JULY 27–AUGUST 2, 2026
NYIMBO NA. 56 Muzikonda Kwambiri Choonadi Panokha
Pitirizani Kukhala pa Ubwenzi Wolimba ndi Yehova Pamene Mukuchita Maphunziro Owonjezera
“Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.”—AFIL. 3:16.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona mfundo 4 za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kuti mukhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ngati mwasankha kuchita maphunziro owonjezera.
1-2. (a) Ngati mwasankha kuchita maphunziro owonjezera, kodi muyenera kupitiriza kuchita chiyani? (b) Kodi ‘kupitiriza kupita patsogolo pochita zomwe tikuchita’ kumatanthauza chiyani? (Afilipi 3:16)
ENA mwa atumiki a Yehova amasankha kuchita maphunziro owonjezera akamaliza maphunziro akusekondale. Iwo amaona kuti maphunzirowo angadzawathandize kupeza ntchito yomwe izidzawathandiza potumikira Yehova. Ngati mwasankha kuchita maphunziro owonjezera, kodi mungatani kuti mupitirizebe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? (Yak. 4:8a) N’zosachita kufunsa kuti pa zaka zomwe munali kusukulu m’mbuyomo, munkakumana ndi mayesero. Panopa mukufunika ‘kupitiriza kupita patsogolo pochita zomwe mukuchitazo.’ Izi zikutanthauza kuti muyenera kupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ngati mmene munkachitira pa nthawiyo.—Werengani Afilipi 3:16.
2 Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo” nthawi zambiri ankagwiritsidwa ntchito ponena za asilikali omwe amachita zinthu mogwirizana kwambiri akamaguba. Ngati mwasankha kuchita maphunziro owonjezera, muyenera “kumaguba” mogwirizana ndi Akhristu anzanu pamene mukutumikira Yehova, osati kungoima pamodzimodzi kapena kubwerera m’mbuyo. Munkhaniyi tikambirana mfundo 4 za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuchita zimenezi. Mfundo zake mukuzidziwa kale. Munazigwiritsapo kale ntchito m’mbuyomo ndipo mukuyenera kupitiriza kuzigwiritsa ntchito pamene mukuchita maphunziro owonjezera komanso pambuyo poti mwamaliza maphunzirowa.
PITIRIZANI KULIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA
3. Kodi kuchita maphunziro owonjezera kungakhudze bwanji zomwe mumachita tsiku lililonse?
3 Vuto lomwe limakhalapo. Maphunziro owonjezera angapangitse kuti muzipanikizika zomwe zingakhudze mmene mumachitira zinthu tsiku lililonse. Chifukwa choti mumafuna muzikhoza bwino m’kalasi, mungayambe kuona kuti kutumikira Yehova si kofunika kwenikweni. Mungamanyalanyaze kusonkhana, kulalikira, kuphunzira Baibulo komanso kupemphera.—Chiv. 2:4.
4. N’chiyani chingakuthandizeni kuti “muzikhala ndi zochita zambiri pa ntchito ya Ambuye”? (1 Akorinto 15:58)
4 Werengani 1 Akorinto 15:58. Kuti njinga iziyenda, mumafunika kupitiriza kupalasa. Mofanana ndi zimenezi, kuti mupitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova mumafunika kukhala ndi “zochita zambiri pa ntchito ya Ambuye.” Mufunika kumaika zinthu zokhudza kulambira pa malo oyamba osati kumangozichita mwa apo ndi apo. Choyamba, muyenera kumadziona kuti ndinu mtumiki wa Yehova ndipo chachiwiri muzidziona kuti ndinu mwana wasukulu. (Mat. 22:37) Mlongo wina wachitsikana dzina lake Samatha ananena kuti, “Ndinadzilonjeza kuti ngati maphunziro anga angandisokoneze potumikira Yehova, ndidzasiya sukulu.”
5. Kodi mungatani kuti muzichita zambiri potumikira Yehova?
5 Zimene mungachite musanayambe maphunziro owonjezera. Muzidziwiratu zinthu zimene zimafunika kukhala pamalo oyamba pa moyo wanu. Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndakonza mapulani otani kuti nthawi zonse ndizidzasonkhana, kulalikira komanso kuphunzira Baibulo?’ (Yos. 1:8; Mat. 28:19, 20; Aheb. 10:25) Mukaganizira zomwe munkachita muli kusekondale, n’chiyani chinkakuthandizani kuti muziika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba? Ngati mukuona kuti pali zina zomwe mukanachita bwino pa nthawiyo, kodi mungatani kuti panopa ziyende bwino? Muzikhala otsimikiza mtima kuti mupitirizabe kuchita khama potumikira Yehova pamene mukuchita maphunziro owonjezera. N’zoona kuti mumafunika kumakhoza kusukulu, koma simukuyenera kusinthanitsa maphunziro ndi kulambira Yehova.a—Mat. 6:24.
6. Kodi mungadzifunse funso liti kuti muone ngati mukupitirizabe kuika Yehova pamalo oyamba? (Onaninso chithunzi.)
6 Mukamachita maphunziro owonjezera nthawi ndi nthawi muzidzifufuza, mwina pakatha mwezi kapena kuposa. Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndikupitirizabe kuika zinthu zofunika kwambiri pamalo oyamba?’ Muzikhala tcheru ndi zinthu zomwe zingasonyeze kuti mwayamba kulowa pansi mwauzimu monga chizolowezi chosafika pamisonkhano kapena kufika mochedwa, kumaganizira za zochita zimene akupatsani kusukulu misonkhano ili mkati kapena kumangochita misonkhano pavidiyokomfelensi. Muzikhala tcheru kuti muone ngati simukukondanso kupemphera kapena kuwerenga Baibulo ngati mmene munkachitira kale kapenanso ngati simukumaikirapo mtima pa ntchito yolalikira moti mumangoigwira n’cholinga choti muthane nayo basi. Mukaona kuti zimenezi zayamba kukuchitikirani, muzichitapo kanthu mwamsanga. Musamalole kuti maphunziro anu akulepheretseni kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba.
Musamalole kuti maphunziro akulepheretseni kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba (Onani ndime 6)
‘MUZITETEZA LUSO LANU LOGANIZA’
7. Kodi maphunziro owonjezera angakhudze bwanji mmene mumaganizira?
7 Vuto limene limakhalapo. Potengera kosi imene mwatenga, maphunziro owonjezera angachititse kuti musokonezedwe ndi “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake,” zomwe zikuphatikizapo kusakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso mfundo yakuti zamoyo zinachita kusintha. (Akol. 2:8) Maphunzirowo angachititsenso kuti muyambe kukhala ndi mtima wodzidalira kwambiri. M’bale wina wachinyamata ananena kuti: “Sikuti ankangotiphunzitsa kuti tikhale ndi luso koma ankatiphunzitsanso mmene tingamaganizire ndipo kaganizidwe kake kankakhala kosagwirizana ndi mmene Yehova amaonera zinthu. Mwachitsanzo, tinkaphunzitsidwa kuti luso lathu ndi limene lingathandize kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo. Maganizo amenewa anandichititsa kuyamba kuona kuti sindikufunika kudalira Yehova kuti ndizisangalala. Ndipotu zinali zovuta kwambiri kuti ndizimudalira.”
8. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti ‘muziteteza luso lanu loganiza’? (Miyambo 5:1, 2)
8 Werengani Miyambo 5:1, 2. Baibulo limatichenjeza kuti ‘tiziteteza luso lathu loganiza.’ Timateteza chinthu chimene tikuona kuti chikhoza kuwonongedwa kapena kulandidwa. Ndi mmenenso zilili ndi luso lathu loganiza. (1 Pet. 5:8) Zimene dzikoli limalimbikitsa zingachititse kuti muzikayikira zimene mumakhulupirira zokhudza makhalidwe abwino, mmene moyo unayambira komanso kuti kuli Mulungu. Anthu akhoza kumaganiza kuti maganizo awo ndi “apamwamba” koma kwenikweni amakhala opanda pake. Ndipotu “kwa Mulungu nzeru zamʼdzikoli nʼzopusa.”—1 Akor. 3:18-20.
9. Kodi mungatani kuti muziteteza luso lanu loganiza?
9 Zimene mungachite musanayambe maphunziro owonjezera. Kuti muteteze luso lanu loganiza, muzionetsetsa kuti mukukhulupirira kwambiri kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zoona musanayambe kuchita maphunziro owonjezera. Muzidzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ndimakhulupirira Mulungu? Kodi ndimadziwa bwanji kuti Baibulo ndi Mawu ake? N’chiyani chimandipangitsa kukhulupirira kuti mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino n’zapamwamba kuposa zam’dzikoli?’ Muziganizira mmene zinthu zinalili muli kusekondale. N’zosachita kufunsa kuti mukanatha kusokonezedwa ndi kaganizidwe ka anthu am’dzikoli. Kodi pa nthawiyo chikhulupiriro chanu chinafooka chifukwa chakuti anthu ena ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha? Kodi zinkakuvutani kupewa zoipa zimene anzanu a kusukulu ankachita? Ngati mukuona kuti pali zina zimene mukanatha kuchita bwino, kodi mungatani kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu panopa? Muzikhala otsimikiza mtima kuteteza luso lanu loganiza pamene mukuchita maphunziro owonjezera.—2 Tim. 2:16-18.b
10. Kodi mungatani kuti mupitirize kuteteza luso lanu loganiza?
10 Pamene mukuchita maphunziro owonjezera muzidzifufuza nthawi ndi nthawi. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndayamba kusokonezedwa ndi zochita za anthu omwe salambira Yehova? Kodi ndimatha kuzindikira kuti zomwe ndikuphunzitsidwazi zangokhala nzeru za anthu zomwe n’zopanda pake? Kodi ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi womwe ungathetse mavuto a anthu?’ Kuti muteteze luso lanu loganiza, muziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. Kuphunzira Baibulo komanso kuganizira mozama zimene mwaphunzirazo kudzakuthandizani kuti musamakayikire kuti munapeza choonadi.—1 Tim. 4:15.
MUZIGWIRITSA NTCHITO NTHAWI YANU MWANZERU
11. N’chifukwa chiyani zingakhale zovuta kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu mukamachita maphunziro owonjezera?
11 Vuto limene limakhalapo. Maphunziro owonjezera angachititse kuti muzipanikizika kwambiri makamaka ngati mukukonzekera mayeso kapena ngati muli ndi pulojekiti yoti mumalize pa nthawi inayake. Ngati simungamagwiritse ntchito bwino nthawi yanu, mukhoza kumakhala ndi nkhawa komanso kumatopa kwambiri. N’chifukwa chake n’zofunika kuti muzisamalira thanzi komanso maganizo anu.
12. Kodi mungafunike kumachita zinthu ziti kuti “muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu”? (Aefeso 5:15, 16)
12 Werengani Aefeso 5:15, 16. Nthawi zina zikhoza kukhala zovuta kuti “muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.” Ndipo mungafunike kudziikira malire. Mwachitsanzo, kuwonjezera pa kuchita zinthu zokhudzana ndi sukulu, mumafunikanso kupeza nthawi yochita zinthu ndi Akhristu anzanu komanso anthu a m’mbanja lanu. (Sal. 133:1; Miy. 18:1) Ndipotu chofunika kwambiri ndi kuchita zinthu zokhudza kulambira. (Mat. 6:33) N’kuthekanso kuti muli ndi udindo wosamalira banja lanu komanso muli pa ntchito. Mumafunikanso kusamalira thanzi lanu popeza nthawi yokwanira yopuma komanso kuchita masewera olimbitsa thupi. (Mlal. 4:6; 1 Tim. 4:8) Kuti zonsezi zitheke, mungafunike kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.
13. Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu?
13 Zimene mungachite musanayambe maphunziro owonjezera. Baibulo limanena kuti kukhala ndi pulani kumathandiza kuti zinthu ziyende bwino. (Miy. 21:5) Poganizira zimenezi, musanayambe maphunziro owonjezera mungafunike kukonzeratu ndandanda yomwe muzidzatsatira. Kuti mukwanitse kuchita zimenezi, ganizirani zimene munkachita muli kusekondale. Kodi munkatani kuti muzikwanitsa kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu? Kodi pali zina zimene mukuona kuti mukanachita bwino pa nthawiyo, nanga ndi zinthu ziti zomwe mungasinthe panopa kuti zinthu ziziyenda bwino? Muzikhala otsimikiza mtima kuti inuyo ndi amene muzilamulira nthawi yanu osati kuti nthawiyo izikulamulirani.c
14. Kodi mungadzifufuze pogwiritsa ntchito mafunso ati?
14 Pamene mukuchita maphunziro owonjezera nthawi ndi nthawi muzidzifufuza. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndandanda yanga imandilola kuti ndizipuma mokwanira komanso kuchita masewera olimbitsa thupi? Kodi ndimapeza nthawi yochita zinthu ndi Akhristu anzanga? Kodi ndimakwanitsa kumaliza homuweki pa nthawi yake? Ngati si choncho, kodi n’chifukwa chakuti ndili ndi zochita zambiri kapena ndimachita zinthu mozengereza? Kodi anzanga komanso anthu a m’banja langa akuona kuti pali zina zimene ndikuyenera kusintha?’ Ngati mukuona kuti mukufunika kusintha ndandanda yanu, kapena kuyesetsa kuti muziitsatira, chitani zimenezo mwamsanga. Mungachezenso ndi anthu omwe amatha kugwiritsa ntchito bwino nthawi yawo kuti akuthandizeni.—Miy. 11:14.
PITIRIZANI ‘KUYENDA NDI ANTHU ANZERU’
15. Kodi ndi vuto liti lomwe mungakumane nalo mukamachita maphunziro owonjezera?
15 Vuto limene limakhalapo. Pamene mukuchita maphunziro owonjezera, ophunzira anzanu angamafune kuti muzichita nawo limodzi zosangalatsa. Mwina mukhoza kukopeka nazo chifukwa mumachitira limodzi zinthu zambiri makamaka ngati muli kalasi imodzi. Mukhozanso kumaona kuti mumafanana pa zinthu zambiri ndi anzanuwo kuposa abale ndi alongo. Komabe muyenera kukhala osamala. Kukhala kalasi imodzi ndi anzanuwo sikukutanthauza kuti mumayendera mfundo zofanana. Ndipotu mukamachita nawo zinthu kwambiri, m’pamenenso angasokoneze kwambiri maganizo anu. (1 Akor. 15:33) Michael amene anaphunzira zokhudza magetsi kwa zaka 4 anaona kuti zimenezi ndi zoona. Iye anati, “Wiki iliyonse ndinkagwira ntchito kwa maola oposa 40 ndi anzanga omwe sankalemekeza akazi, ankamvetsera nyimbo zoipa komanso ankatukwana ndipo ndinayamba kuona kuti zimenezi si zolakwika kwenikweni.”
16. Kodi ‘kuyenda ndi anthu anzeru’ kumatanthauza chiyani? (Miyambo 13:20)
16 Werengani Miyambo 13:20. Baibulo limatichenjeza za kuopsa kocheza ndi anthu a makhalidwe oipa. Koma limanena kuti, “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” Apa mfundo ndi yakuti anthu amene timacheza nawo amachititsa kuti tikhale ndi makhalidwe abwino kapena oipa. Choncho muzigwirizana kwambiri ndi anthu omwe amatumikira Yehova ndi mtima wonse ngati mmene inuyo mumachitira.—Sal. 101:6, 7; 119:63.
17. Kodi mungatani kuti musamagwirizane ndi anthu a makhalidwe oipa?
17 Zimene mungachite musanayambe maphunziro owonjezera. Muzisankhiratu kuchuluka kwa nthawi imene muzidzacheza ndi ophunzira anzanu. M’bale wina dzina lake Trenton ananena kuti: “Ndimachita zinthu mokoma mtima ndi anzanga a m’kalasi, koma tikaweruka sindichita nawo zinthu. Ndimawaona kuti ndi anzanga a m’kalasi basi osati anzanga apamtima.” Kodi inuyo mudziikira malire otani pa nkhaniyi? Kuti muyankhe funsoli, ganizirani zimene munkachita muli kusekondale. Kodi munadziikira malire otani? Ngati mukuona kuti pali zina zomwe mukanachita bwino pa nthawiyo, kodi mungasinthe zinthu ziti panopa? Muzikhala otsimikiza mtima ‘kuyenda ndi anthu anzeru’ n’kumapewa kuchita zinthu ndi anthu omwe sakonda Yehova.d
18. Kodi ndi mafunso ati omwe mungadzifunse? (Onaninso chithunzi.)
18 Nthawi ndi nthawi muzidzifufuza podzifunsa kuti: ‘Kodi ndayamba kuchita kwambiri zinthu ndi anthu a m’kalasi mwanga? Kodi ndayamba kutengera makhalidwe awo, mmene amalankhulira komanso mmene amachitira zinthu? Kodi Yehova angavomereze zomwe ndayankha pa mafunso amenewa?’ (Sal. 1:1) Ndiye ngati mukuona kuti mukufunika kusintha, chitani zimenezo mwamsanga. Muzionetsetsa kuti mukugwirizana kwambiri ndi anthu okonda Yehova ngati mmene inuyo mumachitira. Komanso musamazengereze kulalikira anzanu a m’kalasi. Inuyo muli pamalo abwino oti muwathandize kudziwa choonadi.
Musamazengereze kulalikira anzanu a m’kalasi (Onani ndime 18)e
MUZIKONZEKERERATU
19. Kodi mungakonzekere bwanji kudzalimbana ndi zinthu zomwe zingadzasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova pamene mukuchita maphunziro owonjezera? Perekani chitsanzo.
19 Munthu wanzeru akafuna kukwera phiri amakonzekera asanayambe ulendo wake. Ngakhale kuti sangadziwiretu mavuto amene angakumane nawo amakhala kuti wakonzekera bwino, wavala zoyenera ndipo akudziwa kumene akupita. Inunso mungachite zofanana ndi zimenezi mukamakonzekera kuchita maphunziro owonjezera. Pitirizani kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo muzivala “zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu.” Muzikumbukira kuti cholinga chanu ndi kulemekeza Yehova pa chilichonse chimene mukuchita osati kupeza ndalama zambiri kapena kukhala munthu wotchuka m’dzikoli.—Aef. 6:11-13; 1 Akor. 9:26, 27; 10:31.
20. Kodi mungatani kuti ‘mupitirize kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro’?
20 Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akor. 13:5) Mukhoza kuchita zimenezi pamene mukuchita maphunziro owonjezera. Nthawi ndi nthawi muzidzifufuza pogwiritsa ntchito mbali zosiyanasiyana zimene takambirana munkhaniyi. Kodi mukupitiriza kuchita zinthu zokhudza kulambira? Kodi mukuteteza maganizo anu ku nzeru zam’dzikoli? Kodi mukugwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru? Kodi mumagwirizana ndi Akhristu anzanu n’kumapewa kucheza ndi anthu a makhalidwe oipa? Amenewa ndi mafunso amene muyenera kudzifunsa kaya muli kusukulu, kuntchito kapena kwina kulikonse. Muzikhala otsimikiza mtima kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba pa zilizonse zomwe mwakumana nazo. Ndipo musamakayikire kuti Yehova adzakudalitsani mukamayesetsa kuchita zimenezi.—Miy. 3:5, 6.
NYIMBO NA. 87 Bwerani Mudzalimbikitsidwe
a Kuti mudziwe zomwe mungachite kuti mupitirize kuchita khama potumikira Yehova, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa . . . Kodi Ndiyenera Kuchita Chiyani Ndikabatizidwa?—Mbali Yoyamba: Pitirizani Kuchita Zinthu Zofunika.”
b Kuti mudziwe zomwe mungachite kuti muziteteza maganizo anu onani nkhani yakuti, “Tisapusitsidwe ndi ‘Nzeru za M’dzikoli’” mu Nsanja ya Olonda ya May 2019.
c Kuti mudziwe zimene mungachite kuti mukhale ndi ndandanda yochitira zinthu tsiku lililonse, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa . . . Ndingatani Kuti Ndizigawa Bwino Nthawi Yanga?”
d Kuti mudziwe zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha mwanzeru anthu ocheza nawo, onani phunziro 48 lakuti “Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo,” m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pamene akuchita kosi yokhudza kukonza tsitsi, mlongo akuyesetsa kulalikira mnzake wa m’kalasi.