Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira December 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Ngati mpingo uli ndi mabuku a Munthu Wamkulu kapena Mphunzitsi Wamkulu’yo m’sitoko, sonyezani mmene mabukuŵa angagwiritsidwire ntchito bwino mu utumiki panthaŵi yatchuti.
Mph. 15: “Opani Yehova Tsiku Lonse.” Phatikizanipo tanthauzo la kuopa Mulungu lopezeka mu Galamukani! ya January 8, 1998 patsamba 26. Gogomezerani mapindu akuopa Yehova. Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Chisonkhezero cha Mabwenzi ndi Mwayi Wanu Wolalikira.” Nkhani ndi kufunsa. Pemphani anthu amene anasonkhezeredwapo ndi mabwenzi kusimba chimene chinawathandiza kukhalabe achangu mu ntchito yolalikira mosasamala kanthu za zimenezo.
Nyimbo Na. 78 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 18
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Nenani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda pa December 25 ndi pa January 1. Yankhani funso lakuti: Kodi pali chiletso chilichonse chochita nawo mapwando amene angakhale achikunja malinga ngati sakuchitidwira zifukwa zachipembedzo?—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 241-243.
Mph. 12: “Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2001.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Limbikitsani onse kuyendera limodzi ndi ndandanda yawo yoŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu ndiponso kuyesetsa kukwaniritsa zimene apatsidwa m’sukulu.
Mph. 18: “Kodi Mumalalikira Molimba Mtima?” Funsani ndemanga pa malemba a m’nkhaniyi. Gwiritsani ntchito buku la Uminisitala Wathu, tsamba 86 kusonyeza mmene tingakhalire olimba mtima zedi ndiponso ogwira mtima mu utumiki wakumunda. Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 124 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 25
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pemphani omvetsera kusimba zilizonse zimene akumana nazo posachedwapa mu ntchito yawo yochitira umboni. Pendani mabuku ogaŵira m’January.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: “Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe m’Choonadi. Mbali Yachinayi: Mwa Kugonjetsa Zolepheretsa.” Woyang’anira utumiki akambirane ndi bambo papulatifomu. Bambo apereke zifukwa zimene sachitira phunziro la banja. Woyang’anira utumiki agwiritse ntchito mfundo za m’nkhaniyi zogonjetsera zolepheretsa. Kambani zolepheretsa zinayi zotchulidwa m’ndime 2 mpaka 5. Gogomezerani mmene kukonda ana kudzathandizira makolo kuyesetsa kwambiri, monga momwe ikufotokozera ndime 6.
Nyimbo Na. 151 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 1
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Ngati mpingo wanu usinthe nthaŵi za misonkhano m’chaka chatsopano, limbikitsani onse mokoma mtima kumapezekabe pamisonkhano mosaphonya nthaŵi zatsopanozo. Dziŵitsani ophunzira Baibulo ndi anthu ena achidwi za kusintha kulikonse. Thirirani ndemanga pa lipoti la utumiki wakumunda la September la dzikolo ndi la mpingowo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a December.
Mph. 15: Mmene Tingakonzekerere Maulendo Obwereza. Bambo akambirane ndi banja lake mmene angakhalire obala zipatso kwambiri mu utumiki wawo. Agogomezere zifukwa za m’Malemba zopitira konse kumene anthu asonyeza chidwi. Mogwiritsa ntchito malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999 patsamba 22 ndime 18, banjalo likonzekere kupanga maulendo ena obwereza. Onse akuvomereza kuti anapeza anthu amene akufunika kukawafikiranso. Aliyense afotokoze chidwi chimene anapeza paulendo woyamba, ndipo ena a m’banjalo apereke malingaliro ndi lemba lofunika kugwiritsa ntchito paulendo wobwereza. Apeze mfundo mu bulosha la Mulungu Amafunanji zimene zingagwiritsidwe ntchito mogwira mtima. Makolowo auze mwana mmodzi kuyeserera zimene akanena paulendo wake wobwereza. Kenako akonze nthaŵi yeniyeni yopanga maulendo obwereza mlungu winawo.
Mph. 25: “Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 212 ndi pemphero lomaliza.