AUGUST 17-23, 2026
NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana
Tingatani Kuti Tipitirize Kugwirizana ndi Akhristu Anzathu?
“Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa komanso kuleza mtima.”—AKOL. 3:12.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene tingachite kuti tilimbane ndi mavuto amene angachititse kuti tisiye kugwirizana ndi Akhristu anzathu.
1. Kodi anzathu enieni tingawapeze kuti?
“MASIKUWA moyo ukuvuta, patokha n’zovuta. Yehova amadziwa tikufunika mabwenzi.” Kodi mwakumbukira mawu amenewa omwe ali kumayambiriro kwa nyimbo ya mu Broadcasting yakuti “Mabwenzi Enieni”? Ndi mwayi waukulu kupeza anzathu enieni m’gulu la Yehova. (Sal. 119:63) Tili m’banja lauzimu lomwe anthu ake amakondana.
2. Kodi timafuna kuti tikhale pa ubwenzi wotani ndi Akhristu anzathu?
2 Timafuna kuti tizigwirizana kwambiri ndi Akhristu anzathu osati kungowadziwa mwapamwamba chabe. Tili m’banja la anthu amene amakonda kwambiri Yehova ndi Yesu ndipo chikondi chimenechi ndi chomwe chimatigwirizanitsa. (Yoh. 13:35) Sikuti zimangochitika zokha kuti tizigwirizana ndi Akhristu anzathu. Pamafunika khama. Koma popeza tonsefe si angwiro, nthawi zina pangakhale mavuto omwe angachititse kuti tisiye kugwirizana.
3. N’chifukwa chiyani nthawi zina zingakhale zovuta kuti tipitirize kugwirizana ndi Akhristu anzathu?
3 N’zoona kuti tingamagwirizane kwambiri ndi anthu ena kuposa ena, mwina chifukwa choti timakonda, kuganiza komanso kuchita zinthu m’njira yofanana. Koma tingamaonenso kuti n’zovuta kupitiriza kugwirizana ndi abale ndi alongo ena. Nthawi zina tingasemphane maganizo ndipo zimenezi zingachititse kuti tisamagwirizane. Mwina chifukwa choti timasiyana kwambiri mmene timaganizira komanso mmene timachitira zinthu, sitingamasangalale kuchita nawo zinthu limodzi. Ndipo nthawi zina tingamavutike kugwirizana ndi ena ngati akudwala matenda aakulu kapena ngati akuvutika maganizo. Munkhaniyi, tikambirana mmene chitsanzo cha Yesu chingatithandizire kupitiriza kugwirizana ndi anzathu pakakhala mavuto. Koma choyamba tiyeni tione mmene makhalidwe a Chikhristu angatithandizire kuti tipitirize kugwirizana ndi abale ndi alongo.
MAKHALIDWE A CHIKHRISTU AMATITHANDIZA KUTI TIPITIRIZE KUGWIRIZANA NDI ANZATHU
4. Tingatani kuti tizigwirizana kwambiri ndi anzathu?
4 Kuti tizigwirizana kwambiri ndi Akhristu anzathu, tiziona makhalidwe awo abwino. Njira imodzi imene ingatithandize ndi kupeza nthawi yochitira nawo zinthu limodzi. Mtumwi Paulo ankafunitsitsa kuonana ndi abale ndi alongo ake. Iye analembera Akhristu a ku Tesalonika kuti: “Tinayesetsa kwambiri kuti tikuoneni pamasomʼpamaso.” (1 Ates. 2:17) Ambiri amaona kuti kucheza pamasom’pamaso kumathandiza kuti azigwirizana kwambiri ndi anzawo. Timachita zimenezi tikamagwira nawo ntchito yolalikira, kupezeka pamisonkhano ya mpingo, misonkhano yadera komanso misonkhano ikuluikulu. Komabe kungochitira limodzi zinthu ndi anzathu pakokha sikungachititse kuti tisakumane ndi mavuto amene angasokoneze mgwirizano wathu.
5. N’chiyani chingatithandize kuti tipitirize kugwirizana ndi anzathu pakachitika zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wathu? Perekani chitsanzo. (Akolose 3:12)
5 Makhalidwe a Chikhristu angatithandize kuti tipitirizebe kugwirizana ndi anzathu ngakhale kuti pali zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathuwo. (Werengani Akolose 3:12.) Tikamayesetsa kukhala odzichepetsa, oleza mtima, okoma mtima komanso achifundo, tikhoza kuthana ndi mavuto amene angachititse kuti tisiye kugwirizana ndi anzathu. Mwachitsanzo, kuti zitsulo zamuinjini zisamakhulane pamafunika oilo. Mofanana ndi zimenezi, makhalidwe a Chikhristu amatichititsa kupewa mavuto amene angachititse kuti tisamagwirizane. Tsopano tiyeni tikambirane mavuto atatu amene angasokoneze ubwenzi wathu ndi Akhristu anzathu. Ndipo tiona mmene kutsanzira makhalidwe a Yesu monga kudzichepetsa, kukoma mtima, kuleza mtima komanso chifundo angatithandizire kuti tizigwirizana kwambiri ndi anzathu.
MUKASEMPHANA MAGANIZO
6. Kodi kusemphana maganizo kungasokoneze bwanji ubwenzi wathu?
6 Vuto limene limakhalapo. Pakakhala kusemphana maganizo, aliyense akhoza kumaona kuti maganizo ake ndi olondola. Taganizirani za abale awiri amene akusiyana maganizo pa nkhani ya njira yabwino ya mmene kagulu kawo ka utumiki kangamagwirire ntchito yolalikira. Aliyense akuona kuti njira yakeyo ndi yabwino kwambiri. Kodi mukutha kuona kuti zimenezi zingachititse kuti zikhale zovuta kuti apitirize kumagwirizana? Mtima wonyada ukhoza kuwasokoneza. Ngati sangakambirane bwinobwino n’kuithetsa nkhaniyi, akhoza kuyamba kusungirana zifukwa. Nthawi ikamapita, angasiye kuchitira zinthu limodzi mpaka kusiyiratu kugwirizana chifukwa cha nkhani yaing’ono ngati imeneyi.
7. Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kudziwa kuti kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti athetse kusamvana?
7 Zimene tingaphunzire pa kudzichepetsa kwa Yesu. Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti kudzichepetsa ndi khalidwe lofunika kwambiri akamafuna kuthetsa kusamvana. Kwa kanthawi ndithu, iwo ankakangana pa nkhani ya amene anali wamkulu pakati pawo. Ophunzirawo ankaona kuti kukhala wamkulu n’kofunika kwambiri. Pofuna kuwathandiza, Yesu anawauza kufunika koti aziona ena kukhala owaposa. (Mat. 20:25-28) Apatu ankawaphunzitsa kuti akhale odzichepetsa. Ngakhale usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu ‘anawapatsa chitsanzo’ posambitsa mapazi awo, ntchito imene inkagwiridwa ndi akapolo. (Yoh. 13:3-5, 12-16) Pochita zimenezi, anawathandiza kudziwa zimene angachite kuti apitirize kugwirizana ndi anzawo. Zikanakhala kuti ankaona ena kukhala owaposa, sakanavutika kuti azilolera akasemphana maganizo komanso azigwirizana ngakhale pamene akuona zinthu mosiyana.
8. Kodi kudzichepetsa kungakuthandizeni bwanji kuti muzigwirizanabe ndi Akhristu anzanu mukasemphana maganizo? (Akolose 3:13) (Onaninso zithunzi.)
8 Zimene mungachite kuti musasiye kugwirizana. Kudzichepetsa kungakuthandizeni kuti muzingonyalanyaza zinthu zing’onozing’ono zimene mwasemphana maganizo n’kukhululukirana ndi mtima wonse. (Werengani Akolose 3:13.) Kungakuthandizeninso kuti musamafulumire kukwiya, zomwe zingachititse kuti muzigwirizanabe. (Sal. 4:4) Ngakhale mnzanu atakulankhulani mawu opweteka, muzikumbukira kuti tonsefe timalankhula zinthu zomwe timanong’oneza nazo bondo. (Mlal. 7:21, 22) Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi chofunika kwambiri n’chiyani pakati pa kukakamira maganizo oti ndine wosalakwa ndi ubwenzi wathu?’ Nthawi zina mumangofunika kulolera maganizo a mnzanuyo. Mukhoza kukhala ndi mtendere wamumtima ngati mutasankha kuti musamangoganizira za nkhaniyo kapena kudzailankhulanso m’tsogolo.
Kudzichepetsa kungakuthandizeni kuti muzinyalanyaza zinthu zing’onozing’ono zomwe mwasemphana maganizo komanso kukhululukirana ndi mtima wonse (Onani ndime 8)a
9. Kodi kudzichepetsa kungakuthandizeni bwanji ngati mukulephera kuthetsa kusamvana? (Miyambo 17:9)
9 Kudzichepetsa kungakuthandizeninso ngati mukulephera kuthetsa kusamvana. Musamakangane ndi ena pongofuna kusonyeza kuti maganizo anu ndi olondola. (Werengani Miyambo 17:9; 1 Akor. 6:7) Muzikhala ndi cholinga choti mupitirizebe kugwirizana ndi mnzanuyo. Ambiri zinthu zimawayendera bwino akasankha zoti akambirane n’kuthetsa vutolo. (Sal. 34:14) Mwina munganene kuti, ‘Iwe ndi ine tinadziwana kalekale, bwanji tingokambirana nkhaniyi?’ Muzikhala okonzeka kuvomereza kuti pali zinthu zimene inunso munalakwitsa. Muzivomerezanso kuti munakhumudwitsa mnzanuyo n’kupepesa. Ndipo ngati m’bale kapena mlongo wanuyo nayenso akupepesa, muzivomereza modzichepetsa. (Luka 17:3, 4) Muzikumbukira kuti cholinga chanu sikupeza wolakwa kapena wosalakwa koma kuthetsa kusamvana n’kupitiriza kugwirizana ndi mnzanuyo.—Miy. 18:24.
NGATI MUMAGANIZA KAPENA KUCHITA ZINTHU MOSIYANA
10. N’chiyani chingachititse kuti zikhale zovuta kuti tipitirize kugwirizana ndi anzathu?
10 Vuto limene limakhalapo. Tingamavutike kupitiriza kugwirizana ndi anzathu amene amachita kapena kuona zinthu m’njira yosiyana ndi ifeyo. Ena akhoza kukhala ndi makhalidwe omwe satisangalatsa. Enanso angamavutike kuchita zinthu ndi anzawo chifukwa choti ankachitiridwa nkhanza m’mbuyomo kapena chifukwa choti akuchokera m’zikhalidwe zimene anthu ake samasuka kwenikweni kapenanso amamasuka kwambiri. Tikhozanso kukhala ndi umunthu wosiyana. Mwina ife ndi amanyazi pamene anzathuwo amamasuka ndi anthu.
11. Kodi Yesu ankakwanitsa bwanji kumagwirizanabe ndi anzake omwe anali ndi makhalidwe osiyana ndi ake?
11 Zimene tingaphunzire pa kuleza mtima kwa Yesu. Iye anapitiriza kugwirizana ndi anzake omwe anali ndi makhalidwe osiyana ndi ake. Mwachitsanzo, mtumwi Yakobo ndi Yohane anasonyeza kudzikuza pamene anapempha malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. (Maliko 10:35-37) Mosiyana ndi zimenezi, Yesu anadzichepetsa n’kusiya udindo wapamwamba komanso ntchito yapadera yomwe anali nayo kumwamba n’kubwera padzikoli. (Afil. 2:5-8) Apatu anasonyeza kuti anali ndi makhalidwe osiyana kwambiri ndi a Yakobo ndi Yohane. Ngakhale zinali choncho, Yesu ankalezera mtima Yakobo, Yohane komanso atumwi ena.
12. Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuti azichita zinthu moleza mtima ndi anzake?
12 Yesu sankayembekezera zinthu zomwe anzake sangakwanitse. Iye ankadziwa kuti zimene Yakobo ndi Yohane anapempha zinkasonyeza maganizo ampikisano omwe ophunzira ambiri anali nawo. (Maliko 9:34) Yesu ankamvetsa chifukwa chake ophunzirawo ankaganiza choncho. Mofanana ndi iwowo, nayenso anakulira m’chikhalidwe chimene anthu ake ankaona kuti kutchuka ndi udindo n’zofunika kwambiri. Iye ankawalezera mtima ndipo sankayembekezera kuti asintha kamodzin’kamodzi maganizo onyada komanso odzikuza omwe anali atakhala nawo kwa zaka zambiri.—Maliko 10:42-45.
13. Kodi kuleza mtima kungatithandize bwanji kuti tipitirizebe kugwirizana ndi anzathu? (Aefeso 4:2)
13 Zimene mungachite kuti mupitirizebe kugwirizana ndi anzanu. Mungasonyeze kuti mukuyesetsa kupitiriza kukhala oleza mtima, pongovomereza kuti anthu ena ali ndi makhalidwe enaake omwe sakusangalatsani. (Miy. 14:29) Tonsefe tili ndi makhalidwe enaake omwe si olakwika kwenikweni koma zangokhala kuti ndi mmene tilili basi. Ndiye timayamikira anthu ena akamatimvetsa. (Werengani Aefeso 4:2.) Komanso tizikumbukira kuti anthu ena sangamachite zinthu ndendende ngati ifeyo. Taganiziraninso khama limene limafunika kuti munthu wosalankhulalankhula komanso wamanyazi akwanitse kucheza ndi anthu ena. Ngakhale zili choncho, mumafunikanso kulezera mtima munthu amene ndi wolankhulalankhula komanso womasuka kwambiri. Sitingayembekezere kuti munthu aliyense akhale mnzathu wapamtima. Koma tizikumbukira kuti ngakhale Akhristu amene ali ndi makhalidwe osiyana kwambiri akhoza kumachita zinthu mogwirizana.
14. Kodi kuleza mtima kumatithandiza kuti tiziganizira kwambiri za chiyani?
14 Kuleza mtima kumatithandiza kuti tiziganizira kwambiri makhalidwe abwino amene anzathu ali nawo. Zimenezi zimatithandiza kuti tisalole kuti kusiyana makhalidwe kutilepheretse kumagwirizana nawo. Ngakhale kuti Yakobo ndi Yohane ankafuna malo apamwamba, maganizo awowa anasonyeza kuti ankaona kuti Ufumu wa kumwamba ndi weniweni. Yesu anadziwa zimenezi ndipo anaona kuti ali ndi chikhulupiriro. Tikamaona zabwino mwa anzathu timakhala kuti tikutsanzira Yesu komanso Atate wake, Yehova.
15. Kodi ndi ndani angatithandize kuti tipitirize kugwirizana ndi anzathu omwe ali ndi makhalidwe osiyana ndi athu?
15 Chofunika kwambiri n’chakuti tizipempha Yehova kuti atithandize kuti tipitirizebe kugwirizana ndi anzathu omwe ali ndi makhalidwe osiyana ndi athu. Muzioneratu mavuto amene angakhalepo ndipo muzipemphera kuti mavutowo akadzabwera, mudzakhale odekha. Muzikumbukira kuti Mlengi wathu Yehova, amadziwa kuti aliyense wa ife ndi wosiyana ndi mnzake. Ndiye mukamapemphera, musamakayikire kuti Yehova akudziwa zimene mukufunikira kuti mupitirize kupirira. Ngati mukuona kuti zikukuvutani kukhala woleza mtima, muzipempha kuti akupatseni mzimu woyera kuti ukuthandizeni kuchita zinthu modekha.—Luka 11:13; Agal. 5:22, 23.
ABALE NDI ALONGO ATHU AKAKUMANA NDI MAVUTO
16. Kodi abale ndi alongo athu angatichitire zotani ngati akumana ndi vuto linalake?
16 Vuto limene limakhalapo. Abale ndi alongo athu akamadwala kapena akamavutika ndi nkhawa, angachite zinthu zotikhumudwitsa. Mwachitsanzo, angamafune kukhala paokha, sangamachedwe kukhumudwa komanso akhoza kuchita zinthu zomwe sitimayembekezera. Mwinanso angalankhule kapena kuchita zinthu zomwe zingatikhumudwitse. (Yobu 6:2, 3) Popeza sitimadziwa mavuto amene abale ndi alongo athu akukumana nawo, nthawi zina tingamayembekezere zambiri kuchokera kwa iwo.
17. Kodi tikuphunzira chiyani pa mmene Yesu anachitira zinthu ndi Batimeyu amene anali ndi vuto losaona?
17 Zimene tingaphunzire pa kukoma mtima komanso chifundo cha Yesu. Iye ankachita zinthu mokoma mtima komanso mwachifundo ndi anthu amene akuvutika ngakhale omwe anali asanakumanepo nawo. Mwachitsanzo, taganizirani mmene anachitira zinthu ndi Batimeyu yemwe anali ndi vuto losaona. Iye atamva kuti Yesu akudutsa anayamba kukuwa n’cholinga choti Yesuyo amuone. Anthu ena omwe anali pagululo anauza Batimeyu kuti akhale chete. Koma popeza ankafunitsitsa kuti Yesu amuchiritse, iye anapitiriza kukuwa. N’kutheka kuti anthu ena pagululo sanasangalale ndi zimene Batimeyu anachitazi. Komabe, Yesu ‘anagwidwa ndi chifundo,’ moti ankafunitsitsa kumuthandiza. (Mat. 20:34; Maliko 10:46-52) Iye analankhula ndi Batimeyu mokoma mtima ndipo anamuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro chake. Kenako anachita zodabwitsa n’kumuthandiza kuti ayambirenso kuona.
18. Kodi muyenera kuchita bwanji zinthu ndi anzanu amene akuvutika? (1 Atesalonika 5:14)
18 Zimene mungachite kuti mupitirize kugwirizana ndi anzanu. Muzikhala okoma mtima komanso achifundo. Makhalidwe amenewa angakuthandizeni kuti “muzilankhula molimbikitsa” kwa abale ndi alongo amene akudwala kapena amene akuvutika ndi nkhawa. (Werengani 1 Atesalonika 5:14.) Muzikumbukira kuti mnzako weniweni ndi amene amakhala wokonzeka kukuthandiza makamaka “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Mnzako weniweni amakumvera chisoni ukamakumana ndi mavuto komanso amachita zonse zimene angathe pokuthandiza ukakhala ndi nkhawa, pokulankhula mawu olimbikitsa komanso kukupatsa thandizo limene ungafunikire.
19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okoma mtima komanso achifundo? (Onaninso zithunzi.)
19 Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe tingachite posonyeza kukoma mtima komanso chifundo? N’zoona kuti sitingathe kuthetsa ululu umene mnzathu akumva. Koma tingayesetse kumvetsa mmene akumvera komanso mmene zinthu zilili pa moyo wake. (Mat. 7:12; 1 Pet. 3:8) Tizimumvetsera akamatifotokozera zimene akukumana nazo. Tiziyesetsa kupeza mawu omwe angamulimbikitse ngati pakufunika kutero. (Miy. 12:25) Tisamafulumire kuganiza kuti tikudziwa zonse zomwe zikumuchitikira. (Miy. 18:13) Tizichita naye zinthu moleza mtima ndipo tisamayembekezere zinthu zomwe sangakwanitse.—Aef. 4:32.
Anzathu enieni amatitonthoza mwachifundo komanso mokoma mtima (Onani ndime 19)
20. Kodi mumafuna kuti anthu ena aziona kuti ndinu mnzawo wotani?
20 Timaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kukhala ndi abale ndi alongo omwe ndi anzathu apamtima. Koma tizikumbukira kuti chifukwa choti si ife angwiro, nthawi zina tikhoza kuchita zinthu zomwe sitimafuna kuchita. Ambirife tinakumanapo ndi zinthu zokhumudwitsa zomwe zinakhudza mmene timachitira zinthu. Choncho timayamikira abale ndi alongo amene amapitirizabe kukhala anzathu n’kumachita nafe zinthu modzichepetsa, moleza mtima, mokoma mtima komanso mwachifundo. Tiyeni ifenso tiziyesetsa kuti anthu ena akamationa, aziona kuti ndife mnzawo wotero.
NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse
a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale wachikulire komanso m’bale wachinyamata, asiyana maganizo pa nkhani ya mmene angagawire gawo la mpingo wawo. Kenako akulalikira limodzi mosangalala.