Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 June tsamba 14-19
  • Kagulu ka Utumiki Wakumunda Kamatithandiza Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kagulu ka Utumiki Wakumunda Kamatithandiza Kwambiri
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • WOYANG’ANIRA KAGULU NDI WOMUTHANDIZA WAKE
  • MUZITHANDIZA KUTI ZINTHU ZIZIYENDA BWINO M’KAGULU KANU KA UTUMIKI
  • MMENE KAGULU KA UTUMIKI KAMATITHANDIZIRA
  • Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Kagulu Kanu ka Utumiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Ulaliki Wagulu Umasangalatsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 June tsamba 14-19

AUGUST 24-30, 2026

NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo

Kagulu ka Utumiki Wakumunda Kamatithandiza Kwambiri

“Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse pamsonkhano wa anthu owongoka mtima.”—SAL. 111:1.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene kagulu ka utumiki wakumunda kamatithandizira.

1-2. Kodi anthu ambiri amamva bwanji chifukwa choti ali m’kagulu ka utumiki wakumunda?

KODI mukukumbukira tsiku limene munavomerezedwa kukhala wofalitsa wa uthenga wabwino? Pa tsiku losangalatsali, munakhala m’gulu la anthu omwe amalambira Yehova komanso kutamanda dzina lake. (Sal. 148:​1, 2, 12, 13) N’kuthekanso kuti pa tsikulo munakhalanso m’kagulu ka utumiki wakumunda ka abale ndi alongo ochepa. Magulu a utumiki wakumunda amatithandiza kukwanitsa kugwira nawo ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mat. 24:14.

2 Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimene gulu linakonza zoti pazikhala magulu a utumiki wakumunda? Mlongo wina dzina lake Wendya anati: “Kukhala m’kagulu ka utumiki wakumunda kwandithandiza m’njira zambiri. Ndaphunzira kulalikira komanso kuphunzitsa mwaluso, ena anandithandiza kukhala ndi zolinga zauzimu komanso kuzikwaniritsa ndiponso ndapeza anzanga abwino kwambiri.” M’bale wina dzina lake Rich anati: “Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira monga woyang’anira kagulu. N’zoona kuti ofalitsa ena amathandiza munthu kuti afike pobatizidwa, koma woyang’anira kagulu amakhala ndi mwayi wapadera wothandiza wofalitsayo kupitiriza kukhala wolimba mwauzimu nthawi ikamapita.” Mlongo wina dzina lake Dinah ananena kuti: “Gulu linachita bwino kwambiri kukonza zoti pazikhala timagulu ta utumiki, moti abale ndi alongo a m’kagulu kathu ndimangowaona ngati anthu a m’banja langa.”

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi choyamba, tikambirana udindo wa woyang’anira kagulu komanso womuthandiza wake ndipo tiona zimene abalewa amachita posamalira anthu a m’kagulu kawo. Kenako, tikambirana zimene tonsefe tingachite kuti zinthu ziziyenda bwino m’kagulu kathu. Pomaliza tiona mmene kagulu ka utumiki wakumunda kamatithandizira.

WOYANG’ANIRA KAGULU NDI WOMUTHANDIZA WAKE

4. (a) Kodi udindo waukulu wa woyang’anira kagulu ndi wotani? (b) Kodi woyang’anira kagulu amachita zotani ndi anthu a m’kagulu kake? (Onani bokosi lakuti, “Mfundo Zimene Zingathandize Woyang’anira Kagulu.”)

4 Woyang’anira kagulu ndi mkulub amene amasankhidwa ndi bungwe la akulu kuti azithandiza ofalitsa m’kagulu kake kupita patsogolo mwauzimu. Kodi amachita bwanji zimenezi? Choyamba, amachita chidwi ndi munthu aliyense wa m’kagulu kake. (Miy. 27:23) Iye amakhala m’busa watcheru komanso wachikondi ndipo amalankhulana ndi anthu a m’kagulu kake pafupipafupi. Zimenezi zimamupatsa mwayi woti aziwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kuwalimbikitsa akakhala ndi nkhawa komanso kuwathandiza m’njira zina. (Miy. 12:25; Yes. 32:2; Yak. 2:​15-17) Chachiwiri, amathandiza wofalitsa aliyense kuti azichita khama pa ntchito yolalikira. Iye amayesetsa kuti azitsogolera kagulu kake pa ntchito yolalikira wiki iliyonse. Amayesetsanso kulalikira ndi wofalitsa aliyense kuti azimulimbikitsa komanso kumuphunzitsa ntchitoyi. Ngati salowa mu utumiki amaonetsetsa kuti womuthandiza wake kapena wofalitsa wina woyenerera atsogolere kaguluko. Chachitatu, amathandiza abale obatizidwa kuti ayenerere maudindo mumpingo. (1 Tim. 3:1) Iye amayamikira mochokera pansi pa mtima, kupereka malangizo a m’Malemba komanso kuphunzitsa abale kuti ayenerere kukhala atumiki othandiza ndiponso akulu. Poganizira kufunika kwa udindo wa woyang’anira kagulu, bungwe la akulu limasankha mkulu yemwe angakwanitse udindowu kuti akhale woyang’anira kagulu.

Mfundo Zimene Zingathandize Woyang’anira Kagulu

  • Msonkhano wokonzekera utumiki uzikhala wachidule wosapitirira maminitsi 7 kuti ofalitsa asamachedwe kulowa mu utumiki.

  • Ngati n’zotheka muziyesetsa kulowa mu utumiki ndi wofalitsa aliyense m’kagulu kanu, kuphatikizapo amene sapezekapezeka pamsonkhano wokonzekera utumiki. Mwina mungakonze zoti muzilalikira ndi ofalitsa amenewa madzulo kapena tsiku lina.

  • Muzichita ubusa nthawi ndi nthawi kwa anthu onse a m’kagulu kanu. Mukhoza kuchita zimenezi kunyumba ya ofalitsa, ku Nyumba ya Ufumu kapenanso malo ena oyenerera. Mukhozanso kuchita ulendo wa ubusa poimba foni kapena polemba kalata.

  • Muziphunzitsa abale kuti azichita zambiri mumpingo komanso kuti ayenerere maudindo ena.

  • Muzitsogolera kagulu kanu ngakhale pamene kagulu kanuko kakufunika kukumana ndi timagulu tinanso ta utumiki.

5. Kodi ena mwa akulu oyang’anira magulu amakumana ndi mavuto otani?

5 Woyang’anira kagulu akhoza kukumana ndi mavuto ena pomwe akusamalira anthu a m’kagulu kake. Taganizirani za Jörg, woyang’anira kagulu wa ku Germany, yemwe mofanana ndi akulu ambiri, ali ndi maudindo angapo oti awasamalire mumpingo. Iye anati: “Kusamalira maudindo angapo mumpingo si nkhani yamasewera, moti zimandivuta kukwanitsa cholinga changa choti ndizilankhula ndi aliyense m’kagulu kanga.” M’bale wina wazaka 70 wa ku Uganda dzina lake Abel anati: “Mumpingo mwathu muli akulu ndi atumiki othandiza ochepa kwambiri. Ndiye tili ndi magulu a utumiki akuluakulu, zimenezi zimachititsa kuti ndizivutika kuchita maulendo aubusa kwa ofalitsa aliyense pafupipafupi ngati mmene ndimafunira.” Ndipo Obed yemwe ndi mkulu wa ku Suriname anati: “Ndimakonda kuphunzitsa anthu ena. Koma kuphunzitsa ena kumafuna nthawi komanso mphamvu ndipo zotsatira zake sizionekera nthawi yomweyo. Choncho nthawi zambiri sindiphunzitsa ena chifukwa chotanganidwa.” Ndiye n’chiyani chimene chingathandize akulu omwe amakumana ndi mavuto amenewa komanso ena?

6. Kodi kukhala ndi timagulu tating’ono kumathandiza bwanji oyang’anira kusamalira anthu omwe ali m’kagulu kawo?

6 Ngati n’zotheka, timagulu ta utumiki tiyenera kukhala ndi anthu ochepa kuti woyang’anira azitha kudziwa bwino aliyense wa m’kagulu kake n’kumamuthandiza kukhala olimba mwauzimu. Koma bwanji ngati mumpingo muli akulu ochepa? M’malo mopanga magulu akuluakulu zomwe zingachititse kuti woyang’anira kagulu asamakwanitse bwinobwino udindo wake, bungwe la akulu lingakonze zoti kwa kanthawi atumiki othandiza azisamalira timagulu tina. Magulu a utumiki akakhala ang’onoang’ono, woyang’anira savutika kugwira ntchito yofunika kwambiri pa utumiki wake, yomwe ndi kuthandiza abale ndi alongo a m’kaguluko kukhala okhulupirika kwa Yehova komanso kupirira mavuto.

7. M’mipingo imene muli akulu ochepa, kodi woyang’anira kagulu angatani kuti azionetsetsa kuti aliyense m’kagulu kake akusamalidwa bwino? (1 Petulo 5:2) (Onaninso chithunzi.)

7 Ngati mumayang’anira kagulu mumpingo umene uli ndi akulu ochepa, muziphunzitsa wothandiza wanu kuti azikuthandizani kusamalira nkhosa za Mulungu. (Werengani 1 Petulo 5:2.) Muzimupatsa ntchito zina. Mwachitsanzo, nthawi zina mungamupemphe kuti atsogolere utumiki. Muzikambirana mmene ofalitsa akuchitira m’kagulu kanu. Nthawi ndi nthawi muzipita ku maulendo aubusa ndi wothandiza wanu. Musanapite, mungakambirane mmene mungakalimbikitsire ofalitsa ndipo mukabwerako muzimuyamikira pa zimene wachita bwino n’kumupatsa malangizo pa zimene angafunike kukonza. N’kupita kwa nthawi amene amakuthandizaniyo angayenerere kukhala woyang’anira kagulu. (2 Tim. 2:2) Mungapemphenso anthu ena olimba mwauzimu m’kagulu kanu kuti akuthandizeni kuphunzitsa ena. Apainiya ndi ofalitsa ena odziwa zambiri, akhoza kulowa mu utumiki ndi ofalitsa atsopano komanso osadziwa zambiri. Ndipo ofalitsa olimba mwauzimu akhoza kuthandiza ena kuyamba kucheza ndi anthu mu utumiki, kuchita maulendo obwereza komanso kuchititsa maphunziro a Baibulo. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene aliyense wa ife angachite, kuti zinthu ziziyenda bwino m’kagulu kathu ka utumiki.

Woyang’anira kagulu akuphunzitsa m’bale pogwiritsa ntchito kabuku ka “Muzikonda Anthu​—⁠Muziwaphunzitsa.”

Imodzi mwa njira zimene mkulu angaphunzitsire mtumiki wothandiza wa m’kagulu kake, ndi kumupempha kuti achititse msonkhano wokonzekera utumiki (Onani ndime 7)


MUZITHANDIZA KUTI ZINTHU ZIZIYENDA BWINO M’KAGULU KANU KA UTUMIKI

8. Kodi tingathandize bwanji kuti zinthu ziziyenda bwino m’kagulu kathu ka utumiki? (Aroma 1:12)

8 Muzipezekapo. Mukhoza ‘kulimbikitsana’ ndi Akhristu anzanu mukalowa nawo mu utumiki. (Werengani Aroma 1:12.) Kulalikira ndi anthu a m’kagulu kathu kumatithandiza kuti tikhale otetezeka komanso olimba mtima. Ngati nthawi zambiri ntchito imene mumagwira imakulepheretsani kulalikira ndi kagulu kanu, mungachite bwino kupempha abwana anu kuti akusinthireni ndandanda yogwirira ntchito. Mukhoza kudabwa ndi zimene angakuyankheni. (Neh. 2:​4-6) Ngati matenda kapena uchikulire zikukuchititsani kulephera kukumana ndi anthu a m’kagulu kanu, mungachite bwino kulankhula ndi woyang’anira kagulu. Iye angakonze zoti mulumikizane ndi anthu a m’kagulu kanu pogwiritsa ntchito vidiyokomferesi komanso kuchita ulaliki wa makalata kapena wapafoni. Kodi ndinu wachinyamata ndipo muli ndi thanzi labwino koma zimakuvutani kuti muzilowa mu utumiki nthawi zonse? Ngati ndi choncho, mungakonze zoti wiki iliyonse muzilowa mu utumiki ndi winawake wa m’kagulu kanu. Mwina mungafunike kuti muganizirenso zinthu zimene mumaziona kuti n’zofunika kwambiri kapena mungafunike kusintha mmene mumagwiritsira ntchito nthawi yanu. (Aroma 12:11; Akol. 4:5) Kuchita zimenezi kukhoza kukuthandizani kwambiri. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Iye angakupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.”—Afil. 2:13.

9. Kodi tingatani kuti anthu a m’kagulu kathu azikhala osangalala komanso azimva kuti amakondedwa? (Aroma 12:13)

9 Muzikhala ochereza. Timathandiza kuti abale ndi alongo a m’kagulu kathu azisangalala komanso azimva kuti amakondedwa ‘tikakhala ochereza.’ (Werengani Aroma 12:13.) Mwachitsanzo, tingavomere kuti misonkhano yokonzekera utumiki wa kagulu kathu izichitikira panyumba pathu. M’mipingo ina, magulu amasinthana pa nkhani yochereza mlendo wodzakamba nkhani. Ngakhale zitakhala kuti kulibe mlendo, abale ndi alongo a m’timagulu tina amakonza zoti akhale ndi macheza komanso adyere limodzi chakudya pambuyo pa misonkhano. Mpainiya wina wapadera dzina lake Sarah anati: “Ndimada nkhawa ndikaganizira zochereza anthu, ndiye kuti ndisakhale ndi nkhawa kwambiri sindilimbana ndi kuchita zinthu zambirimbiri. Ndimayesetsa kudziwana ndi anthu a m’kagulu kathu m’malo modera nkhawa kuti mwina chakudya chimene ndiphike sasangalala nacho.” Tikamayesetsa kuchita zinthu ngati anthu a m’banja limodzi komanso kucherezana m’kagulu kathu, timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso timagwirizana kwambiri.—Neh. 8:10; Mac. 20:35.

10. Kodi tingatani kuti tikhale aluso mu utumiki? (Miyambo 1:5; 27:17) (Onaninso chithunzi.)

10 Muziyamba ndi inuyo. Tikamawonjezera luso lathu pa nkhani yolalikira komanso kuphunzitsa anthu, m’pamene timasangalalanso kwambiri kulowa mu utumiki ndi kagulu kathu. Kodi pali zimene mukufunika kuchita kuti muzilalikira komanso kuphunzitsa mwaluso? Mungachite bwino kupempha munthu wina, kaya mpainiya kapena wofalitsa wina waluso m’kagulu kanu, kuti akuthandizeni. (Werengani Miyambo 1:5; 27:17.) Mungadziwitse woyang’anira kagulu kanu kuti mukufuna kuwonjezera luso lanu. Iye angakuthandizeni kuti mukwanitse cholingachi. Mungapemphenso ena kuti akuthandizeni. Mlongo wina dzina lake Heather anachita zimenezi. Ngakhale kuti ndi wamanyazi, iye anati: “Ndinapempha mpainiya wina kuti andithandize kuchita maulendo obwereza. Iye anali wachikondi komanso wokoma mtima ndipo ankalowa nane mu utumiki nthawi ndi nthawi moti anandithandiza kuyamba kuphunzira Baibulo ndi munthu wina. Ndimaona kuti ndinachita bwino kupempha ena kuti andithandize. Panopa ndimasangalala kulowa mu utumiki.” Apa n’zoonekeratu kuti pali zambiri zomwe tingachite kuti zinthu ziziyenda bwino m’kagulu kathu ka utumiki.

Mlongo wachitsikana akupempha mlongo wachikulire amene amadziwa zambiri kuti ayende naye mu utumiki.

Kagulu ka utumiki kakakhala kakang’ono zimathandiza kuti tidziwane ndi anthu ena komanso kuti tizilowa nawo mu utumiki (Onani ndime 10)


MMENE KAGULU KA UTUMIKI KAMATITHANDIZIRA

11-12. Kodi kagulu ka utumiki kamakuthandizani bwanji mwauzimu? Perekani chitsanzo.

11 Ubwenzi wabwino ndi Yehova. Dongosolo lokhala ndi timagulu ta utumiki wakumunda limathandiza tonsefe kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mwachitsanzo, woyang’anira kagulu amalimbikitsa anthu omwe Yehova amawakonda mwapadera monga akazi ndi ana amasiye ndiponso achikulire pamene akumana ndi mavuto. (1 Ates. 2:8; Yak. 1:27) Tikamalowa mu utumiki ndi kagulu kathu timaphunzira maluso amene amafunika pa ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wa Mulungu. Abale obatizidwa achitsanzo chabwino amathandizidwa kuti ayenerere maudindo ena mumpingo.—1 Tim. 3:10.

12 Taganizirani mmene kagulu ka utumiki kanathandizira Wendy yemwe tamutchula kale uja. Iye anati: “Chifukwa chakuti bambo anga ankadana ndi choonadi, nthawi zambiri sizinkatheka kuti mayi anga azilowa mu utumiki ndi kagulu kawo kumapeto kwa wiki. Komabe ineyo ankandilola kuti ndizilowa. Mlongo wina wachikulire yemwe anali mpainiya anakhala mnzanga ndipo anandithandiza kukhala ndi maluso amene mpaka pano amandithandiza ndikakhala mu utumiki komanso kumpingo. Ndimakumbukira kuti kangapo konse, woyang’anira kagulu kathu anandipatsa malangizo a m’Malemba omwe amandithandizabe mpaka pano.”

13. Kodi kagulu ka utumiki kamatithandiza bwanji kupeza anzathu omwe amatikonda komanso kutithandiza? (Onaninso chithunzi chapachikuto.)

13 Anzathu omwe amatikonda komanso kutithandiza. Timayamba kugwirizana kwambiri ndi anthu a m’kagulu kathu tikamagwira ntchito yolalikira “mogwirizana.” (Afil. 1:27) Kagulu ka utumiki kakakhala kakang’ono zimakhala zosavuta kuti anthu omwe ndi amanyazi kapena amene amachita mantha pagulu apeze anzawo apamtima. (2 Akor. 6:13) Anzathuwa amakhala odalirika ndipo amatithandiza tikakumana ndi mavuto monga matenda, kuvutika maganizo kapenanso tikakhala ndi chisoni chifukwa choferedwa. (1 Ates. 5:14) N’zosachita kufunsa kuti tikufunikira anzathu abwino pamene chisautso chikuyandikira. (Mat. 24:21) N’zoona kuti mavuto athu sangathe, komabe tikhoza kuwapirira podziwa kuti tili ndi abale amene amatikonda komanso kutithandiza.—Miy. 17:17.

Alongo apachithunzi tachiona chija amaliza kupanga msonkhano wokonzekera utumiki ndipo akulowera limodzi mu utumiki. Abale ndi alongo a m’kagulu kawo ka utumiki nawonso akukalalikira m’gawo lawo.

(Onani ndime 13)


14. Kodi kagulu kathu ka utumiki kamatithandiza bwanji tikakumana ndi zinthu zadzidzidzi?

14 Kuthandizidwa pakachitika zadzidzidzi. Abale a m’kagulu kathu amatithandiza pakagwa mliri, pakachitika ngozi zam’chilengedwe, tikafunika thandizo lachipatala, tikamazunzidwa komanso tikakumana ndi mavuto a zachuma. Mwachitsanzo, mumpingo uliwonse Komiti ya Utumiki ya Mpingo limodzi ndi oyang’anira timagulu amakonza pulani ya mmene angathandizire anthu amene akufunika kuthandizidwa mwapadera. Woyang’anira kagulu amatsogolera pa ntchito yofufuza mabanja a m’kagulu kake komanso kuona zimene mabanjawo akufunikira monga, thandizo la chipatala, madzi, pokhala komanso zovala n’kuonetsetsa kuti alandira thandizo loyenera. Kunena zoona kagulu ka utumiki wakumunda kamatithandiza kwambiri.

15. N’chiyani chimathandiza kuti tonse m’gulu la Yehova tizigwirizana?

15 Monga tafotokozera kale, gulu la Yehova ndi lalikulu kwambiri. Mbali yakumwamba yokha ili ndi angelo okhulupirika mamiliyoni mwinanso mabiliyoni. Pamene mbali yapadziko lapansi ili ndi anthu oposa 9 miliyoni omwe akuwonjezereka tsiku lililonse. (Zek. 8:23; Chiv. 5:11) Atumiki onse a Yehova amachita zinthu mogwirizana pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Chiv. 14:​6, 7) Tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe kuti dongosolo lokhala ndi timagulu ta utumiki wakumunda lizitithandiza kwambiri, makamaka pa nkhani yotamanda Yehova ndi mtima wathu wonse.—Sal. 111:1.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi woyang’anira kagulu ndi womuthandiza wake amatani kuti azisamalira abale ndi alongo a m’kagulu kawo?

  • Kodi tingatani kuti tizithandiza kuti zinthu ziziyenda bwino m’kagulu kathu ka utumiki?

  • Kodi dongosolo lokhala ndi timagulu ta utumiki limatithandiza bwanji?

NYIMBO NA. 61 Pitani Patsogolo Mboninu!

a Mayina ena asinthidwa.

b Ngati pakufunikira, mtumiki wothandiza woyenerera akhoza kumasamalira kagulu mpaka mkulu atapezeka. Mtumiki wothandiza yemwe amagwira ntchito imeneyi amatchedwa mtumiki wa kagulu chifukwa choti si mkulu. Iye amagwira ntchitoyi moyang’aniridwa ndi akulu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena