli. Ngakhale kuti mwina Zadoki analibe luso lomenyera nkhondo, koma anali wolimba mtima. Kodi Zadoki, yemwe anali wansembe, anaphunzira kuti kukhala wolimba mtima? Iye ankakhala ndi anthu omwe anali amphamvu komanso olimba mtima. Ndipo zitsanzo zawo zinamuthandiza kwambiri. Mwachitsanzo, kulimba mtima kwa Davide pamene ‘ankatsogolera Aisiraeli kunkhondo,’ kunalimbikitsa Aisiraeli onse kuti akhale kumbali yake. (1 Mbiri 11:​1, 2) Nthawi zonse Davide ankadalira Yehova kuti amuthandize polimbana ndi adani ake. (Sal. 138:3.) Panali amuna enanso amene anathandiza Zadoki kukhala wolimba mtima. Mwachitsanzo, panali Yehoyada ndi mwana wake Benaya yemwe anali msilikali wamphamvu, ndiponso atsogoleri 22 omwe anali kumbali ya Davide.—1 Mbiri 11:​22-25; 12:​26-28. w24.07 3 ¶5-6

Lachitatu, March 4

Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, . . . nʼcholinga choti ulape.—Aroma 2:4.

Saulo wa ku Tariso anachita zoipa zambiri ndipo ankafunika kulapa kuti akhululukidwe. Iye ankazunza mwankhaza otsatira a Khristu. Akhristu ambiri ayenera ankaganiza kuti iye sangalape n’kusintha. Koma Yesu ankadziwa kuti Saulo akhoza kusintha. Iye ndi Atate wake ankaona makhalidwe abwino omwe Saulo anali nawo. Yesu anati: “Munthu ameneyu ndi chiwiya changa chosankhidwa.” (Mac. 9:15) Yesu anafika pochita zodabwitsa pofuna kuthandiza Saulo kuti alape. (Mac. 7:58–8:3; 9:​1-9, 17-20) Atakhala Mkhristu, nthawi zambiri Saulo, yemwe pambuyo pake ankadziwika kuti mtumwi Paulo, ankayamikira mmene Yehova ndi Yesu anamusonyezera chifundo ndi kukoma mtima. (1 Tim. 1:​12-15) Kodi Paulo anachita chiyani atamva za tchimo lina lachigololo lomwe linachitika mumpingo wa ku Korinto? Iye anasamalira nkhaniyi m’njira imene imatiphunzitsa kufunika kosonyeza chifundo komanso kuti Yehova amatilangiza mwachikondi tikachimwa. w24.08 13 ¶15-16

Lachinayi, March 5

Nʼchifukwa chake Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.—1 Yoh. 3:8.

Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akufotokoza momveka bwino zimene zingathandize anthu ochimwa kuti akhalenso naye pa ubwenzi. Abele yemwe anali mwana wachiwiri wa Adamu ndi Hava anali munthu woyamba kukhulupirira Yehova pambuyo poti makolo ake achimwa. Chifukwa chakuti Abele ankakonda Yehova komanso ankafuna kumusangalatsa ndi kukhala naye pa ubwenzi, anapereka nsembe. Abele anali m’busa choncho anatenga ena mwa ana ankhosa zake n’kuwapereka nsembe. Yehova “anasangalala ndi Abele komanso nsembe yake.” (Gen. 4:4) Yehova anasonyeza kuti ankasangalala ndi nsembe zimene anthu enanso omwe ankamukonda ndi kumukhulupirira monga Nowa ankapereka. (Gen. 8:​20, 21) Povomereza nsembe zimenezi, Yehova anasonyeza kuti anthu ochimwa angathe kukhalanso naye pa ubwenzi komanso kuti iye angathe kumasangalala nawo. w24.08 3 ¶5-6

Lachisanu, March 6

Mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera, mapazi anga anangotsala pangʼono kuterereka.—Sal. 73:2.

Ngati ena atichitira zopanda chilungamo, zingatipweteke kwambiri ndipo tingakhumudwe. (Mlal. 7:7) Atumiki okhulupirika monga Yobu ndi Habakuku anamvanso choncho. (Yobu 6:​2, 3; Hab. 1:​1-3) Ngakhale kuti mwachibadwa zingatipweteke, tiyenera kukhala osamala kuti tisachite zinthu mopanda nzeru, zomwe zingangochititsa kuti zinthu zifike poipa kwambiri. Tikamaona anthu omwe akuchita zopanda chilungamo zinthu zikuwayendera bwino, tingayambe kumaganiza kuti kuchita zoyenera n’kosathandiza. Chitsanzo ndi wolemba masalimo wina yemwe ankaona ngati anthu oipa zinthu zikuwayendera bwino kusiyana ndi olungama. Iye anati: “Izi nʼzimene oipa amachita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.” (Sal. 73:12) Iye anakhumudwanso kwambiri ndi zopanda chilungamo zomwe anaona moti anayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kunali kothandiza. Iye anati: “Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi, zinali zopweteka kwa ine.”—Sal. 73:​14, 16. w24.11 3 ¶5-7

Loweruka, March 7

Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu mabanja a mitundu ya anthu, mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.—Sal. 96:7.

Timapereka ulemerero kwa Yehova chifukwa chakuti timamulemekeza kwambiri. Tili ndi zifukwa zambiri zomulemekezera. Yehova ndi wamphamvu yonse, kutanthauza kuti ali ndi mphamvu zopanda malire. (Sal. 96:​4-7) Timaona nzeru zake mu zinthu zimene analenga. Ndi amene anatipatsa moyo komanso zonse zimene zimatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo. (Chiv. 4:11) Yehova ndi wokhulupirikanso. (Chiv. 15:4) Chilichonse chimene amachita chimayenda bwino ndipo nthawi zonse amakwaniritsa zimene walonjeza. (Yos. 23:14) N’zomveka kuti mneneri Yeremiya anafotokoza za Yehova kuti: “Pakati pa anzeru onse a m’mitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse, palibiretu aliyense wofanana ndi inu.” (Yer. 10:​6, 7) Choncho tili ndi zifukwa zabwino zolemekezera Atate wathu wakumwamba. Sikuti timangolemekeza Yehova, koma timamukondanso kwambiri. Ndipo koposa zonse, timapereka ulemerero kwa Yehova chifukwa timamukonda kwambiri. w25.01 3 ¶5-6

Lamlungu, March 8

Mʼchotseni munthu woipayo pakati panu.—1 Akor. 5:13.

Adani a Mulungu amafuna kuti zinthu zabwino zimene gulu la Mulungu limachita zizioneka ngati zoipa. Mwachitsanzo, timaphunzira kuchokera m’Malemba kuti Yehova amafuna kuti anthu amene amamulambira azikhala aukhondo, amakhalidwe abwino komanso azimulambira m’njira imene amavomereza. Iye amafuna kuti munthu amene amachita makhalidwe oipa ndipo salapa azichotsedwa mumpingo. (1 Akor. 5:​11, 12; 6:​9, 10) Ifeyo timayesetsa kutsatira lamulo la m’Malemba limeneli. Koma adani athu amagwiritsa ntchito zimenezi pofuna kutinena kuti si ife ololera, timaweruza anzathu komanso tilibe chikondi. Tizikumbukira kuti amene akutitsutsa ndi Satana. Satana Mdyerekezi ndi amene amayambitsa nkhani zabodza. Iye ndi “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44; Gen. 3:​1-5) Choncho tisamadabwe kuti Satana amagwiritsa ntchito anthu ake pofalitsa nkhani zabodza zokhudza gulu la Yehova. w24.04 10-11 ¶13-14

Lolemba, March 9

Adzakwaniritsidwa ndithu.—Ezek. 33:33.

Ngakhale chisautso chachikulu chikadzayamba, n’kutheka kuti ena omwe adzaone kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu” adzakumbukira kuti a Mboni za Yehova ananenapo za zinthu zimenezi. Ndiye kodi ena amene adzaone zimenezi adzasintha mitima yawo? (Chiv. 17:5) Zimenezi zingadzakhale zofanana ndi zimene zinachitika ku Iguputo m’nthawi ya Mose. Kumbukirani kuti “gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana” linachoka ku Iguputo limodzi ndi Aisiraeli. N’kutheka kuti ena mwa anthu amenewa anayamba kukhulupirira Yehova ataona kuti zimene Mose anachenjeza zokhudza miliri 10 zikuchitika. (Eks. 12:38) Ngati zimenezi zitadzachitika Babulo Wamkulu atawonongedwa, kodi tidzakhumudwa poona kuti anthu ayamba kutumikira Mulungu kutangotsala nthawi yochepa kuti mapeto afike? Ayi ndithu. Timafuna kutsanzira Atate wathu wakumwamba yemwe ndi “wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi.”—Eks. 34:6. w24.05 11 ¶12-13

Lachiwiri, March 10

Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola.—2 Tim. 1:13.

Kodi n’chiyani chingachitike ngati titasiya kutsatira “chitsanzo cha mawu olondola”? Taganizirani chitsanzo ichi. M’nthawi ya atumwi Akhristu ena ankafalitsa mphekesera yakuti tsiku la Yehova linali litafika. N’kutheka kuti panali kalata imene inanena zimenezi ndipo anthu ankaganiza kuti inalembedwa ndi Paulo. Akhristu ena a ku Tesalonika anayamba kukhulupirira komanso kufalitsa zimenezi asanafufuze. Iwo sakanapusitsidwa zikanakhala kuti anakumbukira zimene Paulo anawaphunzitsa pa nthawi imene anali nawo limodzi. (2 Ates. 2:​1-5) Iye analangiza abale akewo kuti asamangokhulupirira zilizonse zimene amva. Pofuna kuwathandiza kuti izi zisadzawachitikirenso m’tsogolo, Paulo anamaliza kalata yake yachiwiri yopita kwa Atesalonika ndi mawu akuti: “Landirani moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba ndi dzanja langa. Nthawi zonse ndimalemba chonchi mʼmakalata anga onse, kuti mudziwe kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene ndimalembera.”—2 Ates. 3:17. w24.07 12 ¶13-14

Lachitatu, March 11

Mukufunika kukhala opirira.—Aheb. 10:36.

Akhristu a Chiheberi ankafunika kupirira mayesero pamene zinthu zinkaipiraipira ku Yudeya. Ngakhale kuti Akhristu ena anazunzidwa m’mbuyomo, ambiri anakhala Akhristu pa nthawi imene kunali kamtendere. Mtumwi Paulo ananena kuti ngakhale kuti iwo anapirira mayesero ovuta, sanapirire ngati Yesu yemwe anafika pophedwa. (Aheb. 12:4) Chifukwa chakuti anthu ambiri ankalowa Chikhristu, Ayuda otsutsa anayamba kukwiya kwambiri komanso kuwazunza. Zaka zochepa m’mbuyomo, Ayuda oposa 40 ‘analumbira pochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atapha Paulo.’ (Mac. 22:22; 23:​12-14) Ngakhale kuti ankadedwa komanso kuzunzidwa, Akhristuwo ankafunika kumasonkhana, kulalikira uthenga wabwino komanso kumalimbitsa chikhulupiriro chawo. w24.09 12 ¶15

Lachinayi, March 12

[Yesu] anauza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.”—Yoh. 19:26.

Yohane anali mtumwi amene Yesu ankamukonda kwambiri. (Mat. 10:2) Iye anayenda ndi Yesu pa utumiki wake, anaona zodabwitsa zimene ankachita ndipo anali naye pa nthawi yovuta kwambiri. Analiponso pamene ankaphedwa ndipo anamuona ataukitsidwa. Anaonanso pamene mpingo wa Chikhristu unkakula mpaka pamene uthenga wabwino “unalalikidwa padziko lonse.” (Akol. 1:23) Chakumapeto kwa moyo wake, Yohane anali ndi mwayi wolemba nawo Mawu ouziridwa a Mulungu. Iye analemba zinthu zochititsa chidwi zopezeka mu “chivumbulutso chimene Yesu Khristu anapereka.” (Chiv. 1:1) Yohane analembanso buku la Uthenga Wabwino lomwe limadziwika ndi dzina lake. Iye analembanso makalata atatu ouziridwa. Kalata yachitatu inali yopita kwa Mkhristu wina wokhulupirika dzina lake Gayo, yemwe ankamuona ngati mwana wake. (3 Yoh. 1) Zimene wachikulire wokhulupirikayu analemba, zakhala zikulimbikitsa otsatira onse a Yesu mpaka pano. w24.11 12 ¶15-16

Lachisanu, March 13

Inunso amuna, . . . muziwapatsa ulemu.—1 Pet. 3:7.

Mwamuna amene amakonda mkazi wake amaona kuti iye ndi wamtengo wapatali. Amamuona kuti ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. (Miy. 18:22; 31:10) Choncho amachita naye zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu ngakhale pa nkhani yokhudza kugonana. Iye sakakamiza mkazi wake kuti azigonana m’njira imene ingachititse kuti asamamve bwino, azidzimva kuti ndi wachabechabe kapenanso chikumbumtima chake chizimuvutitsa. Mwamunayo amayesetsanso kuti azichita zinthu zimene zingathandize kuti akhale ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Yehova. (Mac. 24:16.) Amuna, dziwani kuti Yehova amaona komanso kuyamikira zimene mumachita polemekeza mkazi wanu. Pitirizani kulemekeza mkazi wanu popewa khalidwe loipa komanso popitiriza kuchita naye zinthu mokoma mtima, mwaulemu ndiponso mwachikondi. Mukamachita zimenezo mudzasonyeza kuti mumamukonda komanso ndi wamtengo wapatali. Mukamalemekeza mkazi wanu, mudzateteza chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanu, chomwe ndi ubwenzi wanu ndi Yehova.—Sal. 25:14. w25.01 13 ¶17-18

Loweruka, March 14

Anadzipereka m’malo mwa ife kuti atilanditse . . . ndiponso kuti atiyeretse, kuti tikhale anthu ake apadera, odzipereka pa ntchito zabwino.—Tito 2:14.

Chinthu chimodzi chomwe chimasiyanitsa atumiki a Yehova ndi anthu ena omwe amati ndi Akhristu, ndi khama limene amachita pa ntchito yolalikira. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tipitirize kukonda ntchito yolalikira komanso kumaigwira mwakhama? Kuganizira chitsanzo cha Yesu kungatithandize kwambiri. Ali padziko lapansi iye sanasiyepo kugwira mwakhama ntchitoyi. Ndipotu anapitiriza kuchita khama mpaka kumapeto kwa utumiki wake. Yesu anali ngati wosamalira munda wa mpesa amene ankasamalira mtengo wa mkuyu kwa zaka zitatu koma sunkabala zipatso. Yesu analalikira kwa Ayuda kwa zaka pafupifupi zitatu ndipo ambiri mwa iwo sankamvetsera uthenga wake. Komabe Yesu sanasiye kuwalalikira. Iye anachita mofanana ndi wosamalira munda uja yemwe sanasiye kusamalira mtengowo, akumayembekezera kuti udzabereka. (Luka 13:​6-9) Kukambirana zimene Yesu anaphunzitsa komanso kuchita, kungatithandize kuti nafenso tipitirize kuchita khama masiku ano. w25.03 14-15 ¶1-4

Lamlungu, March 15

Munthu wochenjera amadziwa zimene akuchita.—Miy. 13:16.

Kodi muzitani ngati mwaona kuti munthu winawake ndi wokuyenererani? Kodi ndi bwino kumuuza nthawi yomweyo mmene mukumvera? Baibulo limanena kuti munthu wanzeru amayamba wadziwa bwino zimene akuchita. Choncho ndi bwino kudzipatsa nthawi yoti mumudziwe bwino iyeyo asakudziwa, musanamufotokozere maganizo anu. Kodi mungachite bwanji zinthu mosamala pamene mukufuna kumudziwa bwino munthu wina? Pamisonkhano yampingo kapena pocheza pagulu, mukhoza kuona mmene munthuyo amakondera Yehova, khalidwe lake komanso mmene amachitira zinthu. Kodi amacheza ndi anthu ati, nanga amakonda kukamba nkhani zotani? (Luka 6:45) Kodi zolinga zake zikufanana ndi zanu? Mungathenso kufunsa akulu mumpingo wake kapena Akhristu ena olimba mwauzimu amene akumudziwa bwino. (Miy. 20:18) Mungawafunse za mbiri yake komanso makhalidwe ake. (Rute 2:11) Pamene mukufuna kumudziwa bwino munthu, muyenera kusamala kuti musakhale ngati mukumulondalonda. Muzilemekeza maganizo ake, musamamupanikize ndipo musamayese kufufuza chilichonse chokhudza iyeyo. w24.05 22 ¶7-8

Lolemba, March 16

Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu.—Sal. 32:5.

Akulu safulumira kuganiza kuti munthu yemwe wachita tchimo sangalape. Anthu ena akhoza kusonyeza mtima wolapa pa nthawi yoyamba yomwe akumana ndi komiti pomwe ena angatenge nthawi. Choncho akulu amakonza kuti akumane ndi munthu wochimwayo maulendo angapo. N’kutheka kuti pambuyo pokumana naye pa ulendo woyamba, Mkhristu yemwe wachita tchimoyo akhoza kuganizira zomwe wauzidwa komanso kupemphera kwa Yehova modzichepetsa. (Sal. 38:18) Ndipo pa ulendo wotsatira, akhoza kukhala ndi maganizo osiyana ndi omwe anali nawo poyamba. Akulu amasonyeza chifundo ndi kukoma mtima kuti athandize munthu wochimwa kuti alape. Iwo amapemphera kwa Yehova ndipo amakhala ndi chiyembekezo kuti iye adalitsa khama lawo pothandiza Mkhristuyo kuti azindikire zomwe walakwitsa ndi kulapa.—2 Tim. 2:​25, 26. w24.08 22-23 ¶12-13

Lachiwiri, March 17

“Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. “Choncho siyani kuchita zoipa kuti mupitirize kukhala ndi moyo.”—Ezek. 18:32.

Yehova safuna kuti aliyense adzawonongedwe. Koma amafuna kuti anthu ochimwa abwerere kwa iye. (2 Akor. 5:20) N’chifukwa chake kwa nthawi yaitali komanso mobwerezabwereza Yehova wakhala akuuza anthu ake monga gulu komanso aliyense payekhapayekha kuti alape ndi kubwerera kwa iye. Akulu amagwira ntchito ndi Yehova pothandiza anthu omwe achita machimo kuti alape. (Aroma 2:4; 1 Akor. 3:9) Kumwamba kumakhala chisangalalo chachikulu wochimwa akalapa. Atate wathu wakumwamba Yehova amasangalalanso kwambiri nkhosa yosochera ikabwerera mumpingo. Timakonda kwambiri Yehova tikaganizira za chifundo chake komanso kukoma mtima kwake kwakukulu.—Luka 1:78. w24.08 31 ¶16-17

Lachitatu, March 18

Yesu atadziwa kuti anthu akufuna kubwera kudzamugwira kuti amuveke ufumu, anachoka nʼkupitanso kuphiri yekhayekha.—Yoh. 6:15.

Yesu akanalola kuti anthu amuveke ufumu, akanalowerera ndale za Ayuda omwe ankalamuliridwa ndi Aroma. Baibulo limanena kuti iye ‘anachoka nʼkupita kuphiri.’ Iye sanayambe kulowerera ndale ngakhale kuti anthu ena ankamukakamiza. Apatu iye anapereka chitsanzo chabwino kwa ifeyo. N’zoonekeratu kuti ena sangatiuze kuti tichulukitse chakudya kapena kuchiritsa anthu modabwitsa. Sangatiuzenso kuti tikhale mfumu kapena wolamulira. Komabe angatilimbikitse kuti tichite nawo zandale povota kapena kuthandiza winawake yemwe akuona kuti angasinthe zinthu. Koma Yesu ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye anakana kulowerera ndale ndipo pa nthawi ina ananena kuti, “Ufumu wanga si wamʼdzikoli.” (Yoh. 17:14; 18:36) Masiku ano, Akhristu ayenera kutsanzira Yesu. Mofanana ndi Yesu, timakhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu, timauza ena za Ufumuwu ndipo timaupempherera. w24.12 4 ¶5-6

Lachinayi, March 19

Aliyense amene ali ndi malamulo anga ndipo amawatsatira, ndi amene amandikonda. Komanso amene amandikonda, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.—Yoh. 14:21.

Mukamaphunzira, muziganizira mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzirazo. Mwachitsanzo, muzitsanzira chilungamo cha Yehova pochita zinthu mopanda tsankho ndi anthu ena. Muzitsanzira mmene Yesu ankakondera Atate wake ndi anthu ena pokhala wofunitsitsa kuchita zimene Yehova amafuna komanso kuthandiza anthu ena ngakhale pamene kuchita zimenezo kuli kovuta. Muzitsanziranso Yesu polalikira kwa ena n’cholinga choti nawonso akhale ndi mwayi wolandira mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. Tikamayesetsa kumvetsa komanso kuyamikira dipo, m’pamenenso timakonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake. Zotsatira zake n’zakuti iwonso adzayamba kutikonda kwambiri. (Yak. 4:8) Choncho tiyeni tipitirize kugwiritsa ntchito zonse zimene Yehova watipatsa kuti tiphunzire zokhudza dipo. w25.01 25 ¶16-17

Lachisanu, March 20

Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.—Yes. 38:17.

Mawu a mulemba lalerowa, angatanthauzenso kuti: “Mwachotsa machimo anga onse kuti musawaonenso.” Mawuwa akusonyeza kuti Yehova amachotsa machimo a munthu amene walapa n’kukawataya kumalo amene sangawaonenso. Mawuwa angafotokozedwenso kuti: “Mwachititsa kuti [machimo anga] akhale ngati sanachitike n’komwe. Baibulo limapitiriza kufotokoza mfundoyi ndi mawu ena a fanizo opezeka pa Mika 7:​18, 19. Mavesiwa amafotokoza ngati kuti Yehova akuponya machimo athu m’nyanja pamalo ozama. Mosiyana ndi masiku ano, kale chinthu chikaponyedwa m’nyanja pamalo ozama sizinkatheka kuti munthu akachitengenso. Mafanizowa akutithandiza kuona kuti Yehova akatikhululukira, timapepukidwa ku machimo athu. Monga mmene Davide ananenera, “osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.” (Aroma 4:7) Kumeneku ndiye kukhululuka ndi mtima wonse. w25.02 9 ¶7-8

Loweruka, March 21

Kondwerani ndipo muzisangalala mpaka kalekale ndi zimene ndikulenga.—Yes. 65:18.

Masiku ano padzikoli pali paradaiso yemwe muli anthu ambiri omwe atanganidwa ndi kuchita zinthu zabwino. M’paradaisoyu muli anthu mamiliyoni ambiri omwe ali pamtendere weniweni. Anthu amene ali m’paradaisoyu safuna kuchokamo. Iwo akufuna kuti anthu enanso ambiri alowemo. Ameneyutu ndi paradaiso wauzimu. N’zochititsa chidwi kuti Yehova wakonza paradaiso wabata ameneyu m’dziko limene Satana wachititsa kuti pakhale chidani komanso muli anthu oipa ndi oopsa. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Mulungu wathu wachikondi amadziwa mavuto omwe ali m’dzikoli ndipo amatiteteza kuti tipitirize kumutumikira mosangalala. Mawu ake amafotokoza kuti paradaiso wauzimuyu ndi “malo othawirako” otetezeka komanso ali ngati “dimba lothiriridwa bwino.” (Yes. 4:6; 58:11) Mothandizidwa ndi Yehova, anthu omwe ali m’paradaisoyu amakhala osangalala komanso amadzimva kuti ndi otetezeka m’masiku otsiriza ovutawa.—Yes. 54:14; 2 Tim. 3:1. w24.04 20 ¶1-2

Lamlungu, March 22

Nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu.—Afil. 4:6.

Ngati mukufuna kulowa m’banja, n’zosachita kufunsa kuti mwapemphera kuti mupeze munthu woyenera. N’zoona kuti Yehova sakulonjeza kuti azipatsa munthu aliyense mnzake womuyenerera. Koma iye amaganizira zimene mumafuna komanso mmene mumamvera ndipo angakuthandizeni pamene mukufufuza munthu woti mukwatirane naye. Choncho pitirizani kumufotokozera zimene mukufuna komanso mmene mukumvera mumtima mwanu. (Sal. 62:8) Muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala woleza mtima komanso akupatseni nzeru. (Yak. 1:5) Ngakhale pamene mwamuna kapena mkazi woyenerera sakupezeka mwamsanga, Yehova akulonjeza kuti apitiriza kukukondani komanso kukusamalirani. (Sal. 55:22) Komabe muyenera kukhala osamala kuti nkhani yofufuza mwamuna kapena mkaziyi, isakhale yofunika kwambiri pa moyo wanu. (Afil. 1:10) Kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kumene kungakuthandizeni kukhala wosangalala kwambiri osati kukhala pa banja. (Mat. 5:3) Ndipotu pa nthawi imene simuli pa banja mungakhale ndi ufulu wochita zambiri mu utumiki. (1 Akor. 7:​32, 33) Muziigwiritsa ntchito bwino nthawi imeneyi. w24.05 21 ¶4; 22 ¶6

Lolemba, March 23

Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.—Afil. 2:4.

Kodi muyenera kukhala pa chibwenzi kwa nthawi yaitali bwanji? Kuchita zinthu mopupuluma nthawi zambiri kumabweretsa mavuto. (Miy. 21:5) Choncho muyenera kukhala pa chibwenzi kwa nthawi yokwanira kuti mudziwe bwino mnzanuyo. Komabe si bwino kukhala pa chibwenzi kwa nthawi yaitali popanda zifukwa zomveka. Baibulo limati: “Chinthu chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala.” (Miy. 13:12) Kodi anthu ena angathandize bwanji anthu omwe ali pa chibwenzi? Tikhoza kuwaitana kuti adzadye nafe chakudya, adzachite nafe kulambira kwa pa banja kapena adzachite nafe zosangalatsa zina. (Aroma 12:13) Kodi akufunika wowaperekeza, kuwathandiza pa nkhani ya mayendedwe kapena malo abwino omwe angakakambirane zinthu zina? Ngati ndi choncho, kodi tingawathandize pa zinthu zimenezi? (Agal. 6:10) Ngati mwapemphedwa kuti muperekeze anthu omwe ali pa chibwenzi, muziona kuti umenewo ndi mwayi woti muthandize anzanuwo. Muzionetsetsa kuti simukuwasiya okhaokha komabe muziwapatsanso mpata woti alankhulane nkhani zawo. w24.05 30 ¶13-14

Lachiwiri, March 24

Ndamupatsa nthawi kuti alape.—Chiv. 2:21.

Akulu amafufuza kuti adziwe zimene zinachititsa kuti munthu achite tchimo. Mwachitsanzo, kodi Mkhristuyo anafooka chifukwa choti anasiya kuphunzira Baibulo payekha kapena kulowa mu utumiki? Kodi sapemphera kawirikawiri kapena amangopemphera mwamwambo? Kodi wakhala akungotengeka ndi zimene amalakalaka? Kodi wakhala akusankha molakwika anthu ocheza nawo kapena zosangalatsa? Kodi zimene amasankhazo zakhudza bwanji mtima wake? Kodi akudziwa mmene zochita zake zakhala zikukhudzira Atate wake Yehova? Akulu akamafunsa mafunso mwanzeru, amathandiza munthu yemwe wachita tchimoyo kuti amasuke ndiponso aganizire zomwe wakhala akuchita. (Miy. 20:5) Iwo akhoza kugwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuthandiza wochimwayo kuti aganizire zimene analakwitsa. Mwina pa ulendo woyamba womwewo munthuyo akhoza kuyamba kumva chisoni ndi zimene wakhala akuchita ndipo akhoza kulapa. w24.08 22 ¶9-11

Lachitatu, March 25

Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.—Luka 4:43.

Yesu ankalalikira mwakhama “uthenga wabwino wa Ufumu” chifukwa ankadziwa kuti ndi zimene Mulungu ankafuna kuti iye achite. Iye ankaona kuti ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri pa moyo wake. Ngakhale chakumapeto kwa utumiki wake, iye ankayenda “mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi” kuphunzitsa anthu. (Luka 13:22) Anaphunzitsanso ophunzira ambiri kuti azigwira nawo ntchito yolalikira. (Luka 10:1) Masiku anonso kulalikira uthenga wabwino ndi ntchito yaikulu imene Yehova ndi Yesu amafuna kuti tizigwira. (Mat. 24:14; 28:​19, 20) Tingapitirize kuchita khama pa utumiki wathu tikamaona anthu ngati mmene Yehova amawaonera. Iye amafuna kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino n’kukhala atumiki ake. (1 Tim. 2:​3, 4) Choncho amatiphunzitsa mmene tingagwirire bwino ntchito yopulumutsa moyoyi. Ngakhale anthu asamvetsere uthenga wathu panopo, mwina angadzakhale ndi mwayi wophunzira za Yehova mkati mwa chisautso chachikulu mapeto asanafike. w25.03 15-16 ¶5-7

Lachinayi, March 26

Aliyense amene wamupatsa moni amakhala ngati akuchita nawo ntchito zake zoipazo.—2 Yoh. 11.

Mkhristu aliyense akhoza kuchita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake pochita zinthu ndi wochotsedwa. Ena angasankhe kumupatsa moni kapena kumulandira kumisonkhano. Komabe sitingalankhule naye kwambiri kapena kucheza naye. Ena akhoza kufunsa kuti, ‘Kodi si paja Baibulo limanena kuti munthu akapereka moni kwa wochotsedwa amakhala ngati akuchita nawo ntchito zake zoipazo?’ (2 Yoh. 9, 11) Nkhani yonse palembali imasonyeza kuti malangizowa ankanena za anthu ampatuko kapena amene amalimbikitsa makhalidwe oipa. (Chiv. 2:20) Choncho ngati munthu amalimbikitsa mpatuko kapena makhalidwe oipa, akulu sangakonze zomuyendera. Komabe pamakhala chiyembekezo chakuti iye angadzasinthe maganizo. Podikira nthawi imene adzasintheyo, munthu wotereyu sitimupatsa moni kapena kumuitanira kumisonkhano. w24.08 30-31 ¶14-15

Lachisanu, March 27

Iwo ankavutikabe kuti amvetse zinthu zonse.—Maliko 6:52.

Yesu atadyetsa gulu la anthu, anauza atumwi ake kuti abwerere ku Kaperenao pa boti ndipo iye anapita kuphiri pofuna kupewa gulu la anthu omwe amafuna kumuveka ufumu. (Yoh. 6:​16-20) Atumwiwo ali panyanja mphepo inayamba ndipo panali mafunde aakulu. Kenako Yesu anabwera akuyenda pamadzi. Ndipo anaitana Petulo kuti nayenso ayende pamadzipo. (Mat. 14:​22-31) Yesu atangofika m’botilo mphepo ija inasiya. Zitatero ophunzirawo anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” (Mat. 14:33) N’zochititsa chidwi kuti iwo ananena zimenezi pambuyo poti Yesu wayenda pamadzi ngakhale kuti anali atachita chodabwitsa podyetsa gulu la anthu lija. Maliko anawonjezeranso mfundo yakuti: “[Atumwiwo] anadabwa kwambiri. Chifukwa choti sanamvetse tanthauzo la mitanda ya mkate ija.” (Maliko 6:​50-52) Iwo anali asanazindikirebe kuti Yehova anali atapatsa Yesu mphamvu zochitira zodabwitsa zambiri. w24.12 5 ¶7

Loweruka, March 28

[Mulungu] amafuna kuti anthu osiyanasiyana apulumuke nʼkukhala odziwa choonadi molondola.—1 Tim. 2:4.

Tingasonyeze kuyamikira chikondi cha Yehova pogwiritsa ntchito bwino nyengo ya Chikumbutso. Kuwonjezera pa kukonzekera kuti tidzapezekepo, tingaitanirenso anthu ena. Poitana anthuwo tingachite bwino kuwauza zimene zikachitike pamwambowo. Tingachitenso bwino kuwaonetsa mavidiyo a pa jw.org monga akuti N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa? komanso Tizikumbukira Imfa ya Yesu. Akulu ayeneranso kuitana anthu amene anafooka. Kumwamba kungakhale chisangalalo chachikulu kwambiri ngati nkhosa imodzi yotayika itabwerera m’gulu. (Luka 15:​4-7) Pa tsiku la Chikumbutso, tidzayesetse kupereka moni kwa abale ndi alongo, koma makamaka atsopano ndi amene anasiya kusonkhana. Tiyeni tidzawachititse kuti akhale omasuka.—Aroma 12:13. w25.01 29 ¶15

Lamlungu, March 29

Mulungu anatumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu . . . chifukwa chakuti anatikonda.—1 Yoh. 4:10.

N’zoona kuti dipo limatithandiza kumvetsa kuti Yehova ndi wachilungamo, koma kwenikweni limatithandizanso kudziwa kuti iye amatikonda kwambiri. (Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:​9, 10) Zimene timaphunzira zokhudza dipo, zimasonyeza kuti Yehova samangofuna kuti tikhale ndi moyo wosatha, koma amafunanso kuti tikhale m’banja lake. Taganizirani izi: Adamu atachimwa, Yehova sanamulolenso kuti akhale m’banja lake. Choncho tonsefe tinabadwira kunja kwa banja la Mulungu. Koma chifukwa cha dipo, Yehova amatikhululukira machimo athu ndipo pa nthawi yake adzabwezeretsa m’banja lake onse omwe amamukhulupirira komanso kumumvera. Ngakhale panopa, tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso Akhristu anzathu. Kunena zoona, Yehova amatikonda kwambiri.—Aroma 5:​10, 11. w25.01 21 ¶6

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 9 kutacha) Yohane 12:​12-19; Maliko 11:​1-11

Lolemba, March 30

Zimene Mulungu anachita potisonyeza chikondi chake.—1 Yoh. 4:9.

Mungavomereze kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. (2 Akor. 9:15) Chifukwa chakuti Yesu anapereka moyo wake, mukhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu. Mungakhalenso ndi chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Mpake kuti tiyenera kumayamikira Yehova potipatsa dipo chifukwa chakuti amatikonda. (Aroma 5:8) Pofuna kutithandiza kuti tiziyamikira dipo komanso kuti tisamalione mopepuka, Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake. (Luka 22:​19, 20) Chaka chino, mwambo wa Chikumbutso udzachitika Lachinayi pa 2 April 2026. Mosakayikira, tonsefe tikukonza zoti tidzapezekepo. Pa nyengo ya Chikumbutsoyi, tidzapindula kwambiri tikamaganizira zimene Yehova ndi Mwana wake anatichitira. w25.01 20 ¶1-2

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 10 kutacha) Yohane 12:​20-50

Lachiwiri, March 31

Landirani malangizo anga osati siliva, komanso kudziwa zinthu mʼmalo mwa golide woyenga bwino kwambiri.—Miy. 8:10.

Mungaphunzire zambiri zokhudza chikondi cha Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu mukamapitiriza kuganizira zimene anakuchitirani. Mwina pa nyengo ya Chikumbutso ya chaka chino mungawerenge mosamala buku limodzi kapena angapo a Uthenga Wabwino. Musamawerenge machaputala ambiri pa nthawi imodzi. Koma muziwerenga pang’onopang’ono ndipo muzifufuza zifukwa zina zomwe zingakuchititseni kuti muzikonda Yehova ndi Yesu. Ngati mwakhala m’choonadi kwa zaka zambiri mwina mungaone kuti simungapeze mfundo zina zatsopano zokhudza chilungamo cha Mulungu, chikondi chake komanso dipo. Koma zoona n’zakuti sitidzamaliza kuphunzira zokhudza nkhani zimenezi ndi zinanso. Choncho muziwerenga komanso kuphunzira nkhani za m’Baibulo zomwe zimapezeka m’mabuku athu. w25.01 24-25 ¶13-15

Kuwerenga Baibulo pa nyengo ya chikumbutso: (Zochitika pa Nisani 11 kutacha) Luka 21:​1-36

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena