Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/98 tsamba 11
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 4/98 tsamba 11

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! June: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, kapena buku lililonse la masamba 192. July ndi August: Mungagwiritsire ntchito lililonse la mabrosha otsatirawa a masamba 32: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, ndi Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Mabrosha akuti Buku la Anthu Onse, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Our Prolems—Who Will Help Us Solve Them?, ndi Will There Ever Be a World Without War? mungawagaŵire pamene kuli koyenera.

◼ Pogwira ntchito m’gawo losagaŵiridwa, ofalitsa angagaŵire buku la Chidziŵitso ndi brosha la Mulungu Amafunanji. Angagaŵire zofalitsa zina zilizonse ngati mwini nyumba ali nazo kale zofalitsa ziŵirizi. Onse ayenera kunyamula matrakiti osiyanasiyana okasiya panyumba popanda anthu kapena opatsa anthu amene sangalandire mabuku. Uthenga wa Ufumu Na. 35 uliwonse umene ofalitsa kapena mipingo ingakhale nawo uyenera kugaŵiridwa kwa eni nyumba. Ayenera kuchita khama kubwerera kwa amene anachita chidwi, makamaka ngati amene akugwira ntchito m’magawo osagaŵiridwa ali apainiya apadera kapena ngati magawowo ali pafupi ndi mipingo.

◼ Pokhala ndi mawikendi asanu athunthu, mwezi wa May uli nthaŵi yoyenera yakuti ambiri achite upainiya wothandiza.

◼ Watchtower Library ya 1997 pa CD-ROM yakonzedwa m’Chingelezi. Zofalitsa zikuyambira mu 1970 (Watchtower ikuyambira mu 1950). Mipingo ingayambe kutumiza maoda a Watchtower Library—1997.

◼ Ngati mpingo wanu ukuyesetsa kukonza akaunti yoipa ya mabuku komanso mukufuna kuoda mabuku angapo, chonde tsatirani njira iyi: Tumizani ku Sosaite (1) ndalama za zimene mukufuna kuoda, (2) fomu ya S-20, ndi (3) fomu ya Literature Request (S-14). Pamwamba pa S-14 lembanipo mawu akuti CWO (Cash With Order). Pamzere wa mabuku pa S-20 lembanipo unyinji wa ndalama zomwe mukutumiza. Ngati zinthu zomwe mwaoda mulibe m’sitoko, ndiye kuti ndalama yanu idzachotsedwa ku ngongole yanu ya mabuku.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zomwe Zilipo:

Buku la Anthu Onse—Chichewa

Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha—Chingelezi

◼ Makompakiti Disiki Atsopano Omwe Alipo:

Kingdom Melodies, Voliyumu 1

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2026 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena