Ndandanda ya Mlungu wa March 9
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 9
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 15, ndime 14-23 ndi bokosi
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 40-42
Na. 1: Genesis 40:1-15
Na. 2: Tifunika Kukana Ziyeso (lr-CN mutu 9)
Na. 3: Samalani ndi Mzimu Wosafuna Kugonjera
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Pemphani wofalitsa mmodzi kapena awiri kuti afotokoze zimene anachita pogawira magazini komanso zotsatira zake.
Mph. 15: Pamene Ena Afunsa Chifukwa. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera, yochokera pakamutu kakang’ono patsamba 177 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene wofalitsa angayankhire mnzake wakuntchito kapena wakusukulu amene akufunsa za chikhulupiriro chathu. Wofalitsayo ayankhe ndi “mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.”—1 Pet. 3:15.
Mph. 15: “Konzekerani Chikumbutso Mokwanira.” Nkhani komanso kukambirana ndi omvera. Fotokozani mwachidule zimene mwakonza kwanuko zokhudza Chikumbutso.