Zochitika mu Utumiki Wakumunda
“Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, . . . ndipo amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo.” (Aheb. 4:12) Mogwirizana ndi mawu amenewa, m’bale wina ali pamalo ake a bizinezi, analalikira Rasi wina. Kuchokera pa nthawi imeneyi, m’baleyu anapitiriza kukambirana ndi munthuyu za m’Baibulo. Kenako anamuitanira ku Nyumba ya Ufumu ndipo anabweradi. Abale anamulandira bwino mosaganizira mmene ankaonekera. Ulendo wotsatira umene munthuyu anabweranso ku Nyumba ya Ufumu, anali atavala bwino komanso atameta tsitsi lake. Tiyeni tipitirize kuthandiza anthu a mitundu yonse kuti adziwe choonadi molondola.—1 Tim. 2:4.