Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mrt nkhani 134
  • Kuchita Zachiwawa Sikungathetse Mavuto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchita Zachiwawa Sikungathetse Mavuto
  • Nkhani Zina
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Yesu ananena
  • Zimene Yesu anachita komanso zimene adzachite m’tsogolo
  • Kodi “Kukonda Adani Anu” Kumatanthauza Chiyani”?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Padziko Lonse Padzakhala Mtendere
    Nkhani Zina
  • Kodi Yesu Anapereka Lamulo Lotani Lokhudza Kuchita Zinthu ndi Ena?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Pitirizani Kuchita Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Nkhani Zina
mrt nkhani 134
Yesu akuphunzitsa gulu la amuna, akazi ndi ana.

PHUNZIRANI KUCHOKERA KWA YESU

Kuchita Zachiwawa Sikungathetse Mavuto

Anthu ambiri masiku ano amaona kuti kuchita zachiwawa kungawathandize pamene asemphana maganizo kapena kukumana ndi vuto linalake. Koma zimenezi n’zosemphana kwambiri ndi zimene Yesu Khristu anaphunzitsa komanso kuchita. Taganizirani zinthu zina zimene ananena komanso kuchita.

Zimene Yesu ananena

Pa ulaliki wake wodziwika bwino wapaphiri, Yesu anaphunzitsa kuti kukwiya, kuchita zinthu mwankhanza kapena kuchita zachiwawa si njira yothetsera kusemphana maganizo. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

  • “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12; Luka 6:31) Mfundo yamakhalidwe abwino imeneyi imatilimbikitsa kuti tizichitira ena zimene tikufuna kuti iwonso atichitire.a Popeza kuti palibe amene amafuna kuti anthu amuchitire zachiwawa, tonsefe tiyenera kuyesetsa kulemekeza komanso kukomera mtima anthu onse, ngakhale amene tasemphana nawo maganizo.

  • “Wina akakumenyani mbama patsaya lakumanja, muzimupatsanso tsaya linalo.” (Mateyu 5:38, 39; Luka 6:29) Apa sikuti Yesu ankatanthauza kuti tiziuza ena kuti atichitire zinthu zankhanza. M’malomwake ankafuna kukonza maganizo olakwika amene atsogoleri ena azipembedzo ankaphunzitsa akuti sikulakwa kubwezera. Iye ankaphunzitsa otsatira ake kuti asamabwezere, m’malomwake azikhala odekha wina akawachitira zinthu zoipa.b

  • “Pitirizani kukonda adani anu.” (Mateyu 5:43, 44; Luka 6:27) Yesu anaphunzitsa kuti tizichita zinthu mokoma mtima ndi anthu amene amadana nafe kapena amene atichitira zinthu zopanda chilungamo. Iye sankatanthauza kuti tizigwirizana ndi makhalidwe awo oipawo.c Koma tikasonyeza kukoma mtima kwa anthu amene amadana nafe, zingathe kufewetsa mtima wawo ngakhalenso kuwalimbikitsa kuti nawonso atichitire zinthu mwachifundo.

Zimene Yesu anachita komanso zimene adzachite m’tsogolo

Yesu ankaphunzitsa kuti kuchita zachiwawa sikungathetse mavuto ndipo zochita zake zinali zogwirizana ndi zimene ankaphunzitsa. Usiku umene Yesu anagwidwa, mmodzi wa otsatira ake anachita zachiwawa pofuna kumuteteza, koma iye ananena kuti: “Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Yesu anasonyeza kuti ankakonda adani ake pokhululukira anthu amene ankamuzunza komanso kuwapempherera.​—Luka 23:33, 34; 1 Petulo 2:23.

Baibulo limanena kuti posachedwapa, Yesu amene ndi Kalonga Wamtendere, athetsa zachiwawa zonse. (Yesaya 9:6, 7) Kuti mudziwe zambiri zokhudza zinthu zochititsa chidwi zimene zidzachitike m’tsogolo, werengani nkhani yakuti “Kodi Nkhondo Komanso Zachiwawa Zidzathetsedwa Bwanji?”

a Kuti mumve zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Yesu Anapereka Lamulo Lotani Lokhudza Kuchita Zinthu ndi Ena?”

b Kuti mumve zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Lamulo Lakuti ‘Diso Kulipira Diso’ Limatanthauza Chiyani?”

c Kuti mumve zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi ‘Kukonda Adani Anu’ Kumatanthauza Chiyani”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena