MUNTHU WOTCHULIDWA M’BAIBULO
Manayeni Ankaona Kuti Kutumikira Yehova N’kofunika Kwambiri pa Moyo Wake
Manayeni anali mmodzi mwa abale amene ankatsogolera mumpingo ku Antiokeya. Iye “anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira chigawo.” (Mac. 13:1) Manayeni anali wophunzira kwambiri ndipo ayenera kuti anakulira m’banja lolemera.
Komabe, iye anasankha kukhala Mkhristu ndipo ankathandiza kwambiri mumpingo. Ngakhale kuti anali wophunzira komanso ankadziwana ndi anthu otchuka, Manayeni sanagwiritse ntchito zimenezi kuti adzipindulitse yekha. M’malomwake ankatumikira abale ake mwakhama.
Zimene Manayeni anachita zikusonyeza kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kutchuka kapena kukhala ndi ndalama zambiri m’dzikoli. Mofanana ndi Manayeni, tiziika kutumikira Yehova pamalo oyamba pa moyo wathu m’malo mofunafuna chuma kapena kutchuka. (Mat. 6:33) Kuwonjezera pamenepa, ngakhale timaona kuti maphunziro ndi ofunika, ‘timasankha zinthu zimene ndi zofunikadi kwambiri’ ndipo timaonetsetsa kuti zinthu zam’dzikoli sizikutilepheretsa kulambira Yehova.—Afil. 1:9, 10.