Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 February tsamba 2-7
  • Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Athu Omwe Satumikira Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Athu Omwe Satumikira Yehova?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIFUNDO CHIZIKULIMBIKITSANI KUTI MUWATHANDIZE
  • ACHIBALE ANU AKALANKHULA KAPENA KUCHITA ZINTHU ZOKUKHUMUDWITSANI
  • MUZIKHALA OLEZA MTIMA N’KUMAYEMBEKEZERA KUTI ADZASINTHA
  • MUZIWASONYEZA KUTI MUMAWAKONDA
  • MUSASIYE KUTHANDIZA ACHIBALE ANU
  • Choonadi Sichibweretsa “Mtendere Koma Lupanga”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Mupeze Mayankho a Mafunso Awa
    Pulogalamu ya Msonkhano Wadera Wokhala ndi Woyang’anira Dera wa 2025-2026
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Mfundo Zoyambirira za M’Baibulo Zingakuthandizenibe Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 February tsamba 2-7

APRIL 6-12, 2026

NYIMBO NA. 82 “Muzionetsa Kuwala Kwanu”

Kodi Tingathandize Bwanji Achibale Athu Omwe Satumikira Yehova?

“Tisasiye kuchita zabwino.”—AGAL. 6:9.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti tipitirize kugwirizana ndi achibale athu omwe si a Mboni komanso mmene tingawathandizire kuti adziwe zokhudza Yehova ngati n’zotheka.

1-2. Kodi n’chiyani chingachititse kuti tisamagwirizane ndi achibale athu tikayamba kuphunzira choonadi?

YESU anauza munthu wina yemwe ankafuna kukhala wotsatira wake kuti: “Pita kunyumba kwa achibale ako ndipo ukawauze zonse zimene Yehova wakuchitira.” (Maliko 5:19) Apa Yesu anasonyeza kuti amadziwa kuti mwachibadwa anthufe timafuna titauzako anthu amene timawakonda nkhani yabwino imene tamva.

2 Kodi munamva bwanji mutamva uthenga wabwino kwa nthawi yoyamba? Muyenera kuti munkafunitsitsa mutauzako ena. Koma mwina achibale anu sanasangalale nazo. Kapenanso mmene munawauzira uthengawo zinachititsa kuti musemphane nawo maganizo. Ngati ndi choncho, mungatani kuti mupitirize kapena muyambirenso kugwirizana ndi achibale anu popanda kuphwanya mfundo za m’Baibulo?

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tikambirana (1) mmene chifundo chingatilimbikitsire kuti tizifunitsitsa kuthandiza achibale athu omwe si a Mboni, ngakhale kuti safuna kuphunzira za Yehova (2) zimene tingachite achibale athu akalankhula kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa (3) mmene tingawathandizire ngati titakhala oleza mtima n’kumayembekezera kuti adzayamba kutumikira Yehova m’tsogolo komanso (4) mmene tingasonyezere kuti timawakonda.

CHIFUNDO CHIZIKULIMBIKITSANI KUTI MUWATHANDIZE

4. Kodi Yesu ankatani ngati anthu sakufuna kumvetsera uthenga wake?

4 Yesu sanasiye kuthandiza anthu amene sankafuna kumvetsera uthenga wake. Iye anadziyerekezera ndi munthu wogwira ntchito m’munda wa mpesa, amene anachita chilichonse chotheka kuti mtengo wa mkuyu umene sunkabereka uyambe kubereka zipatso. (Luka 13:​6-9) Pamene Yesu ankafotokoza fanizoli, anali atayesetsa kwa zaka zoposa zitatu kuthandiza Ayuda anzake kuti azimukhulupirira. Ndiye n’chifukwa chiyani sanasiye kuwathandiza? Iye ankamvera chisoni anthu ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti aziwalezera mtima.

5. N’chiyani chinkalimbikitsa Yesu kuti azimvera chisoni Ayuda anzake?

5 Yesu ankamvera chisoni Ayuda anzake chifukwa atsogoleri achipembedzo sankawathandiza kuti azikhulupirira Mulungu. Iye anaona kuti anthuwo anali “ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa.” (Maliko 6:34) Yesu atatsala pang’ono kufa analilira mzinda wa Yerusalemu podziwa kuti anthu ambiri mumzindawo adzafa chifukwa chopanda chikhulupiriro. (Luka 19:​41-44) Ifenso tikamamvera chisoni achibale athu, timafunitsitsa kuwathandiza.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kumalezera mtima achibale athu omwe si a Mboni? (Agalatiya 6:9)

6 Werengani Agalatiya 6:9. Ngakhale achibale athu atakhala kuti sakufuna kuphunzira za Yehova panopa, tiziwalezera mtima n’kupitiriza ‘kuwachitira zabwino.’ Zimatenga nthawi kuti munthu asiye zimene amakhulupirira kwambiri n’kuyamba kukhulupirira Yehova. Mwina inunso poyamba “munalibe chiyembekezo ndipo Mulungu simunkamudziwa mʼdzikoli.” (Aef. 2:12) Ngati ndi choncho, ndiye kuti munthu wina anakuthandizani kuphunzira za Yehova. Kodi zimenezi sizikukulimbikitsani kuti inunso muthandize achibale anu kuphunzira za Yehova ngati n’zotheka?

ACHIBALE ANU AKALANKHULA KAPENA KUCHITA ZINTHU ZOKUKHUMUDWITSANI

7. N’chiyani chimene chinapangitsa azichimwene a Yesu kuti asamukhulupirire?

7 N’kutheka kuti azichimwene a Yesu anamva zodabwitsa zimene iye anachita ali ku Galileya. (Luka 4:​14, 22-24) Koma poyamba sankamukhulupirira. (Yoh. 7:5) Baibulo silimanena chifukwa chake. Koma limatchula zinthu ziwiri zimene zinachititsa Ayuda ena kuti asakhale ophunzira a Yesu. Ena ankaopa kuti anthu a m’dera lawo asiya kuchita nawo zinthu. (Yoh. 9:​18-22) Pomwe ena ankamudziwa Yesu kuyambira ali mwana ndipo zinkawavuta kukhulupirira kuti angakhale Mwana wa Mulungu. (Maliko 6:​1-4) N’kutheka kuti azichimwene a Yesu analinso ndi maganizo amenewa. Kodi ndi mmenenso zilili ndi achibale anu?

8. N’chiyani chimene chingachititse achibale athu omwe si a Mboni kulankhula kapena kuchita zinthu zotikhumudwitsa?

8 Muziganizira zimene zachititsa kuti alankhule kapena kuchita zinazake. Azichimwene a Yesu ayenera kuti anali m’gulu la achibale ake omwe nthawi ina ananena kuti “wachita misala.” (Maliko 3:21) Kodi mwina analankhula zimenezi chifukwa chiyani? Nkhaniyi imasonyeza kuti Yesu anatanganidwa kwambiri moti analibe nthawi yoti adye. (Maliko 3:20) Ndiye kodi achibale akewo ankaona kuti iye akuchita zinthu monyanyira? N’kutheka. Achibale athu angamaganizenso kuti tikuchita zinthu mokokomeza tikamachita zinthu zokhuza kulambira. Ngati amaona choncho, tingachite bwino kumawasonyeza m’zochita zathu kuti ndife ololera.

9. N’chiyani chingathandize achibale athu kuti azitiona moyenera? (1 Petulo 3:​1, 2) (Onaninso zithunzi.)

9 Azikopeka ndi khalidwe lathu. Zolankhula komanso zochita zathu zingapangitse kuti achibale athu asinthe mmene amationera. (Werengani 1 Petulo 3:​1, 2.) Mwachitsanzo, mwamuna amene si wa Mboni akhoza kukhumudwa mkazi wake akapita kumisonkhano kapena akalowa mu utumiki. Popeza sangafune kuti mwamunayo azimva choncho, mkaziyo angasinthe ndandanda yake yochitira zinthu zokhudza kulambira kuti azikhala ndi nthawi yambiri yocheza naye. Mwachitsanzo, angamalowe mu utumiki pa nthawi imene mwamuna wake wachokapo kapena watanganidwa. Ngati mlongo atakhala wololera komanso wokonzeka kusintha, akhoza kuthandiza mwamuna wake kuti asinthe mmene amaonera a Mboni.

Zithunzi: 1. Mlongo akukonzeratu chakudya chamasana komanso khofi wa mwamuna wake yemwe si wa Mboni, asanapite ku ntchito. 2. Kenako, mlongoyo walowa mu utumiki ndi mlongo wina ndipo akuonetsa mwininyumba mfundo ya m’Baibulo pafoni yake.

Mukamalankhula kapena kuchita zinthu mokoma mtima, zingathandize mwamuna kapena mkazi wanu kusintha mmene amaonera a Mboni za Yehova (Onani ndime 9)f


10. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu anthu ena akamatinyoza?

10 Musamakakamizike kuyankha nthawi iliyonse imene achibale anu akukunyozani. Pamene anthu ankamunena kuti amadya komanso kumwa kwambiri, Yesu sanalimbane nawo. M’malomwake, iye analimbikitsa anthu kuti azichita chidwi ndi zimene amachita n’kuona ngati zinalidi zoipa. (Mat. 11:19) Anasonyezanso kuti sankakhwimitsa zinthu komanso ankapeza nthawi yosangalala pa moyo wake. (Yerekezerani ndi Yohane 2:​2, 6-10.) Mofanana ndi Yesu, nanunso simufunika kuyankha chilichonse chimene anthu akukunenerani. M’malomwake, muziwasonyeza achibale anu mwa zochita zanu kuti simumakhwimitsa zinthu komanso mumapeza nthawi yosangalala. Mukamachita zimenezi, iwo adzazindikira kuti zinthu zabodza zimene amamva zokhudza a Mboni si zoona.

MUZIKHALA OLEZA MTIMA N’KUMAYEMBEKEZERA KUTI ADZASINTHA

11. Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi achibale ake omwe anali osakhulupirira?

11 Nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zimasonyeza kuti Yesu anapitirizabe kuwalezera mtima abale ake. Mwachitsanzo, iwo ayenera kuti analipo ku Kana pamene iye anachita zodabwitsa kwa nthawi yoyamba. (Yoh. 2:​11, 12) Koma monga tafotokozera kale, achibale akewa sanamukhulupirirebe. Komabe Yesu sanasiye kuwakonda. Baibulo limasonyeza kuti patapita zaka pafupifupi zitatu kuchokera pamene anachita zodabwitsa zija ku Kana, iye ankalankhula mokoma mtima kwa azichimwene akewo.—Yoh. 7:​5-8.

12. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tiziyembekezerabe kuti achibale athu omwe satumikira Yehova adzasintha?

12 Zimene taphunzira zokhudza chifundo cha Yehova zimatithandiza kuti tiziyembekezerabe kuti achibale athu adzasintha. Zipembedzo zabodza zikadzawonongedwa, achibale athu akhoza kudzakumbukira kuti tinawauza kuti zimenezi zidzachitika.a (Chiv. 17:16) Mwina nawonso akhoza kudzayamba kutumikira Yehova chisautso chachikulu chitayamba. Komabe ngakhale panopa ngati achibale athu atakumana ndi mavuto, tizichita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize. Iwo akhoza kuyamba kumvetsera uthenga wa m’Baibulo ngati atazindikira kuti timawakonda.

MUZIWASONYEZA KUTI MUMAWAKONDA

13. Ngakhale kuti timatanganidwa ndi kutumikira Yehova, kodi tiyenera kusamala ndi chiyani?

13 Ngakhale kuti timatanganidwa ndi kutumikira Yehova, tisamachititse achibale athu kukhala ndi maganizo akuti tilibe nawo ntchito kapena tinasiya kuwakonda. (Mat. 7:12) Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timawaona kuti ndi ofunika? Taganizirani njira zotsatirazi.

14-15. Kodi ndi njira imodzi iti imene tingasonyezere kuti timakonda achibale athu omwe si a Mboni? Perekani chitsanzo.

14 Muzilankhula nawo pafupipafupi ndipo muzisonyeza kuti mumawakonda. Timasonyeza kuti timakonda achibale athu tikamalankhulana nawo pafupipafupi, kuwafotokozera mmene zinthu zikuyendera pa moyo wathu. Mwachitsanzo, tingawatumizire meseji ndi zithunzi zimene tinajambula pa nthawi imene tinali pa holide, pa ulendo kapenanso pamene timachita zosangalatsa ndi anzathu. Nthawi zina timangofunika kuwapatsa kamphatso kakang’ono kapena kuwalembera kalata kuti tizigwirizana nawo kwambiri. Zinthu ngati zimenezi zimasonyeza kuti timawakonda.

15 Taganizirani za mlongo wina wa ku Armenia dzina lake Anna. Nthawi zambiri anthu a m’banja lake amachitira zinthu pamodzi makamaka pa masiku okumbukira kubadwa komanso maholide ena. Anna ataphunzira choonadi, achibale ake ankada nkhawa kuti zimene waphunzirazo zichititsa kuti asamagwirizane nawo. Iwo ankadanso nkhawa kuti zimene anasankhazi, zoti akhale wa Mboni, zisokoneza tsogolo lake. Ndiye kodi Anna amatani kuti azigwirizana nawo? Iye anati: “Ndikapita kukaona achibale anga ndimawauza zokhudza moyo wanga komanso zimene ndakhala ndikuchita. Ndimawaitaniranso kunyumba kwanga n’kukonza zoti adziwane ndi anzanga. Izi zathandiza kuti abale anga ambiri adziwane bwino ndi anzanga ndipo amamasuka nawo.” Iye anapitiriza kuti: “Achibale anga ambiri amanena kuti ndikusangalala ndipo sadandaulanso za ine.”

16. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda mchimwene wake Yakobo? (Onaninso mawu a m’munsi.)

16 Muzichita nawo chidwi. Ataukitsidwa, Yesu anasonyeza kuti ankakonda mchimwene wake Yakobo poonekera kwa iye payekha. (1 Akor. 15:7) Tangoganizani mmene Yakobo anamvera atazindikira kuti Yesu ankamukondabe. Imeneyi iyenera kuti ndi nthawi yomwe Yakobo anatsimikiza kuti Yesu ndi Mesiya. Pambuyo pokumana ndi Yesu, n’kutheka kuti Yakobo anathandiza abale ake kuzindikira udindo umene Yesuyo ali nawo.b—Mac. 1:14.

17. Kodi tingatsatire bwanji mfundo yopezeka pa Aroma 12:15? (Onaninso chithunzi.)

17 Werengani Aroma 12:15. Tikamathandiza achibale athu pa nthawi imene zinthu zili bwino komanso pamene akumana ndi mavuto, iwo akhoza kusintha mmene amationera.c Mwachitsanzo, ngati mwana wabadwa kwa achibale athu tikhoza kuwapatsa mphatso posonyeza kuti tikusangalala nawo limodzi. Ngati aferedwa, tikhoza kuwalankhula mawu otonthoza, kupeza njira zina zimene tingawathandizire kapenanso kuwalembera kakhadi. Ndipotu tingamawalembere mameseji, kuwaimbira foni kapena kumawayendera pafupipafupi makamaka pamene akukumana ndi mavuto.

Mlongo yemwe tamuona m’zithunzi zoyambirira uja akudzijambula limodzi ndi mwamuna wake komanso apongozi ake aakazi omwe si a Mboni. Apongozi akewo ali panjinga ya olumala.

Mukamathandiza achibale anu pa nthawi imene akufunikira kwambiri thandizo, akhoza kusintha mmene amakuonerani komanso mmene amaonera zimene mumakhulupirira (Onani ndime 17)g


Kodi Muyenera Kupita ku Ukwati Kapena Kumaliro a Wachibale Yemwe Si wa Mboni?

Nthawi zambiri ukwati komanso maliro amachititsa kuti anthu apachibale akumane pamodzi. Musanapite kumaliro kapena ku ukwati mungachite bwino kuganizira mfundo za m’Baibulo zotsatirazi:

  • Kodi pamwambowo padzakhala miyambo yachipembedzo kapena ayi? (2 Akor. 6:​14, 15)

  • Ngati mudzapiteko, kodi mudzakwanitsa kukana kuchita nawo miyambo yosemphana ndi Malemba? (Miy. 22:3)

  • Kodi achibale anu amadziwa kuti simuchita nawo miyambo yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo?

  • Ngati mwapita kumwambo womwe ukuchitikira m’tchalitchi, kodi zimenezi zingakhudze bwanji Akhristu ena? (Afil. 1:10)

Kaya mwasankha zotani, nthawi zonse muzifotokozera achibale anu momveka bwino zimene mumakhulupirira. Koposa zonse, muziyesetsa kukhala ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu.e

18. Kodi tingatsanzire bwanji Andireya?

18 Tiziwathandiza kudziwana ndi abale ndi alongo. Andireya atadziwa kuti Yesu ndi Mesiya, anakaitana mchimwene wake Petulo kuti akakumane naye. (Yoh. 1:​40-42) Ifenso tingachite zofanana ndi zimenezi. Mwachitsanzo, nthawi zina tingaitanire wachibale wathu kumisonkhano kapenanso kuti tidzadye naye limodzi ndi anzathu. Iye akakumana ndi abale ndi alongo, zidzamuthandiza kudziwa kuti a Mboni za Yehova si osiyana ndi anthu ena onse ndipo ndi anthu abwino komanso achikondi.

19. Ngakhale kuti achibale athu sakumvetsa zimene timakhulupirira, kodi tizichita nawo bwanji zinthu? (1 Petulo 3:15)

19 Werengani 1 Petulo 3:15. Achibale athu sangamvetse chifukwa chimene timakanira kuchita zinthu zinazake. Koma nthawi zonse amakumbukira tikawachitira zinthu mokoma mtima komanso mwaulemu. Angayamikirenso tikamayesetsa kupeza nthawi yochita nawo zinthu ngati sitinakhale nawo pa zochitika zinazake. Mwachitsanzo, sitingachite nawo miyambo komanso zikondwerero zosemphana ndi Malemba, koma tikhoza kuwayendera, kudya nawo limodzi komanso kuwapatsa mphatso nthawi zina.

MUSASIYE KUTHANDIZA ACHIBALE ANU

20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chitsanzo cha Yakobo n’cholimbikitsa?

20 Yakobo anataya mwayi wogwira ntchito limodzi ndi Yesu koma kenako anadzakhala wophunzira wake. (Agal. 1:​18, 19; 2:9) Ngakhale kuti sanali m’gulu la ophunzira a Yesu oyambirira, iye ankatsatira ndi mtima wonse zimene Yesu anaphunzitsa. Mwachitsanzo, mouziridwa iye analemba kalata imene mfundo zake zambiri ndi zimene Yesu anatchula pa ulaliki wa paphiri.d

21. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kuthandiza achibale athu omwe si a Mboni?

21 Ngakhale titayesetsa kuthandiza achibale athu kuti adziwe Yehova, nthawi zina sangasonyeze kuti akufuna kuphunzira choonadi. Tizipitirizabe kuwathandiza chifukwa nthawi iliyonse imene tawachitira zinthu mokoma mtima, timakhala tikutsanzira Mulungu wathu Yehova komanso Mwana wake Yesu. (Luka 6:​33, 36) M’kupita kwa nthawi, chikondi chimene timawasonyeza chingawathandize kusintha mmene amationera. Akhozanso kumakumbukira mfundo za choonadi zimene tinawauzapo m’mbuyomo. Ngati sitingasiye kuwathandiza, tidzasangalala kuona achibale athu akuyamba kutumikira Yehova limodzi nafe.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi chifundo chingatilimbikitse bwanji kuti tizithandiza achibale athu omwe si a Mboni?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe oleza mtima n’kumayembekezera kuti achibale athu adzayamba kutumikira Yehova?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda achibale athu omwe si a Mboni?

NYIMBO NA. 60 Akamvera Adzapeza Moyo

a Onani nkhani yakuti “Kodi Tikudziwa Chiyani pa Nkhani ya Mmene Yehova Adzaweruzire Anthu?” mu Nsanja ya Olonda ya May 2024, tsamba 11, ndime 11-13.

b Zikuoneka kuti azichimwene ake a Yesu, Yakobo komanso Yuda, anakhala ophunzira ake pambuyo poti iye waukitsidwa.

c Onani bokosi lakuti “Kodi Muyenera Kupita ku Ukwati Kapena Kumaliro a Wachibale Yemwe Si wa Mboni?”

d Yerekezerani Yakobo 1:2 ndi Mateyu 5:​11, 12; Yakobo 1:19 ndi Mateyu 5:22; Yakobo 1:22; 2:24 ndi Mateyu 7:21; Yakobo 2:13 ndi Mateyu 5:7; 6:​14, 15.

e Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002, komanso ya November 15, 2007.

f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo asanalowe mu utumiki akukonza chakudya cha mwamuna wake.

g MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo yemwe uja wapita kukaona apongozi ake omwe si a Mboni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena