Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/98 tsamba 9-10
  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Timitu
  • Yankhani mafunso otsatirawa:
  • Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
  • Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
  • Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa: Miy. 17:27; Mlal. 9:11; Mat. 10:16; Mac. 10:34, 35; 2 Akor. 4:18
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 4/98 tsamba 9-10

Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa January 5 kufikira April 20, 1998. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa. [Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Pa Machitidwe 15:29, NW, mawu akuti, “Thanzi labwino kwa inu!,” anali lonjezo lakuti, ‘Ngati mupeŵa mwazi ndi dama, mudzakhala ndi thanzi labwino.’ [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 6/15 tsa. 9 ndime 7, mawu a mtsinde.]

2. Akristu alibe udindo wosamalira makolo awo okalamba. [gt-CN mutu 126]

3. Aigupto ankaona Farao monga Horus weniweni wobadwanso m’thupi, mulungu wokhala ndi mutu wa mphamba. [w96-CN 1/15 tsa. 24 ndime 1]

4. Liwu lakuti “Simony,” lomwe linayambira pa zochitika zolembedwa pa Machitidwe 8:9-24, limatanthauza kuchita matsenga. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 6/1 tsa. 17 ndime 8.]

5. Pa Aroma 8:6, 7, “thupi” ndilo mkhalidwe wochimwa wa anthu opanda ungwiro, uchimo wobadwa nawo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 3/1 tsa. 21 ndime 4.]

6. Popeza kuti patapita nthaŵi Yehova anayamba kulandira nsembe za ufa ndi zipatso zina za m’nthaka, nsembe ya Kaini anaikana mwachionekere chifukwa mtima wake unali woipa. (Gen. 4:3-5) [w96-CN 6/15 tsa. 4 ndime 8]

7. Mmene Mkristu akugwiritsira ntchito m’moyo wake malamulo a Baibulo ophunzitsa khalidwe ndi owongolera uzimu wake, wasambitsidwa ndi Mawu a Yehova, “wayeretsedwa” pa zinthu zonse zimene Yehova Mulungu amadana nazo. (1 Akor. 6:9-11) [w96-CN 1/1 tsa. 30 ndime 4]

8. Mtumwi Paulo mwiniyo ndiye anabatiza a pabanja la Stefana ku Korinto. [w96-CN 6/15 tsa. 29 ndime 2]

9. Pa Machitidwe 20:20, mawu akuti “m’nyumba m’nyumba” amatanthauza maulendo akuŵeta basi m’nyumba za okhulupirira anzathu chifukwa nkhani yake ikusonyeza kuti Paulo ankalankhula ndi akulu a mpingo. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 1/15 tsa. 11 ndime 5.]

10. Tikamaphunzitsa mtima wathu kukonda zinthu zauzimu, tikumapempherera mzimu wa Mulungu kuti utithandize pa zimenezi, ndiye kuti tidzapeŵa “nkhaŵa za thupi.” (Aroma 8:6, 7, NW) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 3/1 tsa. 21 ndime 5.]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Kodi nchochitika chiti m’buku la Machitidwe chimene chimasonyeza kuti kungokhala nawo Mawu a Mulungu nkumawaŵerenga si kokwanira kuti munthu apeze chidziŵitso cholongosoka chomtsogolera panjira ya ku moyo? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 9/1 tsa. 19 ndime 16.]

12. Kodi nchiyani chimatiletsa kuweruza abale athu mowasuliza? [w96-CN 3/15 tsa. 22 ndime 5]

13. Kodi nchifukwa chiyani kuti pa Machitidwe 11:26 New World Translation imanena kuti “anayamba kutchedwa Akristu ‘motsogozedwa ndi Mulungu,’ pomwe mabaibulo ena samaphatikizapo lingaliro la “kutsogozedwa ndi Mulungu?” [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 6/1 tsa. 19 ndime 19.]

14. Kodi nchiyani chidzathandiza mkazi wachikristu kulemekeza kwambiri mwamuna wake? (Aef. 5:33) [w96-CN 3/1 tsa. 21 ndime 5]

15. Kodi nchifukwa chiyani Akristu ayenera kukhalabe odekha mtima pamavuto? (Yoh. 19:8-10) [gt-CN mutu 123]

16. Kodi ndi makalata asanu ati amene Paulo analemba ali m’ndende ku Roma? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 5/15 tsa. 26.]

17. Malinga ndi Aroma 12:2, kodi mphamvu ya Mawu a Mulungu imasintha maumunthu a Akristu mpaka pamlingo wotani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 4/1 tsa. 16 ndime 3.]

18. Kodi “chinsinsi” chimene Paulo anatchula pa Aroma 11:25 nchiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/1 tsa. 15 ndime 16.]

19. Kodi nchifukwa chiyani kusali kulakwa pamene mpingo wachikristu uchotsa mumpingo ochimwa osalapa? (1 Akor. 5:11, 13) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g96-CN 9/8 tsa. 29 ndime 2, 3.]

20. Kodi nchifukwa chiyani Paulo anafunitsitsa kupita ku Roma? (Aroma 1:11, 12) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 8/1 tsa. 23.]

Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Malinga ndi Aroma 13:1, olamulira a dziko alipo mwa ․․․․․․․․ ndi Mulungu chabe. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 8/1 tsa. 24.]

22. Anthu a ku Korinto anasonyeza chidwi kwambiri moti Paulo anakhalabe mumzinda umenewo kwa ․․․․․․․․ [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 5/15 tsa. 25.]

23. Mkhalidwe wa ․․․․․․․․ umatithandiza ‘kuyesa ena monga otiposa,’ pamene ․․․․․․․․ kumatithandiza ‘kuleza mtima.’ (Afil. 2:3; 2 Tim. 2:24, 25) [w96-CN 5/15 tsa. 21 ndime 5]

24. Malinga ndi fanizo la Paulo la mtengo wa azitona pa Aroma chaputala 11, monga momwe mafuko 12 a Israyeli anachokera kwa Abrahamu kupyolera mwa Isake, momwenso mafuko 12 ophiphiritsira a ․․․․․․․․ achokera kwa ․․․․․․․․ kupyolera mwa ․․․․․․․․. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/1 tsa. 15 ndime 15.]

25. Monga mmene Yehova anachirikizira Aisrayeli pachigono chawo m’Chipululu cha ․․․․․․․․, ifenso angatichirikize ․․․․․․․․. [w96-CN 8/15 tsa. 7 ndime 1-2]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Yesu atampachika, anampatsa vinyo wokhala ndi mure, koma anakana kumwa chifukwa (lamulo linaletsa; anali m’Naziri; anafuna kukhala ndi nzeru zake zonse). [gt-CN mutu 125]

27. (Paulo; Petro; Luka) anatamanda anthu a ku (Bereya; Makedoniya; Yerusalemu), nawatcha “mfulu.” (Mac. 17:11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 5/1 tsa. 14 ndime 3.]

28. Bodza, kapena chinyengo chotchulidwa pa Aroma 1:25 chikutanthauza (kulambira mafano; chisembwere; kunena bodza). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w91-CN 11/15 tsa. 6 ndime 6.]

29. (Anthu, Mulungu ndi Kristu; Satana ndi ziŵanda) ndiwo oyenera kuimbidwa mlandu zinthu zikalakwika. [w96-CN 9/1 tsa. 5 ndime 3]

30. (Herode; Pilato; Felike), analengeza kasanu konse kuti Yesu analibe mlandu, komabe anadzagonjera Ayuda pakuumirira kwawo ndipo anampereka Yesu kuti akapachikidwe. [gt-CN 124]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa: Miy. 17:27; Mlal. 9:11; Mat. 10:16; Mac. 10:34, 35; 2 Akor. 4:18

31. Ifeyo monga atumiki a Yehova, tiyenera kumaona anthu a mafuko ena monga mmene iye amawaonera. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 5/15 tsa. 16 ndime 6.]

32. Tisamasamale mikhalidwe yathu yaleroyi, koma tisumikebe maso athu pa zinthu zosangalatsa za njira yachikristu. [w96-CN 2/15 tsa. 27 ndime 3-4]

33. Kuzindikira ndi chikondi cha pa abale zidzatithandiza kudziletsa kunena mawu ovulaza. [w96-CN 5/15 tsa. 22 ndime 7]

34. Pokumana ndi chizunzo, Akristu oona afunikira kukhala ochenjera ndi oona mtima polengeza uthenga wa Ufumu kwa ena. [w96-CN 7/15 tsa. 22 ndime 4]

35. Palibe chifukwa chokhulupirira kuti Mlengi ndiye amachititsa ngozi kapena kuti anthu ovulala pangozi akulangidwa mwa njira ina. [w96-CN 9/1 tsa. 5 ndime 4]

S-97-CN Mal, Moz & Zam #294b 4/98

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena