Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 March tsamba 2-7
  • Muziwonjezera ‘Luso Lanu Lophunzitsa’ mu Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziwonjezera ‘Luso Lanu Lophunzitsa’ mu Utumiki
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MUZICHITA NAWO CHIDWI
  • MUZIDALIRA MAWU A MULUNGU
  • MUZIWATHANDIZA KUGANIZIRA KWAMBIRI ZA YEHOVA
  • PITIRIZANI KUWONJEZERA LUSO LANU LOPHUNZITSA
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Afike Poyamba Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • ‘Anthu a Maganizo Abwino’ Adzamvetsera
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 March tsamba 2-7

MAY 4-10, 2026

NYIMBO NA. 53 Kukonzekera Kolalikira

Muziwonjezera ‘Luso Lanu Lophunzitsa’ mu Utumiki

“Lalikira mawu . . . uzichita zimenezi ndi luso la kuphunzitsa ndiponso moleza mtima kwambiri.”—2 TIM. 4:2.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zinthu zitatu zimene tingachite kuti tiwonjezere luso lathu lophunzitsa mu utumiki.

1. Kodi ndi luso liti limene tiyenera kukulitsa, nanga n’chifukwa chiyani? (2 Timoteyo 4:2) (Onaninso chithunzi.)

YESU anauza otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . , muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.” (Mat. 28:​19, 20) Malangizowa akusonyeza kuti Akhristu onse ayenera kukhala aphunzitsi. N’zoona kuti Yehova amakokera kwa iye anthu ‘amaganizo abwino’ ndipo angelo amatitsogolera kwa anthuwa. (Mac. 13:48; Yoh. 6:44; Chiv. 14:6) Komabe, timafunika kuchita mbali yathu. Taganizirani chitsanzo cha mtumwi Paulo ndi Baranaba. Baibulo limati pamene ankalalikira m’sunagoge ku Ikoniyo iwo “analankhula bwino kwambiri moti Ayuda ambiri limodzi ndi Agiriki anakhala okhulupirira.” (Mac. 14:1) N’zosachita kufunsa kuti Paulo ndi Baranaba anali atawonjezera ‘luso lawo lophunzitsa.’ (Werengani 2 Timoteyo 4:2.) Akhristu onse amayeneranso kuchita zimenezi.

Paulo akulankhula mogwira mtima mu sunagoge ndipo anthu akumumvetsera mwatcheru. Baranaba wakhala chapafupi ndipo akuchita chidwi ndi mmene Paulo akuphunzitsira.

Tingaphunzire zambiri zokhudza “luso la kuphunzitsa” kuchokera kwa Yesu ndi ophunzira ake monga mtumwi Paulo ndi Baranaba (Onani ndime 1)


2. N’chifukwa chiyani Akhristu ena amaona kuti sangathe kukulitsa luso lawo lophunzitsa?

2 Ena angamaone kuti sangakulitse luso lawo lophunzitsa chifukwa sanapite patali ndi sukulu kapena alibe luso mwachibadwa. Ndi mmenenso anthu ena otchulidwa m’Baibulo ankamvera. (Eks. 4: 10; Yer. 1:6) Enanso amaona kuti alibe luso lophunzitsa chifukwa chakuti alibe phunziro la Baibulo komanso sapeza anthu achidwi ngati mmene zilili ndi Akhristu ena. Komabe tizikumbukira kuti si onse amene amamvetsera uthenga wabwino. Ndipotu kuti zinthu zitiyendere bwino mu utumiki sizidalira khama lathu lokha. Monga tafotokozera kale, Yehova ndi angelo amaonetsetsa kuti tapeza anthu amaganizo abwino. Komabe tiziyesetsa kulalikira m’njira yowafika pamtima. Kuti zimenezi zitheke, tikambirana zinthu zitatu zimene tingachite kuti tiwonjezere luso lathu lophunzitsa mu utumiki.

MUZICHITA NAWO CHIDWI

3. N’chiyani chinathandiza Yesu kuti aziwafika pamtima anthu?

3 Baibulo limati Yesu “ankadziwa zimene zili mumtima mwa munthu.” (Yoh. 2: 25) Mawuwa akusonyeza kuti Yesu ankadziwa maganizo komanso zolinga za anthu. Iye ankatha kuwafika pamtima chifukwa ankadziwa zimene anthuwo akufunikira. Ankaona kuti iwo anali a njala mwauzimu ndipo ankaponderezedwa ndi miyambo komanso malamulo ambirimbiri a atsogoleri a chipembedzo. (Mat. 9: 36; 23:4) Choncho pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anawaphunzitsa zimene angachite kuti azikhala ndi moyo wabwino. Ambiri ankasangalala ndi uthenga wake chifukwa choti ankawaphunzitsa zinthu zomwe zinkawachitikiradi pa moyo wawo.

4. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira anthu? (Onaninso zithunzi.)

4 Tingasonyeze kuti timaganizira anthu amene timawalalikira poyesetsa kumvetsa zomwe zikuwadetsa nkhawa. Munthu aliyense amakhala kuti akukhudzidwa m’njira inayake ndi mavuto a m’dziko la Satanali. Kukumbukira zimenezi kungatichititse kuti tizifunitsitsa kuthandiza anthu a m’gawo lathu. Mwachitsanzo, kodi pachitika nkhani inayake imene anthu a m’dera lanu akuda nayo nkhawa? Kodi makolo akudera nkhawa za chitetezo cha ana awo kusukulu? Kodi anthu ambiri akusowa ntchito? Muziganizira mmene moyo ulili ‘m’nthawi yapaderayi’ kwa anthu amene alibe chiyembekezo chimene Baibulo limapereka.—2 Tim. 3:1; Yes. 65:​13, 14.

Zithunzi: Pamene akukonzekera kulowa mu utumiki, mlongo akuganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu a m’gawo lake. 1. Mayi wakumbatira mwana wake, pamene bambo wina akuwaopseza ndi chibakera. 2. Mayi akusuta fodya. 3. Dokotala akuuza mayi wachikulire nkhani yokhumudwitsa yokhudza thanzi lake.

Muziyesetsa kumvetsa mmene zinthu zilili pa moyo wa anthu omwe mukuwaphunzitsa n’kuona mmene mungawasonyezere kuti mumawakonda (Onani ndime 4)


5. Kodi Yesu ankasiyana bwanji ndi Afarisi pa nkhani yophunzitsa? (Mateyu 11:​28-30)

5 Yesu ankakonda anthu amene ankamumvetsera ndipo iwo ankatha kuona zimenezi pa zomwe ankawachitira. Iye anali wosiyana kwambiri ndi Afarisi, omwe ankaona kuti anthu wamba ndi opanda pake komanso osafunika. (Mat. 23:13; Yoh. 7: 49) Yesu anali wokoma mtima, waulemu, ‘wofatsa komanso wodzichepetsa’ ndipo izi zinachititsa kuti akhale mphunzitsi wabwino. (Werengani Mateyu 11:​28-30.) Ifenso tizisonyeza makhalidwe amenewa tikamalalikira.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kukoma mtima ndiponso ulemu kwa amene amakana kapena kutsutsa uthenga wathu?

6 Anthu ena amakana komanso kutsutsa uthenga wathu. Ndiye kodi tizitani zikatero? Yesu anatiphunzitsa kuti tisamalimbane ndi anthu amene akutitsutsa. M’malomwake ‘tizichitira zabwino amene akudana nafe,’ ‘tizidalitsa anthu amene akutitemberera,’ komanso ‘tizipempherera anthu amene akutinyoza.’ (Luka 6: 27, 28) Zimenezi sizingamativute tikamakumbukira kuti anthuwo ali ndi zifukwa zowachititsa kuti asamvetsere. N’zoona kuti ena akhoza kukhala kuti akungodana nafe. Komabe, enanso angakhale kuti akukumana ndi mavuto a m’banja kapena akuda nkhawa ndi zinthu zina zimene sizikutikhudza. Nthawi zinanso zimakhala kuti tawapeza pa nthawi yolakwika. Kaya zinthu zili bwanji, tiyenera kutsatira malangizo akuti ‘nthawi zonse mawu athu azisonyeza kuti ndife okoma mtima ndipo azikhala okoma ngati tawathira mchere, kuti tidziwe mmene tingayankhire munthu aliyense.’ (Akol. 4:6) Ngati timamvera chisoni anthu n’kumayesetsa kudziwa mavuto awo, sitingamafulumire kukhumudwa nawo ndipo tikhoza kukhala aphunzitsi abwino.

MUZIDALIRA MAWU A MULUNGU

7. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankadalira Mawu a Mulungu akamaphunzitsa? (Yohane 7:​14-16)

7 Yesu sankadalira nzeru zake. Zimene ankaphunzitsa zinkachokera m’Mawu a Mulungu ndipo ankaphunzitsa m’njira yoti anthu azizimvetsa komanso kuzikumbukira mosavuta. Baibulo limatiuza kuti Yesu ankaphunzitsa ‘monga munthu wa ulamuliro osati ngati alembi.’ Anthu “anadabwa kwambiri” ndi zimenezi. (Maliko 1:22) Alembi akamaphunzitsa ankakonda kutchula mawu amene arabi odziwika bwino ananenapo. Mosiyana ndi zimenezi, Yesu ankakonda kuphunzitsa anthu zimene Mawu a Mulungu amanena. Monga Mwana wa Mulungu, akanatha kugwiritsa ntchito nzeru zake zochuluka kuti agometse anthu amene ankamumvetsera komanso kuwaonetsa kuti palibe chimene amadziwa. Koma sanachite zimenezi. Iye ankaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna ndiponso Mawu ake. (Werengani Yohane 7:​14-16.) Apatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa otsatira ake.

8. Kodi mtumwi Petulo anatsanzira bwanji Yesu?

8 Nawonso ophunzira a Yesu ankadalira Mawu a Mulungu akamaphunzitsa. Taganizirani zimene mtumwi Petulo analankhula pa Pentekosite mu 33 C.E. Iye sanali wophunzira kwambiri, komabe anawafika pa mtima anthu amene ankamumvetsera pofotokoza malemba osonyeza kuti Yesu anakwaniritsa maulosi. (Mac. 2:​14-37) Zotsatira zake, “amene analandira mawu akewo mosangalala anabatizidwa, moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezereka ndi anthu pafupifupi 3,000.”—Mac. 2:41.

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Mawu a Mulungu tikamaphunzitsa?

9 Baibulo lokha ndi limene lili ndi mphamvu zothandiza anthu kusintha moyo wawo n’kumasangalatsa Mulungu. (Aheb. 4:12) Choncho tiyenera kumaligwiritsa ntchito tikamaphunzitsa. ‘Tizilalikira mawu,’ osati maganizo athu. (2 Tim. 4:2) Lemba la Miyambo 2:6 limati: “Yehova ndi amene amapereka nzeru. Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka mʼkamwa mwake.” Choncho tikamagwiritsa ntchito Malemba pophunzitsa zimakhala ngati tikulola Yehova kuti alankhulepo. (Mal. 2:7) Timafuna anthu adziwe kuti m’Baibulo muli nzeru zapamwamba kwambiri kuposa nzeru za anthu. Baibulo linauziridwa ndi Mulungu ndipo limatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizimusangalatsa komanso tizisangalala.—2 Tim. 3:​16, 17.

10. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kuti aziganizira kwambiri Mawu a Mulungu?

10 Mukamakonzekera kukaphunzira ndi munthu, muziganizira mmene mungakamuthandizire kuti aziganizira kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. Ngakhale kuti timagwiritsa ntchito zithunzi komanso mavidiyo, lofunika kwambiri ndi Baibulo. Choncho muziwerenga malemba amene angamuthandize kumvetsa mfundo zofunika komanso kuona mmene angazigwiritsire ntchito. Mukamagwiritsa ntchito zithunzi komanso mavidiyo, muzionetsetsa kuti wophunzirayo akumvetsa mfundo zofunika za m’Baibulo. Kuti zimenezi zitheke, musamalankhule kwambiri kapena kuwerenga malemba ambiri. Koma mukawerenga lemba muzimupatsa nthawi yoti aliganizire n’kulimvetsa ndipo mungaliwerengenso ngati pakufunika kutero. Tikamachita zimenezi, timakhala tikuchititsadi phunziro la Baibulo osati phunziro la buku, phunziro la chithunzi kapenanso phunziro la vidiyo.—1 Akor. 2:13.

11-12. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife oleza mtima kwa ophunzira Baibulo athu? (Machitidwe 17:​1-4) (Onaninso chithunzi.) (b) Kodi anthu ena angakhale kuti sakudziwa chiyani chokhudza Baibulo, nanga tingawathandize bwanji?

11 Ngati wophunzira Baibulo wanu akuvutika kumvetsa mfundo inayake, muzikumbukira kuti muyenera ‘kulalikira mawu . . . moleza mtima kwambiri.’ Anthu amamvetsa zinthu mosiyanasiyana. Ena angafunike nthawi yambiri kuti amvetse mfundo zimene ifeyo timaziona ngati zosavuta. Kuti Ayuda a ku Tesalonika afike pomvetsa mfundo za choonadi, Paulo ankafunika kuwalalikira maulendo angapo komanso kuwafotokozera umboni wa m’Malemba.—Werengani Machitidwe 17:​1-4.

12 Mungasonyezenso kuti ndinu oleza mtima powafunsa mafunso kuti mudziwe zimene akuganiza n’kumapewa kulankhula kwambiri. Muziwamvetsera mwatcheru n’kuona chifukwa chake akuganiza mwa njira inayake. Kenako muziwerenga n’kukambirana nawo malemba amene angawathandize kumvetsa mmene Mulungu amaonera zimene akuganizazo. Taganiziraninso izi: Ena sanaonepo Baibulo komanso sadziwa zimene limaphunzitsa. Anthu oterewa zingakhale bwino kuwasonyeza Baibulo lopulinta. Kuti muwathandize kudziwa zomwe angaphunzire m’Baibulo, mungawasonyeze gawo lakuti “Kodi m’Baibulo Muli Nkhani Zotani?” lomwe lili kumayambiriro kwa Baibulo la Dziko Latsopano. Pofuna kuwasonyeza kuti mfundo za m’Baibulo zingawathandize kukhala osangalala pa moyo wawo, mungagwiritse ntchito lemba limodzi kapena awiri pafunso 15. Mwachidule, mukamasonyeza ophunzira anu kuti Mawu a Mulungu ndi amphamvu, mudzakhala mphunzitsi wabwino.

Mlongo wa m’chithunzi choyambirira uja wakhala pampando panja ndipo akuphunzira Baibulo ndi mayi yemwe amasuta uja. Mlongoyo akumvetsera mwatcheru pamene mayiyo akulankhula.

Mphunzitsi waluso amamvetsera, osati kulankhula kwambiri (Onani ndime 11 ndi 12)


MUZIWATHANDIZA KUGANIZIRA KWAMBIRI ZA YEHOVA

13. Kodi tiyenera kuthandiza wophunzira Baibulo wathu kuganizira kwambiri za ndani? Perekani chitsanzo.

13 Cholinga chathu ndi kuthandiza anthu kudziwa Yehova n’kukhala naye pa ubwenzi. (Yak. 4:8) Ntchito yathu tingaiyerekezere ndi munthu amene wayatsa tochi kuti athandize anzake kuona chinthu chimene chili mumdima. Iye sadziunika yekha koma amaunika chinthu chimene akufuna kuti anthu aonecho. Ifenso tikamaphunzitsa tizichita zofanana ndi zimenezi. Tizithandiza anthu kuganizira kwambiri za Yehova, osati ifeyo.

14. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo wathu kuti aziganizira kwambiri za Yehova?

14 Mukamachititsa phunziro la Baibulo, muzithandiza wophunzira kukhala wofunitsitsa kusangalatsa Yehova. (Miy. 27:11) Muzikumbukira kuti, sikuti mukungomuphunzitsa kudziwa zoyenera ndi zosayenera n’cholinga choti akhale wa Mboni. Koma mukufuna kuti asinthe zinthu pa moyo wake kuti azisangalatsa Yehova. Mwachitsanzo, ngati akuvutika kusiya khalidwe linalake loipa, mungamufunse kuti: “N’chifukwa chiyani Yehova amadana ndi khalidweli? N’chifukwa chiyani akufuna kuti musiye kuchita zinthu zimene zimakusangalatsani? Nanga kodi zimenezi zikusonyeza bwanji kuti amakukondani?” Mukamamulimbikitsa kuti aziganizira kwambiri za Yehova, m’pamenenso amaona kuti Yehova ndi Atate wake wachikondi. Zotsatira zake, amakhala wofunitsitsa kusangalatsa Yehova.

PITIRIZANI KUWONJEZERA LUSO LANU LOPHUNZITSA

15. Kodi mungatani kuti mupitirize kuwonjezera luso lanu lophunzitsa?

15 Mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kudziwa mbali imene mungafunike kuwonjezera luso lanu lophunzitsa. (1 Yoh. 5:14) Kenako muzichita zinthu mogwirizana ndi mapemphero anuwo pogwiritsira ntchito zimene iye amatiphunzitsa pamisonkhano ya mpingo. Mungatengenso abale ndi alongo aluso mukamakachititsa phunziro. Ndiyeno muziwapempha kuti akuuzeni mmene mwachitira. Muzikumbukiranso kuti ngakhale kuti mfundo za m’phunzirolo mukuzidziwa bwino, wophunzira wanuyo sakuzidziwa. Ndiye muziona mmene akumvera pa zomwe mukukambiranazo. Kenako muzimuthandiza kuzindikira kuti zimene akuphunzirazo ndi uthenga wabwino ndipo zingamuthandize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti azisangalala.—Sal. 1:​1-3.

16. N’chifukwa chiyani ndi bwino kupitiriza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa?

16 Kuphunzitsa ena zokhudza Yehova ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimatipangitsa kukhala wosangalala kwambiri. Ntchitoyi tidzaigwiranso kwambiri m’dziko latsopano. Choncho tiyeni tipitirize kusonyeza kuti timakonda anthu amene timawaphunzitsa, tizidalira Mawu a Mulungu komanso tizithandiza wophunzira wathu kuganizira kwambiri za Yehova. Tikamachita zimenezi tikhoza kuwonjezera luso lathu lophunzitsa mu utumiki.

KODI MUNGASONYEZE BWANJI KUTI . . .

  • mumakonda anthu amene mumawaphunzitsa?

  • mumadalira Mawu a Mulungu?

  • mumathandiza wophunzira wanu kuganizira kwambiri za Yehova?

NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena