Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 April tsamba 26-31
  • Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kuti Muzigwirizana Kwambiri M’banja Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kuti Muzigwirizana Kwambiri M’banja Lanu
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI MUNGASANKHE BWANJI MUNTHU YEMWE ANGADZAKHALE MNZANU WAPAMTIMA KWA MOYO WANU WONSE?
  • MUZIPEZA NTHAWI YOCHITIRA ZINTHU LIMODZI
  • MUZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA MUKAKUMANA NDI MAVUTO
  • Kodi Mungatani Kuti Mupeze Munthu Wokwatirana Naye?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Pambuyo pa Tsiku la Ukwati
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 April tsamba 26-31

JUNE 29–JULY 5, 2026

NYIMBO NA. 131 “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”

Muzichita Zinthu Zomwe Zingakuthandizeni Kuti Muzigwirizana Kwambiri M’banja Lanu

“Pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”—MIY. 18:24.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona kuti ngati mwamuna ndi mkazi akufuna kuti azisangalala m’banja lawo, onse ayenera kumakonda Yehova komanso kumagwirizana kwambiri.

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anzathu abwino ndi mphatso yochokera kwa Yehova?

ANZATHU abwino ndi mphatso yochokera kwa Yehova. (Yak. 1:17) Anzathuwo amakonda Mulungu komanso amatikonda. Tikamasangalala, nawonso amasangalala nafe, amatilimbikitsa tikakhala ndi nkhawa komanso amatipatsa malangizo osapita m’mbali pakafunika kutero. Nthawi zonse amatithandiza ndipo timawadalira. Anzathu oterewa ‘amasangalatsa mtima’ wathu.—Miy. 27:9.

2. N’chifukwa chiyani anthu okwatirana amafunika kulimbitsa ubwenzi wawo? (Mateyu 19:6)

2 Mwamuna ndi mkazi wake amafunika kukhala mabwenzi apamtima. Ubwenzi wawo sayenera kuuona mopepuka. Amafunika kupitiriza kuchita khama kuti ukhale wolimba. Ngati sangamachite zimenezi akhoza kuyamba kumadziona kuti ali okhaokha, sangamasangalale komanso akhoza kumakhala okwiya. Koma ngati atapitiriza kulimbitsa ubwenzi wawo akhoza kumagwirizana kwambiri. (Werengani Mateyu 19:6.) Munkhaniyi tikambirana zimene anthu okwatirana angachite kuti azigwirizana kwambiri. Koma choyamba tiyeni tikambirane zimene zingathandize Akhristu omwe sali pabanja kusankha munthu wokwatirana naye amene angadzakhale mnzawo wapamtima kwa moyo wawo wonse.

KODI MUNGASANKHE BWANJI MUNTHU YEMWE ANGADZAKHALE MNZANU WAPAMTIMA KWA MOYO WANU WONSE?

3-4. Kodi n’chiyani chingathandize munthu kupeza mnzake woyenera kukwatirana naye? (Miyambo 18:22)

3 Tisanasankhe zochita pa nkhani iliyonse yaikulu, timafunika kuganizira mavuto amene angakhalepo, ubwino wake komanso zotsatirapo zake. Zimene timasankha zingakhudze moyo wathu wonse, choncho tisanasankhe zochita pa nkhani zikuluzikulu timafunika kuganizira kaye mofatsa.

4 Chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene timafunika kusankha, ndi munthu wokwatirana naye. Popeza Yehova ndi amene anayambitsa banja, n’zomveka kuti timafunika kutsatira malangizo ake tikamasankha munthu wokwatirana naye. Iye amafuna kuti mwamuna apeze mkazi wabwino komanso kuti mkazi apeze mwamuna wabwino. Nthawi zonse Yehova amadziwa zinthu zomwe ndi zabwino kwambiri kwa ife. (Werengani Miyambo 18:22; Yes. 48:​17, 18) Mfundo za m’Baibulo zingathandize Mkhristu kusankha munthu womuyenerera.

5. N’chifukwa chiyani mukafuna kukwatira muyenera kusankha munthu yemwe ndi wobatizidwa?

5 Tikabatizidwa timakhala anzake a Mulungu. (Sal. 25:14) Ndiye mukafuna kukwatira muyenera kusankha munthu yemwe ndi mnzake wa Yehova. (1 Akor. 7:39) Mukachita zimenezi mumasonyeza kuti mukulemekeza mfundo za Yehova komanso mumayamba kuona mnzanuyo monga mphatso imene Yehova anakupatsani. (Miy. 19:14) Mungapewenso mavuto amene amabwera chifukwa ‘chomangidwa mʼgoli ndi wosakhulupirira.’ (2 Akor. 6:14) Kungakhaletu kupanda nzeru kuchita chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira poganiza kuti m’gululi mulibe munthu amene mungamukonde. Komanso kungakhale kusaganiza bwino kuchita chibwenzi ndi munthu yemwe si wa Mboni n’kumaganiza kuti adzaphunzira choonadi m’tsogolo.

6-7. Kodi muyenera kupeza mayankho a mafunso ati mukakhala pachibwenzi?

6 Komabe, sikuti Mkhristu aliyense wobatizidwa angakhale wokuyenererani. Muziona zinthu zofunika kwambiri mwa munthu amene mukumufunayo.a Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi amachita bwanji zinthu ndi anthu a m’banja lake? Kodi amachita zinthu mwaulemu komanso moganizira ena? Kodi anzake ndi otani? Anthu ena akakhala ndi maganizo osiyana ndi ake, kodi amakakamira maganizo ake kapena amalolera ngati mfundo za m’Baibulo sizikuphwanyidwa? Kodi ndalama amaziona bwanji?’

7 Mungadzifunsenso kuti: ‘Kodi amasonyeza kuti amakonda Yehova? Kodi akuvala “umunthu watsopano.” Kodi azidzandithandiza kuchita zambiri potumikira Yehova? Kodi zolinga zathu zauzimu ndi zofanana? Kodi angadzakhale mnzanga wapamtima?’ (Akol. 3:​9, 10) Ngati ndinu mlongo, kodi m’bale amene muli naye pa chibwenziyo angadzakhale mnzanu komanso mutu wabanja wabwino? (1 Akor. 11:3) Ngati ndinu m’bale, kodi mlongo muli naye pa chibwenziyo azidzakugonjerani monga mutu wabanja ngakhale kuti mumalakwitsa zinthu zina? Pamafunika nthawi kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa. Choncho pamene muli pachibwenzi muziyesetsa kumudziwa bwino munthu amene mukufuna kudzakwatirana nayeyo.

8-9. N’chiyani chingathandize munthu yemwe ali pachibwenzi kusankha zinthu mwanzeru? (Onaninso chithunzi.)

8 Pamene muli pachibwenzi mukhoza kusankha zinthu mwanzeru ngati mutayesetsa kumudziwa bwino mnzanuyo. Kodi anthu amamuona bwanji? Mukhoza kufunsa ena zokhudza mbiri yake komanso makhalidwe ake. Mwachitsanzo, kodi amadziwika kuti ndi wodzichepetsa, wokoma mtima komanso wololera? Mlongo wina wa ku French Guiana dzina lake Sarah yemwe anakwatirana ndi M’bale Daniel ananena kuti: “Ndinafunsa zokhudza Daniel kwa m’bale yemwe ankakhala naye komanso kuchita naye upainiya, kwa mkulu wina wa mumpingo wawo, anzathu amene ankatidziwa bwino komanso alongo a mumpingo mwake.” Mungafunsenso chibwenzi chanucho ngati pali zinazake zokhudza iyeyo zomwe zinachitika m’mbuyo kapena zikuchitika panopa zimene mungafunike kudziwa. Tikutero chifukwa zinthu zina kapena makhalidwe ena akhoza kudzayambitsa mavuto aakulu m’banja.

9 Ngati pali zina zokayikitsa kapena ena akuuzani zinazake musamazinyalanyaze. Zimenezi zingakuthandizeni kudziwa ngati mukufunika kupitiriza chibwenzicho kapena kuchithetsa.b Tsopano tiyeni tikambirane zokhudza anthu amene anakwatirana kale.

Anthu omwe ali pa chibwenzi ali kupate ndipo akucheza.

Mukakhala pachibwenzi muziyesetsa kumudziwa bwino mnzanuyo (Onani ndime 8 ndi 9)


MUZIPEZA NTHAWI YOCHITIRA ZINTHU LIMODZI

10. N’chifukwa chiyani n’zofunika kuti mwamuna ndi mkazi wake azipeza nthawi yochitira zinthu limodzi komanso kusonyezana chidwi?

10 Mwamuna ndi mkazi wake angamagwirizane kwambiri komanso banja lawo lingakhale lolimba ngati amapeza nthawi yochitira zinthu limodzi ngakhale kuti amatanganidwa kwambiri. Zimenezi zimawapatsa mwayi wouzana zimene zawachitikira pa tsikulo, kuuzana zakukhosi, kusonyezana chikondi komanso kuchitira limodzi zosangalatsa.

11. N’chiyani chingachititse kuti mwamuna ndi mkazi wake asamagwirizane?

11 Mwamuna ndi mkazi wake omwe amagwirizana kwambiri amachitira zinthu limodzi osati aliyense payekha. N’zoona kuti nthawi zina angafunike kuti asachitire zinthu zina limodzi. Koma kusiyana kwa nthawi yaitali kungakhale koopsa. Mwachitsanzo, anthu ena amakagwira ntchito ku dziko lina zomwe zimapangitsa kuti atalikirane ndi banja lawo kwa nthawi yaitali. Ngakhale kuti zimenezi zingachititse kuti apeze ndalama zambiri, zikhoza kuwononga banja lawo.

12-13. (a) Kodi Akhristu ena okwatirana amatani kuti azipeza nthawi yochitira zinthu limodzi? (Onaninso chithunzi.) (b) Kodi mwamuna kapena mkazi wathu tiyenera kumuika panambala chiyani? (Onani bokosi lakuti “Kodi Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ndi Wofunika Bwanji kwa Inu?”)

12 Taonani zimene mabanja ena anachita kuti azipeza nthawi yochitira zinthu limodzi? Leah wa ku Guam anati: “Ine ndi mwamuna wanga timachitira limodzi zinthu zosangalatsa. Nthawi zambiri timapitira limodzi kokasangalala kapena kokacheza.” Roxanne wa ku United States ananenanso kuti: “Masiku ano timakhala otanganidwa kwambiri choncho tinaona kuti tikufunika kumakonzeratu nthawi yochitira zinthu limodzi ngati mmene timachitira ndi zinthu zina zomwe ndi zofunika kwambiri.” (Yerekezani ndi Amosi 3:3.) Damien wa ku France anati: “Taphunzira kuchita chidwi komanso kukonda zomwe wina amakonda.” (Mat. 7:12) Ndipo Katie yemwenso ndi wa ku United States anati: “Nthawi zina timaika mafoni athu patali kuti asatisokoneze.”

13 Kuposa zonse, muzichitira limodzi zinthu zokhudza kulambira. Myriam wa ku France anati: “Timayamba tsiku lililonse ndi kuwerenga Baibulo ndipo timakambirana zimene zatisangalatsa komanso mfundo zimene tingazigwiritse ntchito pa moyo wathu. Imakhala nthawi yosangalatsa kwambiri kwa ine. Ndimasangalalanso tikamapemphera limodzi n’kumamva mwamuna wanga akutchula zinthu zosonyeza kuti amakonda kwambiri Yehova.” Katie yemwe tamutchula kale uja ananenanso kuti: “Timasangalala kwambiri tikalowera limodzi mu utumiki. Zimakhala zolimbikitsa kumva aliyense akufotokoza zimene amakhulupirira ndipo timaphunzira zinthu zatsopano kwa wina ndi mnzake.”—Miy. 27:17.

Anthu omwe tinawaona pachithunzi choyamba tsopano ali pa banja, akunga tenti ndipo akucheza.

Kuti mulimbitse banja lanu, nthawi zonse muzipeza nthawi yochitira zinthu limodzi monga munthu ndi mnzake (Onani ndime 12 ndi 13)


Kodi Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ndi Wofunika Bwanji kwa Inu?

Tili ndi anzathu ofunika kwambiri kwa ife. Ndiye kodi mwamuna kapena mkazi wathu ali panambala chiyani?—Afil. 1:10.

  1. 1. Yehova. Yehova ndi amene amafunika kukhala pamalo oyamba pamoyo wathu. (Mat. 6:33; Maliko 12:30) Sitingafune kukhala osakhulupirika kwa Yehova pongofuna kusangalatsa mwamuna kapena mkazi wathu.—Mac. 5:29; yerekezerani ndi Genesis 2:​16, 17; 3:6.

  2. 2. Mwamuna kapena mkazi wathu. Tikakwatira timakhala kuti ndife “thupi limodzi.” Choncho timakonda mwamuna kapena mkazi wathu ngati mmene timadzikondera tokha.—Gen. 2:24; Aef. 5:​28, 29, 33.

  3. 3. Anthu ena komanso maudindo. Timakhala ndi udindo wosamalira makolo, achibale, Akhristu anzathu komanso maudindo ena m’gulu la Yehova. Koma kupatulapo Yehova, palibe aliyense kapena chilichonse chimene chiyenera kutilepheretsa kusamalira ndiponso kuchita zimene zingasangalatse mwamuna kapena mkazi wathu.—1 Tim. 5:8.

MUZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA MUKAKUMANA NDI MAVUTO

14-15. N’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kuyesetsa kulimbana ndi mavuto amene angachitike m’banja mwawo? Perekani chitsanzo.

14 Anthu okwatirana amakumana ndi mavuto m’banja mwawo chifuwa chakuti si angwiro. Baibulo linanena mosapita m’mbali kuti “adzakumana ndi mavuto pa moyo wawo.” (1 Akor. 7:28) Mawuwa akunena za mavuto amene anthu ambiri okwatira amakumana nawo. Ndiye akakumana ndi mavuto, n’chifukwa chiyani ayenera kuyesetsa kulimbana nawo komanso kukhala ogwirizana kwambiri?

15 Taganizirani chitsanzo ichi: Ngati nyumba kapena chinthu chinachake chamtengo wapatali chawonongeka, eniake angayesetse kuti akonze. Iwo angagwiritse ntchito ndalama komanso zinthu zambiri pokonza zinthuzo, zomwe mwina zingatenge nthawi yaitali. Angachite zimenezi chifukwa nyumbayo komanso chinthucho n’chamtengo wapatali kwa iwowo. Mofanana ndi zimenezi, mabanja onse ndi amtengo wapatali. Ngakhale mabanja amene amakondana kwambiri amakhala ndi mavuto komanso amatha kusemphana maganizo. Ngati nyumba kapena chinthu chamtengo wapatali chingathe kukonzedwa, mabanja amene ali ndi mavuto akhoza kuyambiranso kuyenda bwino. N’zoona kuti pangafunike nthawi komanso khama komabe Yehova amasangalala ngati anthu okwatirana akuyesetsa kulimbitsa banja lawo n’kumapitiriza kukhalabe limodzi. (Mal. 2:16) Akamachita zimenezi amasonyeza kuti amakondana, kulemekezana komanso kuti amakonda ndi kulemekeza Yehova amene anayambitsa banja.

16. Mogwirizana ndi 1 Akorinto 13:​4-8a, n’chiyani chingathandize anthu omwe ali ndi mavuto aakulu m’banja mwawo? (Onaninso chithunzi ndiponso bokosi lakuti “Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzigwirizana Kwambiri.”)

16 Ngati mwakumana ndi mavuto aakulu m’banja mwanu, musamafulumire kupatukana. (1 Akor. 7:​10, 11) M’malomwake muzidzifunsa kuti, ‘Ndingachite chiyani kuti tizigwirizana kwambiri?’ Muziphunzira zimene Baibulo limanena pa nkhani yosonyezana chikondi ndipo muziganizira zimene mungachite kuti muzisonyeza zimene zili pa 1 Akorinto 13:​4-8a. (Werengani.) M’malo moganiza zongothetsa banjalo, muziyesetsa kuchita zonse zomwe mungathe kuti muyambirenso kukondana. Muziganizira zimene inuyo mungachite kuti banja lanu liyambirenso kusangalala. Muzipempha Yehova kuti akutsogolereni. Muzifufuza malangizo m’mabuku athu, m’mavidiyo, kwa akulu ndiponso Akhristu olimba mwauzimu. Mukamadalira Yehova yemwe ndi chingwe cholimba komanso chachitatu pa “chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu,” banja lanu ‘silingaduke msanga.’—Mlal. 4:12.

Banja lija likukambirana zinthu kunyumba kwawo. Mkazi akulira kwinaku akufotokozera mwamuna wake mmene akumvera ndipo mwamunayo akumumvetsera mwachikondi atamugwira paphewa. Patebulo lomwe lili pambali pawo pali Baibulo lotsegula ndiponso kabuku kakuti “Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala.”

Muziyesetsa kuti musasiye kuchitira zinthu limodzi mukakumana ndi mavuto m’banja lanu (Onani ndime 16)


Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzigwirizana Kwambiri

Yehova amatipatsa zinthu zambiri zimene zimathandiza kuti anthu okwatirana azigwirizana kwambiri komanso kuti athetse mavuto amene ali nawo n’kuyambiranso kukondana. Kodi munayesapo kugwiritsa ntchito malangizo amene ali mu zinthu zotsatirazi?

  • Kabuku kakuti Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala

  • Mavidiyo akuti Mungatani Kuti Banja Lanu Lizisangalala

  • Nkhani zakuti “Mfundo Zothandiza Mabanja”

  • Nkhani za pa jw.org zakuti “Anthu Okwatirana Komanso Mabanja”

17. Kodi anthu amene akufuna kukwatira komanso amene ali m’banja angatani kuti azisangalala?

17 Yehova amafuna kuti atumiki ake onse azisangalala kuphatikizapo amene akufuna kukwatira komanso amene ali kale m’banja. Choncho ngati mukufuna kukwatira muzisankha mosamala munthu amene mukufuna kuti adzakhale mnzanu wa moyo wanu wonse. Ngati ndinu okwatira, pitirizani kuchita zinthu zimene zingathandize kuti muzigwirizana kwambiri. Muziyesetsa kulimbana ndi mavuto amene mungakumane nawo m’banja lanu ndipo muzidalira Yehova kuti akuthandizeni. Mukamachita zimenezi ‘mudzasangalala ndi moyo’ limodzi ndi mwamuna kapena mkazi wanu amene mumamukonda.—Mlal. 9:9.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Akhristu osakwatira angatani kuti asankhe munthu amene angadzakhale mnzawo wabwino kwa moyo wawo wonse?

  • N’chiyani chingathandize anthu okwatira kuti azigwirizana kwambiri?

  • N’chiyani chingathandize anthu okwatira kukhalabe limodzi akakumana ndi mavuto m’banja mwawo?

NYIMBO NA. 132 Tsopano Ndife Thupi Limodzi

a Mafunso otsatirawa angagwire ntchito kwa abale komanso alongo.

b Kuti mudziwe zimene zingakuthandizeni kumudziwa bwino mnzanuyo onani nkhani yakuti “Kodi Mungatani Kuti Chibwenzi Chanu Chiziyenda Bwino? mu Nsanja ya Olonda ya May 2024 pakamutu kakuti “Yesetsani Kuti Mudziwane Bwino.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena