Kodi ndi Chiyani Chimene Chidzachitikire Zipembedzo?—Zimene Baibulo Limanena
Kodi mumakhumudwa kapena kunyansidwa ndi zimene zipembedzo zimachita? Ngakhale kuti zipembedzo zabweretsa zinthu zina zabwino kwa anthu, zachititsanso kuti azivutika. Buku lina lofotokoza za zipembedzo ndi nkhondo linanena kuti: “Nkhondo zina zoopsa kwambiri zimene zachitika m’mbuyomu zachitika chifukwa cha kusiyana kwa zimene zipembedzo zimakhulupirira.” Nthawi zambiri atsogoleri achipembedzo, akhala akugwiritsa ntchito chipembedzo osati polambira Mulungu koma polimbikitsa mfundo zandale. Ndipo atsogoleri ena azipembedzo akhala akubisa milandu yogwirira kapena yokhudza kuba ndalama imene atsogoleri ena azipembedzo achita.
Ngati munakhumudwapo ndi zipembedzo, mwina mungafune kudziwa mmene Mulungu amazionera. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu sasangalala ndi zipembedzo zina chifukwa cha zomwe zakhala zikuchita. Ndipo limatchulanso maulosi ofotokoza zimene iye adzachite ndi zipembedzozi. Pogwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa, Baibulo limafotokoza kuti posachedwapa Mulungu adzachita zinazake zimene sanachitepo kwa zipembedzo zonse padzikoli.
Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza tsogolo la zipembedzo?
Ulosi: Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso, limafotokoza za hule amene amadziwika kuti Babulo Wamkulu. Hule limeneli, lakhala pamsana pa chilombo chofiira kwambiri. Pamapeto pake likuphedwa ndi chilombo chofiira kwambiri chija komanso chilombo china cha nyanga 10.—Chivumbulutso 17:3, 5, 16.
Tanthauzo: Hule kapena kuti Babulo Wamkulu, akuimira zipembedzo zonse zabodza zimene Mulungu sazivomereza.a Chilombo chofiira kwambiri, chikuimira bungwe la United Nations (UN),b ndipo chilombo cha nyanga 10 chikuimira a ndale padziko lonse.c Zimene hulelo likuchita pokhala pamsana pa chilombo chofiira kwambiri, zikusonyeza kuti zipembedzo zabodza zakhala zikuuza a ndale zochita ngakhalenso kuwalamula kumene. Ndiye zimene zilombozi zikuchita popha huleli, zikusonyeza kuti bungwe la UN komanso mayiko ena amene amalithandiza, adzaukira zipembedzo zonse zabodza padzikoli n’kuziwononga. Zochitika zapadera zimenezi zidzachititsa kuti zipembedzo zonse ziwonongedwe.
Kodi zipembedzo zabodza zidzawonongedwa bwanji?
Ulosi: “Nyanga 10 zimene waziona zija komanso chilombo, zidzadana ndi hulelo. Zidzatenga zinthu zake zonse . . . nʼkulipsereza ndi moto. Chifukwa Mulungu anaika pulani mʼmitima yawo [mitima ya atsogoleri] kuti zichite mogwirizana ndi maganizo ake komanso kuti zikwaniritse maganizo awo ofanana aja, popereka ufumu wawo kwa chilombo. . . . Mʼtsiku limodzi, miliri yake idzafika. Miliri yake ndi imfa, kulira komanso njala ndipo adzapserera ndi moto chifukwa Yehovad Mulungu, amene anamuweruza ndi wamphamvu.”—Chivumbulutso 17:16, 17; 18:8.
Tanthauzo: Mulungu adzaika “maganizo ake” m’mitundu ya anthu apadziko lapansi. Iye adzachititsa kuti apereke “ufumu wawo” kapena mphamvu zawo pa ndale ku bungwe la UN. Pamapeto pake, bungwe la UN likadzangolandira mphamvu kuchokera ku mitundu ya anthu, lidzawononga zipembedzo zonse zabodza padziko lonse. Kuwonongedwa kumeneku kudzachitika mofulumira komanso modzidzimutsa ngati kwachitika “mʼtsiku limodzi,” ndipo anthu ambiri adzadabwa chifukwa adzakhala kuti samayembekezera.—Chivumbulutso 18:21.
N’chifukwa chiyani zipembedzo zabodza zidzawonongedwe?
Ulosi: “Machimo ake aunjikana mpaka kumwamba, ndipo Mulungu wakumbukira zochita zake zopanda chilungamo.”—Chivumbulutso 18:5.
Tanthauzo: Kwa zaka zambiri, zipembedzo zabodza zakhala zikuchita zinthu zambiri zosalemekeza Mulungu. Onani ena mwa “machimo ake,” amene achititsa kuti Mulungu amupatse chiweruzo:
Kulowerera ndale. Yesu Khristu anaphunzitsa otsatira ake kuti asamalowerere ndale, m’malomwake aziyembekezera ufumu wa Mulungu, umene ndi boma la kumwamba limene lidzalowe m’malo mwa maboma a anthu.e (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10; Yohane 6:15; 18:36) Koma zipembedzo zabodza zimachita zosiyana ndi zimenezi. Chifukwa chakuti amalowerera kwambiri ndale m’malo mokhala okhulupirika kwa Mulungu, ulosi wa m’buku la Chivumbulutso umanena kuti Babulo Wamkulu ali ndi mlandu ‘wachiwerewere ndipo anam’patsa dzina lomuyenerera lakuti ndi “hule lalikulu.”—Chivumbulutso 17:1, 2; Yakobo 4:4.
Chiwawa. Baibulo limafotokoza kuti zipembedzo zabodza zili ndi mlandu wakupha “onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 18:24) Sikuti zipembedzo zambiri zangolephera kuphunzitsa anthu ake kufunafuna mtendere, koma zakhala zikulimbikitsanso kuti azimenya nkhondo kapena kuchita zauchigawenga.
Dyera. Zipembedzo zabodza ‘zimasangalala ndi chuma mopanda manyazi.’ (Chivumbulutso 17:4; 18:7) Zipembedzo zambiri zakhala zikugwiritsa ntchito mphamvu zake komanso anthu amene amagwirizana nazo kuti zipeze chuma. Mulungu sasangalala ndi dyera limeneli.—Tito 1:7.
Mabodza. Zipembedzo zabodza zimalimbikitsa ziphunzitso komanso miyambo yomwe ndi yosemphana ndi mfundo zachoonadi cha m’Baibulo.f Popeza kuti zipembedzo zabodza zimaphunzitsa zinthu zambiri zabodza komanso kulimbikitsa miyambo imene imasocheretsa anthu zomwe sizilemekeza Mulungu, ulosi umazitchula kuti ndi “mayi . . . wa zonyansa zapadziko lapansi.”—Chivumbulutso 17:5; 18:23.
Kodi zipembedzo zonse zidzawonongedwa?
Ayi. Buku la Chivumbulutso limanena za gulu la anthu ochokera kumitundu yonse lomwe limatchulidwa kuti “khamu lalikulu.” (Chivumbulutso 7:9) Khamu lalikululi likufotokozedwa kuti ‘lavala mikanjo yoyera,’ zomwe zikutanthauza kuti amalambira Mulungu mokhulupirika m’njira imene imamusangalatsa. Anthu amenewa adzapulumuka pa ‘chisautso chachikulu,’ nthawi imene Baibulo limanena kuti ndi nthawi yomwe zipembedzo zabodza komanso adani a Mulungu adzawonongedwe. (Chivumbulutso 7:13, 14; 19:11, 19-21) A khamu lalikulu amene avala mikanjo yoyera ali m’chipembedzo choona chimene chidzakhalepo mpaka kalekale.g
Khamu lalikulu la anthu amene amalambira Mulungu m’choonadi lidzapulumuka zipembedzo zabodza zikamadzawonongedwa
Kodi kuwonongedwa kwa zipembedzo zabodza kudzakukhudzani bwanji?
Kudziwa kuti Mulungu savomereza zinthu zoipa zimene zipembedzo zakhala zikuchita, kungakuthandizeni kukhala ndi mtendere wamumtima. Mukhoza kumayembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo, chifukwa mukudziwa kuti posachedwapa zipembedzo zonse zimene sizilemekeza Mulungu komanso zimachititsa kuti anthu azivutika zidzawonongedwa.
Dziwaninso kuti n’zotheka kumalambira Mulungu m’njira imene iye amasangalala nayo. Baibulo limanena kuti “olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, chifukwa Atate akufuna kuti anthu ngati amenewo azimulambira.” (Yohane 4:23) Mulungu akuwauza kuti: “Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4, 5) Zoonadi, Mulungu akuitana anthu kuti azimulambira m’choonadi. (1 Timoteyo 2:3, 4) Iye akulonjeza anthu amene avomera kumulambira kuti adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.—1 Yohane 2:17.
a Kuti mudziwe zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kudziwa bwino Babulo Wamkulu, werengani nkhani yakuti “Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?”
b Kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kudziwa chilombo chimenechi, werengani nkhani yakuti “Kodi Chilombo Chofiira Kwambiri Chomwe Chimatchulidwa M’chaputala 17 cha Chivumbulutso Chimaimira Chiyani?”
c Kuti mudziwe zimene zingakuthandizeni kuzindikira chilombo chimenechi, werengani nkhani yakuti “Kodi Chilombo cha Mitu 7 Chotchulidwa M’buku la Chivumbulutso Chaputala 13, Chikuimira Chiyani?”
d Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”
e Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
f Kuti muone zitsanzo, onani bokosi lakuti “Kodi Mawu Akuti Babulo Wamkulu Akunenanso za Zipembedzo Zilizonse Zimene Zimati ndi Zachikhristu?”
g Kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni kudziwa chipembedzo choona, werengani nkhani yakuti “Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?”