MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muzimvetsa Mawu a M’Baibulo Oyerekezera Zinthu
M’Baibulo muli mawu ambiri omwe amayerekezera zinthu zina ndi zinazake. Komabe, anthu ambiri amene amawerenga Baibulo amavutika kuzimvetsa. (Mat. 13:13) Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzimvetsa bwino tanthauzo la mawu oyerekezera zinthu omwe ali m’Baibulo? Tayesani izi:
Pezani mfundo yaikulu komanso zimene akuyerekezerazo. Mwachitsanzo, lemba la Chivumbulutso 3:3 limayerekezera kubwera kwa Yesu (mfundo yaikulu) ndi kubwera kwa wakuba (mawu oyerekezera).
Ganizirani kufanana kwa mfundo yaikulu ndi zimene akuyerekezera. Pezani zifukwa zimene zikuchititsa kuti pakhale kufanana pakati pa mfundoyo ndi zomwe akuyerekezerazo.
Yesetsani kuti mumvetse zinthu molondola. Nthawi zina kufanana kwa mfundo yaikulu ndi zimene akuziyerekezera kungachititse munthu kumva zinthu molakwika. Mwachitsanzo, pa zimene tafotokoza zija, sikuti Yesu akubwera kudzaba zinthu ayi. M’malomwake, nkhani yonse ikusonyeza kuti kubwera kwa Yesu kukufanana ndi kubwera kwa wakuba m’njira yakuti adzabwera mosayembekezereka komanso sadzalengeza kuti akubwera.