Ndandanda ya Mlungu wa July 20
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 20
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 22 ndime 15-22 ndi bokosi la patsamba 228
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 25-27
Na. 1: Levitiko 25:39-54
Na. 2: Chifukwa Chake Kuchita Zinthu Zabwino Kumavuta (lr-CN mutu 26)
Na. 3: Kodi Adamu Akanapanda Kuchimwa, Akanapita Kumwamba? (rs-CN tsa. 204 ndime 3 ndi 4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Kumanga Pamaziko a Khristu. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 278, ndime 1 mpaka 4.
Mph.10: Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi Galamukani! ya August. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili m’magaziniwo, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene akuona kuti zingasangalatse anthu a m’gawolo ndiponso chifukwa chake. Pemphani omvera kuti atchule mafunso amene angafunse poyamba kukambirana ndiponso atchule lemba limene angawerenge asanagawire magaziniyo. Pomaliza, chitani zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse.
Mph.10: “Kugawira Magazini.” Nkhani yokambirana ndi omvera, ikambidwe ndi woyang’anira utumiki.