Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • es26 tsamba 47-57
  • May

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • May
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
  • Timitu
  • Lachisanu, May 1
  • Loweruka, May 2
  • Lamlungu, May 3
  • Lolemba, May 4
  • Lachiwiri, May 5
  • Lachitatu, May 6
  • Lachinayi, May 7
  • Lachisanu, May 8
  • Loweruka, May 9
  • Lamlungu, May 10
  • Lolemba, May 11
  • Lachiwiri, May 12
  • Lachitatu, May 13
  • Lachinayi, May 14
  • Lachisanu, May 15
  • Loweruka, May 16
  • Lamlungu, May 17
  • Lolemba, May 18
  • Lachiwiri, May 19
  • Lachitatu, May 20
  • Lachinayi, May 21
  • Lachisanu, May 22
  • Loweruka, May 23
  • Lamlungu, May 24
  • Lolemba, May 25
  • Lachiwiri, May 26
  • Lachitatu, May 27
  • Lachinayi, May 28
  • Lachisanu, May 29
  • Loweruka, May 30
  • Lamlungu, May 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2026
es26 tsamba 47-57

May

Lachisanu, May 1

Mulungu alibe tsankho.—Aroma 2:11.

Atapulumutsa anthu ake ku ukapolo ku Iguputo, Yehova anasankha ansembe kuti azitumikira pachihema. Alevi ankapatsidwa ntchito zosiyanasiyana pachihema chopatulikacho. Kodi amene ankatumikira pachihema komanso anthu omwe ankakhala pafupi ndi chihemacho ankasamalidwa bwino ndi Yehova kuposa anthu ena? Ayi. Tikutero chifukwa Yehova alibe tsankho. Mwisiraeli aliyense anali ndi mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mwachitsanzo, Yehova anaonetsetsa kuti Aisiraeli onse azitha kuona zinthu zodabwitsa monga chipilala cha mtambo komanso chipilala cha moto zomwe zinkakhala pamwamba pa chihema. (Eks. 40:38) Mtambo ukayamba kuyenda, ngakhale amene anali kutali kwambiri ndi chihema ankatha kuuona, kulongedza katundu komanso kuphwasula matenti n’kunyamukira limodzi ndi anzawo. (Num. 9:​15-23) Masiku anonso, kaya timakhala kuti, Yehova amatikonda, kutisamalira komanso kutiteteza. w24.06 4 ¶10-12

Loweruka, May 2

Konzekani msangamsanga! Tiyeni tithawe, chifukwa palibe amene angapulumuke mʼmanja mwa Abisalomu.—2 Sam. 15:14.

Moyo wa Davide unali pangozi. Mwana wake Abisalomu anali atatsimikiza kuti alande ufumu. (2 Sam. 15:​12, 13) Apa Davide ankafunika kuchoka ku Yerusalemu mwamsanga. Pamene atumiki ake ankachoka, Davide anazindikira kuti pankafunika kuti munthu wina atsale kuti azimuuza zimene Abisalomu angakonze. Choncho anatumiza Zadoki ndi ansembe ena mumzindawo kuti akagwire ntchito imeneyi. (2 Sam. 15:​27-29) Iwo ankafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. Davide anapempha Zadoki komanso mnzake wina wokhulupirika dzina lake Husai kuti amuthandize pa nkhaniyi. (2 Sam. 15:​32-37) Potsatira malangizo ake, Husai anachititsa kuti Abisalomu ayambe kumukhulupirira. Iye anapereka malangizo omenyera nkhondo omwe akanapereka mpata kwa Davide kuti akonzeke. Kenako Husai anauza Zadoki ndi Abiyatara zimene anakonzazo. (2 Sam. 17:​8-16) Choncho amuna awiriwa anatumiza uthenga kwa Davide womwe unathandiza kuti Davideyo atetezeke.—2 Sam. 17:​21, 22. w24.07 4-5 ¶9-10

Lamlungu, May 3

Yehova wanena kuti: “Bwerani tsopano, tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.”—Yes. 1:18.

Atumiki ena a Yehova amadziimbabe mlandu chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyo, kaya asanabatizidwe kapena atabazidwa. Koma tingachite bwino kumakumbukira kuti Yehova anapereka dipo chifukwa chakuti amatikonda kwambiri. Choncho n’zoonekeratu kuti iye amafuna kuti tiziyamikira mphatsoyi. Yehova amatitsimikizira kuti ‘akatithandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi iye,’ satiimbanso mlandu pa zimene tinalakwitsazo. Timayamikira kuti Yehova sakumbukiranso zimene tinalakwitsa m’mbuyo. Pa nthawi imodzimodziyo amakumbukira zabwino zimene timachita. (Sal. 103:​9, 12; Aheb. 6:10) Ngati mukuvutika maganizo chifukwa cha zimene munalakwitsa m’mbuyo, muziyesetsa kuti muziganizira zimene mukuchita panopa komanso zimene mudzachite m’tsogolo m’malo moganizira zomwe munalakwitsa m’mbuyo. Palibe chimene mungachite kuti musinthe zimene zinachitika m’mbuyo. Koma mukhoza kumalemekeza Yehova mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu panopa n’kumayembekezera mwachidwi zimene Yehova wakulonjezani kutsogolo. w24.10 8 ¶8-9

Lolemba, May 4

Muvale umunthu watsopano.—Akol. 3:10.

Mukamawerenga Baibulo mukhoza kukhumudwa chifukwa choona kuti pali zinthu zambiri zimene mukufunika kusintha. Tiyerekeze kuti lero mwawerenga Baibulo ndipo mwapeza malangizo okhudza kupewa tsankho. (Yak. 2:​1-8) Ndiyeno mukuganizira mmene mumachitira zinthu ndi anthu ena ndipo mukuona kuti mufunika kusintha. Apo ndiye kuti mwachita bwino. Kenako mawa lake mukuwerenga nkhani yosonyeza kufunika kodziletsa polankhula. (Yak. 3:​1-12) Mukuzindikira kuti nthawi zina simulankhula bwino. Ndiye mukuganiza kuti muzilankhula molimbikitsa nthawi zonse. Tsiku lotsatira mukuwerenga m’Baibulo malangizo oti tizipewa kukhala pa ubwenzi ndi dziko. (Yak. 4:​4-12) Mukuzindikira kuti muyenera kusankha bwino zosangalatsa. Pofika tsiku la 4, mukhoza kukhumudwa mukaganizira kuchuluka kwa zinthu zimene mukufunika kusintha. Koma musamataye mtima, muzikumbukira kuti kuvala “umunthu watsopano” sikutha. w24.09 5-6 ¶11-12

Lachiwiri, May 5

Muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa ndiponso mwaulemu kwambiri.—1 Pet. 3:15.

Yesu ankadziwa kuti Yehova ankaona zopanda chilungamo zomwe zinkamuchitikira. Iye ankakhulupirira kuti Yehova adzathana ndi zopanda chilungamozo pa nthawi yoyenera. Tingatsanzire Yesu poyesetsa kukhala osamala ndi zimene tingalankhule tikachitiridwa zopanda chilungamo. Zinthu zina zopanda chilungamo zimakhala zazing’ono moti tikhoza kungozinyalanyaza. Kapenanso tingasankhe kukhala chete pofuna kupewa kulankhula mawu amene angachititse kuti zinthu ziipe kwambiri. (Mlal. 3:7; Yak. 1:​19, 20) Nthawi zina tingafunike kulankhulapo tikaona zinthu zopanda chilungamo kapena tikafuna kufotokoza zimene timakhulupirira. (Mac. 6:​1, 2) Koma tikafuna kulankhulapo, tiyenera kuyesetsa kuchita zimenezo modekha komanso mwaulemu. Tingatsanzirenso Yesu posiya zonse m’manja mwa “Woweruza amene amaweruza mwachilungamo.”—1 Pet. 2:23. w24.11 5-6 ¶10-12

Lachitatu, May 6

Angelo a Mulungu amasangalala kwambiri chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.—Luka 15:10.

Zimakhala zosangalatsa kwambiri munthu wochimwa akalapa. (Luka 15:7) Kodi zikatero ndi ndani amene amayenera kulemekezedwa? Kodi ndi akulu? Kumbukirani zimene mtumwi Paulo analemba zokhudza anthu ochimwa. Iye anati: “Mwina Mulungu angawalole kulapa.” (2 Tim. 2:25) Munthu wochimwa akasintha maganizo komanso mtima wake, woyenera kulemekezedwa si munthu aliyense koma Yehova chifukwa ndi amene amathandiza munthuyo kuti asinthe. Paulo anafotokozanso zinthu zina zabwino zimene zimachitika munthuyo akalapa. Anafotokoza kuti wochimwayo amadziwa choonadi molondola, nzeru zimamubwerera komanso amapulumuka ku misampha ya Satana. (2 Tim. 2:26) Munthu wochimwa akalapa, akulu omwe anali m’komiti imene inakumana naye amakonza maulendo a ubusa n’cholinga choti apitirize kumuthandiza kupewa misampha ya Satana ndiponso kuwongola njira zake.—Aheb. 12:​12, 13. w24.08 23 ¶14-15

Lachinayi, May 7

Sikuti mukundifunafuna chifukwa choti munaona zizindikiro ayi, koma chifukwa choti munadya mikate nʼkukhuta.—Yoh. 6:26.

Gulu la anthu limene Yesu analidyetsa lija linkangofuna kupeza chakudya. Kodi iwo anachita zotani? Ataona kuti Yesu ndi atumwi ake achoka, anakwera maboti ochokera ku Tiberiyo ndipo anapita ku Kaperenao komwe Yesu anali. (Yoh. 6:​22-24) Kodi iwo anachita zimenezi n’cholinga choti akamve zambiri zokhudza Ufumu? Ayi. Iwo ankangoganizira za chakudya chomwe anawapatsa. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Taonani zimene zinachitika iwo atamupeza Yesu ku Kaperenao. Yesu anawauza mosapita m’mbali kuti iwo anabwera chifukwa chakuti ankangofuna chakudya. Iye anawauza kuti ngakhale kuti ‘anadya mikate nʼkukhuta,’ koma chimenecho chinali “chakudya chimene chimawonongeka.” Choncho anawalimbikitsa kuti ayenera kuyesetsa kupeza “chakudya chomwe chimabweretsa moyo wosatha.” (Yoh. 6:​26, 27) Yesu ananena kuti Atate wake amapereka chakudya chimenecho. w24.12 5 ¶8-9

Lachisanu, May 8

Munthu wanzeru amasankha mawu mwanzeru akamalankhula, ndipo mawu ake amakopa anthu ena.—Miy. 16:23.

Abale, kuti mukhale aphunzitsi ogwira mtima, muyenera kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa komanso kupereka malangizo. Muyenera kuphunzira mwakhama Baibulo komanso mabuku athu. (Miy. 15:28) Mukamaphunzira, muziona mmene mabuku athu akufotokozera Malemba n’cholinga choti muziwagwiritsa ntchito m’njira yoyenera. Ndipo mukamaphunzitsa muziyesetsa kuwafika pamtima anthu. Mukhoza kuwonjezera luso lanu lophunzitsa mukamapempha malangizo kwa akulu amene ali ndi luso. (1 Tim. 5:17) Akulu ayenera kukhala oti angathe kulimbikitsa abale ndi alongo awo ndiponso kudzudzula pakafunika kutero. Koma pochita zinthu zonsezi, nthawi zonse akuluwo ayenera kukhala okoma mtima. Mukakhala odekha komanso achikondi, n’kumaphunzitsa pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, mudzakhala mphunzitsi waluso chifukwa muzitsanzira Yesu yemwe ndi Mphunzitsi Waluso.—Mat. 11:​28-30; 2 Tim. 2:24. w24.11 24 ¶16

Loweruka, May 9

Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina. —Sal. 96:3.

Zimene tingalankhule zokhudza Yehova, zingachititse kuti alandire ulemerero. Monga anthu ake, tikulimbikitsidwa ‘kuimbira Yehova,’ ‘kutamanda dzina lake,’ ‘kulengeza uthenga wabwino wa chipulumutso chake’ komanso ‘kulengeza ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina.’ (Sal. 96:​1-3) Zimenezi ndi njira zimene tingaperekere ulemerero kwa Atate wathu wakumwamba. (Mac. 4:29) Tikhoza kupatsa Yehova ulemerero popereka zinthu zathu zamtengo wapatali. Kuyambira kale, atumiki a Yehova akhala akumupatsa ulemerero m’njira imeneyi. (Miy. 3:9) Mwachitsanzo, Aisiraeli ankapereka zinthu zawo kuti zithandize pa ntchito yomanga ndi kusamalira kachisi. (2 Maf. 12:​4, 5; 1 Mbiri 29:​3-9) Ophunzira ena a Yesu, ‘ankagwiritsa ntchito chuma chawo’ pothandiza iyeyo ndi atumwi ake. (Luka 8:​1-3) Akhristu oyambirira ankaperekanso chithandizo kwa abale ndi alongo awo. (Mac. 11:​27-29) Ifenso masiku ano tikhoza kulemekeza Yehova popereka zinthu zathu. w25.01 4 ¶8; 5 ¶11

Lamlungu, May 10

Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe mʼmadzi?—Mac. 10:47.

Kodi n’chiyani chinathandiza Koneliyo kuti abatizidwe? Timawerenga kuti iye “ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse.” Komanso Koneliyo ankapemphera mochonderera Mulungu nthawi zonse. (Mac. 10:2) Petulo atalalikira uthenga wabwino kwa Koneliyo, iye ndi banja lake anakhulupirira Khristu ndipo nthawi yomweyo anabatizidwa. (Mac. 10:​47, 48) Koneliyo sanazengereze kusintha zilizonse zomwe ankafunikira n’cholinga choti azilambira Yehova limodzi ndi banja lake. (Yos. 24:15; Mac. 10:​24, 33) Udindo wa Koneliyo ukanatha kumulepheretsa kuti akhale Mkhristu. Koma iye sanalole kuti zimenezi zichitike. Kodi inunso mukufunika kusintha zinthu zina pa moyo wanu kuti mubatizidwe? Ngati ndi choncho, dziwani kuti Yehova adzakuthandizani. Iye adzadalitsa zimene mukuyesetsa kuchita kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wanu. w25.03 5 ¶12-13

Lolemba, May 11

Uzipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu.—1 Tim. 4:7.

Mukamva nkhani zoipa zokhudza gulu kapena abale amene akutsogolera, muzikumbukira mmene adani a Mulungu ankachitira ndi Yesu komanso ophunzira ake. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, masiku anonso anthu a Yehova amazunzidwa komanso kuneneredwa zinthu zabodza. (Mat. 5:​11, 12) Nkhani zabodza sizingatisocheretse ngati titazindikira amene akuziyambitsa n’kuchitapo kanthu mwamsanga. Kodi tiyenera kuchita chiyani? Musamamvere nkhani zabodza. Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino zimene tingachite ngati titamva nkhani zabodza. Iye anauza Timoteyo kuti ‘aletse anthu ena . . . kuti asamamvere nkhani zonama’ komanso kuti ‘azipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu.’ (1 Tim. 1:​3, 4) Timakana nkhani zabodza chifukwa timadziwa amene amaziyambitsa. Choncho timagwiritsitsa “mawu olondola” a choonadi.—2 Tim. 1:13. w24.04 11 ¶16; 13 ¶17

Lachiwiri, May 12

Amagwiritsa ntchito mawu okopa ndiponso achinyengo kuti apusitse anthu oona mtima.—Aroma 16:18.

Pitirizani kugwirizana ndi anthu omwe ndi okhulupirika kwa Yehova. Mulungu amafuna kuti tizimulambira mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Tingapitirizebe kukhala ogwirizana ngati tagwiritsitsa choonadi. Aliyense amene amachita zinthu zosemphana ndi choonadi, amayambitsa kuti anthu mumpingo asamagwirizane, n’chifukwa chake Mulungu amatilangiza kuti ‘tiziwapewa.’ Kupanda kutero tingapezeke kuti tapatutsidwa pa choonadi. (Aroma 16:17) Tikazindikira choonadi komanso kuchigwiritsitsa, timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso timakhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Aef. 4:​15, 16) Sitimapusitsidwa ndi mabodza komanso ziwembu za Satana ndipo Yehova adzapitiriza kutiteteza pa chisautso chachikulu. Pitirizani kugwiritsitsa choonadi “ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.”—Afil. 4:​8, 9. w24.07 13 ¶16-17

Lachitatu, May 13

Munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo yothandiza mpaka kalekale.—Aheb. 10:12.

Yesu ankachita chidwi kwambiri ndi anthu amene ankadzimvera chisoni chifukwa choti anali ochimwa ndipo anawapempha kuti akhale otsatira ake. Iye ankadziwa kuti uchimo ndi umene umachititsa mavuto onse amene anthu amakumana nawo. Choncho iye ankathandiza amuna ndi akazi omwe ankadziwika kuti ndi ochimwa. Pogwiritsa ntchito fanizo, iye ananena kuti: “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” Anawonjezeranso kuti: “Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Mat. 9:​12, 13) Zimenezi ndi zomwedi Yesu ankachita. Iye analankhula mokoma mtima komanso anakhululukira mayi wina yemwe anatsuka mapazi ake ndi misozi. (Luka 7:​37-50) Yesu anaphunzitsanso mfundo za choonadi kwa mayi wina wa Chisamariya pachitsime ngakhale kuti ankadziwa kuti mayiyo anali wachiwerewere. (Yoh. 4:​7, 17-19, 25, 26) Mulungu anapatsanso Yesu mphamvu yothetsa imfa yomwe ndi zotsatirapo za uchimo. Tikudziwa bwanji zimenezi? Yesu anaukitsa anthu, amuna ndi akazi, ana ndi achikulire omwe.—Mat. 11:5. w24.08 4 ¶9-10

Lachinayi, May 14

Adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo. Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.—Sal. 96:13.

Kodi Yehova adzalemekeza bwanji dzina lake posachedwapa? Posachedwapa Yehova adzalemekeza dzina lake popereka chiweruzo. Iye adzawononga Babulo Wamkulu chifukwa chonyoza dzina lake loyera. (Chiv. 17:​5, 16; 19:​1, 2) Anthu ena omwe adzaone Babulo Wamkulu akuwonongedwa, adzayamba kulambira nafe Mulungu. Ndipo pa Aramagedo, Yehova adzawononga dziko lonse la Satanali n’kuchotsa anthu onse omwe amamutsutsa komanso kunyoza dzina lake. Koma adzapulumutsa anthu onse omwe amamukonda, kumumvera ndiponso kumupatsa ulemerero. (Maliko 8:38; 2 Ates. 1:​6-10) Pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu komanso mayesero omaliza, Yehova adzakhala atayeretseratu dzina lake. (Chiv. 20:​7-10) Pa nthawiyo “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova, ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” (Hab. 2:14) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri pa nthawiyo, chifukwa aliyense amene adzakhale moyo, azidzapereka kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake. w25.01 7 ¶15-16

Lachisanu, May 15

Muyenera kupirira kuti muphunzitsidwe.—Aheb. 12:7.

Kodi n’chiyani chomwe chikanathandiza Akhristu a Chiheberi pa nthawi yomwe ankazunzidwa? Mtumwi Paulo ankadziwa kuti iwo ankafunika kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya mayesero omwe ankakumana nawo. Choncho iye anawafotokozera kuti Mulungu analola kuti iwo akumane ndi mayeserowo n’cholinga chofuna kuwaphunzitsa. Kuphunzitsidwa mwa njira imeneyi kumathandiza kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino. Kuganizira zimene zikanachitika pambuyo pa mayeserowo kukanathandiza Akhristuwo kuti apirire. (Aheb. 12:11) Paulo analimbikitsa Akhristu a Chiheberi kuti azipirira mayesero ndipo sankayenera kutaya mtima. Zinali zomveka kuti Paulo awapatse malangizo amenewa. Popeza kuti anazunzapo Akhristu, iye ankadziwa zimene Akhristuwo angakumane nazo. Komanso anali atapirirako kuzunzidwa chifukwa atakhala Mkhristu anazunzidwa m’njira zambiri.—2 Akor. 11:​23-25. w24.09 12-13 ¶16-17

Loweruka, May 16

Pitirizani kukhala maso.—Mat. 25:13.

Tsiku lililonse likamadutsa, nthawi yoti tilalikire imakhala ikuchepa kwambiri. Tikutero chifukwa choti nthawi yoti mapeto afike, imakhala ikuyandikira. Taganizirani zimene Yesu ananeneratu zokhudza ntchito yolalikira m’masiku otsiriza zomwe zinalembedwa pa Maliko 13:10. Mogwirizananso ndi zimene Mateyu analemba, Yesu ananena kuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, “mapeto” asanafike. (Mat. 24:14) Mawu amenewa, akunena za mapeto a dziko loipa la Satanali. Yehova wakhazikitsa ‘tsiku ndi ola’ lomwe zimenezi zichitike. (Mat. 24:36; Mac. 1:7) Tsiku lililonse likamadutsa timakhala tikuyandikira ku nthawi imeneyi. (Aroma 13:11) Choncho, panopa tiyenera kupitirizabe kulalikira mpaka mapeto afike. Tikamaganizira za utumiki wathu, tingachite bwino kudzifunsa funso lofunika ili: N’chifukwa chiyani timalalikira uthenga wabwino? Mwachidule, chikondi ndi chomwe chimatilimbikitsa kuti tizilalikira. Tikamagwira ntchito yolalikira timasonyeza kuti timakonda uthenga wabwino, timakonda anthu ndipo koposa zonse, timakonda Yehova ndi dzina lake. w24.05 14-15 ¶2-3

Lamlungu, May 17

Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.—Gen. 1:31.

Makolo, muzilimbikitsa mwana wanu kuti aziganizira zinthu za m’chilengedwe. Mukamayenda ndi mwana wanu m’tchire kapena m’munda, muzimuthandiza kuona kapangidwe kochititsa chidwi ka zinthu za m’chilengedwe. N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezo? Zimenezi zingamuthandize kuzindikira kuti amene anapanga zinthu zimenezi ndi wanzeru. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri asayansi akhala akuphunzira kapangidwe kozungulira ka zinthu zosiyanasiyana. Wasayansi wina dzina lake Nicola Fameli anafotokoza kuti zinthu zambiri zozungulira m’chilengedwechi zimapindika mozungulira maulendo ofanana. Kazunguliridwe kameneka kamatchedwa Fibonacci. Timaona kuzungulira kotereku m’zinthu zambiri za m’chilengedwe monga milalang’amba, chigoba cha nkhono, masamba a zomera zina komanso mpendadzuwa. w24.12 16 ¶7

Lolemba, May 18

Iye ndi amene amapereka moyo.—Deut. 30:20.

Mose, Davide ndi Yohane anakhala ndi moyo pa nthawi yosiyana kwambiri ndi yathu. Komabe timafanana nawo pa zinthu zambiri. Onsewa ankatumikira Mulungu woona ngati ifeyo. Mofanana ndi iwowo, timapemphera kwa Yehova komanso timamudalira kuti azitithandiza ndi kutipatsa malangizo. Ndipotu mofanana ndi amunawa timakhulupirira kuti Yehova amadalitsa anthu omwe amamumvera. Tiyeni tizitsatira malangizo a amuna achikulirewa ndipo tizimvera malamulo a Yehova. Tikatero zinthu zonse zomwe timachita zizitiyendera bwino. Tidzakhala ndi moyo “kwa nthawi yaitali” kapena kuti mpaka kalekale. Tidzasangalala podziwa kuti tikusangalatsa Atate wathu wakumwamba, yemwe amakwaniritsa malonjezo ake m’njira imene sitimayembekezera.—Aef. 3:20. w24.11 13 ¶20-21

Lachiwiri, May 19

Mulungu wapereka zochita kwa munthu aliyense mumpingo.—1 Akor. 12:28.

M’nthawi ya atumwi, abale ena ankaikidwa kukhala atumiki othandiza. (1 Tim. 3:8) N’kutheka kuti abale amenewa ndi amene ankachita “utumiki wothandiza anthu” womwe mtumwi Paulo analemba. Atumiki othandiza ayenera kuti ankagwira ntchito zina zofunika n’cholinga choti akulu aziika maganizo awo pa ntchito yofunika yophunzitsa ndi kuweta nkhosa. Mwachitsanzo, atumiki othandiza ayenera kuti ankathandiza pokopera Malemba kapena kugula zipangizo zogwirira ntchitoyi. Kodi ndi ntchito zina ziti zothandiza zomwe atumiki othandiza amagwira mumpingo wanu? (1 Pet. 4:10) Iwo amasamalira ndalama zampingo kapena kuyang’anira magawo, kuitanitsa mabuku kuti ofalitsa alandire, kusamalira zipangizo zokuzira mawu ndi zoonetsera mavidiyo, kulandira alendo pamisonkhano kapenanso kugwira ntchito yosamalira pa Nyumba ya Ufumu. Ntchito zonsezi zimathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino pampingo.​—1 Akor. 14:40. w24.10 19 ¶4-5

Lachitatu, May 20

Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.—Afil. 4:13.

Tingathe kupirira mayesero alionse kaya aakulu kapena aang’ono ngati timakumbukira kuti Yehova ndi wamoyo ndipo amafunitsitsa kutithandiza. Ndipotu iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo akhoza kutipatsa mphamvu kuti tipirire. Choncho tili ndi zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira kuti tingathe kupirira vuto lililonse. Tikaona Yehova akutithandiza pa mavuto ang’onoang’ono, sitikayikira kuti adzatithandizanso pa mavuto aakulu. Taganizirani zimene zinachitika pa moyo wa Mfumu Davide, zomwe zinachititsa kuti azikhulupirira kwambiri Yehova. Ali wamng’ono, chimbalangondo komanso mkango zinagwira nkhosa za bambo ake zomwe ankaweta. Pa nthawi zonsezi, Davide analimba mtima n’kuthamangitsa zilombozo ndipo anapulumutsa nkhosazo. Koma Davide sanaganize kuti wachita zimenezi ndi mphamvu zake. Ankadziwa kuti Yehova ndi amene wamuthandiza. (1 Sam. 17:​34-37) Kuganizira zimene zinachitikazi kunamuthandiza kukhulupirira kuti Mulungu wamoyo adzamuthandizanso m’tsogolo. w24.06 21 ¶5-6

Lachinayi, May 21

Munthu akayankhira nkhani asanaimvetsetse, kumakhala kupusa ndipo amachita manyazi.—Miy. 18:13.

Tiyerekeze kuti munthu wina wakuitanani kumacheza, kodi muyenera kupita? Ngati munthuyo simukumudziwa bwino komanso simukudziwa kuti macheza ake akakhala otani, mungamufunse mafunso awa: “Kodi machezawo akachitikira kuti, nanga akachitika nthawi yanji? Kodi kukakhala anthu ochuluka bwanji? Ndi ndani azikayang’anira machezawo? Ndi anthu ati amene aitanidwa? Nanga kukakhala zotani? Kodi kukakhala mowa?” Mayankho a mafunsowa angakuthandizeni kuti musankhe bwino zochita. Mukadziwa mfundozo muyenera kufufuzabe bwino kuti mudziwe nkhani yonse. Mwachitsanzo, kodi mungatani mutamva kuti kukakhalanso anthu ena omwe satsatira mfundo za m’Baibulo kapenanso kuti anthu azikamwa mowa popanda wowayang’anira? Kodi macheza amenewo sangasinthe n’kukhala phwando loipa? (1 Pet. 4:3) Mukadziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo mukhoza kusankha bwino zochita. w25.01 15 ¶4-5

Lachisanu, May 22

Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri, adzayera kwambiri.—Yes. 1:18.

Yehova amagwiritsa ntchito mawu a fanizo pofuna kutithandiza kumvetsa mmene amafufutira machimo a anthu amene alapa pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo. Zimakhala zovuta kwambiri kuchotsa zinthu zofiira kapena magazi pachovala. Koma pogwiritsa ntchito fanizoli Yehova akutitsimikizira kuti machimo athu adzayera kwambiri moti sangaonekenso. Machimo amayerekezeredwanso ndi “ngongole.” (Mat. 6:12; Luka 11:4) Choncho nthawi iliyonse imene tachimwa, zimakhala ngati tawonjezera ngongole yathu kwa Yehova. Ndipo ngongole yathu imakhala yaikulu kwambiri. Koma akatikhululukira zimakhala ngati wafufuta ngongole imene timafunika kubweza. Iye sayembekezera kuti tilipire ngongole ya machimo amene anatikhululukira. Fanizoli likufotokoza bwino kuti Yehova akatikhululukira timakhala osangalala. w25.02 9-10 ¶9-10

Loweruka, May 23

Si udindo wa ana kusunga chuma kuti chidzathandize makolo awo, koma makolo ndi amene ayenera kusungira chuma ana awo.—2 Akor. 12:14.

Makolo akakalamba amafunika kuthandizidwa ndi ana awo ndipo ana ambiri amasangalala kuchita zimenezi. (1 Tim. 5:4) Koma makolo a Chikhristu amazindikira kuti angakhale osangalala kwambiri ngati atakhala ndi ana, n’kuwathandiza kukhala atumiki a Yehova, osati kukhala nawo n’cholinga choti adzawathandize m’tsogolo. (3 Yoh. 4) Muziwapatsa ana anu chitsanzo pa nkhani yodalira Yehova. Muziwaphunzitsa kugwira ntchito mwakhama kuyambira ali aang’ono. (Miy. 29:21; Aef. 4:28) Akamakula muziwauza kuti azilimbikira kusukulu. Makolo ayenera kufufuza komanso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothandiza ana awo kuti azigwiritsa ntchito bwino maphunziro. Izi zingadzawathandize kuti azidzapeza zofunika pa moyo uku akutumikira Yehova. w25.03 30-31 ¶15-16

Lamlungu, May 24

Muvale umunthu watsopano.—Aef. 4:24.

Mu chaputala 65 cha buku la Yesaya, Yehova anafotokoza mmene moyo wa anthu omwe adzakhale m’paradaiso wauzimu udzakhalire. Ulosiwu unakwaniritsidwa koyamba mu 537 B.C.E. Pa nthawiyo, Ayuda omwe analapa anamasulidwa ku ukapolo ku Babulo ndipo anabwerera kwawo. Yehova anadalitsa anthu ake ndipo anawathandiza kukonzanso mzinda wa Yerusalemu kuti ukhalenso wokongola komanso kuti amangenso kachisi yemwe anali likulu la kulambira koona. (Yes. 51:11; Zek. 8:3) Kukwaniritsidwa kwachiwiri kwa ulosi wa Yesayawu kunayamba mu 1919 pamene atumiki a Yehova a masiku ano anamasulidwa ku ukapolo wa Babulo Wamkulu. Kenako paradaiso wauzimu anayamba kufalikira padziko lonse. Olalikira Ufumu akhama anakhazikitsa mipingo yambiri ndipo ankasonyeza makhalidwe abwino. Amuna ndi akazi omwe poyamba anali achiwawa komanso ankasonyeza makhalidwe ngati a zinyama, anayamba ‘kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.’ w24.04 20-21 ¶3-4

Lolemba, May 25

Aliyense ayenera kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.

M’mayiko ena, makolo kapena achibale ena akuluakulu ndi amene amapezera munthu mwamuna kapena mkazi woti akwatirane naye. Pomwe m’mayiko ena achibale kapena anzake a munthu ndi amene amakonza kuti mwamuna ndi mkazi akumane n’kuona ngati ali oyenerana. Ngati mwapemphedwa kuti mukonze zoti anthu ena akhale pa chibwenzi kapena akwatirane, muyenera kuganizira zimene aliyense wa anthuwo amafuna komanso zimene amakonda. Mukapeza munthu amene mukuganiza kuti ndi woyenerera, muziyesetsa kumudziwa bwino komanso kudziwa makhalidwe ake. Koma chofunika kwambiri ndi kudziwa ngati amakonda Yehova. Kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndi kofunika kwambiri kuposa ndalama, maphunziro kapena kutchuka. Komabe muzikumbukira kuti m’bale ndi mlongo amene sali pa banjawo ndi amene ayenera kusankha ngati akufuna kukwatirana. w24.05 23 ¶11

Lachiwiri, May 26

Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse.—Miy. 17:17.

Zimene tingasankhe kulankhula kapena ayi, zingathandize anthu omwe ali pa chibwenzi. Nthawi zina tingafunike kudziletsa. (Miy. 12:18) Mwachitsanzo, tingafune kuuza ena kuti wakuti ndi wakuti ali pa chibwenzi komabe mwina anthu omwe ali pa chibwenziwo angafune kuti adzanene okha zimenezi. Sitiyenera kunena miseche yokhudza anthu omwe ali pa chibwenzi kapena kuwaweruza pa nkhani zimene ayenera kusankha okha zochita. (Miy. 20:19; Aroma 14:10; 1 Ates. 4:11) Komanso anthuwo sangasangalale tikamanena zinthu kapena kufunsa mafunso osonyeza kuti akuyenera kukwatirana. Bwanji ngati anthu asankha kuthetsa chibwenzi chawo? Sitiyenera kulowerera nkhani za eni kapena kukhala kumbali ya winawake. (1 Pet. 4:15) Ngati anthu omwe ali pa chibwenzi asankha kuti athetse chibwenzicho, si nthawi zonse pamene zimatanthauza kuti chibwenzicho sichinawathandize. Nthawi zambiri chimakhala kuti chakwaniritsa cholinga chake chifukwa chawathandiza kudziwa zoyenera kusankha. Komabe kutha kwa chibwenziko kungachititse kuti asweke mtima. Choncho tikhoza kupeza njira zowathandizira. w24.05 31 ¶15-16

Lachitatu, May 27

Ukafooka pa nthawi imene ukukumana ndi mavuto, mphamvu zako zidzachepa.—Miy. 24:10.

Chimodzi mwa zinthu zimene zimayesa kwambiri chikhulupiriro chathu komanso kutifooketsa ndi pamene wachibale kapena mnzathu wasiya kutumikira Yehova. (Sal. 78:40) Ngati timamukonda kwambiri munthuyo, zimakhalanso zovuta kwambiri kuti tivomereze zimene zachitikazo. Ngati inunso zimenezi zinakuchitikirani, kukhulupirika kwa Zadoki kungakulimbikitseni. Iye anasankha kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova pamene mnzake Abiyatara anasankha kuchita zinthu mosakhulupirika. Davide atatsala pang’ono kufa, mwana wake Adoniya ankafuna kulanda ufumu wake ngakhale kuti Yehova anali atalonjeza kuti Solomo ndi amene adzakhale mfumu. (1 Mbiri 22:​9, 10) Abiyatara anasankha kukhala kumbali ya Adoniya. (1 Maf. 1:​5-8) Pochita zimenezi, Abiyatara anakhala wosakhulupirika kwa Davide, Zadoki komanso Yehova. Kwa zaka zoposa 40, Zadoki ndi Abiyatara anali atagwira ntchito limodzi monga ansembe.—2 Sam. 8:17; 15:29; 19:​11-14. w24.07 6 ¶14-15

Lachinayi, May 28

Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake.—Miy. 28:14.

Tisamakayikire kuti kukhalabe maso n’kothandiza nthawi zonse. Machimo amangochititsa kuti munthu ‘asangalale kwa nthawi yochepa’ koma kutsatira mfundo za Yehova kumachititsa kuti munthu akhale wosangalala kwambiri. (Aheb. 11:25; Sal. 19:8) Zili choncho chifukwa chakuti anthufe tinalengedwa m’njira yoti tizitsatira mfundo za Mulungu. (Gen. 1:27) Tikamachita zimenezi, timakhala ndi chikumbumtima choyera komanso timayembekezera moyo wosatha. (1 Tim. 6:12; 2 Tim. 1:3; Yuda 20, 21) N’zoona kuti “thupi ndi lofooka.” (Mat. 26:41) Koma sizikutanthauza kuti tilibiretu mtengo wogwira. Yehova ndi wokonzeka kutipatsa mphamvu. (2 Akor. 4:7) Onani kuti Mulungu amapereka mphamvu yoposa yachibadwa. Koma choyamba, tiyenera kugwiritsa ntchito mphamvu yathu yachibadwa polimbana ndi mayesero tsiku lililonse. Tikachita mbali yathu tisamakayikire kuti Yehova adzayankha mapemphero athu potipatsa mphamvu zowonjezereka zomwe tingafunikire. (1 Akor. 10:13) Choncho mothandizidwa ndi Yehova tikhoza kukhala maso n’kumapewa mayesero. w24.07 19 ¶19-21

Lachisanu, May 29

Amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo, uziwadzudzula pamaso pa onse.—1 Tim. 5:20.

Mtumwi Paulo analembera Timoteyo, yemwe anali mkulu mnzake, mawu a mulemba lalerowa pomuuza zoyenera kuchita ndi “anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo.” Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye sankatanthauza kuti anthu “onse” mumpingo akuyenera kudziwa zokhudza nkhaniyo. Koma ankanena za anthu ochepa omwe ankadziwa kale za nkhaniyo. Akhoza kukhala anthu omwe anaona tchimolo likuchitika kapena amene munthu wochimwayo anawafotokozera. Akulu angawafotokozere anthuwo mwanzeru kuti nkhaniyo yasamalidwa ndipo wochimwayo wathandizidwa. Koma nthawi zina zimakhala kuti tchimolo ladziwika mumpingo wonse kapenanso kuti lidzadziwika. Zikatero mawu akuti “onse” angatanthauze mpingo wonse. Choncho mkulu angalengeze kumpingo kuti m’bale kapena mlongo wadzudzulidwa. N’chifukwa chiyani zimenezi ziyenera kuchitika? Paulo anafotokoza kuti: “Kuti ena onsewo akhale ndi mantha” n’cholinga choti asachite tchimo. w24.08 23-24 ¶16-17

Loweruka, May 30

Amenewa ndi mawu oona a Mulungu.—Chiv. 19:9.

Tiyenera kutumikira Yehova mwakhama mpaka mapeto. Odzozedwa ayeneranso kukhalabe maso n’cholinga choti ‘adzatengedwe’ ndi Yesu kuti akalandire mphoto yawo kumwamba. (Mat. 24:40) Iwo akuyembekezera mwachidwi nthawi imene Yesu ‘adzawasonkhanitse’ kupita kumwamba. Pambuyo pa Aramagedo, iwo adzakhala mkwatibwi pa ukwati wa Mwanawankhosa. (2 Ates. 2:1) Ngakhale kuti tsiku la chiweruzo likubwera mofulumira, palibe chifukwa chochitira mantha. Ngati tingakhalebe okhulupirika, Atate wathu wakumwamba adzatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti ‘tidzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.’ (2 Akor. 4:7; Luka 21:36) Kaya tikuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, tidzasangalatsa Atate wathu ngati titamvera machenjezo opezeka m’mafanizo a Yesu. Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova, mayina athu ‘adzalembedwa mʼbuku’ la moyo.—Dan. 12:1; Chiv. 3:5. w24.09 24-25 ¶19-20

Lamlungu, May 31

Koma kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.—Sal. 73:28.

Kodi Mawu a Mulungu angakuthandizeni bwanji kuti mukhale ndi mtendere wamumtima? Muziganizira zinthu zabwino zimene mwapeza. Mwachitsanzo, muziyerekezera madalitso amene Yehova wakulonjezani ndi zinthu zimene dzikoli lingakupatseni panopa. Anthu ena angamadalire zimene akwanitsa kupeza m’dzikoli chifukwa chakuti alibe chiyembekezo chilichonse m’tsogolo. Koma inuyo Yehova wakulonjezani zinthu zabwino kwambiri kuposa zimene mungaziganizire. (Sal. 145:16) Taganiziraninso funso ili: Kodi tinganene motsimikiza mmene moyo wathu ukanakhalira zikanakhala kuti tinasankha zinthu zina? Chomwe muyenera kudziwa ndi chakuti amene amasankha zochita chifukwa chokonda Mulungu ndi anthu, nthawi zonse amapezabe zinthu zowathandiza kukhala osangalala. w24.10 27 ¶12-13

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena