Ndandanda ya Mlungu wa March 30
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 30
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 17, ndime 1-8
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Eksodo 1-6
Na. 1: Eksodo 1:1-19
Na. 2: Yesu Amatiphunzitsa Kupemphera (lr-CN mutu 12)
Na. 3: Kodi Ochiritsa Mozizwitsa Amasiku Ano Amathandizidwa ndi Mzimu wa Mulungu? (rs-CN tsa. 166 ndime 1-4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Phatikizanipo zilengezo zomaliza zokhudza Chikumbutso.
Mph. 15: Konzekerani Kuthandiza Anthu Achidwi Amene Adzapezeke pa Chikumbutso. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki yokumbutsa ofalitsa za udindo wawo wothandiza ophunzira Baibulo, ofalitsa amene anasiya kulalikira, ndi ena onse amene amabwera pa Chikumbutso, monga anzawo ndi achibale awo. (Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 2008, tsamba 8.) Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo ndi munthu wachidwi amene anabwera pa Chikumbutso. Kumbutsani onse kuwerenga malemba okonzekera Chikumbutso omwe akuyamba Lamlungu, pa April 5, ndipo mungafotokoze njira zothandiza zochitira zimenezi.
Mph. 15: “Timalalikira Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino.” Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2005, masamba 18-19, ndime 10-14. Mawu anu oyamba asafike mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.