Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 15: “Timalalikira Uthenga Wabwino.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndipo kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Perekani mfundo zogwira mtima za m’Malemba zimene zingatchulidwe kuchokera m’buku la Chidziŵitso pamene mukugaŵira bukuli mu utumiki.
Mph. 20: “Kodi Tingapange Mwezi wa April 2000 Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?” (Ndime 1-11) Mafunso ndi mayankho. Tchulani chiŵerengero chapamwamba cha apainiya othandiza amene anali mumpingomo m’mbuyomo. Funsani ena mwa amene alimo m’chiŵerengero chimenechi kuti asimbe mapindu amene anapeza mwa kuwonjezera utumiki wawo. Limbikitsani mpingo kugwira ntchito ndi cholinga chofuna kukwanitsa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha apainiya othandiza m’April. Pendani ziyeneretso zoperekedwa m’buku la Olinganizidwa, masamba 113-14. Ofalitsa amene akufuna kuchita upainiya wothandiza angatenge fomu yofunsira upainiyawo pamapeto a msonkhano.
Nyimbo Na. 187 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 20
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Kodi Ndingatani?” Wochititsa phunziro la buku akambirane nkhaniyi ndi mtumiki wotumikira mmodzi kapena aŵiri. Chifukwa cha zopinga zosiyanasiyana, ofalitsa ena angaone kuti amachita zochepa pochirikiza ntchito ya mpingo. Pendani zina mwa njira zambiri zimene tonsefe zingatithandize mwapadera polimbitsa mpingo ndi kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu. Malizani mwa kusonyeza mmene aliyense ‘Angakhalire Ndi Phande M’Lipoti Lotsiriza.’—Onani Olinganizidwa, masamba 108-10.
Mph. 20: “Kodi Tingapange Mwezi wa April 2000 Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?” (Ndime 12-18) Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo chachidule cha mmene tingaitanire mnzathu ku Chikumbutso. Pendani mwezi wa April pa Kalendala ya 2000, ndipo fotokozani ndandanda ya misonkhano yokonzekera utumiki imene yakonzedwa pampingopo. Kumbutsani aliyense kupanga ndandanda yotsatirika yoti aziloŵa nawo mu utumiki m’mene angathere m’mwezi umenewu, ndi cholinga chakuti aliyense mu mpingo atengemo mbali. Limbikitsani onse amene angathe kuchita upainiya wothandiza atenge fomu yofunsira upainiya pamapeto pa msonkhano.
Nyimbo Na. 65 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 27
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo autumiki wakumunda a March. Lengezani mayina a anthu amene adzachite upainiya wothandiza m’April. Fotokozani kuti sikuchedwa kupereka fomu yofunsira upainiya pakalipano. Longosolani ndandanda yonse ya misonkhano yomwe yakonzedwa m’mwezi umenewu yokonzekera utumiki wakumunda. Limbikitsani onse kutenga mbali mu utumiki mapeto a mlungu uno, tikumayamba mwezi wa April mwa kuloŵa nawo mu utumiki. Tidzagaŵira makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! m’mwezi umenewu. Gogomezerani nkhani imodzi ndi mfundo yofunika kwambiri imene ingagwiritsidwe ntchito mogwira mtima mu ulaliki m’kope lililonse la makope atsopano. Aliyense ayenera kukhala ndi bulosha la Mulungu Amafunanji ndi kuyesetsa kuyambitsa nalo maphunziro a Baibulo ndi anthu ochita chidwi.
Mph. 13: “Pemphani Thandizo.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera kochitidwa ndi mkulu. Fotokozani mmene tonsefe timafunikira thandizo linalake nthaŵi ndi nthaŵi. Ndi zoona kuti aliyense adzasenza katundu wake wa iye mwini. (Agal. 6:5) Komabe, pamene tikulephera kugonjetsa vutolo. sitiyenera kuchedwa kupempha thandizo kwa anthu achikulire mwauzimu mu mpingo. Pemphani omvetsera kusimba zimene zinawachitikira zosonyeza mmene thandizo lachikondi la ena linawalimbikitsira.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 12: “Tidzaphunzira Buku la Chimwemwe cha Banja.” Mafunso ndi mayankho. Mwachidule nenani mmene tidzapindulira mwa kuphunzira bukuli. Limbikitsani onse kupezeka pa Phunziro la Buku la Mpingo nthaŵi zonse.
Nyimbo Na. 195 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 3
Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi zokumana nazo za mu utumiki. Gwiritsani ntchito zokumana nazo za posachedwapa za m’gawo lanu zimene zidzalimbikitsa ena kutenga mbali mu utumiki wakumunda.
Mph. 17: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2000 Wakuti ‘Akuchita Mawu a Mulungu.’” Mlembi akambe nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Gogomezerani kufunika kwakuti aliyense akonzeretu masiku okwanira nthaŵi ikadalipo kuti adzakhale patchuthi ndi kudzapezeka patsiku lililonse la msonkhano ndi Lachisanu lomwe. Yamikirani abale potsatira malangizo a Sosaite.
Mph. 18: Kodi Ndiyenera Kuulula Tchimo Lalikulu? Nkhani yofunika yokambidwa ndi mkulu, yokhudza achinyamata. Pabuka mavuto ambiri m’chitaganya chamakonochi amene akuwononga kwambiri achinyamata: kukana miyezo ya makhalidwe abwino, kuchuluka kwa chiwawa, kulowerera ndi mankhwala osokoneza bongo, ndiponso kusapereka ulemu kwa anthu aulamuliro. Achinyamata ena amakhala ndi moyo wachiphamaso, akumabisa makhalidwe awo oipa. Zimenezi zingasokoneze moyo wauzimu wa mpingo wonse. Ena amachita tchimo lalikulu n’kulibisa. Ngati mwadziŵa kuti mbale kapena mlongo mu mpingo wachita chinachake chimene chili cholakwira kwambiri lamulo la Mulungu, kodi muyenera kuchitanji? Pendani mfundo yachikhalidwe ya pa Levitiko 5:1. (Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1997, masamba 27-30.) Onaninso buku la Achichepere Akufunsa masamba 68-9 ndipo fotokozani zimene munthu ayenera kuchita m’mkhalidwe woterewu.
Nyimbo Na. 68 ndi pemphero lomaliza.