Timalalikira Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino
Anthu padziko lonse lapansi masiku ano atopa ndi kumva uthenga woipa. Akatsegula wailesi, amamva nkhani zochititsa mantha zokhudza matenda oopsa komanso kuphulika kwa mabomba amene amawononga nyumba zambiri ndi kupha anthu ambirimbiri osalakwa. Tsiku ndi tsiku kukuchitika zinthu zoopsa, inde, zochitika padzikoli zikusintha ndipo zikuipiraipirabe. (1 Akor. 7:31) Kodi n’zotheka m’dziko loipa chonchi kupeza uthenga wabwino? Tiyeni tikambirane mafunso otsatirawa:
(1a) Kodi Yesaya anaufotokoza motani uthenga umene timalalikira? (1b) Kodi Yesu anadza motani ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, nanga atumiki amakono a Mulungu atengera motani chitsanzo cha Yesu? (Ndime 10-11) (2) Kodi anthu amene amalabadira uthenga wabwino wa Ufumu umawakhudza motani? (Ndime 12) (3) Kodi mneneri Yesaya anafotokoza motani madalitso amene anthu omwe akulabadira uthenga wabwino akupeza panopa? (Ndime 13) (4a) Kodi mawu akuti “ndikamange osweka mtima” akusonyeza chiyani za uthenga wa Ufumu? (4b) Kodi timasonyeza bwanji mmene Yehova amamvera akaona anthu osweka mtima?—Ndime 14.