APRIL 20-26, 2026
NYIMBO NA. 49 Tizisangalatsa Mtima wa Yehova
Yesetsani Kuti Mubatizidwe
“Inoyo ndi nthawi yeniyeni yovomerezedwa.”—2 Akor. 6:2.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona kuti inoyi ndi nthawi yabwino yoti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova n’kubatizidwa.
1. (a) Kodi ndi madalitso ena ati amene timapeza tikabatizidwa? (b) Nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?
KODI munadzipereka kwa Yehova n’kusonyeza zimenezi pobatizidwa m’madzi? Ngati zili choncho ndiye kuti munapempha kuti Mulungu akupatseni chikumbumtima choyera. (1 Pet. 3:21) Munapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata komanso anthu amene angoyamba kumene kusonkhana ndi mpingo wanu. Pamenepatu munasankha bwino kwambiri. Koma bwanji ngati pofika pano simunabatizidwebe? N’zosakayikitsa kuti mumakonda Yehova ndipo mumafuna kuchita zimene iye amafuna. Ubatizo ndi wofunika kuti Yehova akukhululukireni machimo komanso azisangalala nanu. (Mac. 2:38-40) Ngakhale zili choncho, mungamazengereze kuti mubatizidwe. Ndiye kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni? Munkhaniyi tikambirana (1) chifukwa chake anthu ena amazengereza kuti abatizidwe, (2) chifukwa chake nthawi zonse muyenera kumakumbukira kuti mapeto ayandikira komanso (3) madalitso amene mudzapeze chifukwa chobatizidwa mwamsanga.
N’CHIFUKWA CHIYANI ENA AMAZENGEREZA?
2. N’chifukwa chiyani ena amazengereza kubatizidwa?
2 Ena amazengereza kuti abatizidwe chifukwa cha mantha. Mwachitsanzo, ngakhale kuti amafuna atamatumikira Yehova, amaopa kuti sadzakwanitsa kuchita zonse zofunika kuti azimusangalatsa. Ngati mumamva choncho, muziwerenga mavesi a m’Baibulo amene angakutsimikizireni kuti Yehova sayembekezera kuti simuzilakwitsa chilichonse komanso kuti amasangalala mukamachita zonse zomwe mungathe pomulambira. (Sal. 103:13, 14; Akol. 3:23) Ngati mumaopa kuti muzitsutsidwa, muzimupempha kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima ngati wamasalimo yemwe anati: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”—Sal. 118:6.
3. Kodi ndi maganizo ati amene angalepheretse anthu ena kubatizidwa? (Onaninso chithunzi.)
3 Anthu ena amene amakonda Yehova amazengereza kubatizidwa chifukwa amaona kuti sadziwa zambiri. Koma kodi mumafunika kudziwa zinthu zochuluka bwanji kuti mubatizidwe? Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo. Chivomerezi chitagwedeza ndende imene mtumwi Paulo ndi Sila anaikidwamo, iwo analalikira woyang’anira ndendeyo ndi anthu a m’banja lake. Munthuyu limodzi ndi anthu a m’banja lakewo ayenera kuti anazindikira kuti pachitika zinthu zodabwitsa. Kuwonjezera pamenepa, iwo anaphunzira zambiri zokhudza Yehova ndi Yesu usikuwo ndipo “pasanapite nthawi yaitali” anabatizidwa. (Mac. 16:25-33) Ngati inunso mumadziwa Yehova, mumamukonda ndi mtima wanu wonse, mumadziwa mfundo zoyambirira za m’Baibulo, munalapa machimo anu ndipo ndinu wotsimikiza mtima kuti muzitsatira mfundo za Mulungu nthawi zonse, ndiye kuti ndinu wokonzeka kubatizidwa.—Maliko 12:30.
Paulo ndi Sila analalikira kwa woyang’anira ndende limodzi ndi banja lake ndipo “pasanapite nthawi yaitali” anabatizidwa (Onani ndime 3)
4. Kodi n’chiyaninso chimene chimapangitsa kuti ena asamafune kubatizidwa? (Onaninso chithunzi.)
4 Anthu ena amene ali n’cholinga choti abatizidwe amaopa kuchita zimenezo poganizira mtengo wake, kapena kuti zimene angadzafunike kusintha. N’zoona kuti timafunika kuganizira kwambiri mmene zosankha zathu zidzakhudzire moyo wathu. (Luka 14:27-30) Komabe, anthu ena amadera nkhawa zimene adzafunike kusiya kuti azitumikira Mulungu. Mmenemu ndi mmene Candace, yemwe analeredwa m’banja la Mboni, anamvera atapemphedwa kuti aziphunzira Baibulo. Pa nthawiyi n’kuti atakula kale. Iye anati: “Ndinkadziwa ndithu zimene Yehova amafuna kungoti ndinkasangalala ndi zimene ndinkachita m’dzikoli. Ndinkaona kuti zinali zovuta kuti ndisinthe.” Enanso amada nkhawa kuti sazidzakwanitsa kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene anthu obatizidwa amafunika kutsatira. Iwo amaganiza kuti pambuyo poti abatizidwa akhoza kudzachita tchimo lalikulu n’kuchotsedwa mumpingo. Ngati inunso mukuda nkhawa ndi zimenezi, kodi muyenera kuchita chiyani?
Ena amene amafuna kubatizidwa amada nkhawa akaganizira zinthu zimene akufunika kusiya kuti azitumikira Mulungu (Onani ndime 4)
5. Kodi tiziganizira kwambiri za chiyani ngati tikuopa kubatizidwa? (Mateyu 13:44-46)
5 Tikamafuna kugula chinthu, sitimangoganizira za mtengo wake koma timaganiziranso za kufunika kwake. Tikaona kuti chinthucho n’chofunika kwambiri poyerekezera ndi mtengo wake timachigula nthawi yomweyo. Mofanana ndi zimenezi, tikamafuna kubatizidwa tisamangoganizira za mtengo, kapena kuti zinthu zimene tidzafunike kusintha koma tiziganizira kwambiri za kufunika kokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo awiri pomveketsa mfundo imeneyi. (Werengani Mateyu 13:44-46.) Mufanizo lililonse, munthu anagulitsa chuma chake chonse n’cholinga choti akwanitse kugula chinthu chamtengo wapatali chomwe anapeza. Nanunso munapeza chinthu chamtengo wapatali chomwe ndi choonadi chokhudza Ufumu. Ngati mukuona kuti n’zovuta kumatsatira mfundo za choonadi, muyenera kuganizira kwambiri mafanizo a Yesuwa. Mungadzifunse kuti: ‘N’chiyani chimanditsimikizira kuti mfundo zomwe ndinapezazi ndi zamtengo wapatali? Kodi ndimayamikira ubwenzi wapadera umene ndili nawo ndi Yehova, chiyembekezo chimene anandipatsa komanso mwayi wokhala ndi abale ndi alongo achikondi?’ Zimene mungayankhe, zingakuthandizeni kudziwa zimene mungafunike kuchita kuti mubatizidwe.
6. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizigwiritsa ntchito zimene tikuphunzira?
6 Mufanizo lake la wofesa mbewu, Yesu anafotokoza mmene mtima wa munthu ungamulepheretsere kupita patsogolo mwauzimu. Komabe iye anasonyezanso kuti anthu ena a mtima wabwino adzamvetsera uthenga wa Ufumu n’kumaugwiritsa ntchito. (Luka 8:5-15) Ndiye ngati simukudziwa zoti muchite, musataye mtima. Yehova angakuthandizeni kuti mukhale ndi mtima watsopano womwe ungachititse kuti muzimvera malangizo ake. Choncho muzimupempha kuti afewetse mtima wanu n’cholinga choti muzikonda zimene mukuphunzira n’kumazitsatira pa moyo wanu.—Ezek. 18:31; 36:26.
7-8. N’chifukwa chiyani achinyamata ena amalephera kupita patsogolo n’kufika pobatizidwa? (Onaninso chithunzi.)
7 Achinyamata ena amene amakonda Yehova amalephera kupita patsogolo n’kufika pobatizidwa chifukwa cha zimene anthu ena amalankhula kapena kuchita. Mwachitsanzo, aphunzitsi ena akhoza kumachititsa ana a sukulu kuona kuti palibe vuto kuchita makhalidwe enaake, ngakhale amene amaphwanya mfundo za Mulungu. Koma zimenezi zimabweretsa mavuto aakulu. (Sal. 1:1, 2; Miy. 7:1-5) Mungapewe msampha umenewu ngati mutamatsanzira wamasalimo amene anauza Yehova kuti: “Ndine wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse, chifukwa ndimaganizira mozama zikumbutso zanu.”—Sal. 119:99.
8 Malipoti akusonyeza kuti makolo ena a Mboni amachititsa kuti zikhale zovuta kuti ana awo abatizidwe. Iwo amalimbikitsa anawo kuti aphunzire kwambiri komanso adzapeze ntchito yapamwamba. Amalepheranso kuwathandiza kukhala ndi zolinga zauzimu. Ndiye kodi inuyo mukuona kuti pali zinthu zina zimene makolo anu angachite kuti mukwaniritse cholinga chanu choti mubatizidwe? Bwanji osakonza zoti mukambirane nawo za nkhaniyi? Musalole kuti msinkhu wanu ukulepheretseni kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova.—Miy. 20:11.
Muzikambirana ndi makolo anu zokhudza kubatizidwa (Onani ndime 8)
9. N’chifukwa chiyani anthu ena amachedwa kubatizidwa?
9 Anthu ena omwe ndi oyenerera kubatizidwa amachedwa kuchita zimenezi chifukwa chotengera zochita za anzawo. Mwina amadikira kuti munthu wina afikenso kaye poyenerera kubatizidwa. Mwachitsanzo, iwo angamafune kudzabatizidwa tsiku limodzi ndi mnzawo kapena wachibale wawo. Palibe vuto kubatizidwa tsiku limodzi ndi anthu omwe mumawakonda. Koma kodi zimenezi ziyenera kukulepheretsani kuti mubatizidwe panopa? Muzikumbukira kuti munthu amadzipereka kwa Mulungu payekha. Ndiye musamadikire anthu ena kuti mubatizidwe.—Aroma 14:12.
N’CHIFUKWA CHIYANI MUYENERA KUMAKUMBUKIRA KUTI MAPETO AYANDIKIRA?
10. N’chifukwa chiyani ena amazengereza kupita patsogolo mwauzimu?
10 Kuwonjezera pa zifukwa zimene tazifotokoza mu ndime zam’mbuyomu, ena akhoza kumazengereza kuti abatizidwe poganiza kuti nthawi ikanalipo. Koma kodi zimenezi n’zomveka? Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Khalani okonzeka, chifukwa Mwana wa munthu adzafika pa ola limene simukuliganizira.”—Luka 12:40.
11. Tikayamba kudziwa zambiri zokhudza Yehova, kodi timafunitsitsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (Salimo 119:60)
11 Tiyenera kudzipereka kwa Yehova chifukwa chomukonda. Tikamapitiriza kumudziwa bwino m’pamenenso timaona kuti iye amatikonda kwambiri ndipo malamulo amene amatipatsa amathandiza ife tomwe. (Werengani Salimo 119:60.) Yakobo anafotokoza chifukwa china chotipangitsa kuti tizimvera malamulo a Yehova mofulumira. Iye ananena kuti palibe amene amadziwa zimene zichitike mawa. Mwina sitingafike mawa kuti ‘tidzachite zabwino’ mawalo, choncho timafunika kuchitapo kanthu panopa. Inoyi ndi nthawi yoti tichite zimene Yehova akufuna.—Yak. 4:13-17.
12. Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Yesu la munda wa mpesa?
12 Taganizirani za fanizo la Yesu la munda wa mpesa. Iye anafotokoza kuti anthu amene anagwira ntchito kwa ola limodzi lokha analandira malipiro ofanana ndi a anthu amene anagwira ntchito tsiku lonse. Komabe taganizirani chifukwa chimene omwe anagwira ntchito kwa ola limodziwo anapereka, chimene chinawapangitsa kuti asayambe kugwira ntchitoyo mofulumira. Iwo anati: “Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.” Sikuti anthuwo anali aulesi, kungoti panalibe amene anawapatsa ganyu. Koma atangoitanidwa, nthawi yomweyo anayamba kugwira ntchito. (Mat. 20:1-16) Ifenso Yesu watiitana kuti tikhale ophunzira ake komanso kuti tizilalikira zokhudza Ufumu. Ndiye tiyeni tizichita zimene Yesu akutipempha tikangoyamba kuphunzira za iye.
13. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mkazi wa Loti?
13 Anthu amene amazengereza kubatizidwa, akhoza kudzazindikira nthawi itatha kale kuti n’zovuta kusintha moyo wawo pa nthawiyo kuti azisangalatsa Mulungu. M’pake kuti Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Luka 17:31-35) Mkazi wa Loti ankadziwa kuti Yehova watsala pang’ono kuwononga mzinda wa Sodomu ndi Gomora. Koma zikuoneka kuti analephera kusiya zinthu zimene ankazikonda kwambiri. (Gen. 19:23-26) Nkhaniyi imatikumbutsa kuti khomo la chipulumutso silidzakhala lotsegula mpaka kalekale. Nthawi ya Yehova ikadzakwana, khomoli lidzatsekedwa ndipo silidzatsegulidwanso.—Luka 13:24, 25.
14. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala tcheru ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo?
14 Tsiku lililonse zochitika zam’dzikoli zimasonyeza kuti maulosi a m’Baibulo okhudza mapeto akukwaniritsidwa. Mwina simukukhudzidwa mwachindunji ndi zina mwa zochitikazi, komabe zimene zikuchitika m’madera osiyanasiyana zizikuthandizani kudziwa kuti nthawi yatha ndipo mukufunika kubatizidwa. Taganizirani zimene zinachitika m’nthawi ya atumwi. Mtumwi Petulo analimbikitsa Akhristu kuti ‘akhale maso,’ kapena kuti akhale okonzeka chifukwa ‘mapeto a zinthu zonse anali atayandikira.’ (1 Pet. 4:7) Zikuoneka kuti mapeto amene anatchulawa ankaimira kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake. Anthu omwe Petulo anawalemberawa ankakhala kutali ndi Yerusalemu moti sakanakhudzidwa mwachindunji ndi kuwonongedwa kwa mzindawo. (1 Pet. 1:1) Komabe iwo ataona kuti ulosiwu wakwaniritsidwa, zinawathandiza kukhulupirira kwambiri kuti maulosi enanso a Yehova adzakwaniritsidwa. Inunso mukamaona kukwaniritsidwa kwa maulosi okhudza mapeto a dzikoli, zidzakuthandizani kuti muzikhala maso n’kukwaniritsa cholinga chanu choti mubatizidwe.
15. Kodi nthawi ya kubwera kwa tsiku la Yehova tiziiona bwanji? (2 Pet. 3:10-13)
15 M’kalata yake yachiwiri, Petulo anafotokoza mmene tiyenera kuonera nthawi ya kubwera kwa tsiku la Yehova la chiweruzo. Kwa Akhristu a pa nthawiyo, tsikuli linali kutali kwambiri. Komabe iye anawauza kuti azilikumbukira nthawi zonse, kapena kuti kulifunitsitsa. (Werengani 2 Petulo 3:10-13.) Ifenso tingamachite zimenezi ngati titakhala okonzeka komanso kumafunitsitsa kuti libwere, pochita ntchito zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu. Yehovatu amasangalala kukuonani mukuchita zinthu zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa iye ndipo adzasangalalanso kukuonani mukudzipereka n’kubatizidwa.
MADALITSO AMENE MUNGAPEZE CHIFUKWA CHOBATIZIDWA PANOPA
16. Kodi nthawi yabwino yoti munthu abatizidwe ndi iti? (2 Akorinto 6:1, 2) (Onaninso zithunzi.)
16 Nthawi yabwino yoti mubatizidwe ndi inoyi. (Werengani 2 Akorinto 6:1, 2.) Nduna ya ku Itiyopiya yomwe inakumana ndi Filipo inazindikira kufunika kochita zinthu mwachangu. Ndunayi itamvetsa uthenga wabwino n’kuona kuti pali mwayi woti ikhoza kubatizidwa, sinayambe kuganiza kuti: ‘Tamandiphunzitsani kaye, ndikufuna ndidziwe zambiri ndisanabatizidwe. Tipezanso madzi ena kumene tikuloweraku.’ M’malomwake ndunayi inafunsa Filipo kuti: “Chikundiletsa kubatizidwa nʼchiyani?” (Mac. 8:26, 27, 35-39) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino. Ndunayi itabatizidwa, “inapitiriza ulendo wake ikusangalala.”
Mungaphunzirepo kanthu pa zimene nduna ya ku Itiyopiya inachita. Nthawi yabwino yoti mubatizidwe ndi inoyi (Onani ndime 16)a
17. Kodi simukuyenera kukayikira za chiyani?
17 Ngati mukuzengereza kubatizidwa, dziwani kuti Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kuti mukhale mnzake wapamtima. (Aroma 2:4) Angakuthandizeninso kulimbana ndi mantha, nkhawa komanso zinthu zina zomwe zingakulepheretseni kupita patsogolo mwauzimu. Kubatizidwa kudzakuchititsani kuti mukhale ndi chikumbumtima chabwino ndipo mudzasiya kuganizira zinthu zakumbuyo. (Afil. 3:8, 13) Mukatero muzidzaganizira kwambiri za zinthu zakutsogolo zomwe ndi kukwaniritsidwa kwa zimene Yehova analonjeza kwa anthu amene adzipereka kwa iye n’kubatizidwa.—Mac. 3:19.
NYIMBO NA. 38 Adzakulimbitsa
a MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI Pachikuto:: Mofanana ndi nduna ya ku Itiyopiya, imene inauza Filipo kuti ikufuna kubatizidwa, wophunzira Baibulo wapita kwa akulu kukawauza kuti akufuna kubatizidwa.