AUGUST 31–SEPTEMBER 6, 2026
NYIMBO NA. 89 Mvera Kuti Udalitsidwe
Muzimvetsera Mwatcheru Kwambiri
“Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.”—LUKA 8:18.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona chifukwa chake timafunika kumamvetsera mwatcheru tikakhala pamisonkhano ndiponso pa zochitika zina zauzimu komanso mmene tingachitire zimenezi.
1-2. (a) Kodi masiku ano Yehova amasamalira bwanji anthu ake mwauzimu? (Salimo 23:1, 2, 5) (b) Kodi tikambirana chiyani zokhudza misonkhano ya Chikhristu?
MASIKU ano Yehova amatipatsa chakudya chauzimu chambiri. Moti tikugwirizana ndi zimene Davide ananena pamene anaimba kuti: “Yehova ndi Mʼbusa wanga. Sindidzasowa kanthu.”—Werengani Salimo 23:1, 2, 5.
2 Chimodzi mwa zinthu zimene Yehova akugwiritsa ntchito potipatsa chakudya chauzimu ndi misonkhano ya mpingo. Nthawi zambiri pamisonkhanoyi timaphunzira zinthu zimene tikuzidziwa kale. Komabe ngakhale kuti ndife “olimba mʼchoonadi,” timafunika kukumbutsidwa mfundo za Yehova. (2 Pet. 1:12) Koma kodi mwina zimakuvutani kumvetsera mwatcheru, zikakhala kuti mfundo zimene mukuphunzira mwakhala mukuziphunzira mobwerezabwereza? Ngati ndi choncho, nkhaniyi ikuthandizani. Tikambirana chifukwa chake timayenera kumamvetsera mwatcheru tikakhala pamisonkhano. Tikambirananso zimene anthu amene amaphunzitsa mumpingo angachite kuti azithandiza ena kumamvetsera mwatcheru. Ndipo tionanso mfundo zina zomwe zingatithandize kuti tizimvetsera mwatcheru. Koma choyamba, tiyeni tidziwe amene amatiphunzitsa tikhala pamisonkhano.
MUZIKUMBUKIRA KUTI YEHOVA NDI AMENE AMATIPHUNZITSA
3. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito chiyani polankhula nafe, nanga atumiki ake amatani kuti azigwiritsa ntchito bwino Mawu ake?
3 Yehova amalankhula nafe pogwiritsa ntchito Mawu ake Baibulo. (2 Tim. 3:16, 17) Yesu ankadziwa bwino mfundo imeneyi. Iye ankagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwaluso moti anthu omwe ankamumvetsera anafunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu Malemba amenewa anawadziwa bwanji, popeza sanapite kusukulu?” (Yoh. 7:15) Anthu amtima wabwino ankasangalala akamva Yesu akuphunzitsa Mawu a Mulungu. Nawonso Akhristu a m’nthawi ya atumwi monga Paulo ndi Apolo ankagwiritsa ntchito Malemba akamakambirana ndi anthu. (Mac. 17:2, 3; 18:24, 28) Nafenso a Mboni za Yehova nkhani zimene timatulutsa, mavidiyo a pa JW Broadcasting, ma autilaini a nkhani komanso mavidiyo ena mfundo zake zimachokera m’Baibulo. Alendo ambiri akafika pamisonkhano yathu, amachita chidwi akaona mmene anthu a Yehova amagwiritsira ntchito Baibulo. Anthu amene amapatsidwa mbali pamisonkhano amagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pophunzitsa. Sikuti iwo amangowerenga Mawuwo koma amathandizanso omvera kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo zake.—Luka 24:32.
4. Kodi mawu akuti “kumva” komanso “kumvetsera” amatanthauza chiyani?
4 Nthawi zambiri m’Baibulo mawu akuti “kumva” komanso “kumvetsera” amatanthauza kumvera winawake. Yehova akamatilankhula pogwiritsa ntchito Mawu ake tikakhala pamisonkhano, ife n’kumvetsa zimene akufuna kuti tizichita, zimakhala zosavuta kumumvera. Sitikayikira kuti Yehova amasangalala tikamamvetsera zimene akutiuza komanso kuchita zimene akutiuzazo.—Miy. 27:11.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAFUNIKA KUMAMVETSERA MWATCHERU TIKAKHALA PAMISONKHANO?
5. Kodi kukonda Yehova kumatilimbikitsa kuchita chiyani? (Yohane 4:23, 24; 1 Yohane 5:3)
5 Timamvetsera tikakhala pamisonkhano chifukwa timakonda Yehova. (Mat. 22:37) Tikamaphunzira zambiri zokhudza Yehova m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri. Chikondi chimenechi chimatilimbikitsa kuti tikhale ofunitsitsa kumumvetsera, kumumvera komanso kumulambira m’njira imene iyeyo amatiuza m’Mawu ake.—Werengani Yohane 4:23, 24; 1 Yohane 5:3.
6. Kodi timaphunzira zotani zokhudza kuthandiza ena tikakhala pamisonkhano yathu?
6 Timamvetsera tikakhala pamisonkhano chifukwa timakonda anthu. (Mat. 22:39) Pamisonkhano yathu, Yehova amatiphunzitsa mmene tingathandizire Akhristu anzathu komanso anthu omwe samudziwa. Mwachitsanzo, kabuku kakuti Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa kamatithandiza kukhala ndi makhalidwe omwe amachititsa kuti zinthu zizitiyendera bwino mu utumiki. Kodi nthawi zina mumavutika kuyamba kucheza ndi anthu? Ngati ndi choncho, muzichita chidwi abale ndi alongo akamachita zitsanzo pamisonkhano yamkati mwa wiki.
7. N’chifukwa chiyani timafunika kupitirizabe kumvera Yehova?
7 Timamvetsera tikakhala pamisonkhano chifukwa timakonda moyo wathu. Mogwirizana ndi zimene Yehova anauza atumiki ake akale, ngati tikufuna kukhala ndi moyo wosangalala komanso kudzapeza moyo wosatha, tizimvera Mawu ake. (Deut. 32:44-47) Tikamamvetsera pamisonkhano yathu timalimbikitsidwa ndipo zimatithandiza kuti tiziyembekezera mopirira dziko latsopano. (Aroma 8:25) Panopa m’pamene tikufunika kwambiri kumamvera Yehova chifukwa tikukhala m’masiku otsiriza ndipo tiyenera kukhala maso mwauzimu.—Mat. 24:42-44; Chiv. 1:3.
TIZITHANDIZA ANTHU ENA KUTI AZIMVETSERA PAMISONKHANO
8. N’chifukwa chiyani abale amene amakamba nkhani papulatifomu amafunika kuwonjezera luso lawo lophunzitsa?
8 Abale amene amakamba nkhani papulatifomu, makamaka nkhani za onse, ayenera kupitiriza kuwonjezera luso lawo lophunzitsa. M’bale akakonzekera bwino nkhani, n’kuonetsetsa kuti mfundo zake zikuchokera m’Baibulo, akhoza kuthandiza anthu omwe si a Mboni kuphunzira choonadi komanso Akhristu anzake kupitiriza kukonda choonadi. Ndipo ngati mwapatsidwa mbali pamisonkhano, muzikumbukira kuti mbali yanuyo ikhoza kuthandiza anthu ena kuposa mmene mungaganizire. Ngati mwapatsidwa mwayi wokamba nkhani, taonani mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zotsatirazi. Ngakhale kuti mfundozi zakonzedwera abale amene amakamba nkhani za onse, zikhoza kuthandiza aliyense amene wapatsidwa nkhani pamisonkhano.—2 Tim. 4:2; Tito 1:9.
9. Kodi mungatani kuti nkhani yanu izikhala yotsatirika?
9 Muzisanja mfundo zanu m’njira yotsatirika. Muzikamba nkhani m’njira yoti omvera asamavutike kuitsatira. Ngati nkhani yanu itakhala ndi mfundo zambiri, omvera anu akhoza kusokonezeka. Ndiye kodi mungatani kuti nkhani yanu izikhala yotsatirika? Muzitsatira mfundo izi: (1) Mukamayamba nkhani yanu, muziwadziwitsa omvera anu mfundo zikuluzikulu za munkhaniyo. (2) Muzifotokoza mfundozo imodzi ndi imodzi ndipo mukamaliza mfundo imodzi yaikulu, muziima kaye kenako n’kutchula mfundo yotsatira musanayambe kuifotokoza. (3) Muzibwereza mfundozo mwachidule kumapeto kwa nkhani yanu.
10. N’chifukwa chiyani mumafunika kufika pokonda kwambiri mfundo za munkhani yanu?
10 Muzikonda mfundo zimene zili munkhani yanu. Zimakhala zosavuta kuti mfundo zimene mumazikonda muzifotokoze ndi mtima wonse. (Miy. 2:4, 5; Mac. 4:20) Kuti zimenezi zitheke, mumafunika kuganizira kwambiri Malemba komanso mfundo zimene zili munkhaniyo. M’bale wina wa ku United States wazaka za m’ma 70 amakumbukirabe nkhani imene anamvetsera ali wachinyamata. Iye ananena kuti: “M’bale amene anakamba nkhaniyo anatilimbikitsa kuti tiziganizira mozama tikamawerenga Mawu a Mulungu. Ankalankhula ndi mtima wonse ndipo anatifotokozera momveka bwino mmene tingachitire zimenezi. Nkhaniyo inasintha kwambiri moyo wanga ndipo inandithandiza kusintha mmene ndinkawerengera Baibulo moti ndinakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.”
11. N’chifukwa chiyani wokamba nkhani ayenera kufotokoza mwachindunji mmene abale ndi alongo angagwiritsire ntchito mfundo za munkhani yake? (1 Tim. 4:13-16)
11 Muziganizira mfundo zimene omvera anu akufunikira ndipo muziwafotokozera mmene angazigwiritsire ntchito. M’malo mofotokoza mfundo mozungulira, muzigwiritsa ntchito Malemba polimbikitsa omvera anu komanso kuwathandiza kudziwa zoyenera kuchita. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauza Timoteyo zinthu zingapo mwachindunji zomwe zikanamuthandiza kukhalabe wolimba mwauzimu pamene ankachita utumiki wake ku Efeso. (Werengani 1 Timoteyo 4:13-16.) Choncho muziganizira zomwe omvera anu akufunikira ndipo muziwathandiza kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo za munkhani yanu pa moyo wawo.
12. N’chifukwa chiyani mumafunika kulankhula mwachibadwa mukamakamba nkhani?
12 Muziyeserera nkhani yanu mokweza mawu kuti mudzaikambe m’njira yokambirana. Zimakhala zosavuta kuti anthu azimvetsera komanso kutsatira mfundo za munkhani yanu ngati mukuikamba mwachibadwa m’malo molemba chilichonse chomwe mukufuna kulankhula n’kumakangowerenga. Kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso kamanena kuti: “Muzilankhula mwachibadwa komanso kuchokera mumtima kuti anthu adziwe mmene nkhaniyo ikukukhudzirani komanso kuti mumawaganizira.” Mukamalankhula kuchokera mumtima omvera anu amamvetsera mwatcheru, amasangalala ndi nkhani yanu ndipo amafunitsitsa kugwiritsa ntchito mfundo zake pa moyo wawo.
13. N’chifukwa chiyani anthu omwe amakamba nkhani mumpingo amayenera kupempha malangizo kwa abale aluso omwe akhala akukamba nkhani kwa nthawi yaitali? (Onaninso chithunzi.)
13 Muzipempha malangizo kwa m’bale waluso yemwe wakhala akukamba nkhani kwa nthawi yaitali. Mungachite zimenezi pomuonetsa m’baleyo zomwe mwakonzekera musanakaikambe nkhaniyo kenako n’kugwiritsa ntchito zimene angakuuzeni pokamba nkhaniyo. Mungamupemphenso kuti amvetsere nkhani yanu n’cholinga choti akuuzeni zimene mungakonze kuti mukhale mphunzitsi waluso. (Miy. 1:5) Nthawi zina sitingadziwe zinthu zomwe tikufunika tikonze komanso ngati tikufotokoza mfundozo m’njira yomveka bwino yoti zithandize anthu. Choncho timafunika kuwonjezera luso lathu lophunzitsa kuti amene akutimvetsera azipeza mfundo zomwe zingawathandize m’Mawu a Mulungu.a
Muzipempha m’bale waluso yemwe wakhala akukamba nkhani kwa nthawi yaitali kuti akuthandizeni (Onani ndime 13)
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIMVETSERA MWATCHERU
14. N’chifukwa chiyani timafunika kukhala ndi maganizo ofanana ndi a munthu amene analemba Salimo 119? (Salimo 119:24, 111, 167)
14 Tingamamvetsere mwatcheru ngati timayamikira mfundo zimene Yehova amatikumbutsa. Timafunika mfundo za Yehova kuti tikwanitse kupirira mavuto amene tikukumana nawo ‘m’nthawi yapadera komanso yovutayi.’ (2 Tim. 3:1) Ngati nthawi zina timaona kuti mfundo zimene zikufotokozedwa tinazimvapo kambirimbiri, tiyenera kukhala ndi maganizo a munthu amene analemba Salimo 119, okhudza mfundo zimene Yehova amatikumbutsa.—Werengani Salimo 119:24, 111, 167.
15. Kodi tingatani kuti tipitirize kuyamikira chakudya chauzimu chimene timalandira pamisonkhano?
15 Timafunika kupitiriza kuona moyenera chakudya chauzimu chimene timalandira, ngati mmene zinalili ndi Aisiraeli, omwe ankafunika kupitiriza kumaona moyenera mana amene Yehova ankawapatsa m’chipululu. (Eks. 16:15, 31) N’zosachita kufunsa kuti poyamba Aisiraeli ankasangalala ndi mana. Chakudyachi chinali chochokera kwa Yehova, chinali chokoma komanso chinkawathandiza kukhala ndi moyo. Komabe n’kupita kwa nthawi Aisiraeli ena anatopa ndi kudya mana tsiku lililonse. (Num. 21:5) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Ifenso chakudya chauzimu chimene timapatsidwa pamisonkhano takhala tikuchilandira mobwerezabwereza komabe sitikuyenera kumachiona kuti ndi chosafunika. M’malomwake, tiyenera kumakumbukira kuti chimachokera kwa Yehova. Tizikumbukiranso kuti kapolo wokhulupirika amasankha mosamala zimene tikuyenera kuphunzira pamisonkhano. Komanso tisamaiwale kuti zimene timaphunzira zimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru ndiponso kudzapeza moyo wosatha.—Miy. 3:13, 16-18; Yoh. 17:3.
16. Kodi n’chiyani chathandiza anthu omwe akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali kuti azimvetsera mwatcheru pamisonkhano? (Onani bokosi lakuti “Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzimvetsera Mwatcheru.”)
16 Pali mfundo zingapo zimene tingatsatire kuti tizimvetsera mwatcheru. Taonani zimene zathandiza anthu ena omwe akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali kuti azimvetsera mwatcheru akakhala pamisonkhano. Ashley amene wakhala akutumikira Yehova kwa zaka 30 ananena kuti: “Nkhani yagona pa kukonzekera. Ngati sindinakonzere zimandivuta kuyankha komanso maganizo anga amangoyendayenda.” József yemwe wakhala akutumikira Yehova kwa zaka 52 ananena kuti: “Ndimasangalala kumvetsera nkhani zimene ndikuzidziwa kale chifukwa zimandithandiza kuti ndiyambe kuziona komanso kuzimvetsa mwanjira ina.” Iye ananenanso kuti: “Ngati m’bale yemwe akukamba nkhani si waluso kwenikweni, ndimaganizira kwambiri za uthenga wa m’Baibulo umene akufotokoza osati mmene akuphunzitsira.”
17. Kodi mungatani kuti muzimvetsera mwatcheru pamisonkhano? (Onaninso chithunzi.)
17 Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti muzimvetsera mwatcheru pamisonkhano: (1) Ngati mumafunika kudya musanapite kumisonkhano, muzidya chakudya chopepuka kuti musamakagone. (2) Muzipita mofulumira ndipo muzipeza malo okhala misonkhano isanayambe. (3) Muzitchera foni kapena tabuleti yanu kuti isakusokonezeni misonkhano ili m’kati. (4) Muziganizira mfundo zimene muphunzire. (5) Muziyesetsa kuyang’ana wokamba nkhani. (6) Muzilemba notsi zachidule kapena kujambula zithunzi zomwe zingakukumbutseni mfundo zikuluzikulu. (7) Muzikhala tcheru ndi malemba amene akuwerengedwa n’kuona kugwirizana kwa mfundo zake. (8) Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mfundozi pothandiza anthu a mumpingo kapena m’gawo lathu?’ (9) Pamisonkhano yadera komanso ikuluikulu, muzioneratu mutu wa tsiku lililonse, nkhani zimene zikambidwe komanso malemba amene akutsogolera nkhani iliyonse. (10) Muzikonzekeretsa mtima wanu pokhala pansi n’kumamvetsera mwatcheru nyimbo komanso mavidiyo a nyimbo omwe amakhala kumayambiriro kwa pulogalamu yamsonkhano.
Muzimvetsera Yehova akamakulankhulani ndipo musamalole kuti zipangizo zamakono zizikusokonezani (Onani ndime 17)
PITIRIZANI KUMVETSERA YEHOVA AKAMAKUPHUNZITSANI
18. N’chifukwa chiyani timafunika kupitiriza kumvetsera tikakhala pamisonkhano?
18 Tiyenera kupitiriza kumvetsera tikakhala pamisonkhano chifukwa tikamachita zimenezi timakhala tikulola kuti Yehova azititsogolera “munjira zachilungamo.” (Sal. 23:3; 31:3) Timafunika kupatsidwa malangizo kuti tisakhale ngati boti limene limangotengeka kupita uku ndi uku chifukwa cha mphepo. Choncho “muzimvetsera mwatcheru kwambiri” n’kumagwiritsa ntchito malangizo amene Yehova amakupatsani pamisonkhano ya mpingo. (Luka 8:18) Anthu amene amamvetsera Yehova akamawaphunzitsa amakhala osangalala ndipo adzapeza moyo wosatha.—Sal. 119:2, 14.
NYIMBO NA. 87 Bwerani Mudzalimbikitsidwe
a Kuti mupeze mfundo zina zomwe zingakuthandizeni kuwonjezera luso lanu lophunzitsa, onani kabuku kakuti Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso ndiponso buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.