PHUNZIRANI KUCHOKERA KWA YESU
Padziko Lonse Padzakhala Mtendere
Aliyense amafunitsitsa kukhala m’dziko lamtendere. Kuyambira kalekale, atsogoleri padziko lonse akhala akuyesetsa kukhazikitsa mtendere m’mayiko amene muli nkhondo. Nthawi zina zimathandizadi kubweretsa mtendere kwa kanthawi kochepa. Koma pakapita nthawi, kawirikawiri anthu amayambanso kumenyana. Kodi n’zothekadi kuti padziko lonse padzakhale mtendere? Inde n’zotheka. Kuti muone umboni wa zimenezi ganizirani zimene Yesu adzachite komanso zimene anaphunzitsa.
Zimene Yesu adzachite
Baibulo limafotokoza zimene Yesu achite posachedwapa kuti abweretse mtendere padziko lonse.
“[Yesu] adzapatsidwa dzina lakuti . . . Kalonga Wamtendere. Ulamuliro wake udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, Yesu adzakhazikitsa mtendere padziko lonse womwe sudzatha.
“Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo . . . ndi aliyense amene alibe womuthandiza.” (Salimo 72:12-14) Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zimene ali nazo pokhazikitsa chilungamo chenicheni, kuthetsa nkhondo zonse, ziwawa komanso kuvutika.
“Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Mu ulamuliro wa Yesu anthu onse adzaphunzira kukhala mwamtendere ndi ena osati kumenya nkhondo.
Kuti mudziwe zimene Yesu adzachite kuti abweretse mtendere umenewu komanso zomwe mungachite kuti mudzakhale m’dziko lamtendereli, onerani kavidiyo kachidule kakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Zimene Yesu anaphunzitsa
Ngakhale panopa, zimene Yesu anaphunzitsa zikuthandiza anthu mamiliyoni ambiri kukhala mwamtendere. Pa ulaliki wake wotchuka wapaphiri, Yesu anaphunzitsa mfundo zimene zikuthandiza anthu kukhala mwamtendere. Onani zitsanzo zotsatirazi.
“Osangalala ndi anthu amene amabweretsa mtendere.” (Mateyu 5:9) Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti azipewa mikangano komanso kuti azilimbikitsa mtendere.
“Choyamba pita ukakhazikitse mtendere ndi mʼbale wakoyo. Kenako ukabwerenso nʼkudzapereka mphatso yakoyo.” (Mateyu 5:23, 24) Yesu analimbikitsa anthu amene ankamumvetsera kuti azithetsa mwamsanga kusemphana maganizo. Iye anaphunzitsa kuti ngati tikufuna kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu tikuyenera kukhazikitsa mtendere ndi anthu ena.
“Siyani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Mateyu 7:1) Yesu anatichenjeza kuti tisamaweruze ena mwankhanza kapena kuwayembekezera kuti azichita zinthu zimene ifeyo sitichita, chifukwa zimenezi zingayambitse mikangano. M’malo mopezera ena zifukwa, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti ‘apitirize kukhululukira anthu’ zolakwa zawo.—Luka 6:37.
Anthu padziko lonse akugwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsazi. Ngakhale m’madera amene kukuchitika zachiwawa kapena nkhondo, anthu akuphunzira kuthetsa kusamvana modekha, akukhululukira ena komanso akusonyeza chikondi ngakhale pamene akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo.
Kuti muone umboni wosonyeza kuti zimene Yesu ankaphunzitsa zathandiza anthu kupeza mtendere, werengani nkhani yakuti“Mungatani Kuti Muzikhala Mwamtendere Ngakhale Kuti Kuli Nkhondo Komanso Zachiwawa?”