Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 February tsamba 8-13
  • Kodi Kubatizidwa Kumatanthauza Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kubatizidwa Kumatanthauza Chiyani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI UBATIZO UMATANTHAUZA CHIYANI?
  • MMENE UBATIZO WA CHIKHRISTU UMACHITIKIRA
  • “MʼDZINA LA ATATE, LA MWANA NDI LA MZIMU WOYERA”
  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kuti Mukhale Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Tanthauzo la Ubatizo Wanu
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Munthu Ayenera Kubatizidwa Kuti Akhale Mkhristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kodi Ubatizo Umatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 February tsamba 8-13

APRIL 13-19, 2026

NYIMBO NA. 52 Kudzipereka Monga Mkhristu

Kodi Kubatizidwa Kumatanthauza Chiyani?

“Pitani mukaphunzitse anthu . . . Muziwabatiza.”—MAT. 28:19.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene ubatizo umatanthauza, chifukwa chake timafunika kubatizidwa komanso mmene uyenera kuchitikira.

1. N’chiyani chikusonyeza kuti ubatizo ndi imodzi mwa mfundo zofunika kwambiri za m’Baibulo?

TIMASANGALALA kwambiri tikaona anthu atsopano akubatizidwa. Kodi mukudziwa kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi nawonso anasangalala, anthu ambiri atabatizidwa pa nthawi imene anachita msonkhano wawo koyamba? Pamsonkhanowu panakambidwa nkhani ya ubatizo imene inasonyeza kuti n’zofunika kuti anthu azibatizidwa. (Mac. 2:​38, 40, 41) Patapita nthawi, Paulo analemba za “mfundo zoyambirira zokhudza Khristu” zomwe zikuphatikizapo “chiphunzitso chokhudza ubatizo.” (Aheb. 6:​1, 2) Choncho, ubatizo ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zimene timaphunzira m’Baibulo ndipo tiyenera kuumvetsa bwino. N’chifukwa chiyani tikutero?

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsa bwino zokhudza ubatizo?

2 Mofanana ndi mmene maziko olimba amathandizira nyumba kuti isagwe kukakhala chimphepo, kumvetsa bwino zokhudza ubatizo, kumatithandizanso kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Timafunika kumvetsa zimenezi kaya tikufuna kubatizidwa kapena tinabatizidwa zaka zambiri zapitazo. Ndiye munkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi ubatizo umatanthauza chiyani? Kodi ubatizo uyenera kuchitika bwanji? Nanga n’chifukwa chiyani timabatizidwa m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera?

KODI UBATIZO UMATANTHAUZA CHIYANI?

3. Kodi ubatizo umaimira chiyani?

3 Munthu akabatizidwa amasonyeza poyera kuti anavomereza choonadi chokhudza Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu, analapa machimo, anasintha moyo wake kuti azitumikira Yehova, anazindikira kuti Yesu ndi njira imene Mulungu akuigwiritsa ntchito populumutsa anthu komanso anadzipereka kwa Yehova m’pemphero kuti azimutumikira mogwirizana ndi gulu lake. Mukalonjeza kuti muzimutumikira, kapena kuti kudzipereka kwa iye, mumakhala kuti mwayamba kuyenda panjira yopita ku moyo wosatha.

4. Kodi kuviikidwa m’madzi kumaimira chiyani? (Onaninso chithunzi.)

4 Mukamabatizidwa, mumaviikidwa thupi lonse m’madzi kenako n’kuvuulidwa.a Zimakhala ngati munafa n’kuikidwa m’manda kenako n’kuukitsidwa. (Yerekezerani ndi Akolose 2:12.) Ubatizo umasonyeza kuti munasintha kwambiri moyo wanu. Kodi umasonyeza bwanji zimenezi? Mukamizidwa m’madzi, mumasonyeza kuti mwasiya zoipa zomwe munkachita poyamba. Mukavuulidwamo, mumayamba moyo watsopano wogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.

Zithunzi: Munthu akubatizidwa pambuyo poti wakwanitsa kulimbana ndi mavuto angapo. 1. Akusangalala pomwe akuonera masewera a nkhonya pa TV. 2. Akusuta fodya. 3. Akumwa mowa mwauchidakwa. 4. Kenako akubatizidwa.

Mukabatizidwa mumasiya moyo wanu wakale n’kuyamba moyo watsopano wogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna (Onani ndime 4)


5. Kodi zimene mumachita pokonzekera kubatizidwa zimafanana bwanji ndi zimene Nowa anachita pomanga chingalawa? (1 Petulo 3:​18-21)

5 Werengani 1 Petulo 3:​18-21. Tingayerekezere zimene mukuchita pokonzekera kubatizidwa ndi ntchito imene Nowa anagwira pomanga chingalawa. Ngati mwangoyamba kumene kuphunzira za Yehova, mungamaone kuti ndi chintchito kuti mufike poyenerera kubatizidwa. Zingamaoneke zovuta kwambiri ngati mmene zinalili pamene Nowa ankamanga chingalawa. Ndiye kodi muyenera kuyesetsabe kuti mubatizidwe? Taganizirani za Nowa. Mulungu ndi amene anapereka malangizo omangira chingalawacho ndipo Nowa ankafunika kuwatsatira mosamala kuti zamoyo zipulumuke pa Chigumula. Iye anamvera malangizowo n’kumanga chingalawa, chifukwa choti anali ndi chikhulupiriro komanso ankathandizidwa ndi Mulungu. Mofanana ndi Nowa, inunso mukhoza kutsatira ‘zonse zimene Mulungu analamula.’—Gen. 6:22.

6. Kodi ubatizo ungakuthandizeni bwanji kuti mudzapulumuke?

6 Pavesi 21, mtumwi Petulo analemba kuti ubatizo ‘ukupulumutsa inuyo.’ Kungomizidwa m’madzi si kumene kumachititsa kuti mudzapulumuke kapenanso kukuchotserani machimo, koma magazi a Yesu okha ndi amene angakuyeretseni ku machimo. (1 Yoh. 1:7) Komabe kubatizidwa n’kofunika chifukwa ndi zimene Yehova anatilamula kuti tizichita komanso timakhala kuti ‘tikupempha chikumbumtima chabwino’ kwa iye. Zikatero, Yehova amakhala wofunitsitsa kukukhululukirani machimo pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu. Choncho tingati ubatizo ‘ukukupulumutsani,’ kapena kuti ukukuthandizani kuti mudzapulumuke.

MMENE UBATIZO WA CHIKHRISTU UMACHITIKIRA

7. Kodi ubatizo umachitika bwanji?

7 Baibulo limanena kuti munthu akamabatizidwa amayenera kuviikidwa thupi lonse m’madzi koma silifotokozanso zina kuwonjezera pamenepa. Komabe, Malemba amatithandiza kudziwa zoyenera kuchita. Mwachitsanzo, mfundo za m’Baibulo zimathandiza anthu amene akukabatizidwa kudziwa mmene angavalire moyenera. Zimathandizanso amene akuonerera kudziwa zoyenera kuchita pa nthawi ya ubatizo. (1 Akor. 14:40; 1 Tim. 2:9) Masiku ano, akulu ndi amene amabatiza anthu koma sitimawapatsa ulemu wapadera chifukwa cha zimenezi. (1 Akor. 1:​14, 15) Ubatizo umakhala wovomerezeka kaya pali anthu ambiri oonerera kapena ayi.—Mac. 8:36.

8. Kodi anthu amene akukabatizidwa amafunsidwa mafunso ati, nanga n’chifukwa chiyani? (Machitidwe 2:​38-42) (Onaninso chithunzi.)

8 Baibulo limasonyeza kuti timafunika ‘kulengeza poyera chikhulupiriro chathu kuti tidzapulumuke.’ (Aroma 10:​9, 10) N’zomveka kuti timafunika kuchita zimenezi tikamabatizidwa, chifukwa ubatizo umatithandiza kuti tidzapulumuke. Choncho, okabatizidwa amafunsidwa mafunso awiri. Loyamba, “Kodi munalapa machimo anu, kudzipereka kwa Yehova komanso kuvomereza njira yake yopulumutsira anthu kudzera mwa Yesu?” Cholinga cha funsoli ndi kudziwa zimene munthu wachita pokonzekera kubatizidwa ndipo ndi lofanana ndi mawu amene Petulo anauza gulu la anthu pa Pentekosite. Funso lachiwiri, “Kodi mukudziwa kuti mukabatizidwa muzidziwika kuti ndinu wa Mboni za Yehova komanso kuti muli m’gulu lake?” Funsoli limatikumbutsa kuti timayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene tinalonjeza, potsatira malangizo a gulu la Yehova komanso kumutumikira ndi Akhristu anzathu, ngati mmene Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachitira. (Werengani Machitidwe 2:​38-42.) Anthu amene amayankha mafunsowa mochokera pansi pa mtima kuti inde, ndi amene amayenera kubatizidwa.

Anthu a misinkhu yosiyanasiyana omwe akufuna kubatizidwa pamsonkhano wadera, aimirira kutsogolo ndipo akulengeza poyera za chikhulupiriro chawo.

Mukamabatizidwa ‘mumalengeza poyera za chikhulupiriro chanu kuti mupulumuke’ (Onani ndime 8)d


9. Kodi aliyense amayenera kuchita chiyani kuti Mulungu azisangalala naye?

9 Ngakhale musanaphunzire choonadi, n’kutheka kuti munali ndi makhalidwe abwino ndipo simunachitepo machimo akuluakulu. Mwinanso munaleredwa ndi makolo a Mboni, omwe anakuthandizani kuti muzikonda Yehova. Ngati zili choncho, kodi mukuyenerabe kulapa n’kubatizidwa kuti Mulungu azisangalala nanu? Inde. Posatengera mmene tinakulira, tonsefe timafunika kuzindikira mfundo yakuti tinatengera uchimo, umene umatichititsa kuti titalikirane ndi Mulungu. (Sal. 51:5) Koma pamene tikuphunzira za Yehova, timasankha kuti tiziika zimene iyeyo amafuna pamalo oyamba. Kenako timalapa n’kutembenuka, kutanthauza kuti timayamba kuchita zinthu zimene zimasangalatsa Atate wathu wakumwamba. Tikatero, zimakhala zotheka kubatizidwa.—Mac. 3:19.

10. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati munabatizidwa kale kuchipembedzo china?

10 Ngati poyamba munabatizidwa kuchipembedzo china, mukuyenerabe kubatizidwa kuti mukhale wa Mboni za Yehova. Tikutero chifukwa pa nthawiyo munali musanamvetse mfundo zokhudza Yehova Mulungu ndi Yesu. Ndipotu ngakhale kuti munadzipereka kwa Mulungu m’pemphero, munachita zimenezi musanamvetse zimene iye amafuna. Mtumwi Paulo atakumana ndi anthu ena ku Efeso, omwe anali atabatizidwa asanamvetse mfundo zolondola zokhudza Yesu, anakonza zoti anthuwo abatizidwenso.b (Mac. 19:​1-5) Masiku anonso ubatizo umakhala wovomerezeka, ngati munthu waphunzira mfundo zolondola zokhudza zimene Mulungu amafuna.

“MʼDZINA LA ATATE, LA MWANA NDI LA MZIMU WOYERA”

11. Kodi kubatizidwa “mʼdzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera” kumatanthauza chiyani? (Mateyu 28:​18-20)

11 Yesu analamula kuti ophunzira ake atsopano azibatizidwa “mʼdzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera.” (Werengani Mateyu 28:​18-20.) Kodi ankatanthauza chiyani? M’Baibulo, mawu akuti “dzina” nthawi zambiri amatanthauza mbiri ya munthu. Dzina likhoza kuimiranso udindo kapena mphamvu zimene munthu ali nazo. Ndiye tikamachita zinthu “m’dzina la” winawake kapena chinachake, timakhala kuti tikuzindikira mphamvu zimene mwiniwake wa dzinalo ali nazo. (Yerekezerani ndi Mateyu 10:41.) Choncho tiyeni tikambirane zimene tingachite posonyeza kuti tikuzindikira udindo komanso mphamvu za Atate, Mwana ndi mzimu woyera.

12. Kodi timabatizidwa bwanji m’dzina la Atate? (Chivumbulutso 4:11) (Onaninso zithunzi.)

12 M’dzina la Atate. Timavomereza kuti Yehova ndi Atate wathu wakumwamba amene anatipatsa moyo. Iye ndi Mulungu wamphamvuyonse komanso amene analenga zinthu zonse. (Werengani Chivumbulutso 4:11.) Timadziwa kuti amamva tikamapemphera. Timagwiritsa ntchito dzina lake mwaulemu komanso momasuka tikamapemphera ndiponso kuuza ena zokhudza iye. (Sal. 65:2) Komabe pali zinthu zambiri zimene munthu amayenera kumvetsa kuti abatizidwe m’dzina la Atate. Anthu omwe ankamumvetsera Petulo pa Pentekosite, ankadziwa kale zokhudza Yehova. Koma tsopano iwo ankafunika kuzindikira kuti iye amapereka moyo wosatha kudzera mwa Yesu Khristu yekha basi.—Aroma 5:8.

Mmodzi mwa alongo omwe abatizidwa aja ali m’nyumba akupemphera.

Pambuyo poti mwabatizidwa, muzipitiriza kumvera Atate (Onani ndime 12)


13. Kodi timabatizidwa bwanji m’dzina la Mwana? (Onaninso zithunzi.)

13 M’dzina la Mwana. Timadziwa kuti Yesu ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Yesu ndi “njira,” kapena kuti ndi iye yekha amene angatithandize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Yoh. 14:6) Yesu ndi wotiombola yemwe anatifera kuti tidzapeze moyo. Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tizimutsanzira tsiku lililonse, osati pa nthawi yokhayo imene tangobatizidwa. (1 Yoh. 2:6) Mofanana ndi iye, timalalikira mwakhama ndipo sitilola chilichonse kutisokoneza. (Luka 4:43) Timaloleranso kuzunzidwa chifukwa chotumikira Yehova mokhulupirika. (2 Tim. 3:12) Timalemekeza Yesu monga “mutu wa mpingo” ndipo timamvera mofunitsitsa abale amene anawapatsa udindo wotsogolera komanso kusamalira otsatira ake.—Aef. 4:​8, 11, 12; 5:23.

Mmodzi mwa abale omwe abatizidwa aja akumuwerengera lemba bambo wina, pamene akulalikira nyumba ndi nyumba.

Mukabatizidwa, muzizindikira udindo komanso mphamvu zimene Mwana ali nazo (Onani ndime 13)


14. (a) Kodi timabatizidwa bwanji m’dzina la mzimu woyera? (Onaninso zithunzi.) (b) Kodi odzozedwa amabatizidwanso ubatizo wina uti? (Onani bokosi lakuti “Ubatizo wa Odzozedwa.”)

14 M’dzina la mzimu woyera. Timavomereza mfundo za choonadi zokhudza mzimu woyera. Timadziwa kuti mzimu woyera si munthu komanso si mbali ya Utatu koma ndi mphamvu imene Mulungu amaigwiritsa ntchito. Mzimuwu ndi umenenso unkatsogolera aneneri komanso olemba Baibulo, choncho timaliwerenga nthawi zonse n’kumatsatira zimene limaphunzitsa. (2 Pet. 1:​20, 21) Timapewanso kuchita machimo akuluakulu podziwa kuti zimenezi zikhoza kuchititsa kuti Mulungu asamatipatse mzimu wake woyera komanso mzimuwo usamagwire ntchito bwino mumpingo.—Aef. 4:30.

Mmodzi mwa alongo omwe abatizidwa aja ali m’nyumba akuwerenga Baibulo.

Mukabatizidwa, muzilola kuti mzimu woyera uzikutsogolerani (Onani ndime 14)


Ubatizo wa Odzozedwa

Kuwonjezera pa kubatizidwa ndi madzi, Akhristu odzozedwa amabatizidwanso m’njira zotsatirazi:

  • Amabatizidwa ndi mzimu woyera akasankhidwa kuti akatumikire ndi Khristu kumwamba. (Mat. 3:11)

  • ‘Amabatizidwa mwa Khristu’ m’njira yakuti amakhala ogwirizana kwambiri ndi iye moti amatchedwa thupi la Khristu. (Agal. 3:​27, 28; 1 Akor. 12:27)

  • Amabatizidwa mu imfa ya Khristu akamatsatira chitsanzo chake mokhulupirika mpaka atamaliza utumiki wawo wapadziko lapansi n’kuukitsidwa kuti apite kumwamba. (Aroma 6:​3-5)

15. Kodi tiyenera kukhala otsimikiza kuchita chiyani?

15 Ngati munabatizidwa kale, yesetsani kuti mupitirize kumvetsa mfundo zonse zokhudza ‘chiphunzitso cha ubatizo.’c Muzichita zinthu mogwirizana ndi zimene munalonjeza Yehova pamene munadzipereka n’kubatizidwa. Koma bwanji ngati simunabatizidwebe? Kodi pali chimene chikukulepheretsani kubatizidwa? Munkhani yotsatira, tidzakambirana zimene mungachite kuti mubatizidwe.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi ubatizo wa Chikhristu umaimira chiyani?

  • Kodi anthu amene akupita kukabatizidwa amafunsidwa mafunso ati, nanga n’chifukwa chiyani?

  • Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera” kumatanthauza chiyani?

NYIMBO NA. 161 “Ndimasangalala Kuchita Zimene Mumafuna”

a Mawu a Chigiriki akuti ba’pti-sma, amene amamasuliridwa kuti “ubatizo,” amatanthauza “kumiza” kapena “kuviika.” Choncho ubatizo umatanthauza kuviika thupi lonse la munthu m’madzi osati kungomuwaza chabe, ngati mmene zipembedzo zina zimaphunzitsira.

b Anthu a ku Efesowa anali atabatizidwa “ubatizo wa Yohane.” (Mac. 19:3) Yohane M’batizi ankalimbikitsa Ayuda kuti alape machimo amene anachita pophwanya Chilamulo cha Mose. Ndipo amene alapa, iye ankawabatiza. (Maliko 1:​4, 5) Komabe ubatizo wa Yohane unasiya kugwira ntchito Chilamulo chitatha. Kuchokera nthawi imeneyo, Mulungu amavomereza “ubatizo umodzi,” umene umathandiza anthu kuti adzapulumuke.—Aef. 4:5.

c Onani nkhani yakuti “Kodi Ubatizo Umatanthauza Chiyani?” pagawo lakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” pa jw.org komanso pa JW Library.®

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anthu amene akufuna kubatizidwa aimirira pamsonkhano wadera kuti alengeze poyera za chikhulupiriro chawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena