Ndandanda ya Mlungu wa June 24
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 24
Nyimbo Na. 63 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 25 ndime 1-7 ndi mabokosi patsamba 199 ndi 200 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 8–10 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Fotokozani Nkhani Imodzi, Koma Asiyireni Magazini Awiri.” Nkhani. Mukamaliza kukamba nkhaniyi, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro Loweruka loyamba la mwezi wa July, pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4. Kwa mphindi imodzi, fotokozani nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a July zimene anthu a m’gawo lanu angachite nazo chidwi.
Mph. 10: Ntchito Yathu Simapita Pachabe. (Aheb. 6:10) Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2013 tsamba 113 mpaka 115. Kambirananinso nkhani yakuti, Zochitika mu Utumiki Wakumunda. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Mph. 10: Mabuku Ogawira mu July ndi August. Nkhani yokambirana. Kambiranani mwachidule nkhani zimene zili m’timabuku tomwe tidzagawire m’miyezi imeneyi. Chitani chitsanzo cha mmene tingagawirire tiwiri mwa timabukuti. Chitsanzo chimodzi chikhale chogawira kabuku kakuti Uthenga wabwino pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chomwe chili patsamba 8 kapena chimodzi mwa zitsanzo za ulaliki zomwe zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2013.
Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero