“Adzamva Bwanji?”
1 Yesu ananena motsindika kuti: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Ngakhale kuti tayesetsa mwakhama, pali anthu ambirimbiri amene sanalalikidwepo. Maboma ena amaletsa ntchito yathu. M’mayiko ambiri muli anthu ochuluka ndipo chiŵerengero chawo chikukula mofulumira. Ndiye chifukwa chake pali funsoli lakuti, “adzamva bwanji?”—Aroma 10:14.
2 Khulupirirani Yehova: Tikumbukire kuti Yehova amadziŵa mtima wa munthu aliyense. Kaya moyo wake ndi wotani, koma ngati afunafuna choonadi cha Mulungu ndi mtima wonse, adzachipeza.—1 Mbiri 28:9.
3 Abrahamu anadera nkhaŵa anthu a m’Sodomu ndi Gomora. Koma Mulungu anam’tsimikizira kuti sadzawononga Sodomu ngati mutapezeka anthu olungama khumi. (Gen. 18:20, 23, 25, 32) Yehova sanawonongepo olungama limodzi ndi oipa. Kupulumuka kwa Loti ndi ana ake aakazi kunasonyeza zimenezi.—2 Pet. 2:6-9.
4 Nthaŵi ina Eliya anaganiza kuti ndi yekhayo amene anali kutumikira Mulungu woona. Koma Yehova anam’tsimikizira kuti sanali yekha ayi ndi kuti ntchito imene anali ataiyamba idzamalizidwa. (1 Maf. 19:14-18) Nanga bwanji za mmene zinthu zilili masiku ano?
5 Khalani Otanganidwa ndi Utumiki wa Mulungu: Sitikudziŵa kuti ntchito yathu yolalikira imene yatsala yoti tiichite n’njaikulu bwanji. Yehova ndiye mwini ntchito imeneyi ndipo akugwiritsa ntchito angelo kuiyang’anira. (Chiv. 14:6, 7) Iyeyo ndiye akudziŵa mlingo umene tiyenera kufikapo kuti ulaliki uperekedwe kwa anthu a mitundu yonse. Ngati Yehova akufuna, atha kuonetsetsa kuti uthenga wa Ufumu ukufalitsidwa mwa njira zimene sitikuzidziŵabe kuti anthu ambiri “amve mawu a Uthenga Wabwino, nakhulupire.” (Mac. 15:7) Zimene Yehova amachita zimagwirizana kwambiri ndi umunthu wake womwe ndi chikondi, nzeru ndi chilungamo.
6 Ndife odala kugwira ntchito mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova ndi kuchita zonse zotheka kuti aliyense amve uthenga wabwino.—1 Akor. 9:16.