Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/09 tsamba 2
  • Kugawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 7/09 tsamba 2

Kugawira Magazini

Mwezi uliwonse, Utumiki Wathu wa Ufumu umakhala ndi nkhani ya mutu wakuti: “Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani!” yomwe timakambirana pa Msonkhano wa Utumiki. Cholinga cha nkhani imeneyi n’kuthandiza ofalitsa kudziwa bwino nkhani zimene zili mu Nsanja ya Olonda yogawira ndiponso Galamukani! tisanayambe kugawira magaziniwa. Komabe, zikuoneka kuti ofalitsa akumagawira magaziniwa nthawi yake isanakwane, ndipo akumasowa oti abweretse pa Msonkhano wa Utumiki panthawi yokambirana nkhaniyi. Chifukwa cha zimenezi, cholinga cha nkhaniyi sichikukwaniritsidwa. Mwachitsanzo, tangokambirana kumene nkhani yokhudza kugawira Nsanja ya Olonda ya August 1 ndiponso Galamukani! ya August. Koma zikanakhala kuti magazini amenewa anagawiridwa kale mu utumiki wakumunda ndipo abale analibe magazini oti abweretse pamsonkhanowu, ndiye kuti nkhaniyi ikanakhala yopanda phindu.

Mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2008 munali chilengezo ichi: “Mipingo izipereka kwa ofalitsa magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akangofika. Zimenezi zidzathandiza kuti ofalitsa athe kudziwiratu bwino nkhani zimene zili m’magaziniwo asanawagawire mu utumiki wa kumunda.” Ngakhale kuti magazini akangofika, ena angaganize zogawira mu utumiki wakumunda nthawi yomweyo, koma ndi bwino kuti magazini a January azigawiridwa m’mwezi wa January, a February azigawiridwa mu February, chimodzimodzinso ndi miyezi ina. Choncho, ndi bwino kuti ofalitsa azisunga magaziniwo mpaka mwezi wake wogawira magaziniwo utafika. Zimenezi zidzathandiza kuti azikhala ndi magaziniwo pa Msonkhano wa Utumiki, pokambirana nkhani yakuti, “Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani!”

N’zoona kuti nthawi zina magazini a wofalitsa angathe chifukwa chakuti ndi wachangu mu utumiki wakumunda. Choncho, angachite bwino kugwiritsa ntchito magazini a miyezi ya m’mbuyomo kapenanso timabuku. Komabe, ngati woyang’anira utumiki ndiponso mtumiki wa magazini adziwiratu miyezi imene ofalitsa adzachite zochuluka muutumiki, monga kulembetsa upainiya wothandiza, ayenera kukonzekera bwino kuti padzakhale magazini okwanira. Ofalitsa angalimbikitsidwe kuwonjezera chiwerengero cha magazini amene amaodetsa ndipo mpingo ungaitanitse magazini mogwirizana ndi maodawo. Ngati dongosolo limeneli litatsatiridwa, abale adzakhala ndi magazini okwanira ndipo ‘zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.’—1 Akor. 14:40.

Ofalitsa akulimbikitsidwa kuti azibweretsa magazini amene adzagwiritse ntchito pokambirana nkhani yakuti, “Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani!”

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena