Konzekerani Chikumbutso Mokwanira
Otsatira Khristu amasangalala kwambiri komanso amaona kuti ndi dalitso kukonzekera mokwanira tsiku lokumbukira imfa ya Yesu Khristu. (Luka 22:19) Kodi tingachite chiyani pokonzekera Chikumbutso?
◼ Nthawi ndi Malo: Aliyense ayenera kudziwa bwino nthawi komanso malo amene Chikumbutso chidzachitikire. Ngati mipingo ingapo idzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, ndi bwino kufika pa nthawi yake komanso kutuluka mwamsanga mukamaliza, chifukwa nthawi imakhala yochepa. Mudzaonetsetse kuti mwakonza dongosolo labwino kuti anthu asadzapanikizane pakhomo, panja kapenanso pamalo oimika magalimoto.
◼ Mapepala Oitanira Anthu: Kodi ofalitsa onse alandira mapepala awo ndi kuwawerenga bwinobwino? Kodi mwayeserera zimene munganene pogawira mapepalawa? Kodi mudzaitana ndani? Yesetsani mmene mungathere kuti mugawire mapepala onse oitanira anthu.
◼ Kayendedwe: Anthu ena achidwi komanso abale ndi alongo ena angafunikire thandizo la kayendedwe kapena lina lililonse. Kodi mwakonza zotani pofuna kudzathandiza anthu amenewa?
◼ Mkate ndi Vinyo: Mudzaonetsetse kuti mkate ndi vinyo zidzayendetsedwe dzuwa litalowa. Muyenera kukonza zoti zinthu zimenezi zikaperekedwe kwa wodzozedwa aliyense amene sadzatha kubwera chifukwa cha matenda kapena ukalamba. Muyeneranso kupeza mkate ndi vinyo woyenerera komanso mbale ndi matambula.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2003, masamba 14-15, ndime 14, 17.
◼ Nyumba ya Ufumu: Nyumbayi iyenera kuyeretsedwa bwinobwino pasadakhale. Mbale, matambula a vinyo, tebulo ndi nsalu yoyala patebulo, ziyenera kubweretsedwa ndi kuikidwa m’malo ake ku Nyumba ya Ufumu mwambowu usanayambe. Ngati mudzagwiritsira ntchito malo ena, mudzaonetsetse kuti muli ndi zokuzira mawu kuti aliyense wosonkhana adzathe kupindula. Muyenera kusankha akalinde ndi operekera mkate ndi vinyo pasadakhale ndiponso kuwauza ntchito yawo, dongosolo limene adzayenera kutsatira komanso kuti adzavale modzilemekeza.
Tonsefe, aliyense payekha komanso monga mpingo, tiyenera kukonzekera mokwanira mwambo wofunika kwambiri wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Khristu. Sitikukayikira kuti Yehova adzadalitsa anthu onse amene amasonyeza mtima woyamikira zonse zimene Yehova wachitira anthu kudzera mu nsembe ya Mwana wake wokondedwa, Yesu Khristu.