Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/00 tsamba 1
  • ‘Kodi Ndingatani?’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kodi Ndingatani?’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Muzithandiza Mpingo Wanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kudzipereka Ife Eni Mwaufulu Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kodi Tingathandize Bwanji Kulimbitsa Mgwirizano Wathu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Mpingo Uyenera Kulimbikitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 3/00 tsamba 1

‘Kodi Ndingatani?’

1 ‘Kodi ndingatani?’ Mosakayikira, funso limeneli n’lomwe linali m’maganizo a mamembala a m’kagulu kakang’ono ka ophunzira Baibulo kolinganizidwa ndi Charles Taze Russell cha m’ma 1870. Pamene anali kupita patsogolo m’kamvedwe kawo ka chifuno cha Mulungu, ophunzira Baibulo oyamba amenewo ayenera kuti anali kudzifunsa zimene angachite kuti athandize ena kuphunzira za chifuno cha Mulungu. Mwachiwonekere, inali ntchito yaikulu kwambiri kuti afalitse padziko lonse chidziŵitso cha Baibulo chimene anali kupeza.

2 Chosangalatsa kwa ife n’chakuti, anagonjetsa vuto limenelo. Motani? Munthu aliyense anachita mbali yake ngakhale yooneka ngati yaing’ono, kotero kuti lerolino Mboni za Yehova zikudziŵika padziko lonse—gulu la ofalitsa Ufumu pafupifupi 6 miliyoni amene akutumikira m’mipingo 90,000 m’mayiko 234 ndi m’zilumba za m’nyanja!—Yes. 60:22.

3 Chirikizani Mmene Mungathere: N’kofunika kuti aliyense wa ife atengeko mbali m’ntchito yaikulu imene Yesu ananeneratu kuti idzachitika m’masiku otsiriza ano. (Marko 10:13) Kunena zoona, ntchito imeneyi singasiyidwire chiŵerengero chochepa cha akulu okha basi; kapena kuti ntchito yolalikira si ya apainiya okha ayi. Kwenikweni, Mkristu aliyense wodzipatulira ali ndi mbali yofunika yoti achite. Tonsefe tingachite nawo mbali iliyonse ya ntchito yolalikira. (1 Tim. 1:12) Ku mlingo uliwonse umene timachita zimenezi, timapindula tokha komanso kupindulitsa ena.—1 Tim 4:16.

4 Aliyense wa ife angachirikize ubale wathu wachikristu m’njira zinanso zambiri. Tingachirikize misonkhano yampingo mwa kupezekapo nthaŵi zonse ndiponso mwa kutengamo mbali mwachangu. (Sal. 122:1, 8, 9) Tingachite mbali yathu kuti tisunge mpingo uli woyera mwa makhalidwe. Tingachirikize ndi ndalama ku ntchito yapadziko lonse, malinga n’kupeza kwathu. Tingagwire nawo ntchito yoyeretsa Nyumba ya Ufumu. Aliyense angachirikize mzimu wabwino wachikondi ndi umodzi mu mpingo mwa kuthandiza achatsopano, achinyamata, ndi achikulire omwe.—Akol. 3:12, 14.

5 Chotero mungafunse kuti, ‘Kodi Ndingatani?’ Ngakhale khama lanu likhale lochepa, mwa kuchita mbali yanu, mungathandize mpingo kukhala wolimba, wachangu, ndi wamphamvu. Motero tonsefe tili ndi mbali yofunika polemekeza dzina la Yehova!

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena