AUGUST 3-9, 2026
NYIMBO NA. 113 Yehova Amatipatsa Mtendere
Muzilemekeza Zimene Ena Asankha
“Musamaweruze amene ali ndi maganizo osiyana ndi anu.”—AROMA 14:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene tingachite kuti tizilemekeza Akhristu anzathu akasankha zinthu zimene sitikugwirizana nazo.
1-2. N’chifukwa chiyani nthawi zina zimene timasankha zimasiyana ndi zomwe Akhristu ena angasankhe?
KODI munayamba mwamvapo kuti simunaweruzidwe mwachilungamo chifukwa cha zimene munasankha? Kapena munaweruzapo Mkhristu mnzanu chifukwa cha zimene anasankha? N’zosachita kufunsa kuti tonsefe tingayankhe kuti inde pa mafunso onsewa.
2 Sitiyenera kudabwa kuti zimene tingasankhe zingakhale zosiyana ndi zimene Akhristu enanso okhulupirika angasankhe. Tikutero chifukwa anthufe ndi osiyana. Sitiona zinthu mofanana. Timaganiza mwanjira inayake chifukwa cha chikhalidwe chathu, banja lomwe tinakulira komanso zomwe takumana nazo pa moyo. Koma tisamalole kuti kusiyana maganizo kumeneku kuzisokoneza mtendere komanso mgwirizano wa mumpingo.—Aef. 4:3.
3. N’chiyani chingachititse kuti tiweruze Mkhristu mnzathu chifukwa cha zimene wasankha?
3 Mkhristu mnzathu akasankha zinthu zomwe sitikugwirizana nazo, tingamaone kuti tikufunika timuthandize kusintha maganizo kapena tingayambe kuuza ena zomwe zikutidetsa nkhawa pa zimene wasankhazo. Nthawi zambiri timakhala ndi zolinga zabwino tikamachita zimenezi. Timakonda abale ndi alongo athu ndipo timawafunira zabwino. (Miy. 17:17) Choncho sitimafuna kuti asankhe zinthu zomwe anganong’oneze nazo bondo kapena zimene zingasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova.
4-5. Kodi tizitani ngati Mkhristu mnzathu wasankha zinthu zosiyana ndi zimene ifeyo tikanasankha?
4 Kodi timafunika kukambirana ndi m’bale wathu ngati sitikugwirizana ndi zimene wasankha? Zingatengere ndi mmene zinthu zilili. Mwachitsanzo, tikaona kuti zimene akufuna kuchita zikuphwanya lamulo linalake la m’Baibulo, chifukwa cha chikondi tiziyesetsa kumuthandiza kuti asinthe mmene akuganizira. (Miy. 27:5, 6) Komabe, kodi tizitani ngati m’bale wathu wasankha zinthu zimene sizikuphwanya malamulo a Mulungu, koma zikungosiyana ndi zimene ifeyo tikanasankha? Yankho tikulipeza mulemba lomwe likutsogolera nkhaniyi, limene likuti: “Musamaweruze amene ali ndi maganizo osiyana ndi anu.”—Aroma 14:1.
5 Komabe, mwina zingamativute kuti tilemekeze zomwe wasankhazo. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tiyenera kulemekeza zimene ena asankha ndiponso mmene tingachitire zimenezi. Koma choyamba, tiyeni tikambirane zinthu zina zomwe zingachititse kuti tiyambe kuweruza abale ndi alongo athu pa zimene asankha.
ZIMENE ZINGACHITITSE KUTI TIYAMBE KUWERUZA ENA PA ZIMENE ASANKHA
6-7. Kodi ndi pa zochitika ngati ziti pamene tingayambe kuweruza ena pa zimene asankha?
6 Monga mmene tafotokozera kale, tingamaone kuti zinthu zikuyenera kuchitika m’njira inayake chifukwa cha mmene tinakulira kapena zimene tinakumana nazo pa moyo wathu. Tingamaganize kuti anthu ena akuonanso chimodzimodzi. Koma zikhoza kukhala kuti si mmene zilili. Taganizirani zochitika zotsatirazi. 1: M’bale wina anakulira m’banja limene bambo ake ankamwa mowa mwauchidakwa. M’baleyo ali kumacheza, akuona Akhristu ena akumwa mowa. Iye wakhumudwa nazo ndipo akuwauza kuti zomwe akuchitazo ndi zolakwika. 2: Mlongo wakwanitsa kulimbana ndi matenda enaake aakulu ndipo wachira. Kenako, wamva zoti mlongo wina akudwalanso matenda omwewo. Pofuna kuthandiza mnzakeyo, mlongo amene anachirayo akumukakamiza kuti atsatire zimene iyeyo anachita. Mwina angamuuze kuti azipewa kapena kudya zakudya za mtundu winawake, azigwiritsa ntchito mankhwala enaake kapenanso azichita zinazake zomwe zingamuthandize. 3: M’bale wina poyamba anali m’chipembedzo chabodza ndipo safuna kuchita chilichonse chokhudza chipembedzo chake chakalecho. Ndiye wakhumudwa atamva kuti Mkhristu wina anapita kumwambo wa maliro umene unachitikira m’tchalitchi.a
7 Taganiziraninso zochitika zotsatirazi. 4: M’bale anakula pa nthawi imene anthu ambiri ankaona kuti si zoyenera kuti abale azisunga ndevu kapenanso kuti alongo azivala mathalauza kumisonkhano ndiponso mu utumiki. Ngakhale kuti m’baleyo akudziwa zimene gulu lasintha posachedwapa pa nkhaniyi, akukakamiza abale kuti asamasunge ndevu komanso kuti alongo azivala madiresi akamachita zinthu zokhudza kulambira. 5: Mkulu akudziwa zokhudza m’bale wina yemwe anachita maphunziro owonjezera ndipo kenako anasiya choonadi. Ndiye m’bale wina wachinyamata mumpingo mwawo wasankha zoti akachite maphunziro owonjezera. Mkuluyo akumudera nkhawa ndipo akuyesetsa kuthandiza m’baleyo ndi makolo ake kuti asinthe maganizo awo.
8. (a) N’chiyani chingachititse kuti makolo ayambe kuweruza makolo anzawo? (b) Ngati tili ndi mtima wokonda kuweruza ena, kodi zimenezi zingakhudze bwanji abale ndi alongo?
8 Taganizirani zomwe zingachitikire makolo. 6: Monga makolo, mumayesetsa kulera ana anu “powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.” (Aef. 6:4) Koma mumaona kuti makolo ena a Chikhristu amalekerera ana awo pa zinthu zina. Mwachitsanzo, amalola ana awo kuti azifika mochedwa panyumba, azisewera magemu ena omwe si achiwawa kapenanso kuwalola kuti akhale ndi foni akanali aang’ono. Ndiye mwina zimenezi zimachititsa mwana wanu kumaona kuti ndinu okhwimitsa zinthu. Angakufunseni kuti, “Bwanji simumandipatsa ufulu ngati mmene makolo a mnzanga uja amachitira ndi ana awo?” Zimenezi zingachititse kuti muyambe kuweruza makolo anzanuwo. Mfundo ndi yakuti: Ngati Mkhristu wina wasankha zinthu zosiyana ndi zimene tingakonde, tikhoza kukhumudwa nazo. Mwachitsanzo, tikhoza kumaona kuti sagwiritsa ntchito bwino ndalama zake, amangokhalira kupita kokasangalala kapenanso tingamaone kuti zosangalatsa zimene amakonda si zoyenera. Komabe tizikumbukira kuti chofunika kwambiri si mmene tikumvera koma kulimbikitsa mgwirizano mumpingo.
9. Kodi tiyenera kumakumbukira chiyani? (Onaninso chithunzi.)
9 Ngati Mkhristu wasankha zinthu zosiyana ndi zimene Mkhristu wina wasankha, sizitanthauza kuti wina akulondola ndipo winayo walakwitsa. (Aroma 14:5) N’zoona kuti Akhristu amalangizidwa kuti azikhala ndi “maganizo ogwirizana” pa nkhani yotsatira mfundo za Yehova, koma zimenezi sizikutanthauza kuti tizikhala ndi maganizo ofanana pa chilichonse. (2 Akor. 13:11) Tikhoza kuyerekezera zosankha zathu ndi msewu umene tingasankhe kudutsa kuti tikafike kumalo enaake. Nthawi zambiri pamakhala misewu ingapo yokafikira kumaloko. Ndiye timasankha msewu umene tikufuna komanso umene tikuona kuti ndi wabwino kwambiri kwa ifeyo. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu akhoza kusankha zinthu mosiyana pa nkhani zimene aliyense amafunika kusankha yekha koma tonsefe cholinga chathu ndi chimodzi: Timafuna kusangalatsa Yehova. Choncho sitimaweruza ena pa zimene asankha.—Mat. 7:1; 1 Ates. 4:11.
Anthu angasankhe misewu yosiyana popita kumalo enaake. Akhristunso akhoza kusankha zinthu mosiyana pamene akutumikira Yehova (Onani ndime 9)
N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAFUNIKA KULEMEKEZA ZIMENE ENA ASANKHA?
10. Mogwirizana ndi Yakobo 4:12, kodi tilibe udindo wochita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
10 Baibulo limafotokoza zifukwa zingapo zotichititsa kuti tizilemekeza zimene ena asankha. Taonani zina mwa zifukwazi. Tilibe udindo woweruza ena pa nkhani zimene amayenera kusankha okha. (Werengani Yakobo 4:12.) Yehova ndi Wopereka Malamulo komanso Woweruza wachilungamo. Iye yekha ndi amene ali ndi ufulu wokhazikitsa mfundo komanso malamulo oti tiziyendera pa moyo wathu. Choncho abale ndi alongo athu amayenera kuyankha kwa Yehova, osati kwa ifeyo. (Aroma 14:10) Tilibe ufulu woweruza kapena kunyoza ena pa zimene asankha potengera mfundo zathu kapena mmene tikuonera zinthu.b
11. Tingatani kuti tilimbikitse mgwirizano mumpingo? (Onaninso chithunzi.)
11 Yehova amafuna kuti anthu ake akhale ogwirizana, osati azifanana pa chilichonse. Ndipotu Mulungu wathu amasangalala kutiona kuti ndife anthu osiyanasiyana. Timapeza umboni wa zimenezi m’chilengedwechi. Mwachitsanzo, masamba awiri a mtengo umodzi sangakhale ofanana ndendende. Taganiziraninso za anthufe. Pa anthu oposa 8 biliyoni omwe ali padzikoli, palibe amene amaoneka, kuganiza kapena kuchita zinthu mofanana ndendende ndi mnzake. Yehova anatilenga kuti tikhale osiyana. Safuna kuti tizitengera ndendende mmene ena amachitira zinthu. Koma amafuna kuti tizigwirizana. Choncho timavomereza kuti ndife osiyana ndipo timalimbikitsa mtendere. Timaona kuti chofunika kwambiri si maganizo athu kapena zimene timakonda koma kugwirizana ndi Akhristu anzathu.—Aroma 14:19.
Yehova anatilenga kuti tikhale osiyana ndi ena, koma amafuna kuti tikhale ogwirizana (Onani ndime 11)
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZILEMEKEZA ZOSANKHA ZA ENA
12-13. Kodi tizikumbukira chiyani ngati tikuona kuti wina wayamba kulowera “njira yolakwika”? (Agalatiya 6:1; onaninso bokosi lakuti “Ngati Simukugwirizana ndi Zimene Wina Wasankha.”)
12 Anthu ena akasankha zochita. Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi munthuyo wayamba kulowera “njira yolakwika” kapena wangosankha zinthu zosiyana ndi zimene ndingakonde?’ Ngati wayamba kulowera njira yolakwika, kapena kuti kuchita zosemphana ndi zimene Baibulo limanena, muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndine woyenerera mwauzimu kumuthandiza, kapena pali wina woyenera monga mkulu, amene angafunike kumuthandiza?’ Ngati ndinu woyenera kumuthandiza, yesetsani kumuthandiza ndi mzimu wofatsa. (Werengani Agalatiya 6:1.) Komabe, nthawi zambiri mukhoza kuzindikira kuti zimene wasankhazo zangokhala zosiyana ndi zimene inuyo mungasankhe. Ngati ndi choncho, simukuyenera kumukayikira kapena kulankhula zolakwika zokhudza zimene wasankhazo. Muzilemekeza ufulu wake ndipo musamamuweruze.—Aroma 14:2-4.
13 Taganizirani chitsanzo ichi: Ngati mwapita kulesitilanti ndi mnzanu, kodi mungamukakamize kuti aitanitse chakudya chofanana ndi chimene inuyo mwaitanitsa? Ayi. Mukhoza kulemekeza ufulu wake wosankha zimene akufuna kudya. Ndipotu zimene wasankha kuti adyezo sizikukhudzani mwanjira iliyonse. Ngakhale mutakhala kuti ndi inuyo, simungafune kuti mnzanuyo akusankhireni chakudya potengera zimene iyeyo amakonda. Mofanana ndi zimenezi, tingasonyeze kuti timalemekeza ena powalola kuti azisankha zinthu paokha, popanda kuwakakamiza kuti atsatire maganizo athu.
14. Mungatani kuti mulimbikitse mgwirizano mukamasankha zochita? (1 Akorinto 8:12, 13)
14 Mukamasankha zochita zokhudza inuyo. Mungalimbikitse mgwirizano mukamayesetsa kupewa kukhumudwitsa anthu ena. (Werengani 1 Akorinto 8:12, 13.) Nthawi zina mungazindikire kuti zimene mukufuna kusankha “n’zololeka,” kapena kuti n’zovomerezeka. Koma kodi zingakhale “zopindulitsa” ngati zingakhumudwitse m’bale wanu?c (1 Akor. 10:23, 24) Pa nthawi ngati zimenezi, m’malo mokakamira ufulu wanu, mungachite bwino kuganizira mmene ena akumvera. (Aroma 15:1) Koma kodi si paja takambirana kuti anthu ena ayenera kulemekeza zimene tasankha? Inde. Anthu ena ayenera kulemekeza zosankha zathu, ndipo ifenso tiyenera kulemekeza zosankha zawo. Koma tisamaiwalenso malangizo a m’Baibulo a pa Aroma 12:18, akuti: “Yesetsani mmene mungathere kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu onse.” Choncho timachita zonse zomwe tingathe kuti tizikhala mwamtendere ndi ena n’kumapewa kuwakhumudwitsa mwadala.
15. Kodi akulu angatani kuti azilimbikitsa mgwirizano mumpingo? (1 Akorinto 4:6)
15 Akulu amalemekeza zimene ena asankha. Iwo amalimbikitsa mgwirizano mumpingo popewa kupanga malamulo pa zimene aliyense amayenera kusankha yekha komanso ‘posapitirira zinthu zimene zinalembedwa’ m’Baibulo. (Werengani 1 Akorinto 4:6.) Amapewanso kuchita zinthu mopitirira malangizo ochokera m’Baibulo omwe amapezeka m’mabuku athu. Kuwonjezera pamenepa, Mkhristu akawapempha malangizo, akulu amakhala osamala kuti asamupatse malangizowo pongotengera zimene iwowo akuona kuti n’zothandiza. M’malomwake ayenera kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu.—Yes. 48:17, 18.
16. Kodi mkulu angasonyeze bwanji kuti akulemekeza zimene bungwe la akulu lasankha?
16 Mkulu ayeneranso kulemekeza zimene bungwe lonse la akulu lasankha. Bungwe la akulu likapempha mzimu woyera, kufufuza malangizo a m’Malemba n’kusankha zochita, mkulu aliyense ayenera kugwirizana ndi zosankhazo ngakhale zitakhala kuti zikusiyana ndi maganizo ake. (Aef. 5:17) Kuwonjezera pamenepa, akulu ayenera kukhala osamala kuti asamawerenge malangizo a gulu m’njira yakuti agwirizane ndi zimene iwowo akufuna. Mwachitsanzo, sizingakhale bwino kuti mkulu amatule chiganizo chimodzi m’mabuku athu n’cholinga choti maganizo ake aoneke ngati abwino.
17. Kodi kulemekeza zosankha za ena kumatithandiza bwanji?
17 Monga mmene taphunzirira, anthufe ndi osiyana. Aliyense ali ndi zimene amakonda komanso amaona zinthu mosiyana ndi mnzake. Koma kusiyana kumeneku n’kwabwino. Chifukwa choti timasiyana kochokera komanso makhalidwe athu, zimenezi zimathandiza kuti aliyense azisangalala mumpingo. Choncho m’malo molola kuti kusiyana kwathu kuzitigawanitsa, timayesetsa kulimbikitsa mtendere. Timakhala osamala kuti tisakhumudwitse ena n’kumalemekeza zosankha zawo. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa ndipo tidzasangalala kukhala mumpingo umene anthu ake ndi ogwirizana.—Sal. 133:1; Mat. 5:9.
NYIMBO NA. 89 Mvera Kuti Udalitsidwe
a Mkhristu ayenera kuganizira mfundo zosiyanasiyana ngati akufuna kupita kumaliro kapena ku ukwati umene ukachitikire m’tchalitchi. Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002.
b Nthawi zina akulu angafunike kuweruza anthu amene aphwanya malamulo a m’Baibulo. Komabe ayenera kukumbukira kuti akuweruza m’malo mwa Yehova potengera mfundo zake zolungama, osati maganizo awo.—Yerekezerani ndi 2 Mbiri 19:6.
c Mwachitsanzo, onani buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale phunziro 35, mfundo 5.