JULY 20-26, 2026
NYIMBO NA. 133 Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata
Muzisankha Mwanzeru pa Nkhani ya Maphunziro Owonjezera
“Wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.”—MIY. 14:15.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tikambirana mfundo za m’Baibulo komanso zinthu zina zimene zingatithandize kudziwa ngati tikufunika kuchita maphunziro owonjezera kapena ayi.
1-2. (a) Kodi achinyamata amafunika kusankha zochita pa nkhani iti? (b) Kodi mawu akuti “maphunziro owonjezera” amatanthauza chiyani? (Onani “Tanthauzo la Mawu Ena.”)
“KODI umafuna kudzagwira ntchito yanji ukadzakula?” Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kuti mwafunsidwapo funso limeneli kambirimbiri. Dziwani kuti ntchito yabwino kwambiri imene mungasankhe ndi kuchita utumiki wa nthawi zonse. Komabe mudzafunikanso kumadzapeza ndalama kuti muzidzadzisamalira. (2 Ates. 3:10) N’zosachita kufunsa kuti munaganizirapo za ntchito imene mukufuna kudzagwira mukadzakula.
2 Achinyamata ena akamaliza maphunziro akusekondale, amakambirana ndi makolo awo za maphunziro owonjezera omwe angachite, kuti adzagwire ntchito inayake.a N’kutheka kuti inunso munaganizirapo zochita maphunziro owonjezera. Ngati ndi choncho, kodi ndi maphunziro ati omwe mungachite? Munkhaniyi tikambirana mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusankha mwanzeru pa nkhani ya maphunziro. Mungasankhe zinthu mwanzeru ngati mutamaganizanso mwanzeru. Ngakhale kuti nkhaniyi ikukhudza kwambiri achinyamata, mfundo zake zingathandize Mkhristu aliyense amene akufuna kuchita maphunziro owonjezera. Zingathandizenso makolo kuti azithandiza ana awo kusankha zinthu mwanzeru pa nkhaniyi.
KODI MUYENERA KUCHITA MAPHUNZIRO OWONJEZERA?
3. N’chifukwa chiyani Akhristu ena amasankha kuchita maphunziro owonjezera?
3 M’madera ena, munthu sachita kufunika kuchita maphunziro owonjezera kuti apeze ntchito yomuthandiza kupeza zofunika pa moyo. Koma m’madera ena kuchita maphunziro owonjezera kungathandize munthu kupeza ntchito yamalipiro abwino komanso yosapanikiza. Kwa Mkhristu, ntchito ngati imeneyi ingamuthandize kukhala ndi nthawi yambiri yolalikira kapena kuchita nawo mautumiki ena. Komabe kuchita maphunziro owonjezera kumafuna kudzimana zinthu zina komanso kukhoza kuchititsa kuti Mkhristu akumane ndi mavuto ena.
4. Kodi ndi ndani akuyenera kusankha ngati Mkhristu akufunika kuchita maphunziro owonjezera? (Onaninso mawu a m’munsi.)
4 Baibulo limati munthu aliyense ayenera “kunyamula katundu wake.” (Agal. 6:5) Choncho Mkhristu aliyense wamkulu ayenera kusankha yekha ngati akufunika kuchita maphunziro owonjezera kapena ayi.b Makolo alinso ndi udindo wosankha zochita pa nkhani ya maphunziro a ana awo. (Aef. 6:1) Ndipo malangizo amene angapereke angathandize mwana wawo kuti akadzakula adzasankhe mwanzeru pa nkhani ya maphunziro.—Miy. 22:6.
5. Kodi ndi pa nthawi iti pamene munthu ayenera kuyamba kuganizira zokhudza maphunziro owonjezera, nanga n’chifukwa chiyani? (Onaninso chapachikuto.)
5 Nthawi zambiri achinyamata asanamalize sukulu amafunika kusankha ngati angadzachite maphunziro owonjezera kapena ayi. Komabe zingakhale bwino ngati wachinyamata atakambirana kaye ndi makolo ake asanasankhe zochita pa nkhaniyi. Zimenezi zingawapatse nthawi yokwanira yoti afufuzire limodzi ndi mwana wawo maphunziro oyenera omwe angadzachite. Makolowo angamuthandize kusankha masabujekiti omwe angamatenge kusukulu omwe angamuthandize kudzachita maphunziro amene akufunawo kapena kupeza ntchito. Ndiye kodi makolo ayenera kusankha zochita mwanayo asanamalize maphunziro akusekondale? Osati kwenikweni. (Miy. 21:5) Achinyamata ena amasankha kuti akamaliza sukulu, apeze ntchito n’kumachita upainiya asanasankhe zochita pa nkhani ya maphunziro owonjezera. Munthu akhozanso kusankha kuti achite maphunziro owonjezera atakula kale.
Makolo Achikhristu akuthandiza mwana wawo kuti asankhe zinthu mwanzeru pa nkhani ya maphunziro owonjezera (Onani ndime 5)
6. N’chiyani chingathandize munthu kuti asankhe mwanzeru pa nkhani ya maphunziro owonjezera?
6 N’chiyani chingakuthandizeni kuti musankhe mwanzeru pa nkhani ya maphunziro owonjezera? Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru. (Yak. 1:5) Kenako muzichita zinthu zotsatirazi: Choyamba, muziganizira chifukwa chake mukufuna kuchita maphunzirowo. (Sal. 26:2) Chachiwiri, muziganizira ubwino wa maphunziro amene mukufuna kuchitawo komanso mavuto amene angakhalepo. (Miy. 14:15) Tsopano tiyeni tikambirane mfundo ziwirizi.
MUZIGANIZIRA CHIFUKWA CHAKE MUKUFUNA KUCHITA MAPHUNZIRO OWONJEZERA
7. Kodi Akhristu ayenera kuganizira zinthu ziti ngati akufuna kuchita maphunziro owonjezera?
7 Ngati mukufuna kuchita maphunziro owonjezera, funso lofunika kwambiri kudzifunsa ndi lakuti, ‘N’chifukwa chiyani ndikufuna kuchita maphunzirowa?’ Anthu ambiri amachita maphunziro n’cholinga choti adzapeze ntchito yoti azidzasangalala nayo kapena ya malipiro ambiri. Kodi kukhala ndi maganizo amenewa n’kulakwa? Osati kwenikweni. (1 Tim. 5:8) Komabe Baibulo limatichenjeza kuopsa kokonda chuma komanso kumaona kuti ndalama n’zofunika kwambiri m’dziko la Satanali. (Miy. 23:4, 5; 1 Tim. 6:8-10; 1 Yoh. 2:17) Ngati cholinga chanu pochita maphunziro owonjezera n’chakuti mudzakhale ndi chuma kapena kutchuka, simudzakhala wosangalala komanso mukhoza kudzasokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova.
8-9. (a) Kodi Akhristu ayenera kuona bwanji maphunziro? (Mateyu 6:33) (b) Kodi mwaphunzira chiyani pa zimene Josefina, Morine komanso Iris ananena?
8 Ndiye kodi maphunziro tiziwaona bwanji? Chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu chiyenera kukhala kutumikira Yehova. (Mat. 22:37, 38; Afil. 3:8) Choncho cholinga chochitira maphunziro chiyenera kukhala kudzatithandiza kupeza zinthu zofunika pamene tikutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse.—Werengani Mateyu 6:33.
9 Taonani zimene zinathandiza Akhristu ena kuti aziona maphunziro owonjezera moyenera. Josefina wa ku Chile ananena kuti: “Ndinachita maphunziro owonjezera n’cholinga choti ndipeze ntchito imene ingamandipatse mpata wokwanira woti ndizitumikira Yehova. Ndinaonetsetsa kuti maphunzirowo asakhale chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga. Ubwenzi wanga ndi Yehova ndi umene unali wofunika kwambiri.” Mlongo wina dzina lake Morine anasankha kuchita maphunziro a chaka chimodzi okhudza kukonza tsitsi. N’chifukwa chiyani anasankha kuchita zimenezi? Iye anati: “Ndinali ndi cholinga chopita kudera kumene kunkafunika olalikira Ufumu ambiri. Ndiye ndinafufuza kosi imene ikanandithandiza kukwaniritsa cholinga chimenechi. Nditamaliza kosiyi ndinayamba ntchito yokonza anthu tsitsi ndipo ndinkasunga ndalama zomwe zikanandithandiza kukwaniritsa cholingachi. Ndiye nditasamukira kuderalo sindinavutike kupeza ntchito chifukwa cha maphunziro amene ndinachita.” Iris yemwe anachita maphunziro a nthawi yayitali kuti akhale dokotala wamano anati: “Kuchita maphunziro owonjezera kuli ndi ubwino wake, koma sikungatithandize kupeza chimwemwe chenicheni. Nkhani yake ndi yosavuta: Nthawi zonse ukamaika Yehova pamalo oyamba pa moyo wako, umakhala wosangalala ndipo zinthu zimakuyendera bwino.” Zoonadi, tikamaona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri, timasankha zinthu zimene zingatithandize kukhala osangalala mpaka kalekale.
MUZIGANIZIRA UBWINO KOMANSO MAVUTO OMWE ANGAKHALEPO
10. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Deuteronomo 32:29, mukamasankha zochita pa nkhani ya maphunziro owonjezera?
10 N’kutheka kuti mumaganizira zochita maphunziro okhudza ntchito inayake. Koma ndi bwinonso kuganizira maphunziro okhudza ntchito zina, mwina ofanana ndi ntchito imene mukuganizirayo kapena ayi. (Yerekezerani ndi Miyambo 18:17.) Masiku ano kuli mwayi wa maphunziro umene kale kunalibe monga maphunziro a pa intaneti. Muziganiziranso ngati mungakwanitse kumadzisamalira popanda kuchita maphunziro owonjezera. Mwachitsanzo, Johanna wa ku Finland sanachite maphunziro owonjezera. Iye anati: “Nditamaliza sukulu, ndinayamba kugwira ntchito masiku ochepa komanso kuchita upainiya. Ndagwirapo ntchito zingapo ndipo ndaona mmene Yehova amakwaniritsira lonjezo lake loti adzatipatsa zomwe tikufunikira.” Muzikumbukira kuti zilizonse zomwe mungasankhe pa nkhani ya maphunziro owonjezera zili ndi ubwino komanso mavuto ake. Choncho muzidzifunsa kuti: ‘Kodi maubwino ake ndi ambiri kuposa mavuto omwe angakhalepo?’ (Werengani Deuteronomo 32:29; 1 Akor. 10:23) Tiyeni tikambirane mfundo zina zimene zingatithandize kuyankha funsoli.
11. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuganizira kuchuluka kwa nthawi yomwe izidzafunika wiki iliyonse? (Onaninso zithunzi.)
11 Nthawi imene izidzafunika wiki iliyonse. Ganizirani kuchuluka kwa maola omwe azidzafunika wiki iliyonse kuti mukhale m’kalasi, muphunzitsidwe zinthu zina komanso mulembe homuweki. Kodi muzidzapeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira komanso kusamalira maudindo anu m’banja? (Afil. 1:10) Kodi maphunzirowo azidzachititsa kuti muzitopa kwambiri moti simuzidzakwanitsa kupeza nthawi yokonzekera misonkhano kapena kuwerenga Baibulo panokha? Zimenezi ndi zimene zinachitikira Jeroz wa ku India. Iye anati: “Ndinkavutika kwambiri kuchita zinthu zokhudza kulambira. Nthawi zina sindinkapita kumisonkhano. Panopa ndinazindikira kuti ndinawononga nthawi ndi mphamvu zanga pochita maphunzirowa.” Koma pali makosi ena omwe safuna nthawi yambiri. Ena amafuna kulowa m’kalasi mwa apo ndi apo ndipo sakhala ndi mahomuweki ambiri. Mwachitsanzo, Rabeca wa ku Mozambique amasangalala ndi maphunziro amene anasankha kuchita. Iye anati: “Ndinkafunika kumaphunzira maola awiri okha basi patsiku. Choncho zinali zotheka kuti ndipitirize kuchita upainiya wokhazikika.”
Ngati mukuganiza zochita maphunziro owonjezera, muyenera kuonetsetsa kuti muzidzapeza nthawi yochitira zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri (Onani ndime 11)
12. Kodi munthu angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi pamene akuchita maphunziro enaake? (Mlaliki 12:1)
12 Kuchuluka kwa nthawi. Muziganizira kuti maphunzirowo adzatenga miyezi kapena zaka zingati kuti mumalize. Kodi mudzakhala mukugwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru ngati mutachita maphunzirowo? (Aef. 5:15-17) Ngati ndinu wachinyamata, kodi maphunzirowo azidzakupatsani mpata woti muzichita zonse zomwe mungathe potumikira Yehova, mwinanso kuchita utumiki wanthawi zonse? (Werengani Mlaliki 12:1.) Kodi pali makosi ena a nthawi yochepa, amene angakuthandizeni kuphunzira ntchito imene mukufunayo? Mwachitsanzo, masukulu ena ophunzitsa maluso angakuthandizeni kuti muphunzire ntchito kwa nthawi yochepa kuposa mayunivesite. Mario wa ku Chile anati: “Ndinasankha kuchita kosi ya zaka ziwiri imene inali yotchipa kuposa maphunziro akuyunivesite. Ndinkalowa m’kalasi masiku 4 pa wiki, ndipo ndinkatha kuchita upainiya uku ndikuchita kosiyo.”
13. Kodi chingachitike n’chiyani ngati mukufunika kukachita maphunziro kutali ndi kumene mumakhala?
13 Malo amene muzikachitira maphunziro. Mukhoza kuchita maphunziro anu kufupi ndi kwanu. Koma bwanji ngati mukufunika kukachita maphunziro kutali? Komanso bwanji ngati mukufunika kuti muzigonera kusukulu komweko? Dziwani kuti kuchoka kunyumba kwanu n’kumakakhala ndi anthu ena, makamaka amene satumikira Yehova, kungasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. (Miy. 22:3; 1 Akor. 15:33) Matias wa ku Mozambique anachita maphunziro otchipa kwa chaka chimodzi. Komabe amanong’oneza bondo. Iye anati: “Pa nthawi yonseyi ndinkafunika kumagonera kusukulu komweko. Tsiku lililonse ndinkayesedwa kuti ndichite zolakwika. Ndikuona kuti ndi bwino kuti munthu azichita maphunziro amene sangachititse kuti achoke kwawo.” Mlongo wina wa ku Russia anati: “Ndinapewa mavuto komanso mayesero chifukwa ndinasankha kumakhala kunyumba ndi makolo anga m’malo momagonera kusukulu konko.” Ndipotu mukhozanso kumaphunzira pa intaneti mukukhala kwanu.
14. Kodi mfundo ya pa Luka 14:28, ingakuthandizeni bwanji ngati mukuganiza zochita maphunziro owonjezera?
14 Ndalama zimene zingafunike. Makosi ena safuna ndalama zambiri kapenanso boma ndi limene limalipira. Ngati ndi choncho, simungavutike kuchita maphunziro owonjezera omwe angakuthandizeni kukhala ndi maluso n’kudzapeza ntchito. Koma m’madera ambiri maphunziro owonjezera ndi odula. Pangakhale zinthu zina zofuna ndalama monga kupeza mphunzitsi wapatitayimu kuti azikuphunzitsani n’cholinga choti muyenerere kukachita maphunzirowo. Makosi ena amachititsa kuti ophunzira akhale ndi ngongole yomwe angafunike kubweza kwa zaka zambiri. Adilson wa ku Mozambique amanong’oneza bondo chifukwa cha maphunziro amene anachita. Iye anati: “Agogo anga ankalephera kugula chakudya komanso zinthu zina zofunika n’cholinga choti azikwanitsa kundilipirira maphunziro a zaka 4 omwe ndinkachita.” Ndiye mukamaganizira maphunziro amene mukufuna kuchita, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi padzafunika ndalama zingati? Kodi ineyo kapena achibale anga adzakwanitsa kulipira? Kodi palibe kosi ina yotchipirako?’ (Werengani Luka 14:28.) ‘Ngati nditatenga ngongole, kodi zinganditengere nthawi yayitali bwanji kuti ndibweze? Kodi ntchito imene ndidzagwire idzandithandiza kumapeza zinthu zofunika kwinaku ndikubweza ngongoleyo?’—Miy. 22:7.
15. N’chifukwa chiyani muyenera kuganizira ntchito zimene zimapezeka mosavuta musanasankhe maphunziro oti muchite?
15 Kodi mudzapeza mwayi wa ntchito? Muziganizira ntchito zimene zimapezeka mosavuta m’dera lanu kapena kumene mukufuna kudzakhala. Kodi maphunzirowo adzakuthandizani kupeza ntchito? Makosi ena samathandiza munthu kuphunzira luso lomwe lingamuthandize kupeza ntchito. M’malomwake amangophunzitsa maganizo ndi nzeru za anthu. (Akol. 2:8) Mlongo wina wa ku India anati: “Kosi imene ndinatenga sinandithandize kuphunzira maluso omwe olemba anthu ntchito amafuna. Zotsatira zake sindinapeze ntchito yogwirizana ndi zimene ndinaphunzira.” Makosi ena amakhala okhudza ntchito zomwe ndi zosowa. Sublime wa ku Central African Republic anachita kosi yokonza zipangizo zoziziritsira m’nyumba. Komabe iye anati: “Kumene ndimakhala anthu ambiri amakonza okha zinthu zikawonongeka, choncho zinali zovuta kuti ndipeze ntchito.”
16. N’chifukwa chiyani ndi bwino kuganizira mtundu wa ntchito imene mudzagwire mukadzamaliza maphunziro anu?
16 Muziganiziranso mtundu wa ntchito yomwe mudzagwire. Kodi muzidzasangalala nayo? (Mlal. 3:12, 13) Nanga muzidzagwirira pamalo otani komanso ndi ndani? Kodi izidzaika moyo wanu pangozi, kukupangitsani kuti muzidzachita zinthu mwampikisano komanso kukupanikizani? Muzidzalandira ndalama zingati? Kodi izidzakuthandizani kupeza zinthu zofunika? Kodi mudzafunika kumapitabe kusukulu kuti ntchito isakuthereni? Ndipo funso lofunika kwambiri ndi lakuti, kodi izidzakupatsani mpata woti muziika zinthu za Ufumu pamalo oyamba? (Mlal. 12:13) N’zoona kuti ngati ntchito n’zosowa, zikhoza kukhala zovuta kuti tisankhe ntchito imene timafuna. Koma maphunziro omwe mungasankhe kuchita ndi amene angakuthandizeni kuti mudzapeze ntchito mosavuta kapena ayi. Tabitha wa ku India anasankha kuchita kosi ya utelala ya miyezi 6. Iye anati: “Ndinaona kuti utelala udzandithandiza kuti ndizidzachita upainiya. Nthawi zonse anthu amafuna matelala. Ndizidzasankha ndekha nthawi yogwirira ntchito komanso sindidzafunika ndalama zambiri kuti ndiyambe kugwira ntchitoyi.” Kosiyi inamuthandiza kupeza ntchito yomwe inkamuthandiza pamene ankachita upainiya.
17. (a) Kodi Mkhristu angatani kuti adziwe zinthu zomwe zingamuthandize kusankha mwanzeru pa nkhani ya maphunziro? (b) Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe zingakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru? (Onani bokosi lakuti “Mfundo za M’Baibulo Zofunika Kuziganizira.”)
17 Pofika pano takambirana mfundo zosiyanasiyana zofunika kuziganizira pa nkhani ya maphunziro owonjezera. Ndiye kodi mungatani kuti mudziwe zinthu zomwe zingakuthandizeni kusankha mwanzeru? Muzikafufuza zokhudza makosi omwe mungaphunzire kusukulu kumene amaphunzitsa makosiwo kapena pawebusaiti yawo. Muzifufuza kuchuluka kwa ntchito zimene zimapezeka pa kosi yomwe mukufunayo. Mukhozanso kufunsa anthu omwe anachita kosiyo kapena amene akugwira ntchito zogwirizana ndi kosiyo. (Miy. 13:10) Muziwafunsa kuti: “Kodi maphunzirowa kapena ntchitoyi ili ndi ubwino komanso mavuto otani?” Muzichezanso ndi anthu omwe akutumikira Yehova mosangalala. (Miy. 15:22) Kodi ndi maphunziro komanso ntchito ziti zomwe amaona kuti n’zabwino? Akhoza kukuuzani zokhudza ntchito zina zimene mwina simunaziganizire.
18. Kodi tiyenera kumakumbukira chiyani?
18 Monga mmene taonera, maphunziro owonjezera ali ndi ubwino komanso mavuto ake. Choncho muzipemphera n’kuganizira zomwe mukufuna kusankha. N’zoona kuti maphunziro owonjezera angadzakuthandizeni kupeza ndalama zokwanira kuti muzidzadzisamalira, koma muzikumbukira kuti munthu amapeza chimwemwe chenicheni ngati ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (Sal. 16:9, 11) Nthawi zonse Yehova amasamalira anthu ake posatengera kuti anachita maphunziro otani. (Aheb. 13:5) Koma bwanji ngati mwasankha zoti muchite maphunziro owonjezera? N’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova pa nthawi yomwe mukuchita maphunzirowo? Tikambirana zimenezi munkhani yotsatira.
NYIMBO NA. 45 Zimene Ndimaganizira Mozama
a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Munkhaniyi komanso yotsatira, mawu akuti “maphunziro owonjezera” akunena za maphunziro alionse amene munthu amachita pambuyo pomaliza maphunziro akusekondale monga maphunziro akuyunivesite, kukoleji ndiponso masukulu ophunzitsa ntchito kapena luso linalake.
b M’mbuyomu mabuku athu sankalimbikitsa Akhristu kuchita maphunziro ena owonjezera. Mwachitsanzo nkhani yakuti, “Makolo—Kodi Ana Anu Mukuwafunira Tsogolo Lotani?” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2005, inafotokoza mavuto amene amabwera chifukwa chochita maphunziro apamwamba. Ngakhale kuti mavuto omwe anatchulidwawo adakalipobe, aliyense ayenera kusankha yekha ngati akufuna kuchita maphunziro owonjezera kapena ayi. Mkhristu aliyense ndiponso ngati ndi ana, mutu wabanja aliyense ayenera kupemphera, kuganizira mfundo za m’Baibulo komanso zinthu zina zokhudza maphunziro owonjezera enaake asanasankhe zochita. Mkhristu aliyense kuphatikizapo akulu, sakuyenera kuweruza Mkhristu mnzake pa zimene wasankha pa nkhaniyi.—Yak. 4:12.