Imagination World/stock.adobe.com
Uthenga Wochokera M’Mawu a Mulungu—Pali Chiyembekezo kwa Anthu Othawa Kwawo
Chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri amaona kuti akuyenera kuthawa kwawo kuti akhale otetezeka. Kodi inunso mukukumana ndi vuto limeneli? Ngati ndi choncho, dziwani kuti pali winawake amene angakuthandizeni kuthana ndi vuto limeneli. Mulungu akukupatsani chiyembekezo cha moyo wabwino, ndipo mungaphunzire zambiri zokhudza moyo umenewu m’Malemba Opatulika.
A Christos Stylianides, omwe ndi kazembe wa European Uniona ananena kuti: “Anthu othawa kwawo sikuti akungofunika kuwathandiza mwamsanga basi, koma amafunikiranso . . . kuwapatsa chiyembekezo cha tsogolo labwino.”b Anthu amene ali ndi chiyembekezo amakhala ndi chifukwa chabwino choyembekezera kuti zinthu zidzasintha m’tsogolo. Koma kuwonjezera pa kukhala ndi chiyembekezo, anthu othawa kwawo akufunikanso kulimbikitsidwa kuti athe kupirira mavuto amene akumana nawo.
“Pamene ndinkafunika kuthawa kwathu n’kusiyana ndi achibale anga, zinandipweteka kwambiri. Ndinali ndi mantha aakulu, chisoni komanso nkhawa.”—Emmanuel, Haiti.
Kodi inunso zimenezi zinakuchitikiranipo? Ngati munathawa kwanu, mukufunikira winawake woti akulimbikitseni komanso kukupatsani chiyembekezo. Kodi Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu, lingakuthandizeni bwanji?
Mawu a Mulungu Angakutonthozeni
Baibulo limanena kuti: “Yehovac . . . amakonda mlendo.”—Deuteronomo 10:17, 18.
Zimenezi zikutanthauza kuti simuli nokha. Yehova Mulungu yemwe ndi Mlembi Wamkulu wa Baibulo, akumvetsa zimene zikukuchitikirani, amakukondani ndipo akufunitsitsa kuti zinthu zikuyendereni bwino.
Baibulo limanena kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana.”—Salimo 145:18.
Zimenezi zikutanthauza kuti mukamapemphera, Yehova amamvetsera. Angakuthandizeni kuti mupeze mtendere wamumtima. Amaperekanso nzeru kudzera m’Baibulo, zimene zingakuthandizeni kuti mupirire.
Baibulo limanena kuti: “Nʼzosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa . . . Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.”—Yobu 34:10, 12.
Zimenezi zikutanthauza kuti si Mulungu amene amachititsa kuti muzivutika. Sakukulangani kapena kukuyesani pokubweretserani mavuto pa moyo wanu.
Mawu a Mulungu Angakupatseni Chiyembekezo
Baibulo limafotokoza zimene Mulungu adzatichitire m’tsogolomu. Taganizirani mmene mfundo imeneyi ikuthandizira anthu amene anathawa kwawo.
Baibulo limanena kuti: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.
Zimenezi zikutanthauza kuti mavuto amene tikukumana nawowa adzatha. Mulungu akulonjeza kuti adzathetsa mavuto onse amene akuchititsa kuti tizisowa mtengo wogwira masiku ano.
“Posachedwapa Mulungu athetsa zinthu zopanda chilungamo komanso zoipa zonse zimene zikuchitika m’dzikoli. Kudziwa zimenezi kumandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri tsiku limene mavuto onsewa adzathe.”—Karla, El Salvador.
Baibulo limanena kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso, kapena kuvutitsa maganizo.”—Yesaya 65:17.
Zimenezi zikutanthauza kuti sitidzavutikanso mumtima chifukwa chokumbukira zinthu zopweteka zimene zinatichitikira. Mulungu adzaonetsetsa kuti simukuvutikanso maganizo chifukwa chokumbukira zinthu zoipa zimene zinakuchitikirani.
“Baibulo limalonjeza kuti sitidzakumbukiranso zinthu zopweteka zimene zinatichitikira kapena zinthu zimene tinataya. Lonjezo limeneli limandithandiza kupirira mavuto amene banja langa likukumana nawo chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa mavuto onsewa atheratu.”—Natalia, Ukraine.
Baibulo limanena kuti: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene . . . udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa.”—Danieli 2:44.
Zimenezi zikutanthauza kuti boma labwino kwambiri lakumwamba lidzalamulira dziko lapansili. Posachedwapa, Mulungu achotsa maboma onse a anthu padziko lapansili n’kukhazikitsa boma lake lakumwamba. Boma limeneli ndi limene lidzabweretse mtendere komanso chitetezo chenicheni, moti aliyense zinthu zizidzamuyendera bwino chifukwa lidzakhala boma la chilungamo.—Mika 4:3, 4.
“Ndimalimbikitsidwa kudziwa kuti mavuto ngati kuponderezedwa, kuzunzidwa, kukaikiridwa komanso kusankhana mitundu n’zosakhalitsa. Ufumu wa Yehova uthetsa mavuto onsewa posachedwapa.”—Mustafa, Middle East.
Uthenga wa m’Baibulo womwe ndi wopatsa chiyembekezo ungakulimbikitseni
Nzeru Zopezeka M’Mawu a Mulungu
Nzeru zothandiza zopezeka m’Baibulo zingakuthandizeni kupirira mavuto amene mwakumana nawo. Zingakuthandizeninso kupirira zinthu zosayembekezereka zimene zakuchitikirani ngati kuwonongeka kwa chuma chanu. Onani mmene mfundo zotsatirazi zikuthandizira anthu ena amene anathawa kwawo:
Zimene Baibulo limanena: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.
Mmene mawu anzeruwa angakuthandizireni kupirira: Sitikukayikira kuti zimene zakuchitikiranizi zakusokonezani kwambiri ndipo ndinu wokhumudwa chifukwa mwasiya zinthu zambiri kwanu. Koma ngati mutakhala phee n’kuganizira kuti moyo wanu ndi wamtengo wapatali, zingakuthandizeni kuti muzione moyenera zinthu zanu zonse zimene zawonongeka.
“Moyo ndi wofunika kwambiri kuposa chuma. Pa zochitika zina, chuma kapena ndalama sizingakuthandizeni.”—Natalia, Ukraine.
Baibulo limanena kuti: “Usanene kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?’”—Mlaliki 7:10.
Mmene mawu anzeruwa angakuthandizireni kupirira: N’kutheka kuti mukuvutika kwambiri panopa, koma musamayerekezere mmene zinthu zinalili kale ndi mmene zilili panopa chifukwa zingakuchititseni kuti muzingokhala wokwiya.
“Kuvomereza mmene zinthu zilili panopa, kwandithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera.”—Eli, Rwanda.
Baibulo limanena kuti: “Ngati tili ndi chakudya, zovala ndi pogona, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.
Mmene mawu anzeruwa angakuthandizireni kupirira: Yesetsani kuti muzikhutira ndi zinthu zofunika pa moyo zimene muli nazo. Mukakhala wokhutira simuzikhala wopanikizika ndipo zimenezi zidzakuthandizani kuti musamadandaule kwambiri.
“Baibulo likundithandiza kuti ndiziona zinthu moyenera m’malo momangoganizira zinthu zimene tinasiya kwathu. Ine ndi mkazi wanga tikusangalala kuti tili ndi moyo ndipo tili m’malo otetezeka.”—Ivan, Ukraine.
Baibulo limanena kuti: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—Mateyu 7:12.
Mmene mawu anzeruwa angakuthandizireni kupirira: Mukhoza kumagwirizana ndi anthu ena ngati mutayesetsa kumachita zinthu moleza mtima komanso mwachifundo. Zimenezi zingathandize kuti muzigwirizana ndi anthu ena komanso kuti asamakusaleni.
“Anthu ambiri amasangalala mukamachita nawo zinthu mwaulemu, mokoma mtima komanso mwachikondi. Zimenezi zimachititsa kuti muzigwirizana ndi anthu amene mumakhala nawo pafupi.”—Angelo, Sri Lanka.
Baibulo limanena kuti: “Muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza; mukatero, mtendere wa Mulungu . . . udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.
Mmene mawu anzeruwa angakuthandizireni kupirira: Muzimuuza Mulungu mmene mukumvera, zimene mukufunikira, zomwe zikukuchititsani mantha komanso kukudetsani nkhawa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti musamakhale ndi nkhawa komanso kuti musamapanikizike chifukwa cha mavuto amene mukukumana nawo.
“Nthawi zonse ndikakumana ndi mavuto, ndimapemphera kwa Mulungu ndipo amandiyankha. Zimene ndaphunzira m’Baibulo zandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wa mumtima.”—Yol, South Sudan.
“Malangizo a m’Baibulo andithandiza kuti ndipeze mtendere weniweni umene ndimafunikira kuti ndikwanitse kupirira mavuto amene ndikukumana nawo.”—Valentina, Ukraine.
“Ndinalimbikitsidwa kwambiri nditadziwa kuti Yehova Mulungu akulonjeza kuti adzatipatsa moyo wabwino.”—Emmanuel, Haiti
Kodi mungakonde kudziwa malonjezo a m’Baibulo olimbikitsa omwenso amatipatsa chiyembekezo komanso chifukwa chake muyenera kuwakhulupirira? Pemphani wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kwa ulele. Iwo adzasangalala kukuthandizani.
a Nthambi ya Bungwe la United Nations yoona za anthu othawa kwawo, imanena kuti anthu othawa kwawo akuphatikizapo anthu omwe akakamizika kuchoka kwawo kupita m’dera lina m’dziko lawo lomwelo komanso ena amene akukhala m’dziko lina, omwe malinga ndi malamulo sali m’gulu la anthu othawa kawo.
b Kazembe wa Bungwe la European Union amene amaonetsetsa kuti anthu amene akumana ndi mavuto akulandira thandizo loyenera, [European Union Commissioner for Humanitarian Aid and Crisis Management.]
c Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?”