Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira January 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Kambiranani bokosi lakuti “Kukumbutsa Zopereka Malipoti.”
Mph. 25: Pindulani ndi Makonzedwe Abwino. Nkhani yokambidwa ndi mkulu woyenera yozikidwa pa autilaini ya December 1, 2001 yochokera ku ofesi ya nthambi. Mpingo uyenera kukhala ndi mtokoma wokwanira wa zinthu zotsatirazi zoti mugaŵire ofalitsa: Khadi la Chidziŵitso kwa Madokotala/Chowamasula ku Mlandu ndi Khadi la Mwana. Ofalitsa obatizidwa alandira zinthu zimenezi lero tikamaliza msonkhano koma ASAZILEMBE lero. Makadiŵa adzasainidwa, kuikira umboni ndi kulembapo deti pamapeto pa Phunziro la Buku la Mpingo lotsatira ndipo amene afuna thandizo wochititsa phunziro la buku adzawathandiza. Osaina monga mboni ayenera kumuonadi mwinikhadilo akusaina. Ofalitsa osabatizidwa angalembe makadi awoawo oti azigwiritsa ntchito iwo ndi ana awo, mwa kukopera mawu a pakhadili ndi kuwasintha kuti agwirizane ndi mikhalidwe yawo komanso zikhulupiriro zawo.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo. Apempheni ofalitsa asimbe zimene akumana nazo pogwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, pogaŵira mabulosha ena kuti ayankhe mafunso a anthu, kapena powatonthoza mtima ndi Malemba otengedwa m’bulosha la Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Mungachite chitsanzo cha chokumana nacho chimodzi kapena ziŵiri.
Nyimbo Na. 55 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kambiranani bokosi lakuti ‘Muzipatulapo Kanthu.’
Mph. 13: Kodi Mukusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku? Banja likambirana. Pofuna kuwonjezera mapindu a makambirano awo a lemba la tsiku ndi tsiku, akukambirana Nsanja ya Olonda ya December 15, 1996, tsamba 18, ndime 13-14. Pendani mwachidule malemba a tsiku aŵiri kapena atatu amene munakambirana posachedwa, ndipo fotokozani mmene mfundo zake zinakuthandizirani. Gogomezani kuti pulogalamu yokhazikika ya phunziro la Baibulo la banja iyenera kuphatikizapo kusanthula Malemba tsiku ndi tsiku kumene cholinga chake ndi kuthandiza banja kukhala lachangu mwauzimu.
Mph. 22: “Ikanibe Ufumu Patsogolo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mafunso angapo pa mfundo zazikulu za mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1998, masamba 19-21.
Nyimbo Na. 168 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 28
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Akumbutseni ofalitsa kupereka malipoti a January a utumiki wa kumunda.
Mph. 15: “Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini.” Zitsanzo za mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya January 15 ndi Galamukani! ya January 8. Limbikitsani ofalitsa onse kupezeka Tsiku la Magazini.
Mph. 20: “Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambira Ukhanda Wawo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1998, tsamba 32. Afunseni makolo afotokoze mapindu amene apeza chifukwa chophunzitsa ana mwauzimu kuyambira ukhanda wawo.
Nyimbo Na. 202 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 4
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zili patsamba 8, sonyezani chitsanzo cha maulaliki aŵiri achidule a magazini, wina wa Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi wina wa Galamukani! ya January 8. Tchulani buku logaŵira m’February ndi kutchula mabuku omwe mpingo uli nawo.
Mph. 15: “Adzamva Bwanji?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Afunseni omvera anene mmene malembawo akugwirira ntchito. Phatikizanipo mafunso a ndime 17-18 patsamba 20 mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1998.
Mph. 20: “Maulaliki Amene Mungagwiritse Ntchito mu Utumiki wa Kumunda.” Kukambirana ndi omvera. Amene asamalire nkhaniyi ndi woyang’anira utumiki. Mphatika imeneyi ili ndi maulaliki owagwiritsa ntchito amene anatuluka m’makope a m’mbuyomu a Utumiki Wathu wa Ufumu, komanso ena ndi atsopano. Mizera yosalembapo kanthu mungaigwiritse ntchito kulembapo maulaliki ena amene angatuluke m’tsogolo amene angakhale ogwira mtima m’gawo lanu. Apempheni omvera anene maulaliki amene awakonda kwambiri ndi chimene awakondera. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki umodzi kapena aŵiri amene mungagwiritse ntchito limodzi ndi buku logaŵira mu February. Limbikitsani ofalitsa kusunga mphatika imeneyi ndiponso kuti aziigwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri pokonzekera utumiki.
Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.