Ndandanda ya Mlungu wa August 12
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 12
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 27 ndime 10-18 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Aroma 5–8 (Mph. 10)
Na. 1: Aroma 6:21–7:1-12 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Akhristu Ena Amapita Kumwamba Kukakhala ndi Khristu?—rs tsa. 217 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Kukonda Kwambiri Zinthu Zakuthupi Kuposa Zinthu Zauzimu Kumabweretsa Mavuto?—Mat. 6:33; 1 Tim. 6:10 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Mawu a Mulungu Ndi Opindulitsa pa Kuphunzitsa.” Mafunso ndi mayankho. Lengezani masiku a msonkhano wadera ngati akudziwika.
Mph. 10: Kodi Kukhala ndi Autilaini mu Utumiki N’kothandiza Bwanji? Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 167 ndime 1 mpaka 168, ndime 1. Pogwiritsa ntchito magazini yogawira mweziwo, sonyezani wofalitsa akulankhula yekha kwa mphindi zingapo pokonzekera zimene akanene mu utumiki.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Machitidwe 8:26-31. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki wathu.
Nyimbo Na. 61 ndi Pemphero