Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/00 tsamba 2
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 12/00 tsamba 2

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu December: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena lililonse la mabuku a masamba 192 lomwe mpingo ungakhale nalo. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kufunsira mabaundi voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 2000 pofunsira mabuku awo a December. Mabaundi voliyumuwa adzakhalapo m’Chingelezi. Mpaka pamene mabaundi voliyumu adzakhalapo ndi kutumizidwa, adzaonekera monga “Zoyembekezera” pa mpambo wolongedzera mabuku wa mipingo. Mabaundi voliyumu ndi zinthu zofunsira mwapadera.

◼ Chikumbutso cha chaka cha 2002 chidzakhalako Lachinayi, March 28, dzuŵa litaloŵa. Taneneratu zimenezi kuti abale apangiretu makonzedwe ofunikira ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo ikufunikiradi kupeza malo ena. Akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti chochitikachi chisadzadodometsedwe ndi zochitika zina za pamalowo kuti Chikumbutsocho chidzachitike mwamtendere ndi mwadongosolo. Popeza kuti chochitikacho n’chapadera, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mkulu yemwe alidi woyenerera, osati kumangosinthana kapena kuti chaka chilichonse azingokamba mbale mmodzimodzi yemweyo. Zingatero pokhapokha ngati pali wodzozedwa amene ali mkulu komanso angathe kukamba nkhaniyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena